Rahabi—Anayesedwa Wolungama ndi Ntchito za Chikhulupiriro
TANGOYEREKEZERANI! Mkazi wadama anayesedwa wolungama m’lingaliro la Mulungu. “Kutalitali!” ambiri angatero. Komabe, zimenezo nzimene zinachitika kwa hulelo Rahabi wa ku Yeriko, mzinda wakale wa Akanani.
Wolemba Baibulo Yakobo akusimba kuti: “Munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha. Ndipo momwemonso sanayesedwa wolungama Rahabi mkazi wa damayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira ina? Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.” (Yakobo 2:24-26) Kodi nchifukwa ninji Rahabi anayesedwa wolungama? Kodi anachitanji kuti apatsidwe mwaŵi wa kaimidwe kolandirika kwa Mulungu?
Aisrayeli Akudza!
Tiyeni tibwerere kumbuyo m’chaka cha 1473 B.C.E. Yerekezerani mkhalidwewo. Yeriko ngwotetezeredwa kwambiri ndi malinga. Pamwamba pa malinga a mzindawo pali nyumba ya Rahabi wadamayo. Ali pamwamba pamenepa, iye mwinamwake akhoza kuyang’ana chakummwaŵa kumtsinje wa Yordano wa madzi osefukira. (Yoswa 3:15) Mmphepete cha kummaŵa kwa mtsinjewo, mwina iye akuona chigono cha Aisrayeli, chokhala ndi gulu la ankhondo oposa 600,000. Iwo ali pamtunda wa makilomita angapo chabe!
Rahabi wamva za zipambano za Israyeli m’nkhondo. Iye wamvanso za kusonyezedwa kwa mphamvu ya Yehova, makamaka pakutsegulira Israyeli njira yopulumukira pa Nyanja Yofiira. Pamenepo, ndithudi, madzi osefukira a Yordano sadzakhala chopinga. Imeneyi ndinthaŵi ya mavuto! Kodi Rahabi adzachita motani?
Rahabi Asankha
Posapita nthaŵi, Rahabi akulandira alendo aŵiri amene afika mwadzidzidzi—azondi ochokera kuchigono cha Aisrayeli. Iwo akufunafuna malo ogona, ndipo akuwaloŵetsa m’nyumba mwake. Koma mbiri ya kukhalapo kwawoko yafika kwa mfumu ya Yeriko. Nthaŵi yomweyo iyo ikutuma adindo ake osungitsa lamulo kukawagwira.—Yoswa 2:1, 2.
Pamene adindo a mfumu akufika, Rahabi wasankha kuima kumbali ya Yehova Mulungu. “Tulutsa amunawo anafika kwanu,” adindo a mfumuwo akulamula motero. Rahabi wabisa azondiwo pakati pa mitengo ya nthamza yoyanikidwa patsindwi la nyumba yake. Iye akuti: “Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziŵa uko afuma; ndipo mmene akadati atseke pachipata [cha mzinda], kutada, anatuluka amunawo; uko anamuka amunawo osakudziŵa ine; muwalondole msanga, pakuti mudzawapeza.” (Yoswa 2:3-5) Amuna a mfumuwo akuchita zimenezo—mosaphula kanthu.
Rahabi wasocheza adaniwo. Nthaŵi yomweyo akuchita kanthu kenanso kamene kakusonyeza chikhulupiriro chake mwa Yehova ndi ntchito. Akukwera patsindwi nauza azondiwo kuti: “Ndidziŵa kuti Yehova wakupatsani dzikoli.” Rahabi akuvomereza kuti nzika zonse za dzikolo zili ndi mantha chifukwa chakuti zamva kuti Mulungu “anaphwetsa madzi a m’Nyanja Yofiira” pamaso pa Aisrayeli zaka 40 pasadakhale. Anthuwo akudziŵanso kuti Aisrayeli anawononga mafumu aŵiri a Aamori. “Ndipo titamva ichi,” Rahabi akutero, “mitima yathu inasungunuka; analibenso mtima ndi mmodzi yense, chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa m’mwamba umo, ndi padziko lapansi.”—Yoswa 2:8-11.
Rahabi akuchonderera kuti: “Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakuchitirani chifundo, kuti inunso mudzachitira chifundo a m’nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa chizindikiro chowona, kuti mudzawasunga ndi moyo atate wanga ndi mayi wanga, ndi alongo anga ndi abale anga, ndi zonse ali nazo.”—Yoswa 2:12, 13.
Amunawo akuvomereza nauza Rahabi zimene ati achite. Pazenera lake, iye ayenera kulenjekapo chingwe chofiira chimene watsitsira azondiwo kunja kwa malinga a Yeriko. Ayenera kusonkhanitsira abale ake m’nyumba mwake, mmene ayenera kukhala kuti atetezeredwe. Rahabi akuuza azondi amene akuchokawo chidziŵitso chothandiza cha malo a dzikolo ndipo akuwauza mmene angazembere amene akuwafunafunawo. Azondiwo akuchita zimenezi. Atamangirira chingwe chofiiracho ndi kusonkhanitsa abale ake, Rahabi akuyembekezera zochitika zina.—Yoswa 2:14-24.
Kodi nchiyani chimene Rahabi wachita? Aha, wasonyezadi kuti waika chikhulupiriro chake mwa Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova! Adzakhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo yake. Inde, ndipo adzayesedwa wolungama chifukwa cha ntchito zotero za chikhulupiriro.
Malinga Akugwa!
Milungu ingapo yapita. Atatsagana ndi ansembe—ena okhala ndi mphalasa za nyanga za nkhosa ndipo ena atanyamula likasa lopatulika la chipangano—amuna ankhondo Achiisrayeli akuzungulira Yeriko. Iwo akhala akuchita zimenezi kamodzi patsiku kwa masiku asanu ndi limodzi tsopano. Komabe, patsiku lachisanu ndi chiŵirili, aguba mozungulira mzindawo kasanu ndi kamodzi. Akuzunguliranso!
Kuzungulira kwachisanu ndi chiŵiri kwatha, kulira kwa mphalasa kwanthaŵi yaitali kukumveka. Ndiyeno Aisrayeliwo akufuula ndi mfuu yamphamvu. Pamenepo, Yehova akuchititsa malinga otetezera a Yeriko kugwa ndi mkokomo waukulu. Chigawo chokha chimene chikuchirikiza nyumba ya Rahabi chikutsalira. Mzinda wonsewo ndi okhalamo ake awonongedwa. Chikhulupiriro chake chitasonyezedwa ndi ntchito, mkazi wadama wolapayo akupulumutsidwa limodzi ndi banja lake, ndipo akuyamba kukhala pakati pa anthu a Yehova.—Yoswa 6:1-25.
Kupenda Mikhalidwe ya Rahabi
Rahabi sanali mlesi, pakuti patsindwi pa nyumba yake panali mitengo ya nthamza imene inayanikidwa padzuŵa. Ulusi wa nthamza ukagwiritsiridwa ntchito kuombera nsalu. M’nyumba mwa Rahabi munalinso mulu wa chingwe chofiira. (Yoswa 2:6, 18) Chotero iye mwina anali kuwomba nsalu ndipo mwinamwakenso anali mmisiri wonika nsalu. Inde, Rahabi anali mkazi wokangalika. Koposa zonsezo, anafikira pakukhala ndi mantha aulemu pa Yehova.—Yerekezerani ndi Miyambo 31:13, 19, 21, 22, 30.
Bwanji za ntchito inayo ya Rahabi? Iyetu sanali konse mkazi wolandira anthu wamba panyumba ya alendo. Ayi, Malemba amamdziŵikitsa mwa kugwiritsira ntchito mawu Achihebri ndi Achigiriki otanthauza munthu wadama. Mwachitsanzo, liwu Lachihebri lakuti zoh·nahʹ nthaŵi zonse nlogwirizanitsidwa ndi maunansi a kugonana kosaloledwa. Kunena zowona, pakati pa Akanani kuchita dama sikunali malonda oipa.
Kugwiritsira ntchito kwa Yehova mkazi wadama kumasonyeza chifundo chake chachikulu. Kaonekedwe ka kunja kangatinyenge, koma Mulungu “ayang’ana mumtima.” (1 Samueli 16:7) Chifukwa chake, mahule amene amalapa dama lawo angakhululukidwe ndi Yehova Mulungu. (Yerekezerani ndi Mateyu 21:23, 31, 32.) Rahabi mwiniyo anatembenuka panjira yoipa kutsata yolungama yokhala ndi chivomerezo chaumulungu.
Azondi Achiisrayeli anakhala ndi moyo mogwirizana ndi Chilamulo cha Mulungu, chotero sanaloŵe m’nyumba ya Rahabi kaamba ka zifukwa zachisembwere. Lingaliro lawo lingakhale linali lakuti panali kuthekera kochepa kwa kunyumwira kukhalapo kwawo m’nyumba ya mkazi wadama. Malo a nyumbayo pamwamba pa malinga akachititsanso kuthaŵa kwawo kukhala kosavuta. Mwachionekere Yehova anawatsogolera kwa munthu wochimwa amene mtima wake unayambukiridwa bwino ndi mbiri ya zochita za Mulungu ndi Aisrayeli kwakuti iye analapa nasintha njira zake. Mawu a Mulungu akuti Israyeli akawononge Akanani chifukwa cha machitachita awo oipa, ndi dalitso lake pa Rahabi ndi pachilakiko cha Yeriko, zimapereka umboni wakuti azondiwo sanachite chisembwere.—Levitiko 18:24-30.
Bwanji za mawu osokeretsa a Rahabi kwa olondola azondiwo? Mulungu anavomereza njira yakeyo. (Yerekezerani ndi Aroma 14:4.) Iye anadziika pangozi kotero kuti atetezere atumiki a Mulungu, akumasonyeza umboni wa chikhulupiriro chake. Pamene kuli kwakuti kunama kovulaza nkoipa m’maso mwa Yehova, munthu sali woumirizika kuvumbula chidziŵitso chowona kwa anthu ena amene ali osachiyenerera. Ngakhale Yesu Kristu sananene zonse kapena kuyankha mwachindunji pamene kuchita motero kukanadzetsa ngozi yosafunikira. (Mateyu 7:6; 15:1-6; 21:23-27; Yohane 7:3-10) Mwachionekere, njira ya Rahabi yosocheretsa adindo amene anali adani iyenera kulingaliridwa motero.
Mfupo ya Rahabi
Kodi Rahabi anafupidwa motani chifukwa cha kusonyeza chikhulupiriro? Kupulumutsidwa kwake mkati mwa chiwonongeko cha Yeriko kunalidi dalitso lochokera kwa Yehova. Pambuyo pake, anakwatiwa ndi Salimoni (Salima), mwana wa kalonga wa m’chipululu Nasoni wa fuko la Yuda. Monga makolo a Boazi wowopa Mulungu, Salimoni ndi Rahab anagwirizanitsa mzera wa mbadwa umene unafikira kwa Mfumu Davide wa Israyeli. (1 Mbiri 2:3-15; Rute 4:20-22) Mwatanthauzo kwambiri, Rahabi amene anali wadama kaleyo ndimmodzi wa akazi anayi otchulidwa ndi Mateyu m’mzera wobadwira wa Yesu Kristu. (Mateyu 1:5, 6) Limeneli ndidalitso lotani nanga lochokera kwa Yehova!
Ngakhale kuti sanali Mwisrayeli ndipo poyambapo wadama, Rahabi ali chitsanzo chapadera cha mkazi amene anasonyeza ndi ntchito zake kuti anakhulupirira Yehova kotheratu. (Ahebri 11:30, 31) Mofanana ndi ena, mwa amene ena a iwo aleka moyo wadama, iye adzalandira mfupo inanso—kuukitsidwa kwa akufa ndi kukhala ndi moyo m’dziko lapansi laparadaiso. (Luka 23:43) Chifukwa cha chikhulupiriro chake chochirikizidwa ndi ntchito, Rahabi anavomerezedwa ndi Atate wathu wakumwamba wachikondi ndi wokhululukirayo. (Salmo 130:3, 4) Ndipo chitsanzo chake chabwino kwambiricho chimapereka chilimbikitso kwa onse okonda chilungamo kuti ayembekezere Yehova Mulungu kudzawapatsa moyo wosatha.
[Chithunzi patsamba 23]
Rahabi anayesedwa wolungama chifukwa chakuti ntchito zake zinasonyezadi kuti anali ndi chikhulupiriro
[Zithunzi patsamba 24]
Ofukula m’mabwinja afukula zotsalira za Yeriko wakale, kuphatikizapo chigawo chaching’ono cha linga lakalelo
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.