Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 1/1 tsamba 20-23
  • Chuma Chosayerekezereka Chogaŵana ndi Ena

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chuma Chosayerekezereka Chogaŵana ndi Ena
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chitsanzo Chosonkhezera cha Amayi
  • Kugaŵana Chuma Chathu ndi Ena Kwanthaŵi Yonse
  • Kukwaniritsa Chonulirapo
  • Malta ndi Libya
  • Gawo Latsopano
  • Malo a Akhate
  • Kuchirikizidwa ndi Chumacho
  • Yehova Anandiphunzitsa Kuchita Chifuniro Chake
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kuchereza kwa Melita Kudzetsa Madalitso
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kusumika Maso ndi Mtima Pamphoto
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Sindidzasiya Kutumikira Mlengi Wanga
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 1/1 tsamba 20-23

Chuma Chosayerekezereka Chogaŵana ndi Ena

YOSIMBIDWA NDI GLORIA MALASPINA

Pamene gombe la Sicily linazimiririka, ine ndi mwamuna wanga tinayamba kulingalira za komwe tinali kupita, ku chisumbu cha m’Mediterranean cha Malta. Ha, chinali chiyembekezo chokondweretsa chotani nanga! Pamene sitima ya panyanja inali kudutsa nyanjayo, tinakumbukira chokumana nacho cha mtumwi Paulo pa Melita [Malta] mkati mwa zaka za zana loyamba.​—MACHITIDWE 28:1-10.

CHAKACHO chinali 1953, ndipo panthawiyo Malta sanaloleze ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova. Chaka chake chapitacho, tinali titangomaliza kumene maphunziro ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ndipo tinagaŵiridwa ku Italy. Titangophunzira Chitaliyana kwanthaŵi yaifupi, tinali ofunitsitsa kuona zimene zinali kutiyembekezera pa Malta.

Kodi ndimotani mmene ineyo, mkazi wachichepere, ndinafikira kukhala mmishonale wa dziko lachilendo? Lekani ndilongosole.

Chitsanzo Chosonkhezera cha Amayi

Mu 1926, pamene banja lathu linali kukhala ku Fort Frances, Ontario, ku Canada, amayi analandira kabukuko Millions Now Living Will Never Die kwa Wophunzira Baibulo wina (monga momwe Mboni za Yehova zinadziŵidwira panthawiyo). Analiŵerenga ndi chidwi chachikulu, ndipo mlungu womwewo anafika pa kagulu ka phunziro la Baibulo, akumagwiritsira ntchito magazini a Watch Tower. Amayi anali woŵerenga Baibulo wakhama, ndipo analandira uthenga wonena za Ufumu wa Mulungu monga chuma chimene anali kufunafuna. (Mateyu 6:33; 13:44) Mosasamala kanthu kuti Atate anawatsutsa mwachiwawa, ndipo ngakhale kuti iwo anali ndi ana aakazi atatu oti awasamalire, anachirimika pa zimene anali kuphunzira.

Chikhulupiriro chosagwedera cha amayi mkati mwa zaka 20 zotsatira chinachititsa ine ndi akulu angawo, Thelma ndi Viola, kuzindikira chiyembekezo chabwino kwambiri cha moyo wosatha m’dziko latsopano lachilungamo. (2 Petro 3:13) Iwo analimbana ndi mayesero ambiri ovuta, komano sitinakayikire konse za kulondola kwa njira yawo imene anasankha.

Mu 1931, pamene ndinali ndi zaka khumi zokha, tinasamukira ku famu ina kumpoto kwa Minnesota, U.S.A. Kumeneko tinali tokhatokha osasonkhana ndi Mboni za Yehova mokhazikika koma sitinasiye kulandira malangizo a Amayi a m’Baibulo. Utumiki wawo wodzipereka monga mkoputala, kapena mtumiki wanthaŵi yonse, unandisonkhezera kufuna kugwirizana nawo m’ntchito imeneyo. Mu 1938 ine ndi akulu anga aŵiriwo tinasonyeza kudzipatulira kwathu kwa Yehova mwa kubatizidwa pa msonkhano wina ku Duluth, Minnesota.

Nditamaliza sukulu ya sekondale mu 1938, Amayi anandilimbikitsa kulembetsa kosi yophunzira ntchito za muofesi kotero kuti ndidzadzichirikize monga mpainiya (dzina latsopano la mkoputala). Zimenezi zinakhaladi chilangizo chabwino, makamaka popeza kuti Atate anasankha kuchoka ndi kutisiya tokhatokha.

Kugaŵana Chuma Chathu ndi Ena Kwanthaŵi Yonse

Potsirizira pake ndinasamukira ku California, ndipo mu 1947, ndinayamba ntchito yaupainiya ku San Francisco. Pamene ndinali pa ntchito yokonzekera Msonkhano wa “Chifutukuko cha m’Mitundu Yonse” ku Los Angeles, ndinakumana ndi Francis Malaspina. Chonulirapo chathu chimodzi cha ntchito yaumishonale chinachititsa kuti tikondane. Tinakwatirana mu 1949.

Mu September 1951, ine ndi Francis tinaitanidwa kukaloŵa kalasi la 18 la Gileadi. Patsiku la kumaliza maphunziro, February 10, 1952, pambuyo pa miyezi isanu ya maphunziro akuya, maiko amene tinali kutumizidwako anatchulidwa m’dongosolo la mndandanda wa malembo ndi pulezidenti wa sukuluyo, Nathan H. Knorr. Pamene anati: “Italy, Mbale ndi Mlongo Malaspina,” tinali paulendo kale m’maganizo mwathu!

Milungu ingapo pambuyo pake, tinakwera sitima ya panyanja ku New York kaamba ka ulendo wa panyanja wamasiku khumi kumka ku Genoa, Italy. Giovanni DeCecca ndi Max Larson, antchito a kumalikulu a Brooklyn, anali padokopo kudzatsazikana nafe. Ku Genoa tinalandiridwa ndi amishonale ena amene anali ozoloŵerana ndi njira zovuta zoloŵera m’dzikolo.

Tili ndi chidwi ndi zinthu zonse zotizinga, tinakwera sitima ya pamtunda kumka ku Bologna. Zimene tinaona pamene tinafika ndizo mzinda umene unali chikhalirebe wowonongedwa ndi mabomba a Nkhondo Yadziko II. Komanso panali zinthu zina zokondweretsa zambiri, monga ngati kununkhira kotenga mtima kwa khofi wowotcha kumene kunamveka ponseponse mmaŵa ndi fungo la zokoleretsa za mu msuzi wabwino kwambiri umene unali kuphikidwa woika m’mitundu yambiri ya pasta.

Kukwaniritsa Chonulirapo

Tinayamba kupita muutumiki tili ndi ulaliki woloŵezedwa pamtima, ndipo tinaupereka mobwerezabwereza kufikira utalandiridwa kapena kukanidwa pamakomo. Chikhumbo cha kunena zakukhosi chinatisonkhezera kuphunzira mwakhama chinenero. Pambuyo pa miyezi inayi, tinatumizidwa kukakhala m’nyumba ina yatsopano ya amishonale ku Naples.

Mzinda waukulu umenewu ngwotchuka ndi malo ake okongola kwambiri. Tinasangalala ndi utumiki wathu kumeneko, komano pambuyo pa miyezi ina inayi, mwamuna wanga anatumizidwa m’ntchito ya dera, kapena yoyendayeda, akumachezera mipingo kuyambira ku Rome kufikira ku Sicily. M’kupita kwa nthaŵi, tinachezeranso Malta ndipo ngakhale Libya ku Northern Africa.

Munthu anayenera kulimba pa maulendo a sitima ya pamtunda kuchokera ku Naples kumka ku Sicily mkati mwa zaka zimenezo. Tinkakwera sitimayo yodzala ndi kuimirira pakati pa mipando podzala anthu, nthaŵi zina kwa maola asanu ndi limodzi kufikira kumaola asanu ndi atatu. Komabe, zimenezi zinatipatsa mpata wabwino wa kudziŵa awo amene anatizinga. Nthaŵi zambiri botolo lalikulu la vinyo wopangidwa panyumba linali mpando wokhalapo mwini wake, amene panthaŵi ndi nthaŵi anali kumwamo vinyo kupha ludzu lake paulendo wautaliwo. Kaŵirikaŵiri mapasinjala aubwenzi ankagaŵana nafe buledi wawo ndi salami, chisonyezero cha ubwenzi ndi chothutsa mtima chimene tinayamikira.

Ku Sicily tinkalandiridwa ndi mabwenzi amene ankatinyamulira masutikesi kukwera nawo pa phiri kwa maola atatu ndi theka mosapuma kumka kumpingo wokhala pamwamba pake. Kutilandira kwa abale athu Achikristu kwachikondi kunatipangitsa kuiŵala za kutopa kwathu. Nthaŵi zina tinkakwera pa nyulu zoyenda mosakhumudwa, koma sitinayang’ane kumapompho kumene tikanagwera ngati nyulu ikanaphonyetsa phazi lake. Kuchirimika kwa abale athu pa choonadi cha Baibulo mosasamala kanthu za mavuto awo kunatilimbikitsa, ndipo chikondi chimene tinasonyezedwa chinatipangitsa kukhala oyamikira kukhala nawo.

Malta ndi Libya

Pokhala odzazidwa ndi zikumbukiro za abale athu ku Sicily, tinayenda ulendo wa pamadzi kumka ku Malta. Kumeneko mtumwi Paulo anapezako anthu okoma mtima, ndipo nafenso tinatero. Mkuntho wochitika pa St. Paul’s Bay unatipangitsa kuzindikira ngozi imene ngalawa zazing’ono zinakumana nayo m’zaka za zana loyamba. (Machitidwe 27:39–28:10) Komabe tinali ndi Libya patsogolo pakepo. Kodi zinthu zikatiyendera motani m’dziko limeneli la mu Afirika kumene ntchito yathu inaletsedwa?

Kachiŵirinso tinakumana ndi anthu a miyambo ina yosiyana kwambiri. Malo ndi chinenero cha mzinda wa Tripoli zinandichititsa chidwi pamene tinali kuyenda m’misewu yokhala ndi zipilala ya dera lina la m’tauni. Amuna anavala zovala zoombedwa ndi ubweya wa ngamila kudzitetezera pa kutentha kwakukulu kwa Sahara Desert masana ndi pa kuzizira kwa usiku. Tinaphunzira kumvetsetsa ndi kulemekeza mmene anthu amasinthira pamikhalidwe ya kumalo kumene amakhala.

Changu chosamala cha abale chinatiphunzitsa zambiri ponena za kudalira pa Yehova kotheratu ndi kutsatira malangizo a awo amene ali ndi chidziŵitso chambiri ponena za kulalikira m’mikhalidwe yotero. Abale athu Achikristu anali a mitundu yosiyanasiyana; komabe anagwira ntchito mogwirizana m’kutumikira kwawo Yehova.

Gawo Latsopano

Chifukwa cha chitsutso pa ntchito yathu yolalikira, tinafunikira kuchoka mu Italy, koma mwachisangalalo tinalandira gawo lathu latsopano lolalikirako ku Brazil mu 1957. Ine ndi Francis tinasinthira ku moyo ndi miyambo yake, ndipo pambuyo pa miyezi isanu ndi itatu, Francis anapemphedwa kuti achite ntchito yoyendera dera. Tinkayenda ndi basi, ndi ndege, ndiponso ndi miyendo. Kuyenda m’dziko lalikulu kwambiri ndi lokongola limeneli kunali monga ngati phunziro la geography.

Dera lathu loyamba linali ndi mipingo khumi mu mzinda wa São Paulo, ndiponso matauni aang’ono khumi okhala mkati mwake ndiponso m’mbali mwa dera la gombe la kummwera la boma la São Paulo. Panthaŵiyo, m’matauni amenewo munalibe mipingo. Tinkapeza malo okhala, ndipo titakhazikika, tinkafikira nyumba iliyonse ndi uthenga wa Ufumu. Tinkasiyanso mapepala oitanira anthu kuti adzaonerere imodzi ya mafilimu ophunzitsa a Watch Tower Society.

Kukwera m’basi ndi mafilimu, projekitala, transformer, mafaelo, mabuku, mapepala oitanira anthu, ndi chidindo chodindira mawu pamapepala osonyeza malo okaonetsera filimu sikunali ntchito yaing’ono. Poyerekezera, sutikesi yathu yaing’ono ya zovala sinali chinthu chachikulu. Projekitalayo inafunikira kuikidwa pamiyendo pathu kotero kuti isamasuke paulendo wa pamisewu yokumbika.

Titapeza malo oonetsera filimuyo, tinkapita kukhomo ndi khomo ndi kusiya mapepala oitana anthu kudzaona filimu. Nthaŵi zina tinkapeza chilolezo chosonyeza filimu mu lesitilanti kapena mu hotela. Panthaŵi zina tinkangolenjeka shitibedi mopingasa pamitengo iŵiri pabwalo. Oonenerera oyamikira, amene ambiri a iwo anali asanaonepo zithunzithunzi zoyenda, ankaimirira ndi kumvetsera mosamalitsa pamene Francis anaŵerenga mawu ake ofotokozera. Pambuyo pake, tinkagaŵira mabuku ofotokoza Baibulo.

Kuti tifike kumidzi, tinkayenda pa basi. Mitsinje ina inalibe milatho, chotero basi inkakwezedwa pachikepe chachikulu ndi kuiyandamitsira kutsidya lina. Tinkalangizidwa kutuluka m’basiyo, ndi kuti ngati tiona kuti basiyo ikutererekera mu mtsinjewo tinayenera kudumphira kumbali ina ya chikepecho kuti tisamire. Mokondweretsa, palibe basi iliyonse imene inagwera mu mtsinje​—umenewo unalidi mwaŵi, makamaka popeza kuti mtsinjewo unali kudziŵika kukhala ndi nsomba za piranha zakudya nyama!

Titaloŵa msonkhano wamitundu yonse mu New York mu 1958, tinabwerera ku Brazil, kumene posapita nthaŵi tinayambanso ntchito yoyendayenda. Chigawo chathu chinali kufika ku malire ndi Uruguay kummwera, Paraguay kumadzulo, boma la Pernambuco kumpoto, ndi Atlantic Ocean kummaŵa kwa Brazil.

Malo a Akhate

Pakati pa ma 1960, tinalandira chiitano cha kukaonetsa imodzi ya mafilimu a Sosaite ku malo a akhate. Kunena zoona ndinali ndi mantha pang’ono. Sitinkadziŵa zambiri ponena za khate, kusiyapo zimene tinaŵerenga m’Baibulo. Titaloŵa m’malowo, amene nyumba zake zinapakidwa utoto woyera, anatiloŵetsa mu holo yaikulu. Pakati pake panali chigawo chokhalapo ife limodzi ndi makina athu chimene chinachingidwa ndi chingwe.

Wokonza magetsi amene anali kutithandiza anali nzika ya pamalopo ya zaka 40. Anali wodyeka manja kufikira mu mfundo mwa manjawo ndiponso mbali zina za thupi lake. Anali wopunduka moipa. Poyamba ndinadodoma, komano mkhalidwe wake wansangala ndi luso lake pogwira ntchito yake zinakhazika mtima wanga pansi. Posapita nthaŵi tinali kukambitsirana za zinthu zambiri pamene tinali kumaliza kukonzekera zofunikirazo. Pakati pa anthu odwala chikwi chimodzi amene anali kukhala pamalo ameneŵa, oposa mazana aŵiri anafikapo. Pamene anali kudza motsimphina, tinaona milingo yambiri yosiyanasiyana ya nthenda imene anali kudwalayo. Chinali chokumana nacho chotichititsa chifundo chotani nanga kwa ife!

Tinalingalira zimene Yesu ananena kwa wakhathe amene anapempha kuti, “Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza.” Pokhudza munthuyo, Yesu ananenetsa kwa iye kuti, “Ndifuna; takonzedwa.” (Mateyu 8:2, 3) Programuyo itatha, ambiri anatifikira kudzatithokoza chifukwa cha kufika, matupi awo owonongeka akumakhaladi umboni wa kuvutika kwakukulu kwa mtundu wa anthu. Pambuyo pake, Mboni zakumaloko zinaphunzira Baibulo ndi awo amene anakhumba kudziŵa zambiri.

Mu 1967 tinabwerera ku United States kukapeza chithandizo cha matenda ena aakulu. Pamene tinali kupitiriza kulimbana ndi matendawo, tinakhalanso ndi mwaŵi wa kutumikira mu ntchito yadera. Kwa zaka 20 zotsatira, ndinagwirizana ndi Francis mu ntchito yoyendayenda mu United States. Mkati mwa nthaŵi imeneyi iye anaphunzitsanso Sukulu Yautumiki Waufumu.

Ha, kunali magwero achilimbikitso otani nanga kwa ine kukhala ndi mwamuna wachikondi ndi bwenzi lokhulupirika amene anasamalira gawo lililonse limene anapatsidwa! Tinali ndi mwaŵi wa kugaŵana pamodzi chuma cha choonadi cha Baibulo pambali zina za pamakontinenti anayi.

Kuchirikizidwa ndi Chumacho

Kalelo mu 1950, Amayi anakwatiwa ndi a David Easter, mbale wokhulupirika amene anabatizidwa mu 1924. Anatumikira limodzi kwa zaka zambiri mu utumiki wanthaŵi yonse. Komabe, mkati mwa mbali yotsiriza ya moyo wa Amayi, nthenda ya Alzheimer inayamba kuonekera. Anafunikira chisamaliro chochuluka pamene nthendayo inafoola kuganiza kwawo. Akulu anga ochirikiza kwambiriwo ndi a David anapitiriza kuchita thayo lolemera la kuwasamalira, popeza kuti iwo sanafune kuti tisiye mwaŵi wathu wapadera wa utumiki wanthaŵi yonse. Chitsanzo chokhulupirika cha Amayi kufikira pa imfa yawo mu 1987 chinatithandiza kwambiri kulinganiza njira ya moyo wathu, ndipo chiyembekezo chimene anali nacho cha mfupo ya kumwamba chinatitonthoza.

Podzafika 1989, ndinazindikira kuti Francis analibe nyonga monga momwe analili poyamba. Sitinazindikire kuti malungo a schistosomiasis, nthenda yodziŵika kwambiri mbali zambiri za dziko, anali kumyambukira mowopsa. Mu 1990, mdani wosalekerera ameneyu anamgonjetsa, ndipo ndinatayikiridwa ndi mnzanga wokondedwa amene ndinachita naye utumiki wa Yehova kwa zaka zoposa 40.

Kusintha kuli mbali ya moyo. Kwina nkosavuta, ndipo kwina nkovuta. Koma Yehova, Mpatsi wa chuma cha choonadi cha Baibulo chosayerekezekacho, anandilimbitsa ndi gulu lake ndi chikondi ndiponso chilimbikitso cha a banja langa. Ndikali kupezabe chikhutiro pamene ndikuyembekezera kukwaniritsidwa kwa malonjezo onse osalephera a Yehova.

[Chithunzi patsamba 23]

Pamene ine ndi mwamuna wanga tinali amishonale ku Italy

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena