Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 10/15 tsamba 21-26
  • Kodi Mumakhululukira Monga Momwe Yehova Amachitira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumakhululukira Monga Momwe Yehova Amachitira?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mose Apembedzera​—Yehova Amvetsera
  • Kupembedza Mafano kwa Manase ndi Chigololo cha Davide
  • Kupatulira Kachisi Kochitidwa ndi Solomo
  • Kukhululukira m’Malemba Achigiriki Achikristu
  • ‘Pitirizani Kukhululukirana Eni Okha’
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Yehova, Mulungu “Wokhululukira”
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Yehova Amakhululuka Kwambiri Kuposa Aliyense
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Nkukhaliranji Wokhululukira?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 10/15 tsamba 21-26

Kodi Mumakhululukira Monga Momwe Yehova Amachitira?

“Ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba. Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.”​—MATEYU 6:14, 15.

1, 2. Kodi timafunikira Mulungu wamtundu wotani, ndipo nchifukwa ninji?

“YEHOVA ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo, wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chochuluka. Sadzatsutsana nawo nthaŵi zonse; ndipo sadzasunga mkwiyo wake kosatha. Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Pakuti monga m’mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuwopa Iye. Monga kummaŵa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuwopa Iye. Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.”​—Salmo 103:8-14.

2 Polandiridwa mu uchimo ndi kubadwira m’mphulupulu, ndipo popeza kuti kupanda ungwiro kwa choloŵa nthaŵi zonse kumayesa kutiloŵetsa mu ukapolo wa lamulo la uchimo, tifunikira kwambiri Mulungu amene ‘amakumbukira kuti ife ndife fumbi.’ Patapita zaka mazana atatu kuyambira pamene Davide anafotokoza Yehova bwino kwambiri m’Salmo la 103, mlembi wina wa Baibulo, Mika, anatamanda Mulungu mmodzimodziyo m’njira yofanana kwambiri ndi imeneyo kaamba ka kukhululukira kwake kwachisomo machimo amene anachitidwa: “Kodi ndi mulungu uti amene angalingane nanu: wakuchotsa zolakwa, kukhululukira mlandu, wosasunga mkwiyo kosatha koma wokonda kusonyeza chifundo? Tichitireninso chisoni, pondapondani zolakwa zathu, ponyerani machimo athu pansi pa nyanja.”​—Mika 7:18, 19, The Jerusalem Bible.

3. Kodi kukhululukira kumatanthauzanji?

3 M’Malemba Achigiriki, liwu la “kukhululukira” limatanthauza “kulekerera.” Onani kuti Davide ndi Mika, ogwidwa mawu pamwambapa, akusonyeza tanthauzo limodzimodzilo m’mawu okopa ndi ofotokoza bwino. Kuti tizindikire mokwanira ukulu wodabwitsa wa kukhululukira kwa Yehova, tiyeni tipende zingapo za zitsanzo zake zambiri zimene zinachitika. Choyamba chimasonyeza kuti maganizo a Yehova angabwezedwe pa chiwonongeko ndi kuikidwa pa kukhululukira.

Mose Apembedzera​—Yehova Amvetsera

4. Kodi ndi pambuyo pa zisonyezero zotani za mphamvu ya Yehova pamene Aisrayeli anali amanthabe kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa?

4 Yehova anatulutsa mu Igupto mtundu wa Israyeli naubweretsa mosungika pafupi ndi dziko limene adawalonjeza kukhala kwawo, koma iwo anakana kupita, chifukwa chowopa anthu wamba m’Kanani. Pambuyo poona Yehova akuwalanditsa kuchokera ku Igupto mwa miliri yowononga khumi, kuwatsegulira njira yothaŵira kudutsa Nyanja Yofiira, kuwononga gulu la nkhondo la Igupto limene linayesa kuwatsatira, kuchita nawo pangano Lachilamulo pa Phiri la Sinai limene linawachititsa kukhala mtundu wosankhika wa Yehova, nawapatsa mana kuchokera kumwamba masiku onse mwanjira yozizwitsa kuti adye, iwo anachitabe mantha kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa chifukwa cha Akanani ena onga zimphona!​—Numeri 14:1-4.

5. Kodi ndimotani mmene azondi okhulupirika aŵiri anayesera kulimbitsa mtima Israyeli?

5 Mose ndi Aroni anagwetsa nkhope zawo movutika mtima. Yoswa ndi Kalebi, azondi aŵiri okhulupirika, anayesa kulimbitsa mtima Israyeli kuti: ‘Dzikolo ndilo lokometsetsa ndithu, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Musamawopa anthu; Yehova ali nafe.’ Mmalo molimbikitsidwa ndi mawu otero, anthu amanthawo ndi opanduka anafuna kuponya miyala Yoswa ndi Kalebi.​—Numeri 14:5-10.

6, 7. (a) Kodi Yehova anasankha kuchitanji pamene Aisrayeli anakana kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa? (b) Kodi nchifukwa ninji Mose sanavomereze chiweruzo cha Yehova pa Israyeli, ndipo panali zotulukapo zotani?

6 Yehova anakwiya! “Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pawo? Ndidzawakantha ndi mliri, ndi kuwachotsera choloŵa chawo, ndipo ndidzakusandutsa iwe mtundu wa anthu waukulu ndi wamphamvu koposa iwowa. Ndipo Mose anati kwa Yehova, Pamenepo Aigupto adzamva; popeza munakweza anthu awa ndi mphamvu yanu kuwachotsa pakati pawo; ndipo adzawauza okhala m’dziko muno. . . . Ndipo mukapha anthu awa ngati munthu mmodzi, pamenepo amitundu amene adamva mbiri yanu adzanena, ndi kuti, Popeza Yehova sanakhoza kuwaloŵetsa anthu awa m’dziko limene anawalumbirira, chifukwa chake anawapha m’chipululu.”​—Numeri 14:11-16.

7 Mose anapempha chikhululukiro, chifukwa cha dzina la Yehova kuti: “Khululukiranitu mphulupulu ya anthu awa, monga mwa chifundo chanu chachikulu, ndi monga mudalekerera anthu awa, kuyambira Aigupto kufikira tsopano. Ndipo Yehova anati, Ndakhululukira monga mwa mawu ako.”​—Numeri 14:19, 20.

Kupembedza Mafano kwa Manase ndi Chigololo cha Davide

8. Kodi Mfumu Manase wa Yuda anapanga mbiri yotani?

8 Chitsanzo chapandera cha kukhululukira kwa Yehova ndiyo nkhani ya Manase, mwana wa Mfumu yabwino Hezekiya. Manase anali ndi zaka 12 pamene anayamba kulamulira mu Yerusalemu. Iye anamanga misanje, namangira Abaala maguwa a nsembe, napanga milongoti yopatulika, nagwadira nyenyezi zakumwamba, nachita matsenga ndi zanyanga, naika obwebweta ndi openduza, naika fano losema m’kachisi wa Yehova, ndipo anapititsa ana ake m’moto m’Chigwa cha Hinomu. “Anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova” ndipo “analakwitsa Yuda ndi okhala m’Yerusalemu, kotero kuti anachita choipa koposa amitundu, amene Yehova anawawononga pamaso pa ana a Israyeli.”​—2 Mbiri 33:1-9.

9. Kodi ndimotani mmene Yehova anapembedzekera kulinga kwa Manase, ndipo panali zotsatirapo zotani?

9 Pomalizira pake, Yehova anachititsa Asuri kuukira Yuda, ndipo anagwira Manase namtengera ku Babulo. “Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wake, nadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake. Anampempha, ndipo anapembedzeka, namvera kupembedza kwake, nambwezera ku Yerusalemu m[u]ufumu wake.” (2 Mbiri 33:11-13) Ndiyeno Manase anachotsa milungu yachikunja, mafano, ndi maguwa a nsembe ndipo anazitayira kunja kwa mzinda. Anayamba kupereka nsembe pa guwa la nsembe la Yehova nachititsa Yuda kutumikira Mulungu woona. Chimenechi chinali chisonyezero chodabwitsa cha kufunitsitsa kwa Yehova kukhululukira pamene kudzichepetsa, pemphero, ndi kuwongolera zinthu kubala zipatso za kulapa.​—2 Mbiri 33:15, 16.

10. Kodi ndimotani mmene Davide anayesera kubisa tchimo lake ndi mkazi wa Uriya?

10 Tchimo la Mfumu Davide lachigololo ndi mkazi wa Uriya Mhiti nlodziŵika bwino. Iye sanangochita naye chigololo komanso anachita machenjera obisa tchimolo pamene mkaziyo anakhala ndi pathupi. Mfumu inalola Uriya kuchoka kunkhondo, akumayembekezera kuti iye akapita kunyumba kwake ndi kugonana ndi mkazi wake. Koma, chifukwa cha kulemekeza asilikali anzake amene anali kunkhondo, Uriya anapeŵa zimenezo. Ndiyeno Davide anamuitanira kuchakudya namledzeretsa, komabe Uriya sanaloŵe kwa mkazi wake. Pamenepo Davide anatumiza uthenga kwa kazembe wake wakuti aike Uriya kumene kunali nkhondo yolimba, kuti Uriya aphedwe, zimene zinachitikadi.​—2 Samueli 11:2-25.

11. Kodi ndimotani mmene Davide anafikira pa kulapa tchimo lake, komabe kodi nchiyani chinamchitikira?

11 Yehova anatumiza Natani mneneri wake kwa Davide kukavumbula tchimo la mfumu. “Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa.” (2 Samueli 12:13) Davide anadzimva kukhala waliwongo kwambiri chifukwa cha tchimo lake ndipo anasonyeza kulapa kwake m’pemphero laphamphu kwa Yehova: “Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka; nsembe yopsereza simuikonda. Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; inu, Mulungu simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.” (Salmo 51:16, 17) Yehova sanapeputsa pemphero la Davide loperekedwa kuchokera mumtima wosweka. Chikhalirechobe, Davide analandira chilango chachikulu, mogwirizana ndi mawu a Yehova ponena za kukhululukira pa Eksodo 34:6, 7 kuti: “Wosamasula wopalamula.”

Kupatulira Kachisi Kochitidwa ndi Solomo

12. Kodi Solomo anapempha chiyani panthaŵi ya kupatuliridwa kwa kachisi, ndipo kodi yankho la Yehova linali lotani?

12 Pamene Solomo anamaliza kumanga kachisi wa Yehova, iye anati m’pemphero la kupatulira nyumbayo: “Ndipo mverani mapembedzero a kapolo wanu ndi a anthu anu Israyeli, popemphera iwo kuloza konkuno; ndipo mumvere Inu m’Mwamba mokhala Inumo, ndipo pakumva Inu, mukhululukire.” Yehova anayankha kuti: “Ndikatseka kumwamba kuti pasakhale mvula, kapena ndikalamulira dzombe lithe za padziko, kapena ndikatumiza mliri mwa anthu anga; ndipo anthu anga otchedwa dzina langa akadzichepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zawo zoipa; pamenepo ndidzamvera m’Mwamba, ndi kukhululukira choipa chawo, ndi kuchiritsa dziko lawo.”​—2 Mbiri 6:21; 7:13, 14.

13. Kodi Ezekieli 33:13-16 amasonyeza chiyani ponena za mmene Yehova amaonera munthu?

13 Pamene Yehova akuyang’anani, amakulandirani monga momwe mulili tsopano, osati monga momwe munalili. Zili monga momwe Ezekieli 33:13-16 amanenera kuti: “Ndikanena kwa wolungama kuti adzakhala ndi moyo ndithu, akatama chilungamo chake, akachita chosalungama, sizikumbukika zolungama zake zilizonse; koma m’chosalungama chake anachichita momwemo adzafa. Ndipo ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu: koma akabwerera iye kuleka tchimo lake, nakachita choyenera ndi cholungama; woipayo akabweza chikole, nakabweza icho anachilanda mwachifwamba, nakayenda m’malemba a moyo wosachita chosalungama, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa. Zoipa zake zilizonse anazichita sizidzakumbukika zimtsutse, anachita choyenera ndi cholungama, adzakhala ndi moyo ndithu.”

14. Kodi nchiyani chimene chili chapadera ponena za kukhululukira kwa Yehova?

14 Kukhululukira kumene Yehova amatichitira kuli ndi mbali yapadera, imene ili yovuta kwa zolengedwa zaumunthu kuiphatikiza pa kukhululukira kumene amachitirana​—iye amakhululukira ndi kuiŵala. Anthu ena amanena kuti, ‘Ndingakhululukire zimene wachita, koma sindingaiŵale (kapena sindidzaiŵala).’ Mosiyana ndi zimenezo, onani zimene Yehova akunena kuti adzachita: “Ndidzakhululukira mphulupulu yawo, ndipo sindidzakumbukira tchimo lawo.”​—Yeremiya 31:34.

15. Kodi Yehova ali ndi mbiri yotani ya kukhululukira?

15 Yehova wakhala akukhululukira alambiri ake padziko lapansi kwa zaka zikwi zambiri. Wakhala akukhululukira machimo amene iwo akudziŵa kuti anawachita limodzinso ndi ambiri amene iwo sakudziŵa. Makonzedwe ake a chifundo, kuleza mtima, ndi kukhululukira akhala osatha. Yesaya 55:7 amati: “Woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.”

Kukhululukira m’Malemba Achigiriki Achikristu

16. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti kukhululukira kwa Yesu kuli kogwirizana ndi kwa Yehova?

16 Nkhani za kukhululukira kwa Mulungu zili zochuluka m’cholembedwa cha Malemba Achigiriki Achikristu. Yesu amalankhula za iko kaŵirikaŵiri, kusonyeza kuti iye amagwirizana ndi lingaliro la Yehova pankhaniyo. Kalingaliridwe ka Yesu kamachokera kwa Yehova, amasonyeza za Yehova, ali chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe cha Yehova; kuona iye ndiko kuona Yehova.​—Yohane 12:45-50; 14:9; Ahebri 1:3.

17. Kodi Yesu anafanizira motani kukhululukira “koposa” kwa Yehova?

17 Mkhalidwe wa Yehova wakuti amakhululukira koposa ukusonyezedwa m’limodzi la mafanizo a Yesu, lija la mfumu imene inakhululukira kapolo wake mangawa a matalente 10,000 (pafupifupi $33,000,000, U.S.). Koma pamene kapoloyo sanakhululukire kapolo mnzake mangawa a madinari zana limodzi (pafupifupi $60, U.S.), mfumuyo inakwiya. “Kapolo iwe woipa, ndinakukhululukira iwe mangawa onse aja momwe muja unandipempha ine; kodi iwenso sukadamchitira kapolo mnzako chisoni, monga inenso ndinakuchitira iwe chisoni? Ndipo mbuye wake anakwiya, nampereka kwa azunzi, kufikira akambwezere iye mangawa onse.” Ndiyeno Yesu anapereka tanthauzo lake kuti: “Chomwechonso Atate wanga adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.”​—Mateyu 18:23-35.

18. Kodi lingaliro la Petro la kukhululukira linali lotani poyerekezera ndi lingaliro la Yesu?

18 Yesu asanapereke fanizo lili pamwambalo, Petro anadza kwa Yesu nafunsa kuti: “Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? kufikira kasanu ndi kaŵiri kodi?” Petro anaganiza kuti anali kusonyeza kuoloŵa manja kwambiri. Ngakhale kuti alembi ndi Afarisi anaika malire a kukhululukira, Yesu anati kwa Petro: “Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kaŵiri, koma kufikira makumi asanu ndi aŵiri kubwerezedwa kasanu ndi kaŵiri.” (Mateyu 18:21, 22) Kasanu ndi kaŵiri sikakakhala kokwanira patsiku limodzi, monga momwe Yesu ananenera kuti: “Kadzichenjerani nokha; akachimwa mbale wako umdzudzule; akalapa, umkhululukire. Ndipo akakuchimwira kasanu ndi kaŵiri pa tsiku lake, nakakutembenukira kasanu ndi kaŵiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira.” (Luka 17:3, 4) Pamene Yehova akhululukira, samatisungira mangawa athu​—ndi mwaŵi wathu umenewo.

19. Kodi tiyenera kuchitanji kuti Yehova atikhululukire?

19 Ngati tili ndi kudzichepetsa kwa kulapa ndi kuulula machimo athu, Yehova amatiyanja: “Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.”​—1 Yohane 1:9.

20. Kodi ndi kufunitsitsa kotani kwa kukhululukira tchimo kumene Stefano anasonyeza?

20 Wotsatira wa Yesu, Stefano, ndi mzimu wodabwitsa wa kukhululukira, anapempha mofuula pamene gulu lokwiya linali kumponya miyala kuti: “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga. Ndipo mmene anagwada pansi, anafuula ndi mawu aakulu, [Yehova, NW], musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo mmene adanena ichi, anagona tulo.”​—Machitidwe 7:59, 60.

21. Kodi nchifukwa ninji kufunitsitsa kwa Yesu kukhululukira asilikali Achiroma kunali kodabwitsa koposa?

21 Yesu anaperekadi chitsanzo chodabwitsa koposa cha kufunitsitsa kukhululukira. Adani ake anali atamgwira, namzenga mlandu mosayenera, namweruza, namjeda, namlavulira malovu, namkwapula ndi mkwapulo wa malamba ambiri amene mwinamwake anali ndi tizidutswa ta mafupa ndi zitsulo, ndipo pomalizira pake namsiya wokhomeredwa pamtengo kwa maola ambiri. Mbali yaikulu ya zimenezi inachitidwa ndi Aroma. Komabe, pamene Yesu anali kufa pamtengo wozunzirapo, iye anati kwa Atate wake wakumwamba ponena za asilikali amene anampachika: “Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziŵa chimene achita.”​—Luka 23:34.

22. Kodi ndi mawu ati a mu Ulaliki wa pa Phiri amene tiyenera kuyesayesa kugwiritsira ntchito?

22 Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anali atanena kuti: “Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu.” Kufikira mapeto a utumiki wake wa padziko lapansi, iye mwiniyo anatsatira lamulo la mkhalidwe limenelo. Kodi zimenezo zimafuna zopambanitsa kwa ife, amene timalimbana ndi zofooka za thupi lathu lochimwa? Tiyenera kuyesayesa kugwiritsira ntchito mawu amene Yesu anaphunzitsa otsatira ake atawapatsa pemphero la chitsanzo: “Ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba. Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.” (Mateyu 5:44; 6:14, 15) Ngati tikhululukira monga momwe Yehova amakhululukira, tidzakhululukira ndi kuiŵala.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi Yehova amachita motani ndi machimo athu, ndipo nchifukwa ninji?

◻ Kodi nchifukwa ninji Manase anaikidwanso pa ufumu wake?

◻ Kodi ndi mbali iti yapadera imene kukhululukira kwa Yehova kuli nayo imene ili yovuta kwa anthu kuitsanzira?

◻ Kodi ndimotani mmene kufunitsitsa kwa Yesu kukhululukira kunalili kodabwitsa koposa?

[Chithunzi patsamba 24]

Natani anathandiza Davide kuona kufunikira kwa chikhululukiro cha Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena