Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 1/15 tsamba 5-7
  • Posachedwapa—Dziko Lopanda Nkhondo!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Posachedwapa—Dziko Lopanda Nkhondo!
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchirikiza Mtendere m’Maganizo
  • Mmene Mulungu Adzabweretsera Mtendere
  • Kuchotsa Zopinga Zachipembedzo
  • Mtendere Weniweni—Kodi Udzachokera Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Funafunani Mtendere Weniweni ndi Kuulondola!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kodi Adzatsogolera Anthu ku Mtendere Ndani?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhondo Idzatha
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 1/15 tsamba 5-7

Posachedwapa​—Dziko Lopanda Nkhondo!

PA DECEMBER 24, 1914, msilikali wachichepere wa ku Britain wotchedwa Jim Prince anadutsa malo opanda mwini kukalankhula ndi msilikali woyenda pansi wa ku Germany. “Ndine wa fuko la Saxon. Ndiwe wa fuko la Anglo-Saxon. Kodi nchifukwa ninji tikumenyana?” anafunsa motero munthu wa ku Germany. Zaka zambiri pambuyo pake, Prince anavomereza kuti: “Sindidziŵabe yankho la funso limenelo.”

Kwa mlungu umodzi wapadera mu 1914, asilikali a magulu ankhondo a Britain ndi Germany anachezerana, kuseŵera mpira, ndipo ngakhale kupatsana mphatso za Krisimasi. Komabe, pangano la kuleka kumenyanalo silinali lovomerezedwa ndi lamulo. Akazembe ankhondowo sanafune kuti magulu awo adziŵe kuti “mdani” sanali chilombo chowopsa chosonyezedwa ndi manenanena ankhondo. Msilikali wa ku Britain Albert Moren pambuyo pake anakumbukira kuti: “Ngati kuleka kumenyanako kukanapitiriza kwa mlungu wina, kukanakhala kovuta kwambiri kuyambanso nkhondoyo.”

Kuleka kumenyana kwamwadzidzidzi kumeneko kumapereka lingaliro lakuti ngakhale asilikali ophunzitsidwa ambiri amalakalaka mtendere mmalo mwa nkhondo. Asilikali ambiri amene adziŵa kuwopsa kwa nkhondo angavomereze mwambi Wachispanish wakuti: “Lekani wosadziŵa nkhondo apite ku nkhondo.” Mosakayikira, kupenda kochitidwa padziko lonse pakati pa anthu wamba kukavumbula kuti ochuluka kwambiri amakonda mtendere osati nkhondo. Koma kodi chikhumbo chapadziko lonse cha mtendere chimenechi chingasinthidwe motani kukhala dziko lopanda nkhondo?

Nkhondo isanathetsedwe, mkhalidwe wamaganizo uyenera kusintha. Lamulo la bungwe la UN la Educational, Scientific, and Cultural Organization limanena kuti: “Popeza kuti nkhondo zimayamba m’maganizo mwa anthu, kuchirikiza mtendere kuyenera kuyamba m’maganizo mwa anthu.” Komabe, chitaganya chamakono, kumene kusadalirana ndi chidani zili zofala, chikupitirizabe kukhala chachiwawa kwambiri, osati chamtendere.

Chikhalirechobe, Mulungu mwini analonjeza kuti tsiku lina mtendere udzakhomerezedwa m’maganizo mwa anthu okonda chilungamo. Kupyolera mwa mneneri wake Yesaya, iye anati: “Iye [Mulungu] adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”​—Yesaya 2:4.

Kuchirikiza Mtendere m’Maganizo

Kodi kusintha kodabwitsa kwa kuganiza koteroko kungachitike? Kodi anthu adzaphunzira konse kutetezera mtendere mmalo molemekeza nkhondo? Talingalirani chitsanzo cha Wolfgang Kusserow. Mu 1942 Anazi anadula mutu munthu wa ku Germany wa zaka 20 zakubadwa ameneyu chifukwa ‘sakanaphunzira nkhondo.’ Kodi nchifukwa ninji iye anasankha kufa? M’ndemanga yolembedwa, anagwira mawu a malamulo a mkhalidwe a Malemba onga, “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini” ndi, “Onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Mateyu 22:39; 26:52) Ndiyeno anafunsa mwachindunji kuti: “Kodi Mlengi wathu analembera mitengo zonsezi?”

Mawu a Mulungu, olembedwa m’Baibulo, “amapereka mphamvu” ndipo anasonkhezera Mboni ya Yehova yachichepere imeneyi kulondola mtendere, mosasamala kanthu za zotulukapo zake. (Ahebri 4:12, NW; 1 Petro 3:11) Koma Wolfgang Kusserow sanali yekha amene analondola mtendere. M’buku lakuti The Nazi Persecution of the Churches 1933-45, J. S. Conway akutchula zolembedwa zalamulo za Nazi zotsimikizira kuti Mboni za Yehova monga gulu zinakana kumenya nkhondo. Monga momwe Conway akunenera, kaimidwe kolimba mtima koteroko kanatanthauza kusankha kwawo imfa.

Lerolino Mboni za Yehova zimapitirizabe kulondola mtendere, mosasamala kanthu za fuko kapena mtundu wawo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti aphunzira m’Baibulo kuti atumiki owona a Mulungu ayenera kusula malupanga awo kukhala zolimira. Alejandro, mwamuna wachichepere wa ku Argentina amene anasamukira ku Israel mu 1987, angachitire umboni mfundo imeneyi.

Kwazaka zitatu Alejandro anakhala pamalo aulimi pamene anali kuphunzira pa yunivesite namagwira ntchito m’mahotela ndi marestiranti osiyanasiyana. Mkati mwa nthaŵi imeneyi, anayamba kuŵerenga Baibulo ndipo anali kufufuza chifuno cha moyo. Koposa zonse, analakalaka kuona dziko limene anthu angasangalale ndi mtendere ndi chilungamo. Alejandro​—Myuda​—anagwirira ntchito pamodzi ndi Ayuda ndi Aluya koma sanakonde kuchita tsankho.

Mu 1990 bwenzi lina limene linali kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova linapempha Alejandro kupita ku msonkhano wa tsiku limodzi ku Haifa. Atadabwa kupeza Ayuda ndi Aluya 600 akuchezera pamodzi mwachimwemwe pamsonkhanopo, iye analingalira mumtima mwake nati, ‘Iyi ndiyo njira yabwino yokhalira ya anthu.’ Mkati mwa miyezi isanu ndi umodzi, anakhala Mboni ndipo tsopano amathera nthaŵi yake yochuluka akumalalikira uthenga wa Baibulo wa mtendere.

Mmene Mulungu Adzabweretsera Mtendere

Ngakhale kuti zitsanzozi nzokhudza mtima, izo nzapadera ndipo siziri zofala m’dziko lerolino. Ngakhale kuti dongosolo lamakono limanena zochirikiza mtendere, limachirikiza nkhondo. Kodi mungakonde kukhala m’khwalala limene nzika zake zimathera pakati pa 7 ndi 16 peresenti ya malipiro awo kugula mfuti ndi kuchinjiriza nyumba zawo? Kwenikweni, zimenezo nzimene maiko akhala akuchita mwa kuwonongera ndalama pazida zankhondo m’zaka zaposachedwapa. Mosadabwitsa, ulosi wa Yesaya umavumbula kuti mtundu wonse wa anthu sudzasula malupanga ake kukhala zolimira kufikira pamene Mulungu ‘adzudzula mitundu yambiri ya anthu.’ Kodi adzachita motani zimenezo?

Njira yaikulu yolungamitsira zinthu ndiyo Ufumu wa Yehova Mulungu. Mneneri Danieli ananeneratu kuti ‘Mulungu wa kumwamba akaika ufumu woti sukawonongeka kunthaŵi zonse.’ Iye akuwonjezera kuti, Ufumu umenewu, “udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [maboma adziko], nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Mawu ameneŵa amavumbula kuti Ufumu wa Mulungu udzakhazikitsa mwamphamvu ulamuliro wake pa dziko lonse lapansi. Mwa kuchotsa malire amaiko, Ufumuwo udzathetseratu mikangano. Ndiponso, popeza kuti nzika zake zidzakhala ‘anthu ophunzitsidwa ndi Yehova,’ mtendere wawo “udzakhala waukulu.” (Yesaya 54:13) Nzosadabwitsa kuti Yesu anatiuza kupemphera kwa Mulungu kuti: “Ufumu wanu udze”!​—Mateyu 6:10.

Kuchotsa Zopinga Zachipembedzo

Mulungu adzachotsanso zopinga zachipembedzo pa mtendere. Chipembedzo chinachititsa nkhondo yomenyedwa kwanthaŵi yaitali koposa m’mbiri​—Nkhondo Zamtanda, kapena “Nkhondo Zopatulika,” zoyambitsidwa ndi Papa Urban II mu 1095 C.E.a M’zaka za zana lathu atsogoleri achipembedzo akhala otsogolera m’kusonkhezera anthu kuchirikiza nkhondo, ngakhale nkhondo za dziko kotheratu.

Ponena za mbali ya matchalitchi wamba Achikristu m’nthaŵi ya Nkhondo Yadziko I, wolemba mbiri Paul Johnson analemba kuti: “Atsogoleri achipembedzo analephera, ndipo kwakukulukulu anali osafunitsitsa, kuika chikhulupiriro cha Chikristu patsogolo pa utundu. Ambiri anasankha njira yokhweka nagwirizanitsa Chikristu ndi kukondetsa dziko la munthuwe. Asilikali Achikristu a zipembedzo zonse anasonkhezeredwa kuphana wina ndi mnzake m’dzina la Mpulumutsi wawo.”

Chipembedzo chachita zambiri kusonkhezera nkhondo koposa kusungitsa mtendere. Kwenikweni, Baibulo limasonyeza chipembedzo chonyenga kukhala “mkazi wachigololo” amene amadyerera olamulira a dziko. (Chivumbulutso 17:1, 2) Mulungu amamutcha kukhala waliŵongo wamkulu wokhetsa mwazi wa onse amene anaphedwa padziko lapansi. (Chivumbulutso 18:24) Chifukwa chake, Yehova Mulungu adzachotsa chopinga chimenechi cha mtendere kamodzi kwatha.​—Chivumbulutso 18:4, 5, 8.

Ngakhale pamene zinthu zogaŵanitsa zoterozo zonga ndale zadziko ndi chipembedzo chonyenga zidzachoka, mtendere sudzakhalabe wotsimikizirika popanda kuchotsedwa kwa wosonkhezera nkhondo wamkulu koposa onse​—Satana Mdyerekezi. Imeneyo ndiyo ntchito yomalizira imene Ufumu wa Mulungu udzachita m’ndandanda yake yobweretsa mtendere wosatha padziko lapansi. Buku la Baibulo la Chivumbulutso limalongosola kuti Satana ‘adzagwidwa’ ndi ‘kumangidwa’ ndi ‘kuponyedwa kuphompho’ kotero kuti “asanyengenso amitundu.” Pambuyo pake adzawonongedwa kotheratu.​—Chivumbulutso 20:2, 3, 10.

Lonjezo la Baibulo la kutha kwa nkhondo silili loto wamba. Makonzedwe a Yehova Mulungu a mtendere anakhazikitsidwa kale. Ufumu wake wakhazikitsidwa kumwamba ndipo ngwokonzekera kuchita zinthu zina zowonjezereka kutsimikizira mtendere wa padziko lonse. Pakali pano, mamiliyoni a Mboni za Yehova, amene amachirikiza boma lakumwamba limeneli, aphunzira kukhala mwamtendere.

Pamenepa, mwachionekere, tili ndi zifukwa zabwino zokhulupirira kuti nkhondo sizili zosapeŵeka. Kuposa pamenepo, tikhoza kuyembekezera tsiku lomwe layandikira pamene Yehova adzathetsa nkhondo kosatha. (Salmo 46:9) Iye adzatsimikizira kuti posachedwapa kudzakhala dziko lopanda nkhondo.

[Mawu a M’munsi]

a Nthaŵi zina atsogoleri achipembedzo eniwo anakhala asilikali. Pa Nkhondo ya Hastings (1066), bishopu Wachikatolika wotchedwa Odo analungamitsa kudziloŵetsa kwake kokangalika mwa kugwiritsira ntchito chibonga mmalo mwa lupanga. Iye ananena kuti ngati mwazi sunakhetsedwe, munthu wa Mulungu akhoza kupha movomerezedwa ndi lamulo. Zaka mazana asanu pambuyo pake, Kadinala Ximenes mwiniyo anatsogolera kuukiridwa kwa North Africa kochitidwa ndi Spain.

[Chithunzi patsamba 7]

Mukhoza kukhala ndi moyo m’dziko latsopano lopanda nkhondo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena