Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 2/15 tsamba 22-25
  • Musayandikire Pamene Muona Ngozi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musayandikire Pamene Muona Ngozi
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mwamuna Amene Anakhala Mumkhalidwe Wangozi
  • Kukhala Patali ndi Ngozi
  • Kuwonjoka ndi Kutalikana ndi Ngozi
  • Mkazi wa Loti Anacheuka
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kumbukirani Mkazi wa Loti
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Konzekerani Kaamba ka Chipulumutso Kuloŵa M’dziko Latsopano
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Tizithandiza Anthu Amene Ali ndi Nkhawa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 2/15 tsamba 22-25

Musayandikire Pamene Muona Ngozi

AMALINYERO amadziŵa bwino kwambiri za ngozi koposa anthu ambiri. Iwo ayenera kukhala maso pakachedwe kakunja, mafunde, ndi kuyandikira kugombe kwa sitima yawo ya panyanja. Pamene mafunde ndi mphepo yomwe zikankhira sitimayo chakugombe, amalinyero amayang’anizana ndi ntchito yovuta kwambiri ndi ngozi.

Atakhala m’mikhalidwe imeneyi​—yodziŵika kukhala yangozi​—mmalinyero amayesayesa kutalikirana ndi gombe, makamaka ngati sitimayo imangoyendetsedwa ndi mphepo yokha. Buku la malangizo aumalinyero likufotokoza kuti ‘kugwidwa mumkuntho pagombe la ngozi mwinamwake ndiko vuto loipitsitsa’ limene mmalinyero angakhale nalo. Kodi nchinthu chabwino chotani chimene mungachite? ‘Musalole chombo chanu kuloŵa mumkhalidwe woipitsitsa wotero.’ Njira yotetezereka kuti mupeŵetse chombo kuloŵa mumchenga kapena kupita kugombe la mathanthwe ndiyo kutalikirana ndi ngoziyo.

Akristu ayenera kudziŵa ngozi zimene zingaswe chikhulupiriro chawo. (1 Timoteo 1:19) Masiku ano, mikhalidwe njovuta kwa munthu kuti asungebe njira yosasintha. Monga momwe bwato lingakankhidwire ndi mphepo ndi mafunde, choteronso miyoyo yathu yopatuliridwayi ingathe kutayikiridwa ndi njira chifukwa cha kulimbana kwathu kosalekeza ndi thupi lathu lopanda ungwiro ndi kukantha kosaleka kwa mzimu wa dziko​—kumene tsopano mphamvu yake ili yofanana ndi chimphepo chachikulu.

Mwamuna Amene Anakhala Mumkhalidwe Wangozi

Nkosavuta chotani nanga kuloŵa mosadziŵa m’madzi auzimu angozi!

Lingalirani za chitsanzo chimene chinachitika pafupi ndi madzi osayenda a Nyanja Yakufa. Tikunena za chitsanzo cha Loti. Chosankha chake cha kukhala mu Sodomu chinamdzetsera mavuto ambiri ndi chisoni chachikulu. Pambuyo pa mkangano wa abusa awo, Abrahamu ndi Loti anavomerezana kukhala m’madera osiyana. Timauzidwa kuti Loti anasankha Chigawo cha Yordano namanga hema wake pakati pa mizinda ya Chigawocho. Pambuyo pake, iye anasankha kukhala mu Sodomu, ngakhale kuti njira ya moyo wa Asodomu inamvutitsa maganizo.​—Genesis 13:5-13; 2 Petro 2:8.

Kodi nchifukwa chiyani Loti anapitirizabe kukhala m’mzinda wotchuka kwambiri ndi chisembwere umene unakwiyitsa kwambiri Yehova ndi kuchititsadi mfuu ya anthu okhala pafupi nawo? Sodomu anali wachuma, ndipo mosakayikira mkazi wa Loti anasangalala ndi mapindu a zinthu zakuthupi a moyo wa m’mzindawo. (Ezekieli 16:49, 50) Mwinamwake ngakhale Loti anakopeka ndi chuma chambiri cha Sodomu. Chilichonse chimene chingakhale chifukwa chake chokhalira kumeneko, iye anafunikira kuchokako mwamsanga koposa mmene anachitira. Banja la Loti potsirizira pake linachoka m’dera la ngozilo kokha litaumirizidwa mofulumira ndi angelo a Yehova.

Cholembedwa cha Genesis chimati: “Pamene kunacha, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako aakazi aŵiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m’mphulupulu ya mudzi.” Komabe ngakhale chenjezo loumirizalo litaperekedwa, Loti “anachedwa.” Potsirizira pake angelowo “anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake aakazi aŵiri; . . . ndipo anamtulutsa iye, namuika kunja kwa mudzi.”​—Genesis 19:15, 16.

Ali kunja kwa mzindawo, angelowo anapatsa banja la Loti malangizo ena otsiriza kuti: “Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa pali ponse; thaŵira kuphiri, kuti unganyeke.” (Genesis 19:17) Komabe ngakhale panthaŵiyo, Loti anapempha chilolezo cha kupita kumzinda wa Zoari wokhala pafupi mmalo mwa kuchoka kotheratu m’chigawocho. (Genesis 19:18-22) Mwachionekere, Loti anali wosafunitsitsa kutalikirana kwambiri ndi ngozi.

Paulendo wake wa ku Zoari, mkazi wa Loti anayang’ana kumbuyo ku Sodomu, mwachionekere akumalakalaka zinthu zimene anali atasiya. Chifukwa cha kunyalanyaza malangizo a angelo, iye anatayikiridwa ndi moyo wake. Loti​—munthu wolungamayo​—anapulumuka pachiwonongeko cha mzindawo limodzi ndi ana ake aŵiri aakazi. Koma ndimtengo waukulu chotani nanga umene iye analipirira chifukwa cha kusankha kukhala pafupi ndi ngozi!​—Genesis 19:18-26; 2 Petro 2:7.

Kukhala Patali ndi Ngozi

Chokumana nacho chopweteka cha Loti chimasonyeza zimene zingachitike ngati tiyandikira kwambiri kapena tizengereza kuchitapo kanthu pamalo angozi. Nzeru ikatiuza, mofanana ndi amalinyero odziŵa, kuti sitiyenera kudzilola ife eni kuloŵa m’mkhalidwe wowopsa wotero. Kodi ndimbali zina ziti zimene zili zangozi zimene tiyenera kutalikirana nazo? Akristu ena asokera mwa kuloŵerera kwambiri m’machitachita a bizinesi, mwa kukulitsa maunansi athithithi ndi atsamwali akudziko, kapena mwa kukhala okondana kwambiri ndi mwamuna kapena mkazi pamene ali osakhoza kuloŵa muukwati.

Njira yanzeru, m’chochitika chilichonsecho, ndiyo ya kutalikirana ndi ngozi. Mwachitsanzo, kodi timakhala amaso pangozi yauzimu imene ilipo pa yotchedwa kuti mipata yabwino ya bizinesi imene ingadze? Abale ena adziloŵetsa m’timagulu tamalonda mwa kuika pachiswe mabanja awo, thanzi lawo, ndi mathayo awo ateokratiki. Nthaŵi zina chokopa ndicho njira ya moyo wabwino kwambiri imene ndalama zingadzetse. Panthaŵi zina ndicho chitokoso cha kusonyeza kukhoza kwawo kuchita bizinesi. Ena angalingalire kuti cholinga chawo ndicho cha kugaŵira mwawi wantchito kwa abale ena kapena kukhala okhoza kupereka zopereka zowonjezereka kwambiri za ntchito ya padziko lonse. Mwinamwake amaganiza kuti pamene bizinesiyo ikuyenda bwino, adzakhala ndi nthaŵi yambiri yopereka kuzinthu Zaufumu.

Kodi nziti zimene zili mbuna zina? Mkhalidwe wosatsimikizirika wazachuma ndi “zochitika zosaonedweratu” zingathetse makonzedwe abwino koposa abizinesi. (Mlaliki 9:11, NW) Kulimbana ndi ngongole yaikulu kwambiri kungadzetse mavuto ndipo kungaphimbe zinthu zauzimu. Ndipo ngakhale pamene bizinesiyo ikupita patsogolo, mwachionekere idzatenga nthaŵi yochuluka ndi nyonga za maganizo, ndipo ingafune kuyanjana kwakutikwakuti ndi mabwenzi akudziko.

Mkulu wina Wachikristu ku Spain anali m’mavuto aakulu azachuma pamene kampani ya inshuwalansi inampatsa lonjezo loyesa. Ngakhale kuti panali ziyembekezo za kupanga ndalama zambiri monga nthumwi ya inshuwalansi yodziimira, potsirizira pake anakana mwaŵiwo. “Chinali chosankha chovuta, koma ndikukondwera kuti ndinakana,” iye akufotokoza motero. “Choyamba, ndinali wosafunitsitsa kupanga ndalama​—ngakhale mwanjira yosakhala yachindunji​—kupyolera mwa mabwenzi anga ateokratiki. Ndipo ngakhale ndinakonda lingaliro la kukhala wodziimira, ndikanafunikira kuyenda maulendo ambiri ndi kuthera maola ambiri pantchitoyo. Mosakayikira konse zikanandichititsa kunyalanyaza banja langa ndi mpingo. Koposa zonsezo, ndikukhulupirira kuti ndikanavomera ntchitoyo, ndikanalephera kulamulira moyo wanga.”

Palibe Mkristu amene angalekerere kulamulira moyo wake. Yesu anasonyeza zotulukapo zatsoka za njira yotero mwa kusimba fanizo la munthu amene anadzikundikira chuma chambirimbiri kotero kuti apume pantchito ndi kusangalala ndi moyo. Koma usiku womwe analingalira kuti anali atasonkhanitsa ndalama zambiri, anafa. “Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu,” Yesu anachenjeza motero.​—Luka 12:16-21; yerekezerani ndi Yakobo 4:13-17.

Tiyeneranso kukhala maso ndi mayanjano owonjezereka ndi anthu akudziko. Mwinamwake angakhale mnansi woyandikana naye, bwenzi la kusukulu, wantchito mnzathu, kapena wochita naye bizinesi. Ife tingalingalire kuti: ‘Amalemekeza Mboni, ali ndi mikhalidwe yabwino, ndipo nthaŵi zina timakambitsirana za chowonadi.’ Komabe, zokumana nazo za ena zasonyezadi kuti m’kupita kwa nthaŵi tingayambe kukonda mabwenzi akudziko otero koposa abale kapena alongo athu auzimu. Kodi ndiziti zimene zili ngozi zina za ubwenzi wotero?

Ife tingayambe kunyalanyaza kufulumira kwa nthaŵi zimene tikukhalamo kapena kukulitsa chikondwerero m’zinthu zakuthupi koposa zinthu zauzimu. Mwinamwake, chifukwa cha kuopa kusakondweretsa mabwenzi athu akudziko, tingalakalakedi kulandiridwa ndi dziko. (Yerekezerani ndi 1 Petro 4:3-7.) Kumbali ina, wamasalmo Davide anakonda kuyanjana ndi anthu amene anakonda Yehova. “Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga: pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani,” iye analemba motero. (Salmo 22:22) Tidzatetezeredwa ngati titsanzira chitsanzo cha Davide, tikumafunafuna ubwenzi umene ungatimangirire mwauzimu.

Njira ina yangozi ndiyo ija ya kukondana motengeka maganizo ndi mwamuna kapena mkazi pamene munthuyo ali wosakhoza kuloŵa muukwati. Ngozi yake ingabuke pamene munthu akopeka ndi wina amene ali wokongola, amene amanena zinthu mosonkhezera mtima, ndi amene ali ndi mikhalidwe yofanana ndi kulankhula zinthu moseketsa mofanana naye. Munthu angasangalale ndi kuyanjana naye kwake, akumalingalira kuti, ‘Ndimadziŵa malire ake. Tangokhala mabwenzi chabe.’ Chikhalirechobe, malingaliro atangodzutsidwa ngovuta kuwalamulira.

Mary, mkazi wina wachichepere wokwatiwa, anakonda kuyanjana ndi Michael.a Iye anali mbale wabwino koma kunali komuvuta kupeza mabwenzi. Anali ndi malingaliro ofanana m’zinthu zambiri, ndipo onsewo ankachita nthabwala. Mary anakondwa poganiza kuti mbale amene ali mbeta anafuna kumuululira zakukhosi. Posapita nthaŵi, zimene zinaonekera ngati ubwenzi wamba zinakhala kukondana kwakukulu. Iwo anathera nthaŵi yowonjezereka pamodzi ndipo potsirizira pake anachita chisembwere. “Ndinayenera kuzindikira ngozi yake pachiyambi pomwe,” Mary akuusa moyo motero. “Pamene ubwenziwo unayamba kukula, unakhala ngati mchenga womatichititsa kutitimiramo kwambiri.”

Sitiyenera kuiŵala konse chenjezo la Baibulo lakuti: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziŵa?” (Yeremiya 17:9) Mtima wathu wonyengawu, monga funde limene limakankhira ngalaŵa kumathanthwe, ungatikankhire m’maunansi otengeka maganizo atsoka. Mankhwala ake? Ngati muli wosakhoza kuloŵa muukwati, yesayesani mwadala kutalikirana mwamalingaliro ndi munthu amene mumakopeka naye.​—Miyambo 10:23.

Kuwonjoka ndi Kutalikana ndi Ngozi

Bwanji ngati tili kale m’ngozi yauzimu? Amalinyero, pamene akankhiridwa kugombe lamathanthwe ndi mphepo ndi mafunde, amayesayesa mwakhama kutembenuzira ngalawa zawozo kunyanja, kapena kubwerera kumene mphepo ikuchokera, kufikira atafika pamalo otetezereka. Mofananamo, tiyenera kumenya nkhondo kuti tidziwonjole. Mwa kulabadira uphungu wa Malemba, kupempherera mwakhama chithandizo cha Yehova, ndi kufunafuna chithandizo kuchokera kwa abale Achikristu achidziŵitso, tikhoza kubwereranso panjira yotetezereka. Kachiŵirinso tidzadalitsidwa ndi mtendere wamaganizo ndi mtima.​—1 Atesalonika 5:17.

Mulimonse mmene mikhalidwe yathu iliri, timakhala anzeru kutalikirana ndi “miyambo ya dziko lapansi.” (Agalatiya 4:3) Mosiyana ndi Loti, Abrahamu anasankha kutalikirana ndi Akanani adziko, ngakhale kuti kumeneku kunatanthauza kukhala m’mahema kwazaka zambiri. Mwinamwake iye analibe zinthu zina zabwino zakuthupi, koma moyo wake wosafuna zambiriwo unamtetezera mwauzimu. Mmalo mwa kusweka kwa chikhulupiriro chake, iye anakhala “kholo la onse akukhulupira.”​—Aroma 4:11.

Monga momwe tazingidwira ndi dziko lodzimwerekeretsamu limene “mzimu” wake uli wamphamvu nthaŵi zonse, tifunikira kutsatira chitsanzo cha Abrahamu. (Aefeso 2:2) Ngati tivomereza chitsogozo cha Yehova m’nkhani zonse, tidzadalitsidwa mwa kulandira mwachindunji chitetezero chake chachikondi. Tidzalingalira monga momwe Davide anachitira kuti: “Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m’mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake. Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga: ndipo ndidzakhala m’nyumba ya Yehova masiku onse.” Palibe kukayikira ponena za zimenezo, kuyenda “m’mabande a chilungamo,” mmalo mwa kupatukira panjira ya ngozi, kudzadzetsa madalitso osatha.​—Salmo 23:3, 6.

[Mawu a M’munsi]

a Maina ena asinthidwa.

[Chithunzi patsamba 24]

Ngati muli wosakhoza kuloŵa muukwati, talikiranani mwamalingaliro ndi munthu wina amene mumakopeka naye

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena