Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 1/15 tsamba 24-30
  • Misonkhano Yosangalatsa Ichirikiza Chiphunzitso Chaumulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yosangalatsa Ichirikiza Chiphunzitso Chaumulungu
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Masana a Tsiku Loyamba
  • Mmaŵa Wachiŵiri
  • Masana Achiŵiri
  • Mmaŵa wa Tsiku Lachitatu
  • Masana a Tsiku Lachitatu
  • Mmaŵa Wachinayi
  • Masana Omalizira
  • Aphunzitsi a Mawu a Mulungu Analimbikitsidwa Kukwaniritsa Ntchito Yawo
    Nsanja ya Olonda—2002
  • “Olengeza Ufumu Achangu” Anasonkhana Mosangalala
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Patsani Mulungu Ulemerero Osati Anthu
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Akuchita Mawu a Mulungu Amapeza Chimwemwe
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 1/15 tsamba 24-30

Misonkhano Yosangalatsa Ichirikiza Chiphunzitso Chaumulungu

LEROLINO, njira zofalitsira nkhani zikuchuluka padziko lonse. Wailesi yakanema ndi wailesi wamba, mabuku kapena makompyuta, zili magwero aakulu kwambiri a chidziŵitso pankhani iliyonse imene mungalingalire. Chikhalirechobe, anthu amadwala ndi kufa. Padziko lonse lapansi pali upandu, njala, ndi umphaŵi ndipo kupsinjika mtima kumayambukira ambiri kuposa ndi kalelonse. Chidziŵitso chonse chimene chilipo chalephera kuwongolera zinthu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti anthu anyalanyaza nzeru ya Mulungu.

Pamenepa, nkoyenera chotani nanga, kuti mutu wakuti “Chiphunzitso Chaumulungu” ndiwo unasankhidwa kukhala mutu wa misonkhano yachigawo ya Mboni za Yehova yaposachedwapa! Programuyo inakumbutsa awo omwe analipo kuti chiphunzitso chopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo, ndicho chokha chimene chili ndi phindu lenileni lopulumutsa moyo.

Msonkhano woyamba unayamba pa Lachinayi, June 3, ku Uniondale, New York, U.S.A. Kuyambira pamenepo, programuyo inaperekedwa m’mizinda yosiyanasiyana m’maiko osiyanasiyana, ikumathera m’kontinenti ya Afrika ndi ya South America.

Masana a Tsiku Loyamba

Tsiku lililonse linali ndi mutu umene unagogomezera mbali ya chiphunzitso chaumulungu. Mwachitsanzo, programu ya tsiku loyamba inazikidwa pa mutu wakuti “Kudziŵa Chiphunzitso Chochokera kwa Mulungu.” (Yohane 7:17) Mfundo imeneyi inafutukulidwa bwino lomwe patsikulo.

Pambuyo pa nyimbo ndi pemphero, tcheyamani wa msonkhano anatsegulira programuyo ndi nkhani yakuti “Chiphunzitso Chaumulungu Chimatigwirizanitsa.” Anasonyeza kuti anthu a Yehova ali ogwirizana mwa kuphunzira njira Zake ndi kuyenda m’mabande Ake. (Mika 4:1-5) Chiphunzitso chaumulungu chimalimbitsa umodzi wawo. Osonkhanawo analimbikitsidwa kukondwera muunansi wawo wogwirizana.​—Salmo 133:1-3.

Pambuyo pake masanawo, misonkhano yanthaŵi zonse ya mpingo inafotokozedwa m’nkhani yosiirana ya mutu wakuti “Misonkhano Imene Imatilangiza za Njira za Yehova.” Wokamba nkhani woyamba anakumbutsa osonkhanawo kuti pamene tisonkhana pamodzi, timalemekeza Yehova ndipo motero timalandira dalitso Lake. Wokamba nkhani wotsatira anagogomezera kufunika kwa kutenga mbali m’misonkhano. Mwa kutero, timatamanda Yehova poyera, kusonyeza chikhulupiriro chathu, ndi kulimbitsa chikhulupiriro cha ena. Wokamba nkhani wachitatu m’nkhani yosiiranayo anasonyeza kufunika kwa kugwiritsira ntchito zimene timaphunzira pamisonkhano. Tiyenera kukhala “akuchita mawu, osati akumva okha.”​—Yakobo 1:22.

Ndiyeno panatsatira nkhani ya kuimbira Yehova zitamando. Nyimbo zoimbidwa ndi mtima wonse zili mbali yofunika ya kulambira kwathu. Nkhani imeneyi inatsatiridwa ndi nkhani yaikulu yakuti, “Chiphunzitso Chaumulungu Chilakika.” Unali mutu wabwino koposa chotani nanga! “Yehova ndiye Magwero a chiphunzitso chabwino choposa chimene aliyense angachilandire,” anatero wokamba nkhaniyo. Ndiyeno, atafotokoza mwachidule kuzizwitsa kwa ubongo wa munthu, anati: “Kwakukulukulu tiyenera kugwiritsira ntchito mphamvu zathu zakulingalira kupezera chiphunzitso chaumulungu. Ndicho chokha chimene chimapatsa nzeru yeniyeni.” Nzowona motani nanga!

Mmaŵa Wachiŵiri

“Pitirizani Kukometsera Chiphunzitso cha Mpulumutsi Wathu, Mulungu” ndiwo unali mutu wa patsiku lachiŵiri la msonkhano. (Tito 2:10) Lamulo la mkhalidwe limeneli linagogomezeredwa m’nkhani yakuti “Chiphunzitso Chaumulungu Molimbana ndi Ziphunzitso za Ziŵanda.” Inde, ziŵanda zili ndi ziphunzitso zawo. (1 Timoteo 4:1) Monga momwe wokamba nkhaniyo anafotokozera, chiphunzitso chaumulungu chimalaka “nzeru” ya Satana mwa kuvumbula ziphunzitso zonama ndi njira zamachenjera za Mdyerekezi. Pachifukwa chimenechi, Akristu a mtima wowongoka pafupifupi 4,500,000 salinso akapolo mumdima wa Satana.​—Yohane 8:32.

Chikhalirechobe, tiyenera kupitirizabe kukaniza Satana. Zimenezi zinagogomezeredwa m’nkhani yakuti “Kodi Mukukana Mzimu wa Dziko?” Mzimu wa dzikoli ngwakupha. Umalimbikitsa makhalidwe oluluzika, lingaliro lopandukira ulamuliro, ndi chikhumbo chosirira zinthu zakuthupi. Mkristu ayenera kudzipenda nthaŵi zonse. Kodi akali ndi miyezo yapamwamba ponena za zimene amaonerera, kumvetsera, kapena kuŵerenga? Molimbikitsa, wokamba nkhaniyo anati: “Tikukuyamikirani, abale, alongo, ndi achichepere, chifukwa cha kuyesayesa kwakhama kumene mukuchita ponena za nkhaniyi.”​—1 Yohane 2:15-17.

Pali chinthu chimodzi chimene chimachititsa kukana mzimu wa dziko kukhala kovuta. Kodi chimenecho nchiyani? Tonsefe ndife opanda ungwiro. Zowona, Yesu anafera machimo athu, koma tifunikira kulimbana ndi chikhoterero chauchimo. Zimenezi zinapendedwa m’nkhani yakuti “Kulimbana ndi Mphamvu ya Uchimo Yolamulira Thupi Lochimwa.” Pakati pa zinthu zina, wokamba nkhaniyo anati tingalake nkhondo yathu yolimbana ndi uchimo ngati tivala umunthu watsopano ndi kupeŵa chilichonse chimene chimakhutiritsa zikhoterero zathu zauchimo.

“Pangani Chiphunzitso Cholama Kukhala Njira Yanu ya Moyo” ndiwo unali mutu wa nkhani yotsatira. Ena amadera nkhaŵa mopambanitsa thanzi lawo lakuthupi. Komabe, kunena zowona, thanzi lauzimu ndilo lofunika koposa. Wokamba nkhani anagogomezera kufunika kwa kuona mathayo athu mwamphamvu pankhaniyi, ndipo anali ndi mawu olimbikitsa kwambiri kwa akazi Achikristu. Iye anati: “Timayamikira kwambiri ponse paŵiri alongo achikulire ndi alongo achichepere amene ali olinganizika bwino m’changu chawo cha utumiki ndi m’kusamalira kwawo mathayo awo aumwini.” Inde, ndipo tonsefe tiyamikira Yehova kaamba ka chiphunzitso cholama chimene chimatilekanitsa ndi dziko.

Nkhani yomwe inamaliza programu ya mmaŵa inali yakuti “Chiphunzitso Chaumulungu Chimavumbula Chifuno cha Moyo.” Wokamba nkhaniyo anati: “Pafupifupi munthu aliyense amadabwa panthaŵi ina kuti, ‘Kodi chifuno cha moyo nchiyani?’” Ndi zigomeko zamphamvu, iye anasonyeza kuti Baibulo lokha ndilo limapereka yankho lenileni la funso limenelo. Ndiyeno, wokamba nkhaniyo anasonyeza kuti malonjezo abwino koposa a Mulungu amatipatsadi chifuno m’moyo. Mwachionekere ambiri mwa omvetsera anali kuganiza kuti, ‘Zimenezi ndizo zimenedi anthu m’gawo langa afunikira kumva.’ Bungwe Lolamulira linalingalira zofananazo. Brosha latsopano, la mutu wakuti Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? linatulutsidwa pamapeto a nkhaniyi. Onse anakondwera chotani nanga! Nthaŵi ya kupuma inapereka mpata wa kupenda chofalitsidwa chatsopano chimenechi.

Masana Achiŵiri

Nkhani yoyamba masana inali ndi mutu wotonthoza wakuti “Msenzetseni Yehova Nkhaŵa Zanu Zonse.” Zinthu zambiri zimachititsa nkhaŵa; komabe, Mawu a Mulungu amanena kuti tiyenera kumsenzetsa nkhaŵa zathu zonse. (1 Petro 5:6, 7) Zowona, mavuto ena amapitirizabe, ndipo ponena za zimenezi wokamba nkhaniyo anati: ‘Khalani woleza mtima. Yembekezerani Yehova. Khulupirirani zolimba kuti kutsatira Baibulo kuli bwino nthaŵi zonse. Ngati tisumika mitima yathu pa Yehova, tidzakhala ndi “mtendere wa Mulungu” wakupambana chidziŵitso chonse.’​—Afilipi 4:6, 7.

Nkhani zinayi zotsatira zinasonyeza kuti chiphunzitso chaumulungu chimagwira ntchito m’moyo wabanja. Yoyamba, “Kupangitsa Ukwati Kukhala Mgwirizano Wokhalitsa,” inakumbutsa osonkhanawo kuti Yehova samaona ukwati monga pangano lokhoza kuswedwa, monga momwe ambiri m’dziko amauonera. Komabe, kuti ukwati ukhale wachipambano, tifunikira kutsatira chitsogozo cha Yehova. Iye anatilenga. Chotero, Mawu ake ouziridwa ndiwo ali ndi uphungu wabwino koposa umene ulipo wa ukwati.

Nkhani yakuti “Gwirani Ntchito Zolimba Kaamba ka Chipulumutso cha Banja Lanu” inafotokoza mavuto a kusamalira banja m’nthaŵi zino zovuta. (2 Timoteo 3:1) Makolo amaphunzitsa ana awo ukhondo, makhalidwe okoma, mmene angagwirire ntchito, ndi mmene angakhalire owoloŵa manja ndi osamalira ena. Chofunika koposa, ayenera kuphunzitsa ana awo kukhala atumiki odzipereka a Yehova.​—Miyambo 22:6.

M’nkhani yotsatira, “Makolo, Ana Anu Amafunikira Chisamaliro Chapadera,” wokamba nkhaniyo anakumbutsa osonkhana kufunika kwa kuyamikira ana, pamene kuli kwakuti sakunyalanyaza zofooka zawo. Makolo ayenera kukhala atcheru kwambiri ndi zizoloŵezi za kusawona mtima, kukondetsa zinthu zakuthupi, kapena dyera.

Makamaka osonkhana achichepere anamvetsera mosamalitsa nkhani yakuti “Achichepere​—Kodi Mumalabadira Ziphunzitso za Yani?” Zinthu nzovuta kwa achichepere Achikristu lerolino. Kuyendera limodzi ndi dziko nkosavuta, koma kumeneku kumadzetsa imfa. Pamene kuli kwakuti kusankha kumamatira ku chiphunzitso chaumulungu kumafuna kulimba mtima kwa munthu wachichepere, kumadzetsa madalitso aakulu tsopano lino ndi moyo wosatha ulinkudza.​—1 Timoteo 4:8.

Tsiku lachiŵiri linatha ndi drama logwira mtima, Achichepere Amene Amakumbukira Mlengi Wawo Tsopano Lino. M’mawu oyamba, wotsogoza anatcha anthu achichepere a m’gulu la Mulungu kukhala “gulu la nkhondo yateokratiki lophatikizidwa mokhulupirika muutumiki wodzipereka kwa Yehova Mulungu ndi Mfumu yake yoikidwa yakumwamba, Kristu Yesu.” Anawonjezera kuti: “Achichepere athu akuchitadi kanthu kena kabwino!” Dramalo linasonyeza bwino lomwe kuti ngati kholo liphunzitsa mwana bwino lomwe, zimenezo zidzathandiza mwanayo pamene akula ndi kutumikira Yehova payekha.

Mmaŵa wa Tsiku Lachitatu

Mutu wa tsiku lachitatu unali wakuti “Pitirizani Kuphunzitsa Anthu Amitundu Yonse.” (Mateyu 28:19, 20) Osonkhanawo mosakayikira anayembekezera uphungu wa panthaŵi yake wa ntchito yolalikira, ndipo sanagwiritsidwe mwala. Nkhani yosiirana ya mutu wakuti “Kukwaniritsa Ntchito Yathu ya Kulalikira ndi Kuphunzitsa Mwachisangalalo” inalimbitsa kutsimikiza mtima kwawo kupitiriza kukhala ndi phande m’ntchito yochitira umboni. Nkhani yoyamba inafotokoza maulendo oyamba; yachiŵiri, maulendo obwereza; ndi yachitatu, maphunziro a Baibulo. Amishonale kuzungulira dziko lonse anali ataitanidwa kubwerera kwawo ndi kukapezeka pamsonkhano ndi mabanja awo ndi mabwenzi. Kumalo ena, amishonale anali ndi phande m’mbali imeneyi ya programu. Kunali kosangalatsa kulandira chidziŵitso cha zipambano zimene akupeza m’magawo awo. Nkhani yotsatira, yakuti “Kufikira Munthu Aliyense ndi Mbiri Yabwino” inafotokoza chiyambukiro cha umboni wamwamwaŵi.

Gawo la m’maŵa linatha ndi nkhani yaubatizo, imene nthaŵi zonse imakhala mbali yapadera pamisonkhano yaikulu ya Mboni za Yehova. Pamisonkhano yosiyanasiyana, magulu aakulu a odzipatulira chatsopano anaima pamaso pa gulu losonkhana ndi kuyankha mwachidaliro kuti inde mafunso aŵiri omwe anafunsidwa. Ndiyeno anabatizidwa poyera. Ndiumboni wamphamvu chotani nanga wa chiyambukiro chachikulu cha chiphunzitso chaumulungu!

Masana a Tsiku Lachitatu

Programu ya masana inayamba ndi nkhani yakuya Yamalemba. Mboni za Yehova nzozolowera mawu a pa Mateyu chaputala 24 ndi Luka chaputala 21. Kodi ena anaganiza kuti panalibe kanthu kena katsopano kamene kakanenedwa pa machaputala a Baibulo ameneŵa? Analakwa chotani nanga! Nkhani yakuti “Kodi Nchiyani Chidzakhala Chizindikiro cha Kukhalapo Kwanu?” ndi yakuti “Tiuzeni, Zinthu Izi Zidzachitika Liti?” zinaloŵetsa osonkhanawo m’kupenda kosangalatsa zigawo za machaputala aŵiriwo ndi kupereka malongosoledwe atsopano a mavesi ena. Panali kukambitsirana kosangalatsa pambuyo pa gawolo pamene osonkhanawo anayerekezera manotsi awo kuona ngati anamvetsetsa mfundozo. Mosakayikira, mafunso ambiri adzayankhidwa pamene chidziŵitso chimenechi chidzafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda.

Mutu wa phunziro Labaibulo unapitirizidwa m’nkhani yakuti “Mayankho Opatsa Chidziŵitso Pamafunso Anu a Baibulo.” Ndiyeno programuyo inatenga njira ina. Chaka cha 1993 chinali cha 50 kuyambira pamene Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower inakhazikitsidwa. Nkhani yakuti “Zaka Makumi Asanu za Kuphunzitsa ndi Ntchito Yaumishonale ya Gileadi” inasonyeza osonkhana zimene zinakwaniritsidwa m’nyengo imeneyo. Ngati panali amishonale alionse pankhani yakuti “Zipambano Zakulalikira m’Munda Wapadziko Lonse,” anapemphedwa kuuza omvetsera zina za zokumana nazo zawo. Kumvetsera nkhani zosimbidwa ndi amishonalewo kunali kosangalatsa!

Nkhani yotsatira yakuti, “Chifukwa Chimene Mboni za Yehova Zimakhalira Zodikira,” inalinso phunziro lina la mbiri. Inasonyeza kuti Akristu akhala odikira kuyambira m’zaka za zana loyamba C.E. kufikira tsopano. Imeneyi inadzetsa chodabwitsa china. Kuchiyambiyambi kwa nkhani yotsatira, ya mutu wakuti “Olengeza Ufumu Ngokangalika Padziko Lonse Lapansi,” wokamba nkhani ananyamula voliyumu yaikulu (ngati inalipo kale m’chinenero cha kumaloko) nati: “Nkosangalatsa kulengeza pano lero za kutulutsidwa kwa buku ili latsopano, la mutu wakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom.” Bukulo lili ndi nkhani yakuya ya mbiri yamakono ya Mboni za Yehova. Limasimba nkhani yosangalatsa ya chipiriro, kutsimikiza mtima, ndi chipambano, likumapereka umboni wamphamvu wakuti mzimu wa Yehova ukugwira ntchito pa atumiki ake.

Mmaŵa Wachinayi

Posapita nthaŵi linali kale tsiku lomalizira la msonkhano. Mutu wa tsikulo wakuti, “Kudzipindulitsa Ife Eni ndi Chiphunzitso Chaumulungu,” unali ndi chimake chabwino cha programuyo. (Yesaya 48:17) Mmaŵa maganizo a osonkhana anasumikidwa pa nkhani yosiirana ya nkhani zitatu zamphamvu. Pokhala ndi mutu wakuti “Uthenga Wochenjeza Wouziridwa wa Yeremiya​—M’Nthaŵi Yakale ndi Yamakono,” nkhani yosiiranayo inali kufotokoza vesi limodzi ndi limodzi la Yeremiya chaputala 23, 24, ndi 25. Machaputala ameneŵa ali ndi uthenga wamphamvu chotani nanga! Israyeli wosakhulupirika wa m’tsiku la Yeremiya ayenera kukhala atanjenjemera ndi machenjezo ake osabisa ouziridwa mwaumulungu. Dziko lonse linanjenjemera koposa pamene machenjezo amenewo anakwaniritsidwa. Kodi lerolino zinthu zili zosiyana? Kutalitali. Mboni za Yehova zimalalikira molimba mtima mauthenga a Mulungu a chiweruzo. Pomalizira pake, dongosolo lonseli la zinthu lidzafunikira kuyang’anizana ndi zochita zachiweruzo za Yehova. Zimenezo zidzatanthauza chiwonongeko chotheratu cha dziko la Satana.

Gawo la mmaŵa pa Sande linatha ndi drama lachiŵiri, Musasocheretsedwe Kapena Kunyoza Mulungu. Mwanjira yoonekera bwino, linasonyeza mmene chiphunzitso chaumulungu chingatitetezerere ku kuyambukiridwa ndi mavidiyo ndi nyimbo zoluluza ndi chikhoterero cha kuyambitsa magaŵano pakati pa Akristu anzathu. Pamapeto pa dramalo, tcheyamani anagwira mawu osonkhezera maganizo a mmodzi wa oseŵerawo kuti: “Tikhoza kuyambukiridwa ndi chisonkhezero cha dziko. Ngati sitilikaniza, dziko mwamachenjera lingaipitse maganizo athu. Ndipo kuti tikukhalabe okhulupirika kapena ayi zidzadalira pa zimene takhala tikufesa.” Nzowona motani nanga!

Masana Omalizira

Msonkhano unali kufika kumapeto mofulumira pamene wokamba nkhani anapita papulatifomu kukakamba nkhani yapoyera, ya mutu wakuti “Chiphunzitso Chothandiza m’Nthaŵi Zathu Zoŵaŵitsa.” Mwanjira yomveka bwino ndi yotsatirika, iye anatchula mavuto aakulu amene amatiyambukira lerolino ndi kusonyeza njira zina zimene chiphunzitso chaumulungu chingatithandizire kukhala ndi moyo wabwino. Iye ananena kuti ngati titsatira chiphunzitso cha m’Malemba tsopano, tidzakhoza kuchitsatira kosatha m’dziko latsopano la Yehova.

Pambuyo pa chidule cha phunziro la mlungu ndi mlungu la Nsanja ya Olonda, nthaŵi ya nkhani yomalizira inafika. Wokamba nkhani anafotokoza mofulumira mfundo zazikulu za programu ya masiku anayi nakumbutsa osonkhanawo zofalitsidwa zatsopano. Analengezanso kuti vidiyo kaseti yachiŵiri mumpambo wotchedwa The Bible​—A Book of Fact and Prophecy ikatulutsidwa posachedwa. Kwenikweni, vidiyo kaseti imeneyo ya mutu wakuti “The Bible​—Mankind’s Oldest Modern Book” ilipo tsopano m’Chingelezi. Malipoti omvetsa chifundo anaŵerengedwa ochokera kumalo kumene kuli zipolowe zowopsa, monga ku Bosnia ndi Herzegovina. Pomaliza, wokamba nkhaniyo anaŵerenga mawu a pa Mlaliki 12:13 akuti: “Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, nusunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”

Nchikumbutso chabwino chotani nanga! Tiyeni tikhalire moyo tsiku limene anthu onse adzatamanda Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova, ndi kulabadira chiphunzitso chake chaumulungu.

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Misonkhano yachigawo ya “Chiphunzitso Chaumulungu” ku Moscow ndi Kiev inadzetsa chisangalalo chachikulu

[Zithunzi pamasamba 26, 27]

1. Mwa kubatizidwa, ambiri anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu

2. Wosonkhana wazaka 100 anakondwa kulandira chofalitsidwa chatsopano

3, 4. Madrama osonkhezera maganizo anayamikiridwa kwambiri

5. Amishonale ofunsidwa pamisonkhano yachigawo anasonyeza mapindu a chiphunzitso chaumulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena