Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 12/15 tsamba 30
  • Kodi Mukukumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukukumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Zithumwa za Mwaŵi Zingakutetezereni?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Nkuvomereranji Cholakwa?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Chitetezo Chenicheni Nchotheka?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • ‘Valani Kuleza Mtima’
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 12/15 tsamba 30

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwasangalala ndi kuŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Chabwino, tiyeni tione ngati mungathe kuyankha mafunso otsatirawa:

▫ Kodi ndichithandizo chopindulitsa chotani chimene chingaperekedwe kwa odwala ndi okalamba mumpingo lerolino?

Mumpingo Wachikristu woyambirira, munasungidwa mpambo wa akazi amasiye ofuna chithandizo chakuthupi. (1 Timoteo 5:9, 10) Mofananamo lerolino, akulu angalembe mpambo wa odwala ndi okalamba amene akufunikira chisamaliro chapadera. Komabe, zimenezi siziyenera kungotuliridwira akulu okha kuti ayambirire kuchitapo kanthu. Onse mumpingo ayenera kuzindikira zosoŵa zotero. (1 Timoteo 5:4-8)​—8/15, masamba 28-9.

▫ Kodi nkhani ya Yona ya m’Baibulo ya kumezedwa kwake ndi chinsomba cha m’nyanja njosakhulupirika?

Ayi, namngumi wotchedwa sperm whale, namngumi wamkulu wotchedwa white shark, kapena namngumi wa whale shark angameze munthu. Ndiponso, Yesu mwiniyo anatsimikizira kuti nkhani ya Yona njowona. (Mateyu 12:39, 40)​—8/15, tsamba 32.

▫ Kodi ndiupandu wotani umene umakhalapo chifukwa cha kugwiritsira ntchito njirisi ndi zithumwa zamatsenga?

Kugwiritsiridwa ntchito kwake kwenikweni kumalefula anthu kuti asachite mwaluntha ndi mavuto awo ndi kuwalimbikitsa kuona mwaŵi monga mankhwala a zovuta zonse. Kumapatsanso wozigwiritsira ntchitoyo lingaliro lonyenga la chisungiko. Chofunika koposa, munthu amene amakhulupirira mphamvu ya njirisi zamatsenga ndi zithumwa za mwaŵi angapereke moyo wake kulamulidwa ndi mphamvu zosaoneka zauchiwanda.​—9/1, tsamba 4.

▫ Kodi ndizinthu zinayi ziti zimene zingathandize ukwati kukhalitsa?

Zimenezi ndizo kufunitsitsa kumvetsera, kukhoza kupepesa, kukhoza kupereka chichirikizo chosalekeza chamalingaliro, ndi chikhumbo cha kusonyeza chikondi. (1 Akorinto 13:4-8; Aefeso 5:33; Yakobo 1:19)​—9/1, tsamba 20.

▫ Kodi ndinjira ina iti imene Yehova amaperekera chipiriro kwa awo amene amayang’anizana ndi mayesero?

Yehova amachita zimenezi kupyolera mwa zitsanzo za chipiriro zolembedwa m’Mawu ake, Baibulo. (Aroma 15:4) Pamene tisinkhasinkha za zimenezi, timalimbikitsidwa kupirira, ndiponso timaphunzira zochuluka ponena za mmene tingapiririre.​—9/15, masamba 11-12.

▫ Kodi kudzipereka kwaumulungu nchiyani?

Kudzipereka kwaumulungu kumatanthauza kudzipereka kwa Yehova kumene kumatisonkhezera kuchita chimene chili chomkondweretsa, ngakhale poyang’anizana ndi mayesero aakulu, chifukwa chakuti timakonda Mulungu kuchokera mumtima.​—9/15, tsamba 15.

▫ Kodi ndimotani mmene tiyenera kuonera chifundo cha Mulungu?

Sitiyenera konse kuona mopepuka chifundo chachikulu cha Mulungu. Tiyenera kukhala monga Paulo ndi kusonyeza chiyamikiro chathu mwa kulimbana ndi kupanda ungwiro kwathu kwa ife eni. (1 Akorinto 9:27) Mwanjira imeneyi tidzasonyeza, ngakhale poyang’anizana ndi zovuta, kuti tili ndi chikhumbo chowona cha kuchita chabwino.​—10/1, tsamba 23.

▫ Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kuti Paulo anatchula kuleza mtima monga mbali yoyamba ya chikondi?

Kwanenedwa kuti sipangakhale unansi Wachikristu popanda kuleza mtima, kapena popanda kulekererana moleza mtima. Zimenezi zili choncho chifukwa tonsefe tili opanda ungwiro, ndipo kupanda ungwiro ndi zophophonya zathu zimaika ena pachiyeso. Nchifukwa chake, kuleza mtima nkofunika ngati pati pakhale chikondi pakati pa abale.​—10/15, tsamba 21.

▫ Kodi Akristu oyambirira anagwiritsira ntchito dzina la Mulungu?

Umboni umasonyeza kuti anatero. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kwa Mulungu kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Ndipo pamapeto a utumiki wake, iye anapemphera kuti: “Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa ine m’dziko lapansi.” (Yohane 17:6) Ndiponso, makope oyambirira a Septuagint anali ndi dzina la Mulungu mumpangidwe wa Tetragrammaton Yachihebri.​—11/1, tsamba 30.

▫ Kodi ndizitsanzo za Baibulo ziti zimene zimasonyeza kuti njira imene timachitira ndi zophophonya zathu ingayambukire miyoyo yathu?

Mfumu Sauli anakana uphungu mouma khosi, ndipo zolakwa zake zinachuluka, potsirizira pake zikumamfikitsa kuimfa ali wopanda chiyanjo cha Mulungu. (1 Samueli 15:17-29) Kumbali ina, mosasamala kanthu za zolakwa zake ndi machimo, Mfumu Davide molapa anavomereza kuwongoleredwa ndipo anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Zitsanzo za Baibulo zimenezi zimasonyeza kuti kuvomereza zolakwa zathu kumatithandiza kusunga unansi wabwino ndi Mulungu ndipo motero kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (Salmo 32:1-5)​—11/15, masamba 29-30.

▫ Kodi ndimotani mmene Yehova amathandizira anthu ake pamene ali m’vuto chifukwa cha masoka achilengedwe kapena mikhalidwe ina?

Yehova amathandiza, osati mwa kubweza mphamvu za chilengedwe mozizwitsa kapena mwa kachitidwe kena kosakhala kachibadwa, koma mwa mphamvu ina imene anthu ochuluka samaidziŵa bwino​—chikondi. Inde, Yehova amakondadi anthu ake, ndipo wawaphunzitsa kukondana kwamphamvu kwakuti akhoza kuwachitira zinthu zimene zimaoneka kukhala monga zozizwitsa. (1 Yohane 4:10-12, 21)​—12/1, tsamba 10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena