Yobu Anapirira—Nafenso Tingatero!
“Taonani tiwayesera odala opirirawo.”—YAKOBO 5:11.
1. Kodi nchiyani chimene Mkristu wina wokalamba ananena ponena za mayesero ake?
‘MDYEREKEZI akunditsata! Ndikudziona ngati Yobu!’ Ndi mawu amenewo A. H. Macmillan anafotokoza malingaliro ake kwa bwenzi lake lapamtima ku malikulu a Mboni za Yehova. Mbale Macmillan anamaliza njira yake ya padziko lapansi pausinkhu wa zaka 89 pa August 26, 1966. Iye anadziŵa kuti thamo la utumiki wokhulupirika wa Akristu odzozedwa monga iye ‘likatsatana nawo pamodzi.’ (Chivumbulutso 14:13) Ndithudi, iwo akapitirizabe kutumikira Yehova mwa kuukitsidwira kumoyo wosafa kumwamba. Mabwenzi ake anakondwera kuti Mbale Macmillan anapeza mfupo imeneyo. Komabe, m’zaka zake zomaliza, anazingidwa ndi mayesero osiyanasiyana, kuphatikizapo mavuto athanzi amene anamchititsa kuzindikira kwambiri zoyesayesa za Satana za kuswa umphumphu wake kwa Mulungu.
2, 3. Kodi Yobu anali yani?
2 Pamene Mbale Macmillan ananena kuti anadziona ngati Yobu, iye anali kunena za munthu amene anapirira mayeso aakulu a chikhulupiriro. Yobu anakhala “m’dziko la Uzi,” mwinamwake kumpoto kwa Arabiya. Monga mbadwa ya mwana wa Nowa, Semu, iye anali wolambira Yehova. Mwachionekere, mayeso a Yobu anachitika panthaŵi ina pakati pa imfa ya Yosefe ndi nthaŵiyo pamene Mose anadzisonyeza kukhala woongoka. Mkati mwa nyengo imeneyo padziko lapansi panalibe munthu amene anafanana ndi Yobu m’kudzipereka kwaumulungu. Yehova anaona Yobu monga munthu wangwiro, woongoka, wa kuwopa Mulungu.—Yobu 1:1, 8.
3 Monga ‘munthu woposa anthu onse a kummaŵa,’ Yobu anali ndi antchito ambiri, ndipo zifuyo zake zinafika 11,500. Komabe chuma chauzimu chinali chofunika koposa kwa iye. Mofanana ndi atate owopa Mulungu a lerolino, mwachionekere Yobu anaphunzitsa ana ake aamuna asanu ndi aŵiri ndi ana ake aakazi atatu za Yehova. Ngakhale pamene iwo sanalinso kukhala m’nyumba mwake, iye anachita monga wansembe wa banjalo mwa kuwaperekera nsembe, kuwopera kuti mwina iwo anali atachimwa.—Yobu 1:2-5.
4. (a) Kodi nchifukwa ninji Akristu ozunzidwa ayenera kulingalira za munthuyo Yobu? (b) Ponena za Yobu, kodi ndi mafunso otani amene tidzalingalira?
4 Yobu ndiye munthu amene Akristu ozunzidwa ayenera kumlingalira kuti adzilimbitse popirira moleza mtima. “Taonani,” analemba motero wophunzira Yakobo. “Tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Mofanana ndi Yobu, otsatira odzozedwa a Yesu ndi “khamu lalikulu” lamakono afunikira chipiriro kuti alimbane ndi mayeso a chikhulupiriro. (Chivumbulutso 7:1-9) Chotero, kodi ndi mayesero otani amene Yobu anapirira? Kodi nchifukwa ninji anachitika? Ndipo kodi tingapindule motani ndi zokumana nazo zake?
Nkhani Yaikulu
5. Kodi nchiyani chimene chinali kuchitika kumwamba, popanda Yobu kudziŵa?
5 Popanda Yobu kudziŵa, nkhani ina yaikulu inali pafupi kudzutsidwa kumwamba. Tsiku lina “ana a Mulungu anadza kudzionetsa kwa Yehova.” (Yobu 1:6) Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, Mawuyo, anali pamenepo. (Yohane 1:1-3) Panalinso angelo olungama ndi ‘ana a Mulungu’ aungelo osamvera. (Genesis 6:1-3) Satana anali pamenepo, pakuti kuthamangitsidwa kwake kumwamba kunali kudzachitika pambuyo pa kukhazikitsidwa kwa Ufumu mu 1914. (Chivumbulutso 12:1-12) M’tsiku la Yobu, Satana akadzutsa nkhani yaikulu. Iye anali pafupi kuyambitsa chikayikiro pa kuyenera kwa ulamuliro wa Yehova pa zolengedwa Zake zonse.
6. Kodi Satana anali kuyesa kuchita chiyani, ndipo kodi iye ananeneza Yehova motani?
6 “Ufuma kuti?” Yehova anafunsa motero. Satana anayankha kuti: “Kupitapita m’dziko ndi kuyendayenda m’mwemo.” (Yobu 1:7) Iye anali kufunafuna wina kuti amlikwire. (1 Petro 5:8, 9) Mwa kuswa umphumphu wa anthu otumikira Yehova, Satana akayesa kusonyeza kuti palibe aliyense amene akamvera Mulungu kotheratu chifukwa cha chikondi. Polunjika pankhaniyo, Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuwopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa.” (Yobu 1:8) Yobu anakwaniritsa miyezo yaumulungu imene inalolera kupanda ungwiro kwake. (Salmo 103:10-14) Koma Satana anayankha kuti: “Kodi Yobu awopa Mulungu pachabe? Kodi simunamchinga iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoŵeta zake zachuluka m’dziko.” (Yobu 1:9, 10) Motero Mdyerekezi ananeneza Yehova mwa kupereka lingaliro lakuti palibe aliyense amene amakonda Iye ndi kumlambira chifukwa cha zimene Iye ali koma kuti Iye amafumbatitsa zolengedwa zake kuti zizilambira Iye. Satana anaumirira kunena kuti Yobu anatumikira Mulungu pa chifukwa cha dyera, osati chifukwa cha chikondi.
Satana Aukira!
7. Kodi Mdyerekezi anatokosa Mulungu m’njira yotani, ndipo kodi Yehova anachita motani?
7 “Koma,” anatero Satana, “mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pankhope panu.” Kodi ndimotani mmene Mulungu akachitira ndi chipongwe chotero? “Taona,” Yehova anatero. “Zonse ali nazo zikhale m’dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako.” Mdyerekezi ananena kuti zonse zimene Yobu anali nazo zinadalitsidwa, kuwonjezeredwa, ndi kutetezeredwa. Mulungu akalola Yobu kuvutika, koma thupi lake lokha silikafunikira kukhudzidwa. Ali wotsimikiza kukachita choipacho, Satana anachoka pamsonkhanopo.—Yobu 1:11, 12.
8. (a) Kodi ndi chuma chakuthupi chotani chimene Yobu anatayikiridwa? (b) Kodi nchiyani chimene chinali choonadi ponena za “moto wa Mulungu”?
8 Posapita nthaŵi, chiukiro chausatana chinayamba. Mmodzi wa antchito a Yobu anambweretsera mbiri yoipa iyi: “Ng’ombe zinalikulima, ndi abulu aakazi analikudya pambali pawo; koma anazigwera Aseba, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa.” (Yobu 1:13-15) Chitetezo chinali chitachotsedwa pa chuma cha Yobu. Pafupifupi nthaŵi yomweyo, mphamvu yauchiŵanda yeniyeni inagwiritsiridwa ntchito, pakuti wantchito winanso anasimba kuti: “Wagwa moto wa Mulungu wochokera kumwamba, wapsereza nkhosa ndi anyamata, nuzinyeketsa.” (Yobu 1:16) Ha, kunali kwauchiŵanda chotani nanga kupangitsa zimenezi kuonekera ngati kuti Mulungu ndiye anali ndi mlandu wa tsoka lotero pa mtumiki wake! Popeza kuti mphezi imachokera kumwamba, Yehova akanaimbidwa mlandu mosavuta, komatu motowo unali wochokera kwa ziŵanda.
9. Kodi ndimotani mmene kuwonongeka kwa chuma kunayambukirira unansi wa Yobu ndi Mulungu?
9 Pamene Satana anapitirizabe kuukirako, wantchito winanso anasimba kuti Akasidi anali atatenga ngamila za Yobu ndipo anali atapha anyamata ena onse. (Yobu 1:17) Ngakhale kuti chuma cha Yobu chinawonongeka motero, zimenezi sizinawononge unansi wake ndi Mulungu. Kodi inu mungapirire pa kutayikiridwa ndi zinthu zambirimbiri popanda kuswa umphumphu wanu kwa Yehova?
Tsoka Lokulirapo Likantha
10, 11. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitikira ana khumi a Yobu? (b) Pambuyo pa imfa yomvetsa chisoni ya ana a Yobu, kodi iyeyo anaona Yehova motani?
10 Mdyerekezi anali asanathane ndi Yobu. Wantchito winanso anasimba kuti: “Ana anu aamuna ndi aakazi analinkudya ndi kumwa vinyo m’nyumba ya mkulu wawo; ndipo taonani, inadza mphepo yaikulu yochokera kuchipululu, niwomba pa ngondya zonse zinayi za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.” (Yobu 1:18, 19) Anthu osadziŵa anganene kuti kuwononga kumene kunachitidwa ndi mphepoyo kunali ‘chochita cha Mulungu.’ Komabe, mphamvu yauchiŵanda inakantha Yobu popweteka.
11 Atadzazidwa ndi chisoni, Yobu ‘anang’amba malaya ake, nameta mutu wake, nagwa pansi, nalambira.’ Komabe, mvetserani mawu ake. “Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.” Cholembedwacho chimanenanso kuti: “Mwa ichi chonse Yobu sanachimwa, kapena kunenera Mulungu cholakwa.” (Yobu 1:20-22) Kachiŵirinso Satana anali atagonjetsedwa. Bwanji ngati tiferedwa monga atumiki a Mulungu? Kudzipereka kwathu kopanda dyera kwa Yehova ndi kumkhulupirira zingatikhozetse kupirira monga osunga umphumphu, monga momwe Yobu anachitira. Odzozedwa ndi mabwenzi awo amene ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi angapezedi chitonthozo ndi nyonga m’cholembedwa chimenechi cha chipiriro cha Yobu.
Nkhaniyo Ikula Kwambiri
12, 13. Pamsonkhano wina kumwamba, kodi nchiyani chimene Satana anapempha, ndipo kodi Mulungu anachita motani?
12 Posakhalitsa Yehova anaitanitsa msonkhano wina kumabwalo akumwamba. Yobu anakhala wopanda mwana, munthu wosautsidwa, woonekera ngati kuti anakanthidwa ndi Mulungu, koma umphumphu wake unali chilimbire. Zoonadi, Satana sanavomereze kuti zinenezo zakezo kwa Mulungu ndi Yobu zinali zonama. Tsopano ‘ana a Mulungu’ anayembekezera kumva chinenezo ndi kutsutsidwa kwa chinenezocho pamene Yehova anachititsa Mdyerekezi kufikitsa nkhaniyo pachimake.
13 Pofunsa Satana, Yehova anati: “Ufuma kuti?” Yankho lake? “Kupitapita m’dziko, ndi kuyendayenda m’mwemo.” Kachiŵirinso Yehova anasonyeza mtumiki wake Yobu kukhala munthu wangwiro, woongoka, wakuwopa Mulungu, amene anali kusungabe umphumphu wake. Mdyerekezi anayankha kuti: “Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake. Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.” Chotero Mulungu anati: “Taona, akhale m’dzanja lako; moyo wake wokha uuleke.” (Yobu 2:2-6) Popereka lingaliro lakuti Yehova anali asanachotsebe zomchinga zonse, Satana anapempha kukhudza fupa ndi mnofu wa Yobu. Mdyerekezi sanaloledwe kupha Yobu; koma Satana anadziŵa kuti nthenda yakuthupi ikamumvetsa ululu ndi kumchititsa kuonekera ngati kuti anali kulangidwa ndi Mulungu chifukwa cha machimo amtseri.
14. Kodi Satana anakantha Yobu ndi chiyani, ndipo nchifukwa ninji panalibe munthu amene akanachiritsa wovutikayo?
14 Atachoka pamsonkhanopo, Satana anapita ali wokondwa mwauchiŵanda. Iye anakantha Yobu ndi “zilonda zoŵaŵa, kuyambira ku phazi lake kufikira pakati pamutu pake.” Ha, ndi nsautso yotani nanga imene Yobu anapirira pamene anakhala pansi m’mapulusa nadzikanda ndi phale! (Yobu 2:7, 8) Palibe sing’anga waumunthu amene akanamchiritsa nthenda yoŵaŵa, yonyansa, ndi yochititsa manyazi imeneyi, pakuti inachititsidwa ndi mphamvu yausatana. Ndi Yehova yekha amene akanachiritsa Yobu. Ngati inu muli mtumiki wa Mulungu amene akudwala, musaiŵale konse kuti Mulungu angakuthandizeni kupirira ndipo angakupatseni moyo m’dziko latsopano lopanda matenda.—Salmo 41:1-3; Yesaya 33:24.
15. Kodi nchiyani chimene mkazi wa Yobu anamsonkhezera kuchita, ndipo kodi iye anachita motani?
15 Potsirizira pake, mkazi wa Yobu anati: “Kodi uumiriranso kukhala [waumphumphu, NW]? chitira Mulungu mwano, ufe.” “Umphumphu” umatanthauza kudzipereka kosanenezedwa, ndipo mwina mkaziyo angakhale atanena mawuwa monyodola kuchititsa Yobu kuti achitire mwano Mulungu. Koma iye anayankha kuti: “Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa?” Ngakhalenso machenjera ameneŵa a Satana sanagwire ntchito, pakuti tikuuzidwa kuti: “Pa ichi chonse Yobu sanachimwa ndi milomo yake.” (Yobu 2:9, 10) Tinene kuti ziŵalo za banja zotsutsa zinanena kuti tinali kuthera mphamvu zathu mopanda nzeru m’ntchito Zachikristu ndi kutilimbikitsa kukana Yehova Mulungu. Ife monga Yobu, tingapirire mayeso otero chifukwa chakuti timakonda Yehova ndipo timakhumba kutamanda dzina lake loyera.—Salmo 145:1, 2; Ahebri 13:15.
Onyenga Atatu Onyada
16. Kodi ndani amene akunenedwa kukhala atadza kudzatonthoza Yobu, koma kodi ndimotani mmene Satana anawagwiritsirira ntchito?
16 Zimene zinalinso machenjera ausatana zinachitika pamene “mabwenzi” atatu anati anadza kudzatonthoza Yobu. Mmodzi wa iwo anali Elifazi, amene mwina anali mbadwa ya Abrahamu kupyolera mwa Esau. Popeza kuti Elifazi ndiye amene anayamba kulankhula, mosakayikira iyeyo anali wamkulu pa onse. Panalinso Bilidadi, mbadwa ya Suwa, mmodzi wa ana aamuna a Abrahamu mwa Ketura. Wachitatu anali Zofari, wa ku Naama, dzina lodziŵikitsa banja lake kapena kwawo, mwinamwake kumpoto chakumadzulo kwa Arabiya. (Yobu 2:11; Genesis 25:1, 2; 36:4, 11) Monga awo amene amayesa kupangitsa Mboni za Yehova kukana Mulungu lerolino, atatu ameneŵa anagwiritsiridwa ntchito ndi Satana kuyesayesa kuchititsa Yobu kuvomereza kukhala waliwongo pa zinenezo zonama ndi kuswa umphumphu wake.
17. Kodi nchiyani chimene ozonda atatuwo anachita, ndipo kodi sanachitenji kwa masiku asanu ndi aŵiri usana ndi usiku?
17 Atatuwo anachita chisonyezero chachikulu cha kugwidwa ndi chisoni mwa kulira, kung’amba malaya awo, ndi kuwaza fumbi kumwamba kuti ligwe pamitu pawo. Komano iwo anakhala pansi ndi Yobu kwa masiku asanu ndi aŵiri usana ndi usiku popanda kulankhula kanthu kotonthoza! (Yobu 2:12, 13; Luka 18:10-14) Onyenga atatu onyada ameneŵa analibiretu mkhalidwe wauzimu kwakuti analibe kanthu kalikonse koti anene kotonthoza ponena za Yehova ndi malonjezo ake. Komabe, iwo anali kulingalira zolakwa nakonzekera kudzazigwiritsira ntchito pa Yobu atangomaliza kuchita mwambo wa kumva chisoniwo. Mokondweretsa, kukhala kwawo chete kumeneko kwa masiku asanu ndi aŵiri kusanathe, mnyamata wina Elihu anadzakhala pamalo apafupi pamene anatha kumvetsera.
18. Kodi nchifukwa ninji Yobu analakalaka kufa kuti apeze mpumulo?
18 Potsirizira pake Yobu anayamba kulankhula. Pokhala wosapeza chitonthozo kwa atatu odzamzondawo, anatemberera tsiku lake la kubadwa nadabwa chifukwa chake moyo wake wamavutowo unali kupitiriza. Analakalaka kufa kuti apeze mpumulo, wosalingalira konse kuti adzakhalanso ndi chisangalalo chenicheni asanafe, popeza kuti tsopano anali wosoŵa, woferedwa, ndi wodwala kwambiri. Koma Mulungu sanalole kuti Yobu akhudzidwe kufikira imfa.—Yobu 3:1-26.
Oimba Mlandu Yobu Aukira
19. Kodi ndi m’nkhani ziti zimene Elifazi anaimba mlandu Yobu monama?
19 Elifazi ndiye amene anayamba kulankhula m’kukambitsirana kwakukulu kwa zigawo zitatu kumene kunayesa umphumphu wa Yobu mowonjezereka. M’kulankhula kwake koyamba, Elifazi anafunsa kuti: “Oongoka mtima alikhidwa kuti?” Iye anati Yobu ayenera kukhala atachita kanthu kena koipa polangidwa ndi Mulungu motero. (Yobu, machaputala 4, 5) M’kulankhula kwake kwachiŵiri, Elifazi ananyodola nzeru ya Yobu namfunsa kuti: “Udziŵa chiyani, osachidziŵa ife?” Elifazi anapereka lingaliro lakuti Yobu anali kuyesa kudzisonyeza kukhala wopambana kwa Wamphamvuyonse. Pomaliza kuukira kwake kwachiŵiriko, iye anafotokoza Yobu kukhala wopalamula mlandu wa mpatuko, wokonda chiphuphu, ndi wachinyengo. (Yobu, chaputala 15) M’kulankhula kwake komaliza, Elifazi anaimba mlandu Yobu monama wa maupandu ambiri—kulanda, kumana osauka mkate ndi madzi, ndi kutsendereza akazi amasiye ndi ana amasiye.—Yobu, chaputala 22.
20. Kodi ziukiro za Bilidadi zinali zotani pa Yobu?
20 Pokhala wachiŵiri m’kukambitsirana kwa zigawo zitatuko, Bilidadi nayenso anangotsatira njira ya Elifazi. Zolankhula za Bilidadi zinali zazifupi komano zopweteka kwambiri. Iye anaimbadi mlandu ana a Yobu wa kuchita zolakwa nayenera kufa chifukwa cha zimenezo. Akumalingalira molakwa, iye anagwiritsira ntchito fanizo ili: Monga gumbwa ndi manchedza auma ndi kufa popanda madzi, moteronso zili chimodzimodzi kwa “onse oiŵala Mulungu.” Mawu amenewo ngoona, komatu anali osagwira ntchito kwa Yobu. (Yobu, chaputala 8) Bilidadi anasimba kuti mavuto a Yobu ndi amene amafikira anthu oipa. (Yobu, chaputala 18) M’kulankhula kwake kwakufupi kwachitatu, Bilidadi ananenetsa kuti munthu ali ngati “mphutsi” ndi “nyongolotsi” ndipo chifukwa chake ngwodetsedwa pamaso pa Mulungu.—Yobu, chaputala 25.
21. Kodi Zofari anaimba Yobu mlandu wa chiyani?
21 Zofari anali wachitatu kulankhula m’kukambitsiranako. Kaŵirikaŵiri, lingaliro lake linali lofanana ndi la Elifazi ndi Bilidadi. Zofari anaimba mlandu Yobu wa kuipa ndi kumlimbikitsa kuleka ntchito zake zauchimo. (Yobu, machaputala 11, 20) Pambuyo pa zigawo ziŵiri Zofari analeka kulankhula. Analibe zowonjezera m’kukambitsirana kwa chigawo chachitatu. Komabe, nthaŵi yonseyi, Yobu anayankha omuimba mlandu ake molimba mtima. Mwachitsanzo, panthaŵi ina iye anati: “Inu nonse ndinu otonthoza mtima mondilemetsa. Kodi adzatha mawu ouluzika?”—Yobu 16:2, 3.
Tingapirire
22, 23. (a) Monga momwe zinalili kwa Yobu, kodi Mdyerekezi angayeseyese motani kuswa umphumphu wathu kwa Yehova Mulungu? (b) Ngakhale kuli kwakuti Yobu anali kupirira mayeso osiyanasiyana, kodi tingafunsenji ponena za mkhalidwe wake wamaganizo?
22 Monga Yobu, ife tingayang’anizane ndi mayesero ambiri panthaŵi imodzi, ndipo Satana angagwiritsire ntchito kulefula kapena zinthu zina m’kuyesayesa kwake kuswa umphumphu wathu. Iye angayese kutichotsa kwa Yehova ngati tili ndi mavuto azachuma. Ngati wokondedwa amwalira kapena ngati tidwala, Satana angayeseyese kutisonkhezera kuimba mlandu Mulungu. Mofanana ndi mabwenzi a Yobu, munthu wina angatiimbedi mlandu monama. Monga momwe Mbale Macmillan anasonyezera, Satana angakhale ‘akutitsata,’ koma ife tingapirire.
23 Monga momwe taonera kufikira pano, Yobu anali kupirira mayesero ake osiyanasiyana. Komabe, kodi iye anali kungopirira? Kodi iye anaswekadi mtima? Tiyeni tione ngati Yobu anatayadi chiyembekezo chonse.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndi nkhani yaikulu iti imene Satana anadzutsa m’tsiku la Yobu?
◻ Kodi Yobu anayesedwa kotheratu m’njira zotani?
◻ Kodi “mabwenzi” atatu a Yobu anamuimba mlandu wotani?
◻ Monga momwe zinalili kwa Yobu, kodi ndimotani mmene Satana angayesere kuswa umphumphu wathu kwa Yehova?
[Chithunzi patsamba 10]
A. H. Macmillan