Tumikirani Yehova ndi Chimwemwe cha Mtima
“Matemberero awa onse adzakugwerani . . . Popeza simunatumikira Yehova Mulungu wanu ndi chimwemwe ndi mokondwera mtima.”—DEUTERONOMO 28:45-47.
1. Kodi pali umboni wotani wakuti awo otumikira Yehova ali achimwemwe, kulikonse kumene akumtumikirira iye?
ATUMIKI a Yehova ali achimwemwe pochita chifuniro chake, kaya ndi kumwamba kapena padziko lapansi. “Nyenyezi za m’maŵa” zaungelo zinafuula mwachimwemwe pokhazikitsidwa dziko lapansi, ndipo mosakayikira konse miyandamiyanda ya angelo akumwamba ‘amachita mawu a Mulungu’ ndi chimwemwe. (Yobu 38:4-7; Salmo 103:20) Mwana wa Yehova wobadwa yekha anali “mmisiri” wachimwemwe kumwamba ndipo anasangalala pochita chifuniro cha Mulungu monga munthu wotchedwa Yesu Kristu padziko lapansi. Ndiponso, “chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira [mtengo wozunzirapo, NW], nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.”—Miyambo 8:30, 31; Ahebri 10:5-10; 12:2.
2. Kodi nchiyani chimene chinasonyeza kuti kaya Aisrayeli anali ndi madalitso kapena matemberero?
2 Aisrayeli anakhala okondwera pamene anasangalatsa Mulungu. Koma bwanji ngati sakanamvera? Iwo anachenjezedwa kuti: “Matemberero . . . [adzapitiriza pa] inu ndi mbewu zanu ngati chizindikiro ndi chozizwa, nthaŵi zonse. Popeza simunatumikira Yehova Mulungu wanu ndi chimwemwe ndi mokondwera mtima, chifukwa cha kuchuluka zinthu zonse; chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiŵa, ndi kusoŵa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufikira atakuwonongani.” (Deuteronomo 28:45-48) Madalitso ndi matemberero anasonyeza poyera amene anali ndi amene sanali atumiki a Yehova. Matemberero oterowo anatsimikizanso kuti sipangakhale kunyalanyaza malamulo a mkhalidwe ndi zifuno za Mulungu osalandira chilango, kapena sangangonyozedwa pachabe. Chifukwa chakuti Aisrayeli anakana kulabadira machenjezo a Yehova onena za chipasuko ndi kutengeredwa kundende, Yerusalemu anakhala “chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.” (Yeremiya 26:6) Chotero tiyeni timvere Mulungu ndi kupeza chiyanjo chake. Chimwemwe ndicho chimodzi cha madalitso aumulungu ambiri okhala ndi anthu aumulungu.
Mmene Tingatumikirire “Mokondwera Mtima”
3. Kodi mtima wophiphiritsira nchiyani?
3 Aisrayeli anafunikira kutumikira Yehova “ndi chimwemwe ndi mokondwera mtima.” Nawonso atumiki a Mulungu amakono ayenera kutero. Kukondwera ndiko “kusangalala; kudzala ndi chikondwerero.” Ngakhale kuti mtima weniweni ukutchulidwa m’Malembawo, uwo sumalingalira kapena kuganiza m’lingaliro lenileni. (Eksodo 28:30) Ntchito yake yaikulu ndiyo kupopa mwazi umene umachirikiza maselo a thupi. Komabe, m’zochitika zambiri Baibulo limanena za mtima wophiphiritsira, umene kwakukulukulu uli phata la chikondi, chisonkhezero, ndi luntha. Umanenedwa kuti umaimira “mbali yapakati, mkati, motero umaimira munthu wamkati monga momwe amadzisonyezera m’zochita zake zonse zosiyanasiyana, m’zikhumbo zake, zokonda, mmene amamverera, zilakolako, zifuno, malingaliro ake, kaonedwe ka zinthu, kuyerekezera m’maganizo, nzeru yake, chidziŵitso, luso, zikhulupiriro zake ndi maganizo ake, chikumbukiro chake ndi chikumbumtima chake.” (Journal of the Society of Biblical Literature and Exegesis, 1882, tsamba 67) Mtima wathu wophiphiritsira umaphatikizapo malingaliro athu ndi mikhalidwe ya mtima, kuphatikizapo chimwemwe.—Yohane 16:22.
4. Kodi nchiyani chimene chingatithandize kutumikira Yehova Mulungu ndi chikondwerero cha mtima?
4 Kodi nchiyani chimene chingatithandize kutumikira Yehova mokondwera mtima? Kuli kothandiza kukhala ndi lingaliro labwino ndi loyamikira madalitso athu ndi mwaŵi wopatsidwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, tikhoza kulingalira mwachimwemwe ponena za mwaŵi wathu wa kupereka “utumiki wopatulika” kwa Mulungu woona. (Luka 1:74, NW) Palinso mwaŵi wina wofananapo wa kunyamula dzina la Yehova monga Mboni zake. (Yesaya 43:10-12) Pa zimenezi tingawonjezepo chisangalalo cha kudziŵa kuti mwa kutsatira Mawu a Mulungu timamkondweretsa iye. Ndipo muli chimwemwe chotani nanga m’kuŵalitsa kuunika kwauzimu mwa kuthandiza anthu ambiri kutuluka mumdima!—Mateyu 5:14-16; yerekezerani ndi 1 Petro 2:9.
5. Kodi nchiyani chimene chimachititsa chimwemwe chaumulungu?
5 Komabe, kutumikira Yehova ndi chimwemwe cha mtima sikuli nkhani ya kulingalira bwino chabe. Inde, kukhala ndi malingaliro abwino nkopindulitsa. Koma chimwemwe chaumulungu sichinthu chimene timakhala nacho mwa kukulitsa umunthu. Icho ndicho chipatso cha mzimu wa Yehova. (Agalatiya 5:22, 23) Ngati tilibe chimwemwe, tiyenera kupanga masinthidwe kotero kuti tipeŵe kalingaliridwe kapena kachitidwe ka zinthu kosakhala ka Malemba kamene kangachititse chisoni mzimu wa Mulungu. (Aefeso 4:30) Komabe, monga anthu odzipereka kwa Yehova, tisaope kuti kusoŵeka kwa chimwemwe cha mtima wonse panthaŵi ina kuli umboni wa kutsutsidwa ndi Mulungu. Tili opanda ungwiro ndi okhoza kuvutika ndi zoŵaŵitsa, chisoni, ndipo ngakhale chipsinjo nthaŵi zina, koma Yehova amatimvetsetsa. (Salmo 103:10-14) Chifukwa chake tiyeni tipempherere mzimu wake woyera, tikumakumbukira kuti chipatso chake cha chimwemwe chimapatsidwa ndi Mulungu. Atate wathu wakumwamba wachikondi adzayankha mapemphero oterowo ndipo adzatikhozetsa kumtumikira ndi chimwemwe cha mtima.—Luka 11:13.
Pamene Chimwemwe Chikusoŵeka
6. Ngati chimwemwe chikusoŵeka mu utumiki wathu kwa Mulungu, kodi tiyenera kuchitanji?
6 Ngati chimwemwe chikusoŵeka mu utumiki wathu, potsirizira pake tingabwerere m’mbuyo m’kutumikira Yehova kapena ngakhale kukhala osakhulupirika kwa iye. Chifukwa chake, kungakhale kwanzeru kulingalira modzichepetsa ndi mwapemphero zolinga zathu ndi kupanga masinthidwe ofunikira. Kuti tikhale ndi chimwemwe chopatsidwa ndi Mulungu, tiyenera kutumikira Yehova kaamba ka chikondi ndipo ndi mtima wonse, moyo, ndi maganizo. (Mateyu 22:37) Sitiyenera kutumikira ndi mzimu wa mpikisano, chifukwa Paulo analemba kuti: “Ngati tili ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende. Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.” (Agalatiya 5:25, 26) Sitidzakhala ndi chimwemwe chenicheni ngati titumikira ndi cholinga cha kupambana ena kapena kufuna chitamando.
7. Kodi ndimotani mmene tingadzutsirenso chimwemwe chathu cha mtima?
7 Muli chimwemwe m’kukwaniritsa kudzipatulira kwathu kwa Yehova. Pamene tinali odzipatulira achatsopano kwa Mulungu, tinayenda mokangalika pa njira ya moyo Wachikristu. Tinaphunzira Malemba ndi kukhala ndi phande m’misonkhano nthaŵi zonse. (Ahebri 10:24, 25) Kukhala ndi phande mu utumiki kunatipatsa chimwemwe. Komabe, bwanji ngati chimwemwe chathu chazilala? Phunziro la Baibulo, kufika pamisonkhano, kukhala ndi phande mu utumiki—indedi, kudziloŵetsa mokwanira m’mbali iliyonse ya Chikristu—kuyenera kupatsa moyo wathu kukhazikika kwauzimu ndi kudzutsanso chikondi chimene tinali nacho poyamba ndi chimwemwe chathu chakale cha mtima. (Chivumbulutso 2:4) Pamenepo sitidzakhala ngati ena amene ali opanda chimwemwe ndipo kaŵirikaŵiri amakhala ofunikira chithandizo chauzimu. Akulu amakhala okondwera kuthandiza, koma aliyense payekha tiyenera kukwaniritsa kudzipatulira kwathu kwa Mulungu. Palibe wina aliyense amene angatichitire zimenezi. Chotero tiyeni tichipange kukhala cholinga chathu kulondola kachitidwe ka zinthu Kachikristu kotero kuti tikwaniritse kudzipatulira kwathu kwa Yehova ndi kukhala ndi chimwemwe chenicheni.
8. Kodi nchifukwa ninji chikumbumtima choyera chili chofunika kwambiri ngati tikufuna kukhala achimwemwe?
8 Ngati titi tikhale ndi chimwemwe chimene chili chipatso cha mzimu wa Mulungu, tifunikira kukhala ndi chikumbumtima choyera. Pamene mfumu ya Israyeli Davide anayesa kubisa tchimo lake, ndi pamenenso anasautsika kwambiri. Kwenikweni, chinyontho cha moyo wake chinaonekera kukhala chitakamuka, ndipo ayenera kuti anadwaladi. Chinali chitonthozo chotani nanga pamene analapa ndi kuulula tchimo! (Salmo 32:1-5) Sitingakhale achimwemwe ngati tibisa tchimo lalikulu. Zimenezo zingachititse kukhala ndi moyo wosautsikadi. Ndithudi, imeneyo sindiyo njira yokhalira ndi chimwemwe. Koma kuulula machimo ndi kulapa kumadzetsa mpumulo ndi kubwezeretsa mzimu wa chimwemwe.—Miyambo 28:13.
Kuyembekezera ndi Chimwemwe
9, 10. (a) Kodi ndi lonjezo lotani limene Abrahamu analandira, koma kodi ndimotani mmene chikhulupiriro ndi chimwemwe chake zinayesedwera? (b) Kodi ndimotani mmene tingapindulire ndi zitsanzo za Abrahamu, Isake, ndi Yakobo?
9 Kupeza chimwemwe pamene tiphunzira za chifuno cha Mulungu panthaŵi yoyamba ndi nkhani ina, koma kukhalabe wachimwemwe m’kupita kwa zaka ndi nkhani inanso. Zimenezi zingasonyezedwe m’nkhani ya Abrahamu wokhulupirikayo. Pamene anayesa kupereka mwana wake Isake atalamulidwa ndi Mulungu, mngelo anapereka uthenga uwu: “Pa ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikaniza mwana wako, mwana wako wa yekha, kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbewu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja; ndipo mbewu zako zidzagonjetsa chipata cha adani awo; m’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mawu anga.” (Genesis 22:15-18) Mosakayikira, Abrahamu anasefukira ndi chimwemwe kaamba ka lonjezo limeneli.
10 Abrahamu angakhale atayembekezera kuti Isake akakhala “mbewu” mwa imene madalitso olonjezedwawo akadzera. Koma kupita kwa zaka popanda kuchitika chilichonse chozizwitsa kudzera mwa Isake kungakhale kutaika pachiyeso chikhulupiriro ndi chimwemwe cha Abrahamu ndi banja lake. Chitsimikiziro cha Mulungu cha lonjezolo kwa Isake ndipo pambuyo pake kwa mwana wake Yakobo chinawatsimikiziritsa iwo kuti kufika kwa Mbewuyo kunali kudakali mtsogolo, ndipo chimenechi chinawathandiza kusunga chikhulupiriro ndi chimwemwe chawo. Komabe, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo anamwalira popanda kuona kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu kwa iwo, koma iwo sanali atumiki a Yehova opanda chimwemwe. (Ahebri 11:13) Nafenso tingapitirize kutumikira Yehova ndi chikhulupiriro ndi chimwemwe pamene tikuyembekezera kukwaniritsidwa kwa malonjezo ake.
Chimwemwe Mosasamala Kanthu za Chizunzo
11. Kodi nchifukwa ninji tingakhalebe achimwemwe mosasamala kanthu za chizunzo?
11 Monga atumiki a Yehova, tikhoza kutumikira Yehova ndi chimwemwe cha mtima, ngakhale pamene tikuvutika ndi chizunzo. Yesu analengeza kukhala achimwemwe awo amene amazunzidwa chifukwa cha iye, ndipo mtumwi Petro anati: “Popeza mulaŵana ndi Kristu zoŵaŵa zake, kondwerani; kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu. Mukatonzedwa pa dzina la Kristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.” (1 Petro 4:13, 14; Mateyu 5:11, 12) Ngati kuti mukupirira chizunzo ndi kuvutika chifukwa cha chilungamo, muli ndi mzimu wa Yehova ndi chiyanjo chake, ndipo zimenezo zimapatsadi chimwemwe.
12. (a) Kodi nchifukwa ninji tingayang’anizane ndi ziyeso za chikhulupiriro ndi kukhalabe achimwemwe? (b) Kodi ndi phunziro lalikulu liti limene tingaphunzire m’chochitika cha Mlevi yemwe anali ku dziko landende?
12 Tingayang’anizane ndi ziyeso za chikhulupiriro ndi chimwemwe chifukwa chakuti Mulungu ndiye Pothaŵira pathu. Masalmo 42 ndi 43 amapereka umboni wa zimenezi. Pa chifukwa chinachake, Mlevi wina anali ku dziko landende. Iye analakalaka kwambiri kulambira pakachisi wa Mulungu kotero kuti anamva monga ngati nswala kapena mbaŵala yaikazi yofa ludzu, imene ikupuma ŵefuŵefu kukhumba madzi m’chipululu chouma. Iye ‘anali ndi ludzu,’ kapena kulakalaka Yehova ndi mwaŵi wa kulambira Mulungu pa kachisi Wake. (Salmo 42:1, 2) Chokumana nacho cha wandendeyo chiyenera kutisonkhezera kusonyeza chiyamikiro cha mayanjano omwe timasangalala nawo ndi anthu a Yehova. Ngati mkhalidwe wotero wonga kubindikiritsidwa chifukwa cha chizunzo utiletsa kwakanthaŵi kukhala nawo pamodzi, tiyenera kulingalira za nthaŵi zimene tinali kukondwera nawo pamodzi mu utumiki wopatulika ndi kupempherera chipiriro pamene ‘tikuyembekeza Mulungu’ kuti atibwezeretse ku ntchito zanthaŵi zonse pamodzi ndi alambiri ake.—Salmo 42:4, 5, 11; 43:3-5.
“Tumikirani Yehova ndi Chikondwerero”
13. Kodi ndimotani mmene Salmo 100:1, 2 limasonyezera kuti chikondwerero chiyenera kukhala mbali ya utumiki wathu kwa Mulungu?
13 Chikondwerero chiyenera kukhala mbali ya utumiki wathu kwa Mulungu. Zimenezi zinasonyezedwa m’nyimbo ya chiyamikiro m’mene wamasalmo anaimba kuti: “Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera.” (Salmo 100:1, 2) Yehova ali “Mulungu wachimwemwe” ndipo amafuna atumiki ake kupeza chikondwerero posonyeza kudzipatulira kwawo kwa iye. (1 Timoteo 1:11, NW) Anthu a mitundu yonse ayenera kusangalala mwa Yehova, ndipo mawu athu achitamando ayenera kukhala amphamvu, mofanana ndi ‘kufuula’ kwachipambano kwa gulu lankhondo lolakika. Popeza kuti kutumikira Mulungu kumatsitsimula, kuyenera kuyendera pamodzi ndi kukondwera. Chifukwa chake, wamasalmo anasonkhezera anthu kudza pamaso pa Mulungu ndi “kumuimbira mokondwera.”
14, 15. Kodi ndimotani mmene Salmo 100:3-5 limagwirira ntchito kwa anthu a Yehova achimwemwe lerolino?
14 Wamasalmoyo anawonjezera kuti: “Dziŵani [zindikirani] kuti Yehova ndiye Mulungu; iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa za pabusa pake.” (Salmo 100:3) Popeza kuti Yehova ndiye Mlengi wathu, ife tili ake monga momwe nkhosa zimakhalira za mbusa. Mulungu amatisamalira bwino kwambiri kwakuti timamtamanda moyamikira. (Salmo 23) Ponena za Yehova, wamasalmo anaimbanso kuti: “Loŵani ku zipata zake ndi chiyamiko, ndi ku mabwalo ake ndi chilemekezo: myamikeni; lilemekezeni dzina lake. Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimamka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.”—Salmo 100:4, 5.
15 Lerolino, anthu achimwemwe a mitundu yonse akuloŵa m’mabwalo a kachisi wa Yehova kuti apereke chiyamikiro ndi chitamando. Mwachimwemwe timadalitsa dzina la Mulungu mwa kulankhula zothokoza Yehova nthaŵi zonse, ndipo mikhalidwe yake yabwino kwambiri imatisonkhezera kumtamanda. Iye ali wabwino m’zonse, ndipo kukoma mtima kwake kapena chifundo chake kwa atumiki ake nchodalirika nthaŵi zonse, pakuti chimapitirizabe ku nthaŵi zomka muyaya. Ku “mibadwomibadwo,” Yehova ali wokhulupirika posonyeza chikondi kwa awo ochita chifuniro chake. (Aroma 8:38, 39) Motero, ife tilidi ndi chifukwa chabwino cha ‘kutumikira Yehova ndi chikondwerero.’
Kondwerani m’Chiyembekezo Chanu
16. Kodi Akristu angakondwere m’ziyembekezo zotani?
16 Paulo analemba kuti: “Kondwerani m’chiyembekezo.” (Aroma 12:12) Otsatira a Yesu Kristu odzozedwa amakondwera m’chiyembekezo chaulemerero cha moyo wosafa wakumwamba umene Mulungu anawatsegulira mwaŵi kupyolera mwa Mwana wake. (Aroma 8:16, 17; Afilipi 3:20, 21) Akristu okhala ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya m’Paradaiso padziko lapansi alinso ndi chifukwa chokondwerera. (Luka 23:43) Atumiki a Yehova onse okhulupirika ali ndi chifukwa chokondwerera m’chiyembekezo cha Ufumu, popeza kuti adzakhala mbali ya boma lakumwamba limenelo kapena adzakhala mu ulamuliro wake wapadziko lapansi. Ha, ndi dalitso lokondweretsa chotani nanga!—Mateyu 6:9, 10; Aroma 8:18-21.
17, 18. (a) Kodi nchiyani chimene chinanenedweratu pa Yesaya 25:6-8? (b) Kodi ndimotani mene ulosi wa Yesaya umenewu ukukwaniritsidwira tsopano, ndi mtsogolonso?
17 Yesaya nayenso ananeneratu za mtsogolo mokondweretsa kwa mtundu wa anthu womvera. Iye analemba kuti: “M’phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino. Ndipo iye adzawononga m’phiri limeneli chophimba nkhope chovundikira mitundu yonse ya anthu, ndi nsalu yokuta amitundu onse. Iye wameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa pa dziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena.”—Yesaya 25:6-8.
18 Madyerero auzimu amene tili nawo lerolino monga alambiri a Yehova ali phwando lokondweretsadi. Kwenikweni, chikondwerero chathu chimasefukira pamene tikutumikira Mulungu mwachangu tikumayembekezera phwando la zinthu zabwino zenizeni limene iye walonjeza m’dziko latsopano. (2 Petro 3:13) Pa maziko a nsembe ya Yesu, Yehova adzachotsa “nsalu” yokuta mtundu wa anthu chifukwa cha tchimo la Adamu. Kudzakhala kokondweretsa chotani nanga kuona kuti uchimo ndi imfa zachotsedwa! Chidzakhala chisangalalo chotani nanga kulandira okondedwa athu oukitsidwa, kuona kuti misozi yachoka, ndi kukhala padziko lapansi laparadaiso, pamene anthu a Yehova sadzatonzedwa koma adzakhala atapatsa Mulungu yankho kwa Wotonza wamkuluyo, Satana Mdyerekezi!—Miyambo 27:11.
19. Kodi ndimotani mmene tiyenera kuchitira ponena za ziyembekezo za Yehova zimene watiikira monga Mboni zake?
19 Kodi simukusefukira ndi chimwemwe ndi chiyamikiro podziŵa zimene Yehova adzachitira atumiki ake? Ndithudi, chiyembekezo chaulemerero choterocho chimawonjezera chimwemwe chathu! Ndiponso, chiyembekezo chathu chodalitsika chimatichititsa kuyembekezera pa Mulungu wathu wachimwemwe, wachikondi ndi wooloŵa manja tikumanena mawu onga aŵa: “Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira iye, tidzakondwa ndi kusekerera m’chipulumutso chake.” (Yesaya 25:9) Posumika maganizo pa chiyembekezo chathu chaulemerero, tiyeni tiyeseyese m’njira iliyonse kutumikira Yehova ndi chimwemwe cha mtima.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimotani mmene tingatumikirire Yehova “mokondwera mtima”?
◻ Kodi tingachitenji ngati chimwemwe chikusoŵeka mu utumiki wathu kwa Mulungu?
◻ Kodi nchifukwa ninji anthu a Yehova angakhalebe achimwemwe mosasamala kanthu za chizunzo?
◻ Kodi ndi zifukwa ziti zimene tili nazo zokondwerera m’chiyembekezo chathu?
[Zithunzi patsamba 17]
Kukhala ndi phande m’mbali zonse za moyo Wachikristu kudzawonjezera chimwemwe chathu