Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 8/15 tsamba 5-7
  • Kutsegula Maso Kuti Aone Mbiri Yabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutsegula Maso Kuti Aone Mbiri Yabwino
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kugonjetsa Khungu Lauzimu
  • Mankhwala Okha Okhalitsa​—Ufumu wa Mulungu
  • Chimwemwe m’Dziko Latsopano la Mulungu
  • Muzithandiza Anthu Osaona Kudziwa za Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani kwa Akhungu?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Amachita Zinthu Bwinobwino Ngakhale Kuti Ndi Osaona
    Galamukani!—2015
  • Afarisi Anatsutsana ndi Munthu Amene Anali Wakhungu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 8/15 tsamba 5-7

Kutsegula Maso Kuti Aone Mbiri Yabwino

“THAMBO silimakhala losabiriŵira kwambiri chifukwa chakuti munthu wakhungu samaliona,” umatero mwambi wa anthu a ku Denmark. Koma kodi m’miyoyo yathu yatsiku ndi tsiku yotanganitsidwayi, timaona kuti thambo nlobiriŵira, monga momwe lili? Kodi timaona mtsogolo ndi chidaliro? Kodi timakhulupiriradi mbiri yabwino imene Mawu a Mulungu, Baibulo, limapereka?

M’nkhani yathu yapitayo, tafotokozamo mbali za khungu lakuthupi. Tsopano tiyeni tipende mtundu wina wa kuona umene uli wofunika kwambiri. Umaloŵetsamo chimwemwe chathu chosatha ndiponso mtsogolo mwa okondedwa athu.

Mosakayikira, tikuyang’anizana ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1) Kodi nchiyani chimene chimachitika pamene anthu akumenyera nkhondo kupeza zokhalira moyo, kupirira zovuta zaumoyo ndi mavuto a m’banja, ndi kulimbana ndi chisalungamo cha chitaganya ndi kupanda chikondi kwake? Mwachisoni, ambiri amapeza kuti kudalira kwawo anthu anzawo, chipembedzo, ndi maboma zimazirala. Pokhala opanda yankho, ena amanena kuti mavuto awo sadzathetsedwa konse m’njira yozoloŵereka. M’nyuzipepala ya ku Brazil Jornal da Tarde, Jacob Pinheiro Goldberg akunena kuti: “Anthu, atayang’anizana ndi mikhalidwe yosautsa, amanyong’onyeka kwambiri ndi zophophonya kwakuti samalingalira mwanzeru, ndipo amadalira pa zipembedzo zachinsinsi zogwiritsa mwala.” Komabe, ngakhale pamene zinthu zilakwika, timafuna kulingalira bwino, kodi sichoncho?

Tangolingalirani kwakanthaŵi kuti inu mukufunafuna nyumba ya banja lanu, ndipo ndalama si vuto. Mwinamwake mukuifunafuna ndipo mukupita kukaona nyumba zosiyanasiyana m’malo osiyanasiyana. Ngakhale kuti osatsa malonda a malo akuyesa kuthandiza pa zofuna zanu, nyumba imene mukulingalira ikukhalabe yosapezeka. Komabe, popeza kuti chikhutiro ndi ubwino wa banja lanu zikuloŵetsedwamo, inu simungaleke kufunafunako, kodi mungatero? Tsopano lingalirani chimwemwe chake pamene potsirizira mupeza nyumba imene munali kukhumba.

Monga momwe mukanathera nthaŵi mukumafunafuna nyumba yatsopano, bwanji osapenda Baibulo kuti muone chothetsera mavuto anu? Monga momwedi tifunikira kupenda zenizeni popanga zosankha ponena za nyumba, choteronso tifunikira kulingalira mwanzeru pa zimene timaŵerenga m’Mawu a Mulungu. Kopindulitsadi kwambiri kuposa kupeza nyumba ndiko kuona kwathu ndi kulandira choonadi chonena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Yesu anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”​—Yohane 17:3.

Koma ngati uthenga wa Baibulo uli wofunika kwambiri, kodi nchifukwa ninji ambiri amakhalabe akhungu ku mbiri yake yabwino? Chimodzi cha zifukwa zimenezi chimene chingadabwitse ambiri nchakuti, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Monga chotulukapo chake, Satana Mdyerekezi “[wa]chititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiŵalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisaŵaŵalire.” (2 Akorinto 4:4) Ngakhale kuti timaona ndi maso athu, ubongo ndiwo umene umazindikiritsa kuŵala kumene kumaloŵa m’diso. Chifukwa chake, kukhala wakhungu kumafotokozedwanso monga “kusakhoza kapena kusafuna kuzindikira kapena kugamula.” Zimenezi zimatikumbutsa za mawu otchuka akuti: “Palibe amene ali wakhungu kwambiri mofanana ndi aja amene samafuna kuona.”

Munthu wakhungu sangathe kuona zimene zili patsogolo pake, chotero iye angakhale pa ngozi ya kuvulala. Khungu lakuthupi la ambiri silingasinthidwe, komabe palibe aliyense amene amakakamizidwa kukhalabe wakhungu mwauzimu.

Kugonjetsa Khungu Lauzimu

Monga momwe mikhalidwe yoipa ya ukhondo ingafooketsere maso, malo oipa angachirikize khungu la makhalidwe. Ndiponso, Yesu Kristu anachenjeza za ziphunzitso ndi miyambo yopangidwa ndi anthu. Ananena momvekera bwino kuti atsogoleri achipembedzo panthaŵiyo anali kusokeretsa gulu lawo: “Ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse aŵiri adzagwa m’mbuna.”​—Mateyu 15:14.

Mmalo mwa kukhala onyengedwa ndi atsogoleri akhungu, n’ngachimwemwe chotani nanga awo amene amatsegula maso awo kuti aone choonadi cha Ufumu wa Mulungu! Yesu analengeza kuti: “Kudzaweruza ndadza Ine ku dziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye.” (Yohane 9:39) Komabe, kodi ndimotani mmene akhungu mwauzimu angafikire pa kuona? Chabwino, tiyeni tipitirizebe kupenda kwathu khungu lakuthupi.

Tsopano pali makonzedwe osiyanasiyana kwa osapenya bwino. Zimenezi sizinali choncho nthaŵi zonse. Panalibe zoyesayesa zazikulu zimene zinapangidwa kuthandiza akhungu Valentin Haüy asanayambitse sukulu yapadera ya akhungu mu 1784. Pambuyo pake, Louis Braille analinganiza dongosolo limene limatchedwa ndi dzina lake; iye anatero kuti athandize anthu osapenya bwino kuŵerenga.

Bwanji za akhungu mwauzimu? M’zaka zaposachedwapa zoyesayesa zazikulu zapangidwa za kulengeza mbiri yabwino ngakhale kumbali zakutali kwambiri za dziko lapansi. (Mateyu 24:14) Mboni za Yehova zimakondwera kubweretsa chiyembekezo kwa akhungu lophiphiritsira ndi lakuthupi lomwe.

Mkazi wina wa ku Brazil analemba kuti: “Ndikufuna kunena kuti mosasamala kanthu za kupunduka kwanga kwakuthupi, ndingathe kuona​—mwauzimu. Ha, ndi Mulungu wabwino chotani nanga! Tili achimwemwe kudziŵa kuti ‘Yehova adzaoloŵetsa dzanja lake ndi kukwaniritsa zamoyo zonse chokhumba chawo.’” (Salmo 145:16) Ndipo Jorge, amene ali wakhungu mwakuthupi, akukumbukira motere: “Moyo wanga ungagaŵidwe bwino lomwe m’zigawo ziŵiri: poyamba ndi pambuyo pa Mboni. . . . Chifukwa cha izo, ndinayamba kuona dzikoli bwino kwambiri. Ndimasangalala ndi unansi wabwino kwambiri ndi aliyense mu mpingo.” Monga mmene zilili zokondweretsamo, Baibulo limatitsimikizira kuti posachedwapa palibe amene adzakhala wakhungu padziko lapansili​—mwakuthupi kapena mwauzimu. Kodi zimenezo zidzakhalako motani? Kodi zidzakhala choncho motani padziko lonse lapansi kuti “Yehova apenyetsa osaona”?​—Salmo 146:8.

Mankhwala Okha Okhalitsa​—Ufumu wa Mulungu

Mosasamala kanthu za chidziŵitso chowonjezereka cha zamankhwala, nthenda zambirimbiri zikupitirizabe kuchititsa khungu, zoŵaŵitsa, ndi imfa. Nangano, kodi nchiyani chimene chikufunika kuthetsa kutupirana, mikhalidwe yoipa ya ukhondo, ndi mavuto amene amachotsa kuona ndi chimwemwe cha moyo? Kuchiritsa kwa Yesu akhungu ndi ena kunali chionetsero chochepa kaamba ka mtsogolo. Mokondweretsa, chiphunzitso chake ndi ntchito yochiritsa zinachitira chithunzi madalitso amene adzaperekedwa padziko lapansi pansi pa boma la Ufumu wa Mulungu.

Kuchiritsa kochitidwa pamlingo wa dziko lonse kuli pafupi.a Programu ya kuchiritsa kwaumulungu imeneyi imasonyezedwa bwino kwambiri ndi mtumwi Yohane: “Anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa. Pakati pa khwalala lake, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziŵiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nawo amitundu.”​—Chivumbulutso 22:1, 2.

Mawu onga akuti “madzi a moyo” ndi “mtengo wa moyo” amasonyeza kuti pambuyo pa kutha kwa dongosolo loipa lalerolino, makonzedwe ochiritsa a Ufumu wa Mulungu adzatukulira mtundu wa anthu mwapang’ong’ono ku ungwiro. Kwenikweni, mapindu a nsembe ya dipo ya Yesu (kuphatikizapo kukhululukidwa kotheratu kwa machimo), limodzi ndi kudziŵa Yesu Kristu ndi Atate wake, kudzadzetsa thanzi langwiro ndi moyo wosatha.​—Yohane 3:16.

Chimwemwe m’Dziko Latsopano la Mulungu

Pamenepo, onani m’malingaliro dziko lopanda upandu, kuipitsa, kapena umphaŵi. Ikani m’chithunzithunzi banja lanu likumakhala mwamtendere m’Paradaiso wobwezeretsedwa. (Yesaya 32:17, 18) Kudzakhala kokondweretsa chotani nanga kuona mitundu yosiyanasiyana ya maonekedwe ndi maganizo ndi mphamvu zangwiro!

“Mkhalidwe wachibadwa kwa munthu ndiwo kukhala ndi moyo m’malo omasintha nthaŵi zonse​—a kuŵala, maonekedwe, mipangidwe. M’chilengedwe mulibe mkhalidwe wosasintha,” akutero Faber Birren. “Maonekedwe ndiwo chimodzi cha zinthu zachibadwa zokondweretsa za dzikoli. Ndiwo mkhalidwe wachilengedwe, nthaŵi zonse, ndipo mbali yaikulu ya moyo wokondweretsa imawadalira.”

Mphatso ya kuona ili yamtengo wapatali chotani nanga! Ha, kudzakhala kosangalatsa chotani nanga pamene maso amene panthaŵi ina anali akhungu​—mwakuthupi kapena mwauzimu​—adzapenya!

Inde, m’Paradaiso wobwezeretsedwa amene akudzayo, khungu ndi kupunduka kwina sizidzadzetsanso chisoni! Palibe amene adzasokeretsedwanso. Popeza chikondi chenicheni chidzafunga, onse adzaunikiridwa mwauzimu. Zimenezo, ndi zina zambiri, zili patsogolopa, koma pakali pano ndiyo nthaŵi ya kukhala ovomerezedwa ndi Uyo amene adzakwaniritsa lonjezo lake laulosi lakuti: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa”!​—Yesaya 35:5.

[Mawu a M’munsi]

a Chonde pendani umboni woperekedwa m’buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, mutu 18, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 7]

Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena