Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 8/15 tsamba 26-29
  • Kusunga Mgwirizano—Pakati pa Akulu ndi Atumiki Otumikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusunga Mgwirizano—Pakati pa Akulu ndi Atumiki Otumikira
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mbali ya Akulu ndi Atumiki Otumikira
  • Zimene Akulu Angachite
  • Atumiki Otumikira Ochirikiza Mgwirizano
  • Atumiki Othandiza Amagwira Ntchito Yofunika Kwambiri
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Akulu—Phunzitsani Ena Kusenza Maudindo
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Atumiki Othandiza Ali Ndi Udindo Wotani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Atumiki Otumikira Amachita Ntchito Yofunika
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 8/15 tsamba 26-29

Kusunga Mgwirizano​—Pakati pa Akulu ndi Atumiki Otumikira

POSAPITA nthaŵi pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E., panabuka zamwadzidzidzi mumpingo Wachikristu wongopangidwa kumene. Makonzedwe anali atapangidwa osamalirira akazi amasiye osoŵa. Koma patapita kanthaŵi pang’ono “kunauka chidandaulo, Aheleniste kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye awo anaiŵalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.”​—Machitidwe 6:1.

Madandaulo ameneŵa anamveka kwa atumwi. “Ndipo khumi ndi aŵiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, Sikuyenera kuti ife tisiye mawu a Mulungu ndi kutumikira podyerapo. Chifukwa chake, abale, yang’anani mwa inu amuna asanu ndi aŵiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi.”​—Machitidwe 6:2, 3.

Zimenezi zimasonyeza lamulo la mkhalidwe lofunika la kakonzedwe ka mkati mwa mpingo Wachikristu. Amuna ena athayo amagwiritsiridwa ntchito kusamalira zinthu zamasiku onse, pamene ena amasamalira mathayo okulirapo auzimu. Zimenezi sizili zopanda chitsanzo chakale. Mu Israyeli wakale, Aroni ndi mbadwa zake anaikidwa kutumikira monga ansembe kuti azipereka nsembe kwa Mulungu. Komabe, Yehova analamula kuti Alevi aziwathandiza mwa ‘kusunga zipangizo zonse za chihema chokomanako.’ (Numeri 3:5-10) Mofananamo, oyang’anira lerolino amathandizidwa ndi atumiki otumikira.

Mbali ya Akulu ndi Atumiki Otumikira

Malemba amalongosola ziyeneretso zapamwamba za akulu ndi atumiki otumikira. (1 Timoteo 3:1-10, 12, 13; Tito 1:6-9) Iwo sali opikisana koma amagwira ntchito ndi cholinga chimodzi​—kumangirira mpingo. (Yerekezerani ndi Aefeso 4:11-13.) Komano, pali kusiyana kwina kwa ntchito imene amachita mumpingo. Pa 1 Petro 5:2, oyang’anira amauzidwa kuti: “Ŵetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokangamiza, koma mwaufulu, . . . osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu.” Iwo ali ndi chifukwa kwa Mulungu cha mmene amasamalirira thayo lopatulika limeneli.​—Ahebri 13:17.

Bwanji ponena za atumiki otumikira? Malemba samafuna kwenikweni kuti iwo akhale ndi luso la kuphunzitsa lofanana ndi la akulu. Ntchito zawo nzosiyana ndi zija za akulu. Mosakayikira, m’zaka za zana loyamba C.E. panali zinthu zambiri zamtundu wakuthupi, zamasiku onse, kapena zofuna ntchito yamanja zimene zinafunikira kusamaliridwa, mwinamwake kuphatikizapo kugula zinthu zolembapo Malemba kapena ngakhale kulemba kwenikweniko.

Lerolino, atumiki otumikira amapitiriza kuchita ntchito zofunika zosiyanasiyana mumpingo, zonga ngati kusamalira maakaunti ndi mathayo a mpingo, kugaŵira abale magazini ndi mabuku, ndi kusamalira Nyumba Yaufumu. Atumiki otumikira ena okhala ndi luso angagwiritsiridwenso ntchito m’kuphunzitsa, nthaŵi zina kuchititsa Maphunziro Abuku Ampingo, kukamba nkhani pa Msonkhano Wautumiki, ndi kupereka nkhani zapoyera.

Pamene akulu ndi atumiki otumikira agwirira ntchito pamodzi mogwirizana, zosoŵa za mpingo​—zakuthupi ndi zakakonzedwe zomwe​—zimasamaliridwa mwanjira yabwino. Ndiyeno ziŵalo za mpingo zimakhala zachimwemwe, zolimba, ndi zobala zipatso mwauzimu. Kumbukirani zimene Paulo analembera odzozedwa ku Efeso: “Lokoŵanidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiŵalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.”​—Aefeso 4:16.

Akulu ndi atumiki otumikira ayenera kuyesayesa kukulitsa mgwirizano wofananawo, ndiko kuti, chimvano, chiyanjano, kugwirizanika ndi umodzi. Komabe, mgwirizano woterowo sumakhalapo mwa uwo wokha. Uyenera kukulitsidwa ndi kutetezeredwa mosamalitsa.

Zimene Akulu Angachite

Sitepe lofunika ndilo kuzindikira kuti unansi pakati pa mkulu ndi mtumiki wotumikira suli uja wa mbuye ndi kapolo wake kapena wa mwini ntchito ndi wantchito wake. Ngati pali mgwirizano weniweni, akulu amaona atumiki otumikira monga atumiki anzawo a Mulungu. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 3:6-9.) “Mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu,” amatero Aroma 12:10. Chotero akulu amapeŵa kuchitira atumiki otumikira mwanjira imene ingaoneke kukhala yowachepetsa kapena yowaluluza. Amachirikiza luso lawo loyenera la kuchita zinthu mmalo molifooketsa. Kuchitira ulemu atumiki otumikira kumakulitsa mikhalidwe yabwino mwa iwo ndipo kumawathandiza kusangalala ndi ntchito yawo mumpingo.

Akulu ayenera kukumbukiranso kuti ntchito yawo ya kuŵeta gulu la nkhosa la Mulungu lili mwa iwo imaphatikizapo abale amene akutumikira monga atumiki otumikira. Zoona, amuna athayo amenewo amayembekezeredwa kukhala Akristu okhwima. Komabe, mofanana ndi gulu lonse la nkhosa, amafunikira kusamaliridwa mwachindunji nthaŵi ndi nthaŵi. Akulu ayenera kusamalira kwambiri za kukula kwauzimu kwa atumiki otumikira.

Mwachitsanzo, pamene mtumwi Paulo anakumana ndi mnyamatayo Timoteo, anazindikira pomwepo kukhoza kwa Timoteo ndipo “anafuna kuti amuke naye.” (Machitidwe 16:3) Timoteo anatumikira monga woyenda naye wa Paulo, akumaphunzira zambiri chifukwa cha zimenezo. Eya, pambuyo pa zaka zambiri Paulo anakhoza kulembera Akristu ku Korinto kuti: “Ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Kristu”!​—1 Akorinto 4:17.

Akulu, kodi mwayamba kugwiritsira ntchito maluso oonekera a atumiki otumikira m’mipingo yanu? Kodi mumawathandiza kupita patsogolo mwa kuwaphunzitsa mwachindunji kulankhula nkhani zapoyera ndi kufufuza za m’Baibulo? Kodi mwapempha oyenerera kutsagana nanu pamaulendo akuŵeta? Kodi mumagwira nawo ntchito mu utumiki wakumunda? M’fanizo la Yesu la matalente, mbuyeyo anauza akapolo ake okhulupirika kuti: “Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika.” (Mateyu 25:23) Kodi nanunso muli owoloŵa manja mwa kutamanda ndi kuthokoza atumiki otumikira amene modekha amachita mathayo awo bwino lomwe? (Yerekezerani ndi Miyambo 3:27.) Ngati simumatero, kodi iwo sadzaona kuti ntchito yawo simayamikiridwa?

Kulankhulana kulinso kofunika kwambiri muunansi wogwirizana wa kugwirira ntchito pamodzi. (Yerekezerani ndi Miyambo 15:22.) Mathayo sayenera kugaŵiridwa kapena kulandidwa mwa njira yosalingalira molama kapena yopanda dongosolo. Akulu ayenera kukambitsirana mwapemphero mmene maluso a mbale angagwiritsidwire ntchito bwino mumpingo. (Yerekezerani ndi Mateyu 25:15.) Pamene mbale apatsidwa thayo, ayenera kulangizidwa bwino lomwe zimene afunikira kuchita. “Popanda upo wanzeru,” imatero Miyambo 11:14, “anthu amagwa.”

Sikwabwino kungouza mbale kuti ayambe kusamalira dipatimenti ya mtumiki wina, ya maakaunti, magazini, kapena mabuku. Nthaŵi zina mtumiki amene wangopatsidwa kumene thayolo angalandire kwa winayo zolembedwa zosalongosoka kapena zosakwanira. Zimenezo nzogwetsa ulesi chotani nanga! “Zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka,” amalangiza motero 1 Akorinto 14:40. Akulu ayenera kuyamba kuphunzitsa abale, kuwazoloŵeretsa za kayendetsedwe ka mpingo ndi kupereka chitsanzo iwo eniwo cha kutsatira kayendetsedweko. Mwachitsanzo, akulu ayenera kulinganiza kuti kuŵerengera maakaunti a mpingo kuzichitidwa pambuyo pa miyezi itatu iliyonse. Kunyalanyaza makonzedwe ofunika otero kungabutse mavuto ndi kululuza ulemu umene atumiki otumikira ali nawo pa malangizo a gulu.

Koma bwanji ngati mbale aoneka kukhala wosasamala posamalira thayo lake? Mmalo mofulumira kumchotsa pathayo lakelo, akulu ayenera kukambitsirana naye nkhaniyo. Mwinamwake vuto nlakuti sanaphunzitsidwe. Ngati mbaleyo apitirizabe kukhala ndi vuto posamalira thayo lake, mwinamwake angachite bwino pathayo lina.

Akulu angachirikizenso mgwirizanowo mwa kusonyeza kudzichepetsa. Afilipi 2:3 amalimbikitsa Akristu kuti “musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini.” Chotero mkulu ayenera kuvomereza ngati kalinde amuuza kukakhala pa mpando wina wake m’holo, popanda kulingalira kuti popeza kuti iye ndi mkulu, safunikira kulabadira. Mwinamwake kalindeyo akungotsatira lingaliro la kukhala m’mbali zosiyanasiyana za holoyo, ngakhale kuti ayenera kukumbukira kuti palibe lamulo lakuti onse ayenera kuchita zimenezo.a Mkulu amapeŵa kusintha mosafunikira malangizo pambali zoikidwa m’chisamaliro cha mtumiki wotumikira.

Atumiki Otumikira Ochirikiza Mgwirizano

“Momwemonso atumiki akhale olemekezeka,” anatero mtumwi Paulo. (1 Timoteo 3:8) Kuona kwawo mathayowo molemekezeka​—monga mbali ya utumiki wawo wopatulika​—kumathandiza kwambiri kuchinjiriza kubuka kwa mikangano. Ngati ndinu mtumiki wotumikira, kodi mumachita ntchito zanu mwakhama? (Aroma 12:7, 8) Kodi mukuyesayesa mwamphamvu kuti mukhale aluso posamalira ntchito zanu? Kodi ndinu wokhulupirika ndi wodalirika? Kodi mumasonyeza mzimu wakufunitsitsa ponena za mathayo? Mtumiki wotumikira wina m’dziko lina mu Afirika amasamalira mathayo atatu osiyanasiyana mumpingo. Kuganiza kwake? “Eya, kumangotanthauza ntchito yolimba yowonjezereka,” iye akutero, “ndipo ntchito yolimba simakupha ayi.” Ndithudi, awo amene amadzipereka amapeza chimwemwe chochuluka.​—Machitidwe 20:35.

Mungachitenso zochuluka kuti muchirikize mgwirizano mwa kugwirizana kwambiri ndi akulu. “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere,” amatero Ahebri 13:17, “pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.” Zoona, akulu ali anthu opanda ungwiro, ndipo kungakhale kosavuta kuwapeza ndi zifukwa. Koma mkhalidwe wosuliza umabala kusadalirana. Ungawononge chimwemwe chanu ndi kuyambukira ena moipa mumpingo. Chotero mtumwi Petro anapereka uphungu uwu: “Anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane . . . Potero dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthaŵi yake akakukwezeni.”​—1 Petro 5:4, 5, 6.

Uphungu wotero uli woyenerera kwambiri makamaka ngati muganiza kuti mukumanidwa mwaŵi wa utumiki. Mwinamwake mwakhala ‘mukukhumba udindo wa woyang’anira,’ koma simunaikidwe. (1 Timoteo 3:1) Kudzichepetsa kungakuthandizeni kukhalabe ndi “mkhalidwe wamaganizo woyembekezera.” (Maliro 3:24, NW) Mmalo mwa kuipidwa ndi akulu​—kumene kudzawonongadi unansi wanu wa kugwirira ntchito pamodzi​—afunseni ngati pali mbali zina zimene mufunikira kuwongolera. Mosakayikira kufunitsitsa kwanu moona mtima kulandira ndi kugwiritsira ntchito uphungu kudzaonedwa monga umboni wa kukula kwauzimu.

Kudzichepetsa kwaumulungu ndi kudekha kungathandize mtumiki wotumikira kusunga uchikatikati wake ngati ali ndi maluso apadera kapena ngati ali wophunzira kapena wapamwamba. Kungakhale kopereka chiyeso chotani nanga kwa iye kuyesa kutchipisa akulu kapena kuonetsera maluso ake! Miyambo 11:2 imatikumbutsa kuti “nzeru ili ndi [odekha, NW].” Mbale wodekha amadziŵa zopereŵera zake. Amafunitsitsa kugwira ntchito mwakachetechete, mosadzionetsera, ndi kugwiritsira ntchito maluso ake kuchirikiza akulu. Kudekha kungamthandizenso kuzindikira kuti pamene ali ndi chidziŵitso malinga ndi dziko, angakhalebe wopereŵera m’mbali zofunika za nzeru ndi luntha lauzimu​—mikhalidwe pa imene akulu angakhale opambana.​—1 Akorinto 1:26–2:13; Afilipi 1:9.

Mwachionekere, akulu ndi atumiki otumikira amachita mbali zofunika. Akhoza kuchitira limodzi zochuluka kumangirira onse mumpingo. Koma kuti achite zimenezo, ayenera kugwirira ntchito pamodzi mogwirizana, “ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi; ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.”​—Aefeso 4:2, 3.

[Mawu a M’munsi]

a Onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1992, tsamba 12.

[Zithunzi patsamba 27]

Akulu amaona atumiki otumikira, osati monga aang’ono, koma monga atumiki anzawo a Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena