Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 2/1 tsamba 4-7
  • Nthumwi za Zoipa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nthumwi za Zoipa
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Wopanduka Woyamba
  • Angelo Ena Apanduka
  • Adani a Anthu
  • Kodi Adzalekereredwa kwa Utali Wotani?
  • Angelo Ena Anaukira Mulungu
    Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
  • Olamulira Okhala m’Malo a Mizimu
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Bwenzi Lathu Lapamtima Lili m’Malo a Mizimu
    Galamukani!—1996
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 2/1 tsamba 4-7

Nthumwi za Zoipa

MALONGOSOLEDWE a Baibulo a thayo la ziŵanda m’zochita za anthu amayankha mafunso aakulu onena za zoipa amene akanakhala osayankhidwa. Mwachitsanzo, talingalirani ndemanga iyi yochokera mu International Herald Tribune yonena za nkhondo yosalekeza ya ku Balkans: “Gulu la ofufuza la bungwe la European Community latsimikizira kuti [asilikali] agwirira chigololo akazi ndi asungwana Achisilamu okwanira 20,000 . . . monga mbali ya dongosolo lolinganizidwa kuwawopseza, kuwanyazitsa ndi kuwakakamiza kuthaŵa kwawo.”

Nkhani ya m’magazini a Time inayesayesa kufotokoza kuti: “Nthaŵi zina, anyamata a kunkhondo angagwirire chigololo kuti akondweretse akuluakulu awo, oyang’anira awo, ndi kupeza mtundu wa unansi wa mwana ndi atate. Kugwirira chigololoko kuli umboni wa kumamatira kwawo ku kuwopsa kwa kagulu kawo. Mnyamata wofunitsitsa kuchita zinthu zoipa wagonjetsa chikumbumtima chake kuti agwirizane ndi zifuno zosasintha za gulu. Munthu amatsimikizira kumvera kwake mwa kuchita nkhanza.”

Koma kodi nchifukwa ninji “zifuno zosasintha za gulu” zili zoluluzika kwambiri kuposa zikumbumtima za mamembala ake? Monga munthu payekha, pafupifupi aliyense amakhumba kukhala pamtendere ndi mnansi wake. Chotero nchifukwa ninji, panthaŵi ya nkhondo, anthu amagwirira chigololo, kuzunza, ndi kuphana wina ndi mnzake? Chifukwa chachikulu nchakuti magulu a ziŵanda ali pantchito.

Kudziŵa thayo la ziŵanda kumaperekanso yankho la limene ena amalitcha “vuto la katswiri wa maphunziro azaumulungu.” Vutolo ndi la mmene angagwirizanitsire malingaliro atatu awa: (1) Mulungu ngwamphamvu zonse; (2) Mulungu ngwachikondi ndipo ngwabwino; ndi (3) zinthu zoipa kwambiri zimachitika. Ena amalingalira kuti nkotheka kugwirizanitsa malingaliro aŵiri alionse a ameneŵa, koma atatu onsewa sangagwirizanitsidwe konse. Mawu a Mulungu enieniwo amapereka yankho, ndipo yankholo limaloŵetsamo mizimu yosaoneka, nthumwi za zoipa.

Wopanduka Woyamba

Baibulo limatiuza kuti Mulungu mwiniyo ndimzimu. (Yohane 4:24) M’kupita kwanthaŵi anakhala Mlengi wa mamiliyoni a zamoyo zina zauzimu, ana aungelo. M’masomphenya, mtumiki wa Mulungu wotchedwa Danieli anaona angelo mamiliyoni zana limodzi. Anthu onse auzimu amene Yehova analenga anali olungama ndi ogwirizana ndi chifuniro chake.​—Danieli 7:10; Ahebri 1:7.

Pambuyo pake, pamene Mulungu ‘anaika maziko a dziko lapansi,’ ana aungelo a Mulungu ameneŵa ‘anaimba limodzi mokondwera’ ndipo “anafuula ndi chimwemwe.” (Yobu 38:4-7) Koma mmodzi wa iwo anakulitsa chikhumbo cha kulanda kulambira kumene moyenerera kunali kwa Mlengi. Mwa kupandukira Mulungu, mngelo ameneyu anadzipanga kukhala satana (kutanthauza “wotsutsa”) ndi mdyerekezi (kutanthauza “woneneza”).​—Yerekezerani ndi Ezekieli 28:13-15.

Akumagwiritsira ntchito njoka mu Edene kulankhula ndi mkazi woyamba, Hava, Satana anamuumiriza kusamvera lamulo lachindunji la Mulungu la kusadya chipatso cha mtengo wina wa m’mundamo. Pambuyo pake, mwamuna wake anagwirizana naye. Motero, anthu aŵiri oyambawo anagwirizana ndi mngeloyo m’kupandukira Yehova.​—Genesis 2:17; 3:1-6.

Pamene kuli kwakuti zochitika za mu Edene zingaonekere kukhala phunziro lomvekera bwino la kumvera, nkhani zofunika ziŵiri za makhalidwe zinadzutsidwa pamenepo ndi Satana. Yoyamba, Satana anatsutsa kaya ngati ulamuliro wa Yehova pa zolengedwa zake unachitidwa molungama ndi mozipindulitsa. Mwinamwake anthu angachite bwino kwambiri kudzilamulira okha. Yachiŵiri, Satana anakayikira ngati cholengedwa chaluntha chilichonse chingakhalebe chokhulupirika ndi chomvera kwa Mulungu pamene kumvera kuonekera kukhala kosabweretsa mapindu akuthupi.a

Kumvetsetsa bwino nkhani zodzutsidwa mu Edene, limodzi ndi chidziŵitso cha mikhalidwe ya Yehova, zimatithandiza kumvetsetsa yankho la “vuto la katswiri wa maphunziro azaumulungu,” lija la kuyanjanitsa kukhalapo kwa zoipa ndi mikhalidwe ya Mulungu ya mphamvu ndi chikondi. Pamene kuli kwakuti nzowona kuti Yehova ali ndi mphamvu zopanda polekezera ndi kuti ndiye chikondi chenicheni, iye alinso wanzeru ndi wolungama. Amasonyeza mikhalidwe inayi imeneyi molinganizika bwino. Motero, iye sanagwiritsire ntchito mphamvu yake yosapeŵeka kuwononga opanduka atatuwo panthaŵi yomweyo. Chimenecho chikanakhala chinthu cholungama koma osati kwenikweni chanzeru kapena cha chikondi. Ndiponso, iye sanangokhululukira ndi kuiwala, njira imene ena angaganize kuti ikanakhala njira yachikondi. Kuchita zimenezo sikukanakhala kwanzeru kapena kolungama.

Panafunikira nthaŵi kuthetsa nkhani zimene Satana anadzutsa. Kukatenga nthaŵi kutsimikizira kaya ngati anthu angadzilamulire bwino popanda kudalira pa Mulungu. Mwa kulola opanduka atatuwo kupitiriza kukhala ndi moyo, Yehova anakupanganso kukhala kotheka kwa zolengedwa kukhala ndi phande m’kutsimikizira zonena za Satana kukhala zonama mwa kutumikira Mulungu mokhulupirika pansi pa mikhalidwe yovuta.b

Yehova anali atanena momvekera bwino kwa Adamu ndi Hava kuti ngati adya chipatso choletsedwacho, iwo akafa. Ndipo anafadi, ngakhale kuti Satana anali atatsimikizira Hava kuti sadzafa. Satana nayenso ali pansi pa chilango cha imfa; pakali pano akupitiriza kusokeretsa mtundu wa anthu. Kwenikweni, Baibulo limati: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.”​—1 Yohane 5:19; Genesis 2:16, 17; 3:4; 5:5.

Angelo Ena Apanduka

Pasanapite nthaŵi yaitali pambuyo pa zochitika za mu Edene, angelo ena anagwirizana m’kupandukira ulamuliro wa Yehova. Baibulo limati: “Ndipo panali pamene anthu anayamba kuchuluka padziko, ndi ana aakazi anawabadwira iwo, kuti ana aamuna a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.” M’kunena kwina, angelo ameneŵa “anasiya pokhala pawopawo [kumwamba]” nabwera padziko lapansi, navala matupi aumunthu, ndipo anasangalala ndi zosangulutsa zachisembwere ndi akazi.​—Genesis 6:1, 2; Yuda 6.

Cholembedwacho chikupitiriza pa Genesis 6:4 kuti: “Padziko lapansi panali [Anefili, NW] masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu ataloŵa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.” Ana a makolo amitundu iŵiri ameneŵa amene anabadwa kwa akazi ndi atate aungelowo anali anyonga yoposa yachibadwa, “anthu amphamvu.” Anali amuna achiwawa, kapena Nephi·limʹ, liwu Lachihebri limene limatanthauza kuti “awo amene amachititsa ena kugwa.”

Nkofunika kudziŵa kuti zochitika zimenezi zinafotokozedwanso pambuyo pake m’nthano za anthu amakedzana. Mwachitsanzo, nthano yokhalako kwa zaka 4,000 yofotokoza mbiri ya Babulo imafotokoza zochita zamphamvu za Gilgamesh, munthu amene theka ali mulungu, wachiwawa chowopsa amene “chikhumbo chake cha chisembwere [sichinasiye] namwali aliyense kwa bwenzi lake.” Chitsanzo china, chochokera ku nthano Zachigiriki, ncha munthu wonga waumulungu Hercules (kapena Heracles). Hercules amene anabadwa kwa munthu wotchedwa Alcmene, ndi atate waumulungu Zeus, anayamba mkupiti wachiwawa pambuyo pakupha mkazi wake ndi ana m’mikangano ya misala. Ngakhale kuti nthano zotero zinapotozedwa kwambiri pamene zinapatsiridwa kumbadwo ndi mbadwo, izo zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena ponena za Anefili ndi atate awo aungelo opanduka.

Chifukwa cha chisonkhezero cha angelo oipa ndi ana awo onga aumulungu, dziko lapansi linadzaza ndi chiwawa kotero kuti Yehova anasankha kuwononga dziko ndi chigumula chachikulu. Anefili anawonongedwa pamodzi ndi anthu onse osapembedza; anthu okha amene anapulumuka anali Nowa wolungamayo ndi banja lake.​—Genesis 6:11; 7:23.

Komabe, angelo oipawo sanafe. Mmalomwake, anavula matupi awo aumunthu nabwerera kumalo a mizimu. Chifukwa cha kusamvera kwawo, sanaloledwe kubwerera m’banja la Mulungu la angelo olungama; ndiponso sanaloledwenso kuvala matupi aumunthu monga momwe anachitira m’tsiku la Nowa. Chikhalirechobe, iwo anapitirizabe kukhala ndi chisonkhezero chosakaza m’zochita za anthu, pansi pa ulamuliro wa “mkulu wa ziŵanda,” Satana Mdyerekezi.​—Mateyu 9:34; 2 Petro 2:4; Yuda 6.

Adani a Anthu

Satana ndi ziŵanda nthaŵi zonse akhala ambanda ndi ankhanza. Mwanjira zosiyanasiyana, Satana anachotsa ziŵeto za Yobu ndipo anapha ambiri a atumiki ake. Kenako, iye anapha ana khumi a Yobu mwa kuchititsa “mphepo yaikulu” kugwetsa nyumba imene anali mkati mwake. Pambuyo pa zimenezo, Satana anakantha Yobu ndi “zilonda zowawa, kuyambira ku phazi lake kufikira pakati pamutu pake.”​—Yobu 1:7-19; 2:3, 7.

Ziŵanda zimasonyeza mkhalidwe woipa wofananawo. M’tsiku la Yesu, zinaletsa anthu kulankhula ndi kuona. Zinachititsa mwamuna wina kudzitematema ndi miyala. Zinagwetsera pansi mnyamata wina ndi “kumng’ambitsa.”​—Luka 9:42; Mateyu 9:32, 33; 12:22; Marko 5:5.

Malipoti ochokera padziko lonse akusonyeza kuti Satana ndi ziŵanda adakali anjiru monga kale. Anthu ena amawakantha ndi matenda. Ena amawasautsa mwa kuwalanda tulo kapena mwa kuwalotetsa maloto owopsa kapena mwa kuwavutitsa mwa kuwagona. Enabe awachititsa misala, kukhala ambanda, kapena kudzipha.

Kodi Adzalekereredwa kwa Utali Wotani?

Satana ndi ziŵanda zake sadzalekereredwa kosatha. Pali chifukwa chabwino chimene Yehova wawalolera kukhalapo kufikira tsiku lathu, koma tsopano nthaŵi yawo yafupika. Kuchiyambi m’zaka za zana lino, sitepe lalikulu linatengedwa kuchepetsa malo awo a ntchito. Buku la Chivumbulutso likulongosola kuti: “Munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli [Yesu Kristu woukitsidwa] ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka [Satana]; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.”​—Chivumbulutso 12:7-9.

Kodi chotulukapo chinali chiyani? Cholembedwacho chikupitiriza kuti: “Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo.” Angelo olungamawo akanakondwera chifukwa chakuti Satana ndi ziŵanda zake sanalinso kumwamba. Koma bwanji ponena za anthu padziko lapansi? Baibulo limanena kuti: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.”​—Chivumbulutso 12:12.

Mu mkwiyo wawo Satana ndi atumiki ake ali okonzekera kuchititsa masoka ochuluka monga momwe angathere mapeto awo oyandikirawo asanafike. M’zaka za zana lino pakhala nkhondo zadziko ziŵiri ndi nkhondo zazing’ono zoposa 150 chiyambire mapeto a nkhondo yadziko yachiŵiri. Mu mpambo wathu wa mawu mwabwera mawu osonyeza chiwawa cha mbadwo uno onga awa: “nkhondo yomenyana mwa kugwiritsira ntchito tizilombo topatsa matenda,” “Chipiyoyo,” “mabwalo ophera anthu,” “misasa yogwiririra chigololo,” “opha anthu motsatizanatsatizana kwa nyengo yaitali,” ndi “bomba.” Nkhani zimadzaza ndi mbiri zonena za anamgoneka, mbanda, kuphulitsa mabomba, kudya anthu kochitidwa ndi amisala, kupululutsa anthu, njala, ndi kuzunza.

Mbiri yabwino njakuti zinthu zimenezi nzakanthaŵi. Posachedwapa mtsogolomu, Mulungu adzachitaponso kanthu molimbana ndi Satana ndi ziŵanda zake. Akumalongosola masomphenya ochokera kwa Mulungu, mtumwi Yohane anati: “Ndipo ndinaona mngelo anatsika kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi, namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi.”​—Chivumbulutso 20:1-3.

Pambuyo pa zimenezo, Mdyerekezi ndi ziŵanda zake ‘adzamasulidwa kanthaŵi,’ ndiyeno adzawonongedwa kosatha. (Chivumbulutso 20:3, 10) Imeneyo idzakhala nthaŵi yabwino chotani nanga! Satana ndi ziŵanda zake atachotsedwa kotheratu, Yehova adzakhala “zonse mu zonse.” Ndipo mowonadi aliyense “adzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—1 Akorinto 15:28; Salmo 37:11.

[Mawu a M’munsi]

a Mfundo imeneyi inamveketsedwa bwino pambuyo pake pamene Satana ananena za Yobu mtumiki wa Mulungu kuti: “Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake. Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.”​—Yobu 2:4, 5.

b Kuti mupeze kukambitsiridwa kwatsatanetsatane kwa chifukwa chimene Mulungu walolera kuipa, onani buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi munthu yekha ndiye ali ndi thayo kaamba ka zinthu zoterezi, kapena kodi mphamvu ina yoipa, yosaoneka ikuphatikizidwa m’mlanduwu?

[Mawu a Chithunzi]

Zitsime zamafuta zikupsa ku Kuwait, 1991: Chamussy/​Sipa Press

[Chithunzi patsamba 7]

Idzakhala nthaŵi yabwino chotani nanga pamene ziŵanda sizidzavutitsanso mtundu wa anthu!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena