Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 3/15 tsamba 21-23
  • “Dyetsani Pakamwa, Osati Mapazi”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Dyetsani Pakamwa, Osati Mapazi”
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Miyambo Yoikira Maliro
  • Zikhulupiriro Zamwambo za mu Afrika
  • Zimene Baibulo Limanena
  • Kodi Nkukhaliranji Osiyana?
  • Kodi Akufa Ayenera Kulemekezedwa?
    Galamukani!—1999
  • Kaonedwe Kachikristu ka Miyambo ya Maliro
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kodi Makolo Athu Ali Kuti?
    Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?
  • Samalani ndi Miyambo Imene Mulungu Sakondwera Nayo
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 3/15 tsamba 21-23

“Dyetsani Pakamwa, Osati Mapazi”

Kupenda Miyambo Yoika Maliro ya mu Afrika

“SAMAIKA akufa awo!” Imeneyi ndi ndemanga imene imanenedwa mofala ponena za Mboni za Yehova ku West Africa. Komabe, nkodziŵika bwino lomwe kuti kwenikwenidi, Mboni zimaika akufa awo.

Kodi nchifukwa ninji anthu amanena kuti Mboni za Yehova sizimaika akufa awo? Amatero chifukwa chakuti Mboni sizimachita miyambo yambiri yofala yoikira maliro yakumaloko.

Miyambo Yoikira Maliro

Aliu amakhala m’mudzi waung’ono m’chigawo cha Pakati pa Nigeria. Pamene amake anamwalira, iye anadziŵitsa achibale ake za imfayo ndiyeno anapanga makonzedwe kuti nkhani ya Malemba ikambidwe m’nyumba mwa amakewo. Nkhaniyo inakambidwa ndi mkulu wa mpingo wa Mboni za Yehova wakumaloko, ndipo inafotokoza za mkhalidwe wa akufa ndi chiyembekezo chotonthoza mtima cha chiukiriro chotchulidwa m’Baibulo. Pamapeto pa nkhaniyo, amake Aliu anaikidwa.

Achibale anakwiya kwambiri. Kwa iwo kuika maliro kumakhala kosakwanira popanda mchezo, kaŵirikaŵiri umene umachitidwa usiku wotsatira pamene munthuyo wafa. M’mudzi mwa Aliu mchezo umakhala nthaŵi ya chikondwerero, osati kulira maliro. Mtembowo umasambitsidwa, kuvekedwa zoyera, ndi kugonekedwa pakama. Oferedwawo amaitanitsa oimba, kugula moŵa ndi zikho za vinyo wa ngole, ndi kupanga makonzedwe akuti ng’ombe kapena mbuzi iperekedwe nsembe. Ndiyeno achibalewo ndi mabwenzi amabwera kudzaimba, kuvina, kudya, ndi kudzamwa kufikira mbandakucha tsiku lotsatira.

Mkati mwa chikondwererocho, chakudya chimaikidwa kumapazi a mtembowo. Tsitsi, zikhadabo za zala zakumanja ndi za kumapazi zimadulidwa ndi kuikidwa pambali kaamba ka “kuika kwachiŵiri.” Kuikako kumachitika patapita masiku, milungu, kapena ngakhale zaka.

Patsiku lotsatira mchezowo, mtembowo umaikidwa, ngakhale kuti madzoma a maliro amapitiriza kwa mlungu umodzi kapena kuposapo. Pambuyo pake, kuika kwachiŵiriko kumachitika. Tsitsi, zikhadabo za zala zakumanja ndi zakumapazi zimakulungidwa m’kansalu koyera, kamene kamamangiriridwa ku kamtengo ka utali wa mamita 1.5 kapena 1.8. M’ligubo la kuimba ndi kuvina, kamtengoko kamanyamulidwa kupita kumanda ndi kukaika pafupi ndi munthu amene kakuimira. Kachiŵirinso, pamakhala kuimba, kumwa, ndi madyerero. Pomaliza chochitika cha malirocho, mfuti imawomberedwa kamodzi kumlengalenga.

Popeza kuti Aliu sanalole chilichonse cha zinthu zimenezi, anaimbidwa mlandu wakusalemekeza akufa kapena miyambo imene imawalemekeza. Koma kodi nchifukwa ninji Aliu, Mboni ya Yehova, anakana kugonjera mwambo? Chifukwa sakanavomereza ndi chikumbumtima chabwino malingaliro achipembedzo amene miyambo imeneyi yazikidwapo.

Zikhulupiriro Zamwambo za mu Afrika

Mu Afrika monse, anthu amakhulupirira kuti anthu onse anachokera kudziko la mizimu ndipo adzabwerera komweko. Anthu a fuko la Yoruba a ku Nigeria amati: “Dziko lapansi ndipamsika, pamene kumwamba ndiko kwathu.” Ndipo mwambi wa anthu a fuko la Igbo umati: “Aliyense wobwera m’dzikoli adzabwerera kwawo, mosasamala kanthu kuti munthuyo akhala kwanthaŵi yaitali motani padziko lapansi.”

Talingalirani za miyambo yomwe yatchulidwa kaleyo. Cholinga cha kuchezera ndicho kuperekeza bwino mzimu. Chovala choyera chimalingaliridwa kukhala chovala choyenerera kudziko la mizimu. Kuika chakudya kumapazi kuli kogwirizana ndi lingaliro lakuti mtembo umadya kudzera kumiyendo ndipo uyenera kudyetsedwa kuti usamve njala paulendo wake wopita kudziko la makolo.

Ndiponso, anthu onse mwachisawawa amakhulupirira kuti pamene mzimu utuluka m’thupi, umayendayenda pafupi ndi amoyo ndipo sumabwerera kwa makolo kufikira utamasulidwa ndi kuika kwachiŵiri. Kusiyapo kokha ngati kuika kwachiŵiriko kutachitidwa, anthu amawopa kuti mzimuwo udzakwiya ndi kukantha amoyo ndi mliri wa matenda kapena imfa. Kuwombera mfutiko kumachitidwa “kutumiza mzimuwo” kumwamba.

Ngakhale kuti miyambo ya maliro imasiyana kwambiri m’malo ndi malo mu Afrika, kaŵirikaŵiri lingaliro lalikulu ndilakuti mzimu umapulumuka imfa ya thupi. Cholinga chachikulu cha miyamboyo ndicho kuthandiza mzimuwo kuvomereza “chiitano cha kubwerera kwawo.”

Zikhulupiriro ndi machitachita ameneŵa zalimbikitsidwa ndi chiphunzitso cha Dziko Lachikristu cha kusafa kwa moyo wa munthu ndi kupembedza kwake “oyera mtima.” Yapadera ndiyo ndemanga ya mtsogoleri wina wachipembedzo wa gulu lankhondo ku Swaziland amene ananena kuti Yesu anadza, osati kudzawononga zikhulupiriro za mwambo, koma kudzazikwaniritsa kapena kutsimikiziritsa. Popeza kuti kaŵirikaŵiri atsogoleri achipembedzo amatsogolera pamadzoma oika maliro, anthu ambiri amaganiza kuti Baibulo limachirikiza ponse paŵiri zikhulupiriro za mwambo ndi madzoma ochitika pamenepo.

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Baibulo limachirikiza zikhulupiriro zimenezi? Ponena za mkhalidwe wa akufa, lemba la Mlaliki 3:20 limati: “Onse [anthu ndi nyama] apita kumalo amodzi; onse achokera m’fumbi ndi onse abwereranso kufumbi.” Malemba amapitiriza kunena kuti: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi . . . Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingalira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.”​—Mlaliki 9:5, 6, 10.

Malemba ameneŵa ndi ena amamveketsa bwino kuti akufa sangatione kapena kutimva kapena kutithandiza kapena kutivulaza. Kodi zimenezi sizogwirizana ndi zimene mwaona? Mungadziŵe za munthu wolemera ndi wotchuka amene anafa ndipo banja lake pambuyo pake linavutika, ngakhale kuti linachita madzoma onse a mwambo wa maliro. Ngati munthu ameneyo ali ndi moyo m’dziko la mizimu, nchifukwa ninji sathandiza banja lake? Iye sangatero chifukwa zimene Baibulo limanena nzowona​—akufa alibedi moyo, “afa, atha,” ndipo chotero sali okhoza kuthandiza aliyense.​—Yesaya 26:14.

Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, anadziŵa kuti zimenezi nzowona. Talingalirani zimene zinachitika Lazaro atafa. Baibulo limanena kuti: “[Yesu] ananena nawo [ophunzira ake], Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take. Chifukwa chake akuphunzira ake anati kwa iye, Ambuye, ngati ali m’tulo adzachira. Koma Yesu adanena za imfa yake.”​—Yohane 11:11-13.

Onani kuti Yesu anayerekezera imfa ndi tulo, kupumula. Pamene anafika ku Betaniya, anatonthoza alongo ake a Lazaro, Mariya ndi Marita. Pomva chisoni, Yesu analira. Komabe, iye sananene kapena kuchita chilichonse chimene chinapereka lingaliro lakuti Lazaro anali ndi mzimu umene unali udakali ndi moyo ndi kufuna thandizo kuti ufike ku dziko la makolo ake. Mmalomwake, Yesu anachita zimene ananena kuti akachita. Anaukitsa Lazaro ku tulo ta imfa mwa chiukiriro. Zimenezi zimapereka umboni wakuti pomalizira pake Mulungu akagwiritsira ntchito Yesu kuukitsa onse amene ali m’manda achikumbukiro.​—Yohane 11:17-44; 5:28, 29.

Kodi Nkukhaliranji Osiyana?

Kodi pali cholakwika ndi kutsatira madzoma amaliro amene ali ozikidwa pa zikhulupiriro zosakhala zamalemba? Aliu ndi mamiliyoni ena a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti chilipo. Amadziŵa kuti kukakhala kolakwa​—ngakhale konyenga​—kwa iwo kuchirikiza mchitidwe uliwonse wozikidwa mwachionekere pa ziphunzitso zonyenga ndi zosokeretsa. Iwo samafuna kukhala ngati alembi ndi Afarisi, amene Yesu anatsutsa chifukwa cha chinyengo chachipembedzo.​—Mateyu 23:1-36.

Mtumwi Paulo anachenjeza wogwira naye ntchito mnzake Timoteo kuti: “Koma mzimu anena monenetsa, kuti m’masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziŵanda, m’maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza.” (1 Timoteo 4:1, 2) Kodi lingaliro lakuti anthu akufa ali ndi moyo m’dziko la mizimu ndichiphunzitso cha ziŵanda?

Inde. Satana Mdyerekezi, “atate wake wa bodza,” anauza Hava kuti sakafa, akumasonyeza kuti akapitiriza kukhala ndi moyo m’thupi. (Yohane 8:44; Genesis 3:3, 4) Zimenezo sizinali zofanana ndi kunena kuti moyo wosafa umapitiriza kukhala ndi moyo pambuyo pa imfa ya thupi. Komabe, Satana ndi ziŵanda zake amayesayesa kupatutsa anthu pa chowonadi cha Mawu a Mulungu mwakuchirikiza lingaliro lakuti moyo umapitiriza kukhalako pambuyo pa imfa. Chifukwa chakuti zimakhulupirira zimene Mulungu amanena m’Baibulo, Mboni za Yehova sizimagwirizana ndi malingaliro ndi machitachita amene amachirikiza mabodza a Satana.​—2 Akorinto 6:14-18.

Mwa kupeŵa machitachita akuika maliro osakhala a m’malemba, atumiki a Yehova adedwa ndi amene sagwirizana ndi malingaliro awo. Mboni zina zamanidwa zoloŵa zosiyidwa ndi makolo awo. Zina zanyanyalidwa ndi mabanja awo. Komabe, monga Akristu owona, izo zimazindikira kuti kumvera Mulungu kokhulupirika kumabweretsa mkwiyo wa dziko. Mofanana ndi atumwi okhulupirika a Yesu Kristu, izo zili zotsimikiza mtima “kumvera Mulungu koposa anthu.”​—Machitidwe 5:29; Yohane 17:14.

Pamene kuli kwakuti amakondwera kukumbukira okondedwa awo amene agona tulo ta imfa, Akristu owona amayesayesa kusonyeza chikondi kwa amoyo. Mwachitsanzo, Aliu anatenga amake kumakhala nawo panyumba pake pamene abambo ake anamwalira ndipo anawadyetsa ndi kuwasamalira kwa moyo wawo wonse. Pamene ena anena kuti Aliu sanakonde amake chifukwa chakuti sanawaike mogwirizana ndi dzoma lofala, iye amatchula mwambi wofala pakati pa anthu ake wakuti: “Dyetsani pakamwa panga musanadyetse mapazi anga.” Kudyetsa pakamwa, kapena kusamalira munthu adakali ndi moyo, nkofunika kwambiri kuposa kudyetsa mapazi, mchitidwe wotchulidwa poyambapo wogwirizana ndi kuchita mchezo munthuyo atafa. Kwenikweni, kudyetsa mapazi sikumapindulitsa konse wakufayo.

Aliu amafunsa omsulizawo kuti, ‘Kodi mungakonde chiyani​—kuti banja lanu likusamalireni muukalamba wanu kapena kuti lidzachite phwando lalikulu mutamwalira?’ Ambiri amasankha kusamaliridwa adakali ndi moyo. Iwo amayamikiranso kudziŵa kuti pamene adzafa, adzakhala ndi nkhani ya chikumbukiro ya maliro yolemekezeka yozikidwa pa Baibulo ndi kuikidwa kwaulemu.

Zimenezo nzimene Mboni za Yehova zimakalimira kuchitira okondedwa awo. Izo zimadyetsa pakamwa, osati mapazi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena