Mboni za Yehova Padziko Lonse—Bahamas
COMMONWEALTH ya Bahamas—zisumbu zazikulu ndi zazing’ono zokwanira 3,000—zili monga unyolo wa m’khosi wa ngale wotantha makilomita 900 m’nyanja ya maonekedwe obiriŵira pakati pa Florida ndi Cuba. Pakati pa nzika zake 267,000 pamamveka nyimbo ya olengeza Ufumu. Nyimbo yawo yachitamando imakumbutsa lemba la Yesaya 42:10-12: “Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse zili mmenemo, zisumbu ndi okhala mommo. . . . Akuwe kuchokera pamwamba pa mapiri. Apereke ulemerero kwa Yehova, anene matamando ake m’zisumbu.”
Chikhulupiriro Chatsopano Chitokosedwa
Mu July 1992, mpainiya wina wokhazikika (mlaliki wa Ufumu wanthaŵi yonse) anagaŵira bwenzi lake la kuntchito chithandizo cha Baibulo chotchedwa Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Mwamunayo ataŵerenga bukulo, anati mumtima, ‘Ndiyenera kupenda chipembedzochi.’ Pa Masande aŵiri otsatira, iye anafika pamisonkhano pa Nyumba Zaufumu za Mboni za Yehova ziŵiri zosiyana. Kenako, anayambitsidwa phunziro la Baibulo. Komabe, patangopita milungu isanu ndi umodzi yokha ya kuphunzira kwake Baibulo, panabuka chitokoso chimene chikayesa chikhulupiriro chake chatsopano—mapwando a kukumbukira tsiku la kubadwa.
Banja la mwinibizinesiyo linali lotanganitsidwa kwambiri m’mapwando otero, koma kukonda kwake Mawu a Mulungu kunamsonkhezera kupitirizabe kuphunzira kwake Baibulo. Pamene chidziŵitso chake cha chowonadi cha Malemba chinakula, kuzindikira kwake nkhani ya mapwando a kukumbukira tsiku la kubadwa ndi maholide ena adziko ndi mmene Yehova amawaonera kunakulanso.
Pamene mkazi wa mwamuna ameneyu analinganiza kusonkhana kwamacheza kaamba ka Father’s Day (Tsiku Lolemekeza Atate), mwamunayo anakana mwaulemu kupezekapo. Komabe, mkaziyo analingalira kuti sakumkondanso ndi kuti anali kuika chipembedzo chake poyamba mmalo mwa mkaziyo ndi banja. Mwamunayo anafotokoza mokoma mtima kuti kugwiritsira ntchito zimene anali kuphunzira m’Baibulo kunali kumthandiza kusintha kukhala mwamuna ndi atate wabwinopo. Potsirizira pake, mkaziyo anayamba kuzindikira za chikondi cha mwamunayo cha chowonadi cha Malemba navomera kuphunzira Baibulo. Tsopano mwamunayo amachititsa phunziro la Baibulo ndi banja lake. Ndipo anasangalala chotani nanga pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Chiphunzitso Chaumulungu” chaka chathachi! Mkazi wake ndi mwana wawo wamkazi analipo ndipo anamuona akubatizidwa.
Alendo Amva Nyimbo Yatsopano
Alendo zikwi zambiri a ku Haiti akusakanizikana ndi anthu a ku Bahamas. Nawonso afunikira kumva nyimbo yatsopano ya chowonadi cha Ufumu. Mboni zokhala m’Bahamas zili zoyamikira kuti mabanja aŵiri, nzika za ku Haiti zokhala ku America zafika. Anthu ameneŵa athandiza kulimbitsa timagulu ta anthu a ku Haiti toumbidwa chatsopano pazisumbu za Grand Bahama ndi Abaco.
Monga chithandizo chinanso kwa anthu okondwerera uthenga wa Ufumu a ku Haiti, msonkhano wachigawo woyamba m’chinenero cha Creole m’Bahamas unachitika kuyambira pa July 31 kufikira August 1, 1993. Chiŵerengero cha ofikapo chinafika 214, limodzi ndi odzipatulira amene anabatizidwa chatsopano atatu. Nzika zambiri za ku Haiti zimene zinaphunzira chowonadi ku Bahamas kuyambira pamenepo zabwerera kuchisumbu chakwawo kapena zasamukira kumalo ena kukawonjezera mawu awo pakuimba chitamando kwa Yehova kochitidwa ndi Mboni zakomweko.
[Bokosi patsamba 8]
ZIŴERENGERO ZA DZIKOLO
Chaka Chautumiki cha 1993a
CHIŴERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OCHITIRA UMBONI: 1,294
KUGAŴA: Mboni 1 pa anthu 197
OFIKA PACHIKUMBUTSO: 3,794
AVAREJI YA OFALITSA AUPAINIYA: 186
AVAREJI YA MAPHUNZIRO A BAIBULO: 1,715
CHIŴERENGERO CHA OBATIZIDWA: 79
CHIŴERENGERO CHA MIPINGO: 22
OFESI YA NTHAMBI: NASSAU
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mupeze chidziŵitso chowonjezereka onani Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1994.
[Chithunzi patsamba 9]
Nyumba Yaufumu yoyamba, limodzi ndi ofesi ya nthambi ndi nyumba ya amishonale
[Chithunzi patsamba 9]
Mboni zimalalikira mbiri yabwino mwachangu
[Chithunzi patsamba 9]
Milton G. Henschel ndi Nathan H. Knorr ndi amishonale ku Nassau zaka pafupifupi 45 zapitazo
[Chithunzi patsamba 9]
Ofesi ya nthambi yatsopano, yopatuliridwa pa February 8, 1992