Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 6/15 tsamba 28-31
  • Kupenya ndi Chiyamikiro pa “Nyumba ya Mulungu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupenya ndi Chiyamikiro pa “Nyumba ya Mulungu”
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Dzina Limene Limafuna Kudzipereka
  • Kupangitsa Utumiki wa pa Beteli Kukhala Wachipambano
  • Kulemekeza Kwambiri Utumiki Wopatulika pa Beteli
  • Madalitso mu “Nyumba ya Mulungu”
  • Kodi Ntchito Iyi Ingakhale Yabwino Kwambiri kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Mukuitanidwa!
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Ntchito Zabwino Zimene Yehova Sangaziiwale
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Kodi Beteli N’chiyani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 6/15 tsamba 28-31

Kupenya ndi Chiyamikiro pa “Nyumba ya Mulungu”

“CHINTHU chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi: kuti ndikhalitse m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa m’Kachisi wake.”​—Salmo 27:4.

Mfumu Davide yoyamikirayo inapenya ndi chisangalalo, kapena chikondwerero, pa kachisi wa Yehova. Kodi mumalingalira mofananamo ponena za maphata a kulambira koona lerolino? Nyumba za Beteli zoposa 95 pa nthambi za Watch Tower Society zili pakati pa malo amene amagwirizanitsidwa ndi kulambira Yehova m’nthaŵi yathu.

“Kukumbukira za kumbuyoku pa zaka zanga zambiri za utumiki wa pa Beteli kumandichititsa kudzazidwa ndi chithokozo ndi chiyamikiro chachikulu, chimene chakula chaka ndi chaka,” akufotokoza motero Helga, amene anayamba ntchito pa nyumbapo mu Germany mu 1948. Helga ali mmodzi wa antchito osangalala a pa Beteli apadziko lonse okwanira 13,828 amene m’chaka chautumiki cha 1993 ‘anaona kukongola kwa Yehova.’ Kodi dzinalo Beteli limatanthauzanji kwenikweni? Kodi ndimotani mmene aliyense wa Mboni za Yehova, kaya amatumikira Mulungu pa Beteli kapena kunja kwake, angapenyere moyamikira pamakonzedwe ameneŵa?

Dzina Limene Limafuna Kudzipereka

“Beteli” ndilo dzina loyenera koposa, pakuti liwu Lachihebrilo Behth-ʼElʹ limatanthauza kuti “Nyumba ya Mulungu.” (Genesis 28:19, NW, mawu amtsinde) Inde, Beteli imafanana ndi nyumba yolinganizidwa bwino, kapena ‘nyumba yomangidwa mwanzeru,’ Mulungu ndi chifuniro chake zikumakhala chifuno chake chachikulu. (Miyambo 24:3) “Kuli monga ngati kukhala m’banja. Tili ndi njira ya tsiku ndi tsiku yochitira zinthu yolinganizidwa bwino,” akutero Herta moyamikira. Iye wakhala akutumikira pa Beteli imodzimodziyo monga Helga kwa zaka zoposa 45. Chiŵalo chilichonse cha banja lalikulu limeneli chili ndi ntchito yake ndi malo ake, zikumachilola kukhala chachimwemwe ndi chosungika. Mogwirizana ndi dzinalo Beteli, kulinganizidwa bwino ndi dongosolo zimasonyezedwa ndi iliyonse ya madipatimenti. Zimenezi zimachirikiza mtendere, kutheketsa kulalikidwa kogwira mtima kwa mbiri yabwino, ndipo zimapatsa mipingo chifukwa chabwino cha kulingalirira “Nyumba ya Mulungu” ndi ulemu waukulu.​—1 Akorinto 14:33, 40.

Kodi nchifukwa ninji malo otero ali ofunika? Mwachitsanzo, magazini ano, anatulutsidwa pa makina osindikizira a pa Beteli. Kulalikidwa kwa uthenga wa Ufumu ndi kugaŵiridwa kwa chakudya chauzimu, zonsezo zoonedweratu ndi Yesu Kristu, zimapangitsa makonzedwe agulu onga a Beteli kukhala ofunika​—ochirikizidwa ndi antchito ofunitsitsa ndi olemekezedwa kwambiri ndi olambira onse a Yehova.​—Mateyu 24:14, 45.

Kodi mungakonde kudziŵa zowonjezereka ponena za kuyambika kwa programu ya tsiku la ntchito kuno? Kumene Helga ndi Herta amakhala, belu lolira mokoma limamveka m’nyumba zonse zokhalamo pa 6:30 a.m., ngakhale kuti ambiri a antchito oposa 800 anthaŵi zonsewo amadzuka mofulumirirapo kuti akonzekere tsikulo. Pofika 7:00 a.m., Lolemba mpaka Loŵeruka, banjalo limasonkhana m’zipinda zodyera kaamba ka kukambitsirana lemba la tsiku, kapena kuti kulambira kwa mmaŵa. Pambuyo pake pamadza mfisulo wokoma. Tsiku la ntchito lililonse limayamba pa 8:00 a.m. ndipo limatenga maola asanu ndi atatu, likumadodometsedwa kokha ndi chakudya chamasana. (Kaŵirikaŵiri banjalo limagwira ntchito mmaŵa wokha pa Loŵeruka.) Kaya kukhale kukhitchini, kunyumba yosindikizira, kochapira, kumaofesi, kunyumba zokonzera zinthu, komamatizira mabuku, kapena ku dipatimenti ina iliyonse, kuli ntchito yambiri.

Madzulo ndi pa kutha kwa milungu, ziŵalo za banja zimayanjana ndi mipingo ya kumaloko pa misonkhano ndi mu ulaliki wapoyera. Abale ambiri a pa Beteli ali akulu kapena atumiki otumikira m’mipingo imeneyi. Mboni za kumaloko zimayamikiradi chigwirizano chimenechi, magulu onsewo akumagwira ntchito mogwirizana monga thupi limodzi, akumalemekezana ndi kumvana. (Akolose 2:19) Wantchito aliyense wa pa Beteli amadziŵa kuti ntchito yake mu “Nyumba ya Mulungu” ili yofunika koposa zochitika zina zonse. Komabe, kutenthedwa maganizo kaamba ka kulalikira ndi kukhala woloŵetsedwa m’zochitika za mpingo, limodzi ndi mkhalidwe wa maganizo wachikatikati, zimalimbitsa mkhalidwe wauzimu wa wantchito wa pa Beteli, kuwonjezera chisangalalo chake, ndi kumpangitsa kukhala chiŵalo chopindulitsa kwambiri cha banjalo. Mmene mikhalidwe imeneyi ilili yofunika kwambiri nanga pogwira ntchito mu “nyumba” imene dzina lake lili logwirizana ndi kudzipereka kwa moyo wonse!

Kupangitsa Utumiki wa pa Beteli Kukhala Wachipambano

Kodi nchiyani chimene chathandiza ambirimbiri a Mboni za Yehova kupanga utumiki wa pa Beteli kukhala wachipambano? Ziŵalo za banja la Beteli mu France zokhala ndi chidziŵitso cha zaka zambiri zikuthirira ndemanga motere: “Kukonda Yehova. Kukhala ndi chitsimikiziro cha kupitirizabe kulikonse kumene angatiike; kudzichepetsa, kugonjera, ndi kumvera zitsogozo zoperekedwa kwa ife ndi Sosaite.” (Denise) “Ndaona mmene kulili kofunika kulemekeza lamulo la mkhalidwe lotchulidwa ndi Paulo pa Aroma 12:10: ‘Mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.’ Lemba limeneli limatisonyeza kufunika osati kwa kuumirira lingaliro lathu kuti livomerezedwe koma, mmalomwake, kulingalira malingaliro a ena. M’mawu ena, kusafunafuna kudziika pamwamba pa ena.” (Jean-Jacques) “Kulemekeza kwathu utumiki wa pa Beteli kungawonongedwe ngati tilingalira zinthu mwakuthupi, mwaumunthu,” akutero Barbara, “pakuti kumeneku kungatichitse kuiŵala chenicheni chakuti Yehova akutsogolera gulu lake. Ulemu wotero ungatayike ngati tikhumudwa ndi kupanda ungwiro kwa ena.”

Aliyense pa Beteli ali wopanda ungwiro, chotero mabwenzi ayenera kusankhidwa mosamala. Achichepere kapena ofika chatsopano amachita bwino kusapanga ubwenzi ndi anzawo ausinkhu wawo okha. Awo amene angasonyeze chikhoterero cha kung’ung’udza kapena kuganiza zoipa sali mabwenzi olimbikitsa pa Beteli kapena mu mpingo. Kumbali ina, kutsanzira “nzeru yochokera kumwamba,” yofotokozedwa pa Yakobo 3:17, kumadzetsa madalitso. Imeneyi “iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, yosadzikometsera pamaso.” Mikhalidwe yotero, limodzi ndi kuleza mtima ndi kukoma mtima, imaoneka pa “Nyumba ya Mulungu,” ikumapangitsa kukhala kwa munthu pamenepo kukhala kokondweretsa ndi kotsitsimula. Ngakhale anthu odzaona amene sali Mboni kaŵirikaŵiri amasirira khalidwe labwino, ubwenzi, ndi mzimu wachisangalalo wa antchitowo.

Anny, amene ali ndi zaka zakubadwa zoposa 70 ndi amene wakhala chiŵalo cha banja la Beteli ku Germany chiyambire 1956, akufotokoza mmene amapitirizira kukhala kwake wokonzekera kutumikira kuti: “Kaamba ka ubwino wanga wauzimu, ndimayesayesa zolimba kuyendera limodzi ndi zofalitsa za Sosaite, kufika pamisonkhano mokhazikika, ndi kukhala ndi phande mokhazikika m’kulalikira. Ndimayesanso kukhala ndi thanzi labwino mwa kuchita maseŵera olimbitsa thupi mmaŵa uliwonse, mwa kupeŵa kugwiritsira ntchito lifiti nthaŵi zambiri, ndi mwa kuyenda ndi miyendo kaŵirikaŵiri monga momwe ndingathere, makamaka mu utumiki wakumunda.”

Ambiri okhala ndi chidziŵitso cha moyo wa pa Beteli angavomerezane ndi Anny. Iwo samanyalanyaza kuphunzira, samaleka kugwira ntchito. Thanzi lakuthupi limafuna kuti apeze tulo tokwanira ndi kulimbitsa thupi ndi kudya ndi kumwa mwachikatikati. Chofunika koposa zonse, samaleka pemphero la munthu mwini ndi phunziro la Baibulo.

Kulemekeza Kwambiri Utumiki Wopatulika pa Beteli

“Kodi mumagwira ntchito kuti?” ndilo funso lofunsidwa mofala kwa ziŵalo za Beteli. Magawo antchito ndi osiyanasiyana, koma lililonse limayenerera kulemekezedwa ndi aliyense. Chifukwa? Chifukwa chakuti gawo lililonse​—kaya likhale la kuyendetsa makina osindikiza chakudya chauzimu, kuchapa zovala, kuphikira ndi kuyeretsa nyumba ya banjalo, kapena kuchita ntchito ya mu ofesi​—lili utumiki wopatulika. Monga momwe kwatchulidwira pamwambapo, Akristu samasankhana. Kumbukirani kuti ntchito zonse zofunika zochitidwa ndi ansembe ndi Alevi pakachisi, m’mabwalo ake ndi m’nyumba zake zodyera, zonsezo zinalingaliridwa kukhala utumiki wopatulika kwa Yehova. Zimenezo zinaphatikizapo kupha ndi kukonza nyama za nsembe, kuthira mafuta mu nyali, ngakhale kuyeretsa ndi kuchita ntchito za alonda. Mofananamo, gawo lililonse pa Beteli lili ntchito yokhutiritsa ndi yofunika “mu ntchito ya Ambuye,” chifukwa chake lili mwaŵi wapadera.​—1 Akorinto 15:58.

Talingalirani pang’ono chikhoterero chimodzi chimene chingaletse kupenya kwathu ndi chiyamikiro pa “Nyumba ya Mulungu.” Akristu okhala pa Beteli ndi akunja omwe afunikira kukhala osamala pa kaduka ndi nsanje, zimene ‘zimavunditsa mafupa.’ (Miyambo 14:30) Palibe munthu amene ayenera kukhala ndi chifukwa chokhalira ndi kaduka pa mwaŵi wa utumiki wa antchito a pa Beteli. Ndiponso, pa Beteli palibe malo ochitira nsanje, imene ili imodzi ya ntchito za thupi. Yembekezerani modzichepetsa​—umenewo ndiwo uphungu wanzeru kwa munthu amene angalingalire kuti wanyalanyazidwa pamene ena akupatsidwa mwaŵi wokulirapo. Ndiponso, anthu osiyana kwambiri m’mikhalidwe ya zachuma amakhalira limodzi pa Beteli. Nkogwiritsa mwala chotani nanga ngati munthu alingalira mikhalidwe yake “moyerekezera ndi munthu wina”! Kukhala wokhutira ndi “zakudya ndi zofunda” kwathandiza ambiri kupitirizabe mokhulupirika kwa zaka makumi ambiri mu “Nyumba ya Mulungu.”​—Agalatiya 5:20, 26; 6:4, NW; 1 Timoteo 6:8.

Mboni za Yehova ndi mamiliyoni ena zimapeza phindu lalikulu m’mautumiki osalipidwa ochitidwa pa Beteli​—ntchito yochitidwa mopanda dyera chifukwa cha kukonda Mulungu ndi mnansi. Nyumba za Beteli ndi nyumba zosikindikizira za Watch Tower Society, mofanana ndi malo ena ateokratiki, zimalipiliridwa ndi zopereka zodzifunira. (2 Akorinto 9:7) Monga Mfumu Davide ndi akalonga ndi akulu a Israyeli, tikhoza kusonyeza ulemu wathu ndi chiyamikiro kaamba ka “Nyumba ya Mulungu” mwa kuchirikiza kwathu Sosaite ndi nyonga ndi ndalama. (1 Mbiri 29:3-7) Tsopano tiyeni tione mmene kulili kothekera “kupenya kukongola kwake kwa Yehova” pa Beteli.

Madalitso mu “Nyumba ya Mulungu”

Pamene muli pa msonkhano, kodi mumakhala wokhutira, mutazingidwa ndi olambira Yehova achimwemwe? Tangolingalirani, mwaŵi wa kutumikira Yehova pakati pa gulu la abale tsiku ndi tsiku umene wantchito wa pa Beteli ali nawo! (Salmo 26:12) Ndi ziyembekezo zabwino chotani nanga za kukula kwauzimu zimene zimenezo zimapereka! Mbale wina ananena kuti anaphunzira zambiri zomthandiza kuumba umunthu wake mkati mwa chaka chimodzi pa Beteli koposa mmene anachitira m’zaka zitatu ali kwina. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti palibe malo ena alionse kumene anali ndi mwaŵi wa kupenyerera ndi kutsanzira chikhulupiriro cha anthu Achikristu achikulire ochuluka motero.​—Miyambo 13:20.

Pa Beteli munthu amazingidwa ndi aphungu achidziŵitso, titero kunena kwake. Ndiponso, pali phindu la kumva ndemanga zokonzekeredwa bwino zoperekedwa mkati mwa kulambira kwa mmaŵa ndi pa Phunziro la Nsanja ya Olonda la banja la Beteli ndi pomvetsera nkhani pa Lolemba madzulo. Atsopano amalangizidwa mu Bethel Entrants’ School ndipo amagaŵiridwa kuŵerenga Baibulo lonse lathunthu mkati mwa miyezi 12.

Malipoti ndi zokumana nazo zoperekedwa ndi alendo akumaiko ena zimapereka chilimbikitso chowonjezereka. Ndiponso, ziŵalo za Bungwe Lolamulira kapena owaimira awo amachezera maofesi anthambi. “Ngakhale kuti amakhala ndi zambiri zoti achite,” akufotokoza motero Helga, “nthaŵi zonse abalewo amapatula nthaŵi ya kucheza kapena kuseka nanu.” Nkolimbikitsa chotani nanga kudzionera wekha mkhalidwe wotsitsimula ndi wodzichepetsa wa amuna okhulupirika otero!

Makamaka pa Beteli munthu angathe kupenya mmene gulu la Mulungu limagwirira ntchito ndi mmene mzimu wake woyera umasonkhezerera mitima ndi manja ofunitsitsa kuchita ntchito. “Pa Beteli munthu amaona kukhala pafupi kwambiri ndi ‘pachimake pa zinthu,’ akufotokoza motero mbale wina, amene wakhala akutumikira pa Beteli ya ku France chiyambire 1949. Iye akupitiriza kuti: “Ndinganenedi kuti kwa ine Beteli ndi mtundu wa utumiki wanthaŵi yonse umene umandilola kupereka nthaŵi yambiri ndi nyonga muutumiki wa Yehova ndi kutumikira abale ambirimbiri.” Ndipo kodi chimenecho sindicho chifuno chathu chenicheni m’moyo​—kuchita chifuniro cha Mulungu? Pa Beteli munthu angathe ‘kupereka chitamando tsiku lonse.’ Ha, ndi dalitso lotani nanga!​—Salmo 44:8.

Monga momwe taonera, munthu wogwira ntchito pa nyumba ya Beteli angathe kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kupeza madalitso ambiri osiyanasiyana. (Ahebri 6:10) Kodi utumiki wa pa “Nyumba ya Mulungu” ungakhale kanthu koyenera kwa inu? Awo amene ali pakati pa Mboni za Yehova amene ali ndi zaka zakubadwa zosachepera pa 19, amenenso ali ndi thanzi labwino lauzimu ndi lakuthupi, ndi amene, monga Timoteo, ‘achitiridwa umboni wabwino [ndi] abale’ angathe kufunsira utumiki wa pa Beteli. (Machitidwe 16:2) Ambiri apanga utumiki wa pa Beteli kukhala ntchito yawo ya moyo wonse, monga awo amene agwidwa mawu pamwambapo. Kwa iwo chikhumbo chachikulu cha wamasalmo​—‘kukhala m’nyumba ya Yehova masiku onse’​—chakhala chenicheni.

Mboni za Yehova zimalemekeza mzimu wodzimana wosonyezedwa ndi abale ndi alongo awo pa Beteli, amene amachita ntchito m’njira zonse ziŵiri mofunitsitsa ndi mwachisangalalo. Kaya tikutumikira Yehova pa Beteli kapena kwina kulikonse, aliyense wa ife ali ndi chifukwa chabwino cha kulingalira monga momwe inachitira Mfumu Davide​—kupenya ndi chiyamikiro, kapena chikondwerero, pa “Nyumba ya Mulungu.”

[Chithunzi patsamba 31]

Akristu awa akondwera kuchita utumiki wopatulika pa Beteli ya ku Germany kwa zaka makumi ambiri

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena