Olengeza Ufumu Ali Okangalika Padziko Lonse Lapansi
“Mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.”—MACHITIDWE 1:8.
1. Kodi ndi uthenga wotani umene Yesu ananena kuti otsatira ake akalengeza m’tsiku lathu?
POLONGOSOLA ntchito imene Yehova anatumizira Mwana wake kudzachita padziko lapansi, Yesu anati: “Kundiyenera ine ndilalikire uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:43) Mofananamo, ponena za ntchito imene ophunzira ake akaichita padziko lapansi pamene akabwerera ndi ulamuliro waufumu, Yesu anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:14.
2. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kuti uthenga wa Ufumu ufalitsidwe mokulira? (b) Kodi ndi funso lotani limene tonsefe tiyenera kudzifunsa?
2 Kodi nchifukwa ninji mbiri yonena za Ufumu wa Mulungu ili yofunika kwambiri? Kodi nchifukwa ninji Ufumuwo ukufunikira kufalitsidwa kwakukulu kotero? Chifukwa chakuti uli Ufumu Waumesiya umene udzalemekeza uchifumu wa Yehova wa chilengedwe chonse. (1 Akorinto 15:24-28) Mwa uwo, Yehova adzapereka chiweruzo motsutsana ndi dongosolo la zinthu lausatana ndi kukwaniritsa lonjezo lake la kudalitsa mabanja onse padziko lapansi. (Genesis 22:17, 18; Danieli 2:44) Mwa kuchititsa umboni wa Ufumuwo kuperekedwa, Yehova wapeza awo amene pambuyo pake waŵadzoza kukhala oloŵa nyumba limodzi ndi Mwana wake. Kupyolera mwa kulengezedwa kwa Ufumuwo, ntchito yolekanitsa ikuchitidwa lerolino. (Mateyu 25:31-33) Yehova akufuna kuti anthu a mitundu yonse adziŵitsidwe za chifuno chake. Akufuna kuti iwo akhale ndi mwaŵi wa kusankha moyo monga nzika za Ufumu wakewo. (Yohane 3:16; Machitidwe 13:47) Kodi mukukhala ndi phande lokwanira m’kulengeza Ufumu umenewu?
Kuyembekezera Mapeto a Nthaŵi za Akunja
3. (a) Moyenerera, kodi ndi nkhani yanji imene C. T. Russell anakamba paulendo wake woyambirira wokalinganiza timagulu tophunzira Baibulo? (b) Kodi Ophunzira Baibulo oyambirirawo anazindikira kuti Ufumu wa Mulungu unayenera kukhala ndi malo otani m’miyoyo yawo?
3 Kalelo mu 1880, Charles Taze Russell, mkonzi woyamba wa magazini a Watch Tower, anatenga ulendo wokayendera chigawo cha kumpoto koma chakummaŵa kwa United States kukalimbikitsa kupanga timagulu tophunzira Baibulo. Moyenerera, nkhani imene anakamba inali yakuti “Zinthu Zokhudza Ufumu wa Mulungu.” Monga momwe kunasonyezedwera m’makope oyambirira a Watch Tower, Ophunzira Baibulo (monga momwe Mboni za Yehova zinadziŵikira panthaŵiyo) anazindikira kuti ngati anati akhale oyenerera kukhala ndi phande mu Ufumu wa Mulungu, anayenera kupanga Ufumuwo kukhala chinthu chofunika koposa kwa iwo, akumagwiritsira ntchito miyoyo yawo mosangalala, maluso awo, ndi chuma chawo mu utumiki wake. Chinthu china chilichonse m’moyo chinafunikira kutenga malo achiŵiri. (Mateyu 13:44-46) Thayo lawo linaphatikizapo kulengeza kwa ena mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. (Yesaya 61:1, 2) Kodi iwo anachita zimenezo kufikira pamlingo wotani asanafike mapeto a Nthaŵi za Akunja mu 1914?
4. Kodi ndi kumlingo wotani umene kagulu ka Ophunzira Baibulo kanafalitsa mabuku ofotokoza Baibulo isanafike 1914?
4 Kuyambira mu 1870 mpaka kudzafika mu 1914, Ophunzira Baibulowo anali ocheperapo m’chiŵerengero. Pofika mu 1914, pafupifupi 5,100 okha ndiwo anali okangalika m’kupereka umboni wapoyera. Koma unali umboni wachilendo chotani nanga! Mu 1881, zaka ziŵiri zokha pambuyo pa kufalitsidwa kwa Watch Tower yoyamba, iwo anayamba kugaŵira buku la masamba 162 lakuti Food for Thinking Christians. M’miyezi yoŵerengeka chabe, anagaŵira makope 1,200,000. M’zaka zoŵerengeka, mamiliyoni makumi ambiri a matrakiti anali kugaŵiridwa m’zinenero zambiri.
5. Kodi akopotala anali ayani, ndipo ndi mzimu wotani umene anasonyeza?
5 Ndiponso kuyambira mu 1881, ena anadzipereka kutumikira monga alaliki aukopotala. Iwoŵa anali akalambula bwalo a apainiya a lerolino (alaliki anthaŵi yonse). Ena a akopotalawo, akumayenda pansi kapena panjinga, anachitira umboni mwaumwini pafupifupi m’mbali iliyonse ya dziko kumene anakhalako. Ena anadzipereka kupita kumaiko achilendo ndipo anali oyamba kupereka mbiri yabwino kumalo oterowo monga Finland, Barbados, ndi Burma (tsopano yotchedwa Myanmar). Iwo anasonyeza changu chaumishonale chofanana ndi cha Yesu Kristu ndi atumwi ake.—Luka 4:43; Aroma 15:23-25.
6. (a) Kodi maulendo a Mbale Russell ofalitsa chowonadi cha Baibulo anali aatali motani? (b) Kodi nchiyani china chimene chinachitidwa kupititsa patsogolo kulalikidwa kwa mbiri yabwino m’magawo achilendo mapeto a Nthaŵi za Akunja asanafike?
6 Mbale Russell iyemwini anayenda kwambiri kufalitsa chowonadi. Anapita ku Canada mobwerezabwereza; anakamba nkhani mu Panama, Jamaica, ndi Cuba; anayenda maulendo ambiri ku Ulaya; ndipo anazungulira mbulunga ya dziko paulendo wolalikira. Anatumizanso amuna ena kukayambitsa ndi kutsogolera ntchito yolalikira mbiri yabwino m’minda ya kumaiko achilendo. Adolf Weber anatumizidwa ku Ulaya pakati pa ma 1890, ndipo utumiki wake unafalikira kuchokera ku Switzerland mpaka mu France, Italy, Germany, ndi Belgium. E. J. Coward anatumizidwa ku dera la Caribbean. Robert Hollister anagaŵiridwa Kummaŵa mu 1912. Kumeneko, matrakiti apadera anakonzedwa m’zinenero khumi, ndipo mamiliyoni a makope ameneŵa anagaŵiridwa mu India yense, China, Japan, ndi Korea ndi nzika za kumeneko. Ngati mukadakhalako panthaŵiyo, kodi mtima wanu ukanakusonkhezerani kuyesayesa mwakhama kufikira ena m’chitaganya chanu ndi kumalo ena ndi mbiri yabwino?
7. (a) Kodi manyuzipepala anagwiritsiridwa ntchito motani kukulitsa umboni? (b) Kodi “Photo-Drama of Creation” inali chiyani, ndipo ndi anthu angati amene anaiona m’chaka chimodzi chokha?
7 Pamene Nthaŵi za Akunja zinali kufika kumapeto ake, manyuzipepala anagwiritsiridwa ntchito kufalitsa maulaliki a Baibulo operekedwa ndi Mbale Russell. Chigogomezero chawo chachikulu sichinali pa chaka cha 1914, mmalo mwake, chinali pa chifuno cha Mulungu ndi kutsimikizirika kwa kukwaniritsidwa kwake. Manyuzipepala ochuluka ofika 2,000 panthaŵi imodziyo, akumafikira oŵerenga 15,000,000, nthaŵi iliyonse anasonyeza maulaliki ameneŵa. Ndiyeno, pamene chaka cha 1914 chinali kufika, Sosaite inayamba kusonyeza poyera kanema ya “Photo-Drama of Creation.” M’zionetsero zinayi za maola aŵiri chilichonse, inasonyeza mfundo za chowonadi cha Baibulo kuyambira pakulenga mpaka mu Zaka Chikwi. M’chaka chimodzi chokha, omvetsera oposa mamiliyoni asanu ndi anayi mu North America, Ulaya, Australia, ndi New Zealand anali ataiona.
8. Pofika mu 1914, kodi ndi maiko angati amene anafikiridwa ndi Ophunzira Baibulo ndi mbiri yabwino?
8 Malinga ndi zolembedwa zimene zilipo, pofika chakumapeto kwa 1914, kagulu kachangu ka alaliki kameneka kanafalitsa chilengezo chawo cha Ufumu wa Mulungu m’maiko 68.a Koma zimenezo zinali chiyambi chabe!
Kulengeza Mwachangu Ufumu Wokhazikitsidwa
9. Pamisonkhano ya ku Cedar Point, kodi ndimotani mmene ntchito yochitira umboni Ufumu inapatsidwira chisonkhezero chapadera?
9 Pamene Ophunzira Baibulo anasonkhana ku Cedar Point, Ohio, mu 1919, J. F. Rutherford, yemwe panthaŵiyo anali prezidenti wa Watch Tower Society, analengeza kuti: “Ntchito yathu inali ndipo ili ya kulengeza ufumu wa Mesiya waulemerero umene ulinkudzawo.” Pamsonkhano wachiŵiri wa ku Cedar Point, mu 1922, Mbale Rutherford anagogomezera mfundo yakuti kumapeto kwa Nthaŵi za Akunja, mu 1914, ‘Mfumu ya ulemerero inadzitengera mphamvu yake yaikulu niyamba kulamulira.’ Ndiyeno, anapereka funso mwachindunji kwa omvetsera ake, akumati: “Kodi mukukhulupirira kuti Mfumu ya ulemerero yayamba ulamuliro wake? Pamenepo bwererani kumunda, inu ana a Mulungu Wam’mwambamwamba! . . . Lengezani uthengawo konsekonse. Dziko liyenera kudziŵa kuti Yehova ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye. Lino ndilo tsiku la masiku onse. Taonani, Mfumu ikulamulira! Inu ndinu oimira ake olengeza.”
10, 11. Kodi ndimotani mmene wailesi, galimoto zokhala ndi mikuza mawu, ndi zikwangwani zonse zinagwiritsiridwa ntchito mogwira mtima kufikira anthu ndi chowonadi cha Ufumu?
10 Zaka zoposa 70 zapita tsopano chiyambire misonkhanoyo ya ku Cedar Point—pafupifupi zaka 80 kuchokera pamene Yehova anayamba kusonyeza uchifumu wake kupyolera mwa ulamuliro Waumesiya wa Mwana wake. Kodi ndi ku ukulu wotani umene Mboni za Yehova zakwaniritsa ntchito imene zatumidwa m’Mawu a Mulungu? Kodi inuyo panokha mulimo ndi mbali yotani?
11 Kalelo m’ma 1920, wailesi inakhala chiŵiya chogwiritsira ntchito kufalitsa mokulira uthenga wa Ufumu. Mkati mwa ma 1930, nkhani za msonkhano zofotokoza Ufumuwo monga chiyembekezo cha dziko zinaulutsidwa pa dongosolo la wailesi kapena nyumba za wailesi zogwirizanitsidwa ndi matelefoni olunzanitsidwa kuzungulira dziko lonse. Galimoto zoikidwa mikuza mawu zinagwiritsiridwanso ntchito kulizapo m’malo apoyera nkhani za Baibulo zojambulidwa. Ndiyeno, mu 1936, mu Glasgow, Scotland, abale athu anayamba kuvala zikwangwani pamene anayenda m’zigawo za malonda akumalengeza nkhani zapoyera. Zonsezi zinali njira zogwira mtima zoperekera umboni kwa anthu ambiri panthaŵiyo pamene tinali ochepa m’chiŵerengero.
12. Monga momwe Malemba amasonyezera, kodi ndi iti imene ili imodzi ya njira zogwira mtima koposa imene aliyense wa ife angaperekere umboni?
12 Ndithudi, Malemba amasonyeza poyera kuti monga Akristu, ifeyo aliyense payekha tili ndi thayo la kupereka umboni. Sitingalole manyuzipepala okha kapena nyumba zawailesi kuchita ntchitoyo. Zikwizikwi za Akristu okhulupirika—amuna, akazi, ndi achichepere—avomereza thayo limenelo. Monga chotulukapo, kulalikira kunyumba ndi nyumba kwakhala chizindikiro chodziŵikitsa Mboni za Yehova.—Machitidwe 5:42; 20:20.
Kufikira Dziko Lonse Lokhalamo Anthu
13, 14. (a) Kodi nchifukwa ninji Mboni zina zimasamukira ku matauni ena, ngakhale ku maiko ena, kukapitiriza ndi utumiki wawo? (b) Kodi ndimotani mmene nkhaŵa yachikondi kwa anthu a m’dziko lobadwira yathandizira kufalitsa mbiri yabwino?
13 Podziŵa kuti uthenga wa Ufumu uyenera kulalikidwa padziko lonse lokhalamo anthu, zina za Mboni za Yehova zapenda mosamalitsa zimene zingachite pazokha kuti zifikire madera otalikirana ndi kwawo.
14 Anthu ambiri aphunzira chowonadi pambuyo posamuka ku malo awo obadwira. Ngakhale kuti angakhale atasamuka chifukwa cha maubwino akuthupi, iwo apeza kanthu kena kamtengo wapatali koposa, ndipo ena akakamizika kubwerera kudziko lakwawo kapena ku malo awo obadwira kukafalitsa chowonadi. Motero, kuchiyambi kwa zaka za zana lino kulalikidwa kwa mbiri yabwino kunafalikira mu Scandinavia, Greece, Italy, maiko a Kummawa kwa Ulaya, ndi madera ena ambiri. Ngakhale tsopano lino, m’ma 1990, uthenga wa Ufumu ukufalikira m’njira imodzimodziyo.
15. Mkati mwa ma 1920 ndi ma 1930, kodi nchiyani chinakwaniritsidwa ndi ena amene mkhalidwe wawo wa maganizo unali wonga uja wosonyezedwa pa Yesaya 6:8?
15 Pogwiritsira ntchito uphungu wa Mawu a Mulungu m’miyoyo yawo, ena akhala okhoza kudzipereka mu utumiki kumalo amene sanayambe akhalako. W. R. Brown (kaŵirikaŵiri wotchedwa “Bible Brown”) anali mmodzi wa ameneŵa. Mu 1923, kuti apititse patsogolo ntchito yolalikira, anasamuka ku Trinidad kumka ku West Africa. Mkati mwa ma 1930, Frank ndi Gray Smith, Robert Nisbet, ndi David Norman anali pakati pa awo amene ananyamula uthenga wa Ufumu namka nawo kumalire akummawa kwa Afirika. Ena anathandiza kulima munda wa South America. Kuchiyambi kwa ma 1920, George Young, wa ku Canada anakhala ndi mbali m’ntchitoyo mu Argentina, Brazil, Bolivia, Chile, ndi Peru. Juan Muñiz, amene anali atatumikira mu Spain, anapitiriza mu Argentina, Chile, Paraguay, ndi Uruguay. Onseŵa anasonyeza mzimu wonga uja wotchulidwa pa Yesaya 6:8 wakuti: “Ndine pano; munditumize ine.”
16. Kodi ndi kuti kwina kuphatikizapo m’malo okhala anthu ochuluka kumene umboni unali kuchitidwa m’zakazo nkhondo isanaulike?
16 Kulalikira mbiri yabwino kunali kufika ngakhale m’madera akutali. Mabwato oyendetsedwa ndi Mboni anali kuchezera madoko akutali onse a Newfoundland, gombe la Norway mpaka mu Arctic, zisumbu za Pacific, ndi kumadoko a Southeast Asia.
17. (a) Pofika mu 1935, kodi ndi maiko angati amene anafikiridwa ndi Mboni? (b) Kodi nchifukwa ninji ntchito inali isanathe panthaŵiyo?
17 Mosangalatsa, pofika chaka cha 1935, Mboni za Yehova zinali zotanganitsidwa kulalikira m’maiko 115, ndipo zinafikira maiko ena 34 kaya pamaulendo okachitira umboni kapena mwa mabuku otumizidwa papositi. Komabe, ntchitoyo inali isanathe. Chaka chimenecho Yehova anatsegula maso awo kuona chifuno chake cha kusonkhanitsa “khamu lalikulu” lomwe likapulumuka ndi kuloŵa m’dziko lake latsopano. (Chivumbulutso 7:9, 10, 14) Panali ntchito yaikulu yochitira umboni yofunikira kuchitidwabe!
18. M’ntchito yolengeza Ufumu, kodi ndi mbali zotani zimene zakwaniritsidwa ndi Sukulu ya Gileadi ndi Sukulu Yophunzitsa Utumiki?
18 Ngakhale pamene Nkhondo Yadziko ya II inakuta dziko lapansi ndipo panali ziletso pa mabuku kapena pa ntchito ya Mboni za Yehova m’maiko ambiri, Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watchtower inayambika kaamba ka kuphunzitsa oyembekezeredwa kukhala amishonale odzachita ntchito yokulirapo ya kulengeza Ufumu m’mitundu yonse. Kufikira lerolino, omaliza maphunziro a Gileadi atumikira m’maiko okwanira 200. Iwo sanagaŵire chabe mabuku ndiyeno ndi kusamukira ku dera lina. Achititsa maphunziro a Baibulo, kulinganiza mipingo, ndi kuphunzitsa anthu kusenza mathayo ateokratiki. Posachedwapa, akulu ndi atumiki otumikira omwe amaliza Sukulu Yophunzitsa Utumiki athandizanso kukwaniritsa zosoŵa zofunika zokhudza ntchito imeneyi m’makontinenti asanu ndi imodzi. Maziko olimba ayalidwa kaamba ka kuwonjezereka kopitirizabe.—Yerekezerani ndi 2 Timoteo 2:2.
19. Kodi atumiki a Yehova alabadira kumlingo wotani chiitano chokatumikira m’madera okhala ndi kusoŵa kokulira?
19 Kodi ena anakhoza kuthandiza kusamalira ena a magawo osagwiridwamo ntchito? Mu 1957, pamisonkhano yachigawo yonse kuzungulira dziko lonse, anthu ndi mabanja—Mboni za Yehova zokhwima—analimbikitsidwa kulingalira za kusamukira ku madera okhala ndi kusoŵa kokulirapo kukakhala kumeneko ndi kupitiriza utumiki wawo. Chiitanocho chinali monga chimene chinaperekedwa ndi Mulungu kwa mtumwi Paulo, amene anaona m’masomphenya munthu akumchonderera kuti: “Muwolokere ku Makedoniya kuno, mudzatithangate ife.” (Machitidwe 16:9, 10) Ena anasamuka mkati mwa ma 1950, ena pambuyo pake. Mboni zokwanira chikwi chimodzi zinasamukira ku Ireland ndi ku Colombia; mazana angapo anasamukira kumalo ena ambiri. Zikwi makumi angapo zinasamukira ku malo okhala ndi kusoŵa kokulira m’dziko mwawomo.—Salmo 110:3.
20. (a) Chiyambire mu 1935, kodi nchiyani chachitidwa m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu pa Mateyu 24:14? (b) M’zaka zoŵerengeka zapitazo, kodi ndimotani mmene pakhalira kufulumizidwa kwa ntchito?
20 Ndi dalitso la Yehova pa anthu ake, ntchito ya kulengeza Ufumu ikupitirizabe patsogolo paliŵiro lodabwitsa. Chiyambire 1935 chiŵerengero cha ofalitsa chawonjezereka kwa nthaŵi pafupifupi makumi asanu ndi atatu, ndipo mlingo wa chiwonjezeko cha apainiya wakhala 60 peresenti kuposa mlingo wa chiwonjezeko m’chiŵerengero cha ofalitsa. Kakonzedwe ka phunziro la Baibulo lapanyumba kanayambitsidwa m’ma 1930. Tsopano pali avareji yoposa mamiliyoni anayi ndi theka ochititsidwa mwezi uliwonse. Chiyambire 1935 maola oposa mamiliyoni zikwi 15 aperekedwa m’ntchito yolengeza Ufumu. Kulalikira kwa nthaŵi zonse kwa mbiri yabwino tsopano kukuchitidwa m’maiko 231. Pamene magawo a Kummawa kwa Ulaya ndi Afirika atseguka kaamba ka kulalikira mbiri yabwino mwaufulu, misonkhano yamitundu yagwiritsiridwa ntchito mopindulitsa kupereka uthenga wa Ufumu kwa anthu. Monga momwe Yehova analonjezera kalelo, pa Yesaya 60:22, ndithudi iye ‘akufulumizitsa ntchito panthaŵi yake.’ Ndi mwaŵi waukulu chotani nanga kwa ife kukhalamo ndi mbali!
Kufikira Aliyense Amene Tingathe Ndi Mbiri Yabwino
21, 22. Kodi tingachitenji patokha kuti tikhale Mboni zogwira mtima kwambiri kulikonse kumene tikutumikira?
21 Ambuye sananenebe kuti ntchito yatha. Zikwi zambiri akulandirabe kulambira kowona. Chifukwa chake funso limabuka lakuti, Kodi tikuchita zonse zimene tingathe kugwiritsira ntchito bwino nthaŵi imene Yehova walola mwa kuleza mtima kwake kaamba ka ntchito yake?—2 Petro 3:15.
22 Si aliyense amene angasamukire ku gawo losafoledwa kwenikweni. Koma kodi mukugwiritsira ntchito mokwanira mipata imene ili yotseguka kwa inu? Kodi mumachitira umboni kwa antchito anzanu? kwa aphunzitsi ndi anzanu apasukulu? Kodi mwasinthira ku mikhalidwe yomasintha ya m’gawo lanu? Ngati, chifukwa cha kusintha kwa kagwiridwe ka ntchito, anthu oŵerengeka chabe ndiwo amapezeka panyumba masana, kodi mwasintha ndandanda yanu kuti muwafikire madzulo? Ngati nyumbazo nzosafikirika ndi alendo osaitanidwa, kodi mumachita umboni wa patelefoni kapena wa kalata? Kodi mumabwerera kwa amene anasonyeza chikondwerero ndi kupempha kuchita nawo maphunziro a Baibulo apanyumba? Kodi mukukwaniritsa utumiki wanu kotheratu?—Yerekezerani ndi Machitidwe 20:21; 2 Timoteo 4:5.
23. Pamene Yehova akupenya zimene tikuchita mu utumiki wake, kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala choonekera ku mbali yathu?
23 Tonsefe tichitetu utumiki wathu mwa njira imene imasonyeza bwino lomwe kwa Yehova kuti tikuyamikiradi mwaŵi waukulu wa kukhala Mboni zake m’nthaŵi zino zovuta. Ukhaletu mwaŵi wathu kukhala mboni zoona ndi maso pamene Yehova akupereka chiweruzo pa dongosolo lakale loipali ndi kuyambitsa Ulamuliro wa Zaka Chikwi waulemerero wa Yesu Kristu!
[Mawu a M’munsi]
a Oŵerengedwa molingana ndi mmene dziko lapansi linagaŵidwira kufikira kuchiyambi kwa ma 1990.
Za Kupenda
◻ Kodi nchifukwa ninji kulalikira uthenga wa Ufumu kuli kofunika kwambiri?
◻ Kodi ndi kumlingo wotani umene mbiri yabwino inalalikidwa kufikira mu 1914?
◻ Kodi ndi umboni waukulu motani umene waperekedwa chiyambire kukhazikitsidwa kwa Ufumu?
◻ Kodi nchiyani chingachititse mbali yathu mu utumiki kukhala yopatsa zipatso kwambiri?
[Bokosi pamasamba 16, 17]
MBONI ZA YEHOVA—Zolengeza Ufumu wa Mulungu
Pamisonkhano yachigawo mazana angapo kuzungulira dziko lonse mkati mwa 1993-94, chilengezo chinaperekedwa cha kutulutsidwa kwa buku latsopano la mutu wakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom. Imeneyi ndi mbiri ya Mboni za Yehova yopatsa chidziŵitso kwambiri ndi yosavuta kumva. Ndi buku la masamba 752, lokhala ndi zifaniziro zokongola, ndi zithunzithunzi zoposa chikwi chimodzi zosonkhanitsidwa kuchokera ku maiko 96 osiyanasiyana. Pofika kumapeto kwa 1993, linali litafalitsidwa m’zinenero 25 ndipo likutembenuzidwa m’zina zowonjezereka.
Kodi nchiyani chimene chapangitsa buku limeneli kukhala la panthaŵi yake? M’zaka za posachedwapa mamiliyoni a anthu padziko lonse akhala Mboni za Yehova. Onsewo ayenera kudziŵa bwino lomwe mbiri ya gulu limene akugwirizana nalo. Ndiponso, kulalikira kwawo ndi njira ya kulambira zaloŵa m’magulu a mitundu ndi mafuko padziko lonse ndipo zalandiridwa ndi achichepere ndi achikulire omwe, a mlingo uliwonse wa chuma ndi maphunziro. Monga chotulukapo, ambiri amene akuona zimene zikuchitika ali ndi mafunso ponena za Mboni—osati ponena za zikhulupiriro zawo zokha komanso ponena za chiyambi chawo, mbiri yawo, gulu lawo, ndi zolinga zawo. Ena alemba nkhani ponena za izo, ngakhale kuti nthaŵi zina amalemba mwatsankho. Komabe, palibe aliyense amene amadziŵa bwino kwambiri mbiri yamakono ya Mboni za Yehova kuposa mmene zimadziŵira Mboni zenizo. Alembi a buku limeneli ayesa ndithu kufotokoza mbiri imeneyo m’njira yosakondera ndi yowona mtima. Mwa kutero, iwo alembanso kukwaniritsidwa kofika panthaŵi ino kwa tanthauzo lenileni la mbali ya chizindikiro cha kukhalapo kwa Kristu kolembedwa pa Mateyu 24:14, ndipo achita zimenezo ndi mfundo zimene zikanaperekedwa kokha ndi awo odziloŵetsa mwakuya kwambiri m’ntchito yonenedweratu pamenepo.
Buku limeneli lagaŵidwa m’zigawo zazikulu zisanu ndi ziŵiri:
Chigawo 1: Mbali imeneyi imapenda mwakuya chiyambi cha mbiri ya Mboni za Yehova. Imaphatikizapo kupenda kopatsa chidziŵitso kwa mbiri yawo yonse yamakono kuyambira mu 1870 mpaka 1992.
Chigawo 2: Munomo timapeza kupenda kosonyeza kupita patsogolo kwa zikhulupiriro zimene zimasiyanitsa Mboni za Yehova ndi magulu ena achipembedzo.
Chigawo 3: Mbali iyi ya bukuli imapenda kuyambika kwa kalinganizidwe ka gulu lawo. Imasimba zinthu zosangalatsa ponena za misonkhano yawo yampingo ndi misonkhano yaikulu, limodzinso ndi njira imene amamangira Nyumba Zaufumu zawo, Nyumba za Msonkhano zazikulu, ndi malo ofalitsira mabuku ofotokoza Baibulo. Imasonyeza changu chimene Mboni za Yehova zimalengeza nacho Ufumu wa Mulungu ndi chikondi chimene chimaonekera pamene zisamalirana wina ndi mnzake m’nthaŵi za mavuto.
Chigawo 4: Mmenemu mudzapezamo mfundo zosangalatsa zosonyeza mmene kulengeza Ufumu wa Mulungu kwafikira kumaiko aakulu ndi ku zisumbu zakutali kuzungulira mbulunga yonse yadziko. Tangolingalirani—kulalikira m’maiko 43 m’chaka cha 1914, koma m’maiko 229 pofika mu 1992! Zokumana nazo za awo amene akhala ndi phande m’kuwonjezereka kwa padziko lonse kumeneku zilidi zothutsa mtima.
Chigawo 5: Kuti ntchito yolengeza Ufumu yonseyi ichitike pafunikira malo a m’mitundu yonse ofalitsira Mabaibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero zoposa mazana aŵiri. Munomo mudzadziŵa za mbali imeneyi ya ntchito yawo.
Chigawo 6: Mbonizo zayang’anizananso ndi ziyeso—zina chifukwa cha kupanda ungwiro kwaumunthu, zina chifukwa cha abale onyenga, ndipo zochuluka chifukwa cha chizunzo chenicheni. Mawu a Mulungu anachenjeza kuti zimenezo zikachitika. (Luka 17:1; 2 Timoteo 3:12; 1 Petro 4:12; 2 Petro 2:1, 2) Chigawo chimenechi cha bukuli chimasimba momvekera bwino zimene zachitikadi ndi mmene chikhulupiriro cha Mboni za Yehova chazikhozetsera kulakika.
Chigawo 7: Pomaliza, bukuli limafotokoza chifukwa chake Mboni za Yehova zili zokhutiritsidwa molimba kuti gulu limene zili mbali yake limatsogoleredwadi ndi Mulungu. Limalongosolanso chifukwa chake zimaona kufunika, monga gulu ndi aliyense payekha, kwa kukhalabe odikira.
Kuwonjezera pa zimene talongosolazi, buku la mpangidwe wochititsa kaso limeneli limaphatikizapo chigawo chokongola ndi chopatsa chidziŵitso kwambiri cha masamba 50 a zithunzithunzi za mtundu weniweni wa maonekedwe zosonyeza malikulu a padziko lonse limodzinso ndi nyumba za nthambi zogwiritsiridwa ntchito ndi Mboni za Yehova padziko lonse.
Ngati simunapezebe kope la buku lochititsa kaso limeneli, chitani zimenezo ndipo mudzapinduladi mwa kuliŵerenga.
Ndemanga Zochokera kwa Ena Amene Aliŵerenga
Kodi awo amene aŵerenga kale buku limeneli akunenanji? Nazi zoŵerengeka chabe:
“Ndangomaliza kumene kuŵerenga mbiri yolembedwa yochititsa chidwi ya Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom. Gulu lokhulupirika ndi lomamatira ku chowonadi modzichepetsa ndilo lokha lingalembe mowona mtima, molimba mtima, ndi mosamalitsa chotero.”
“Limamveka monga buku la Machitidwe, ndi kuwona mtima ndi kusabisa kanthu kwake.”
“Ndi buku lochititsa chidwi chotani nanga! . . . Lili luso lenileni lopanga mbiri.”
Ataŵerenga pafupifupi theka la bukulo, mwamuna wina analemba kuti: “Ndinachita mantha, kuzizira m’mawondo, ndi kutsala pang’ono kugwetsa misozi. . . . M’zaka zanga zonse, sindinaonepo buku lina lililonse limene lakhala losonkhezera maganizo chotere.”
“Mtima wanga umasekera nthaŵi zonse pamene ndilingalira mmene bukuli lidzalimbitsira chikhulupiriro cha achichepere limodzinso ndi atsopano obwera m’gulu lerolino.”
“Nthaŵi zonse ndayamikira chowonadi, koma kuŵerenga bukuli kwanditsegula maso ndi kundithandiza kuzindikira kwambiri kuposa ndi kalelonse kuti mzimu wa Yehova ndiwo umachititsa zonsezi.”
[Zithunzi patsamba 18]
Anthu ambiri anafikiridwa ndi uthenga wa Ufumu ngakhale pamene Mboni zinali zochepa m’chiŵerengero