Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 2/15 tsamba 13-17
  • Kupulumutsidwa Amoyo Kupyola Chisautso Chachikulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupulumutsidwa Amoyo Kupyola Chisautso Chachikulu
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Monga Masiku a Nowa
  • Chitsanzo cha m’Zaka za Zana Loyamba
  • Khamu Lalikulu la Opulumuka
  • Kukhala Odikira
  • Ena “Sadzamwalira Nthaŵi Yonse”
  • Chiyembekezo Chotsimikizirika
  • Kodi Mudzapulumuka Pamene Mulungu Achitapo Kanthu?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kodi Mumatsutsa Dziko mwa Chikhulupiriro Chanu?
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Tifunika Kukhala Maso Kwambiri Tsopano
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Madzi Anawononga Dziko—Kodi Zidzachitikanso?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 2/15 tsamba 13-17

Kupulumutsidwa Amoyo Kupyola Chisautso Chachikulu

“Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.”​—CHIVUMBULUTSO 7:14.

1. Kodi ndayani amene adzalandira oukitsidwa m’kuuka kwa pa dziko lapansi?

PAMENE anthu miyandamiyanda adzaukitsidwa mu “kuuka kwa olungama ndi osalungama,” sadzabwezeretsedwa ku moyo pa dziko lapansi lapululu. (Machitidwe 24:15) Adzaukira m’malo okongola okonzeka bwino kwambiri ndipo adzapeza malo okhala, zovala, ndi chakudya cha mwana alirenji zitakonzedwa kale kaamba ka iwo. Kodi ndani amene adzakonza zonsezi? Mwachionekere, mudzakhala anthu m’dziko latsopano chisanayambe chiukiriro cha pa dziko lapansi. Anthu ati? Baibulo limasonyeza kuti adzakhala opulumuka chisautso chachikulu chilinkudzacho. Mosakayikira, chimenechi ndi chiphunzitso chochititsa chidwi koposa pa ziphunzitso zonse za Baibulo​—chakuti okhulupirira ena adzapulumuka amoyo kupyola chisautso chachikulu ndipo sadzafa konse. Malemba Oyera amachitira umboni chiyembekezo chimenechi.

Monga Masiku a Nowa

2, 3. (a) Kodi pali kufanana kotani pakati pa masiku a Nowa ndi m’nthaŵi yathu? (b) Kodi kupulumuka Chigumula kwa Nowa ndi banja lake kumasonyeza chiyani?

2 Pa Mateyu 24:37-39, Yesu Kristu anayerekezera masiku a Nowa ndi masiku otsiriza, amene tikukhalamo ndi moyo tsopano. Iye anati: “Monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu. Pakuti monga m’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analoŵa m’chingalawa, ndipo iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.”

3 Chigumula cha padziko lonse chinapululutsa onse amene sanatchere khutu ku uthenga wochenjeza wa Mulungu. Komabe, sichinapululutse Nowa ndi banja lake. Iwo “analoŵa m’chingalawa,” monga momwe Yesu ananenera. Chifukwa cha kupembedza kwawo, Yehova anawapatsa populumukira. Petro Wachiŵiri 2:5, 9 amatchula za kupulumuka kwa Nowa ndi banja lake pamene amati: “[Mulungu] . . . anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi aŵiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula. Ambuye adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo.” Yesu anayerekezera masiku a Nowa ndi masiku otsiriza kusonyeza kuti anthu ambiri sadzalabadira uthenga wochenjeza wa Mulungu. Komabe, mwakutero iye anatsimikiziranso kuti Nowa ndi banja lake anamvera Yehova Mulungu, analoŵa m’chingalawa, napulumuka Chigumula chachikulucho. Kupulumuka kwa Nowa ndi banja lake kumasonyeza kupulumuka kwa atumiki okhulupirika a Mulungu pa mapeto a dzikoli.

Chitsanzo cha m’Zaka za Zana Loyamba

4. M’kukwaniritsidwa kwa mawu a Yesu, kodi ndi zochitika ziti zimene zinatsogolera ku chiwonongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E.?

4 Yesu analankhulanso za zochitika zimene zidzachitika pa mapeto a dziko ili. Pa Mateyu 24:21, 22, timaŵerenga kuti: “Pomwepo padzakhala masauko aakulu [“chisautso chachikulu,” NW], monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso. Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.” Mawu ameneŵa anali ndi kukwaniritsidwa koyamba m’zaka za zana loyamba la Nyengo Yathu. Mu 66 C.E., mzinda wa Yerusalemu unalaliridwa ndi magulu a nkhondo a Roma otsogozedwa ndi Cestius Gallus. Asirikali a Roma anafikira pa kugwetsa linga la kachisi, ndipo Ayuda ambiri anali okonzekera kugonja. Komabe, mosayembekezera ndipo popanda chifukwa chenicheni, Cestius Gallus anabweza asirikali ake. Poona Aromawo akubwerera, Akristu analabadira mawu a Yesu, amene analankhula zaka zambiri zapitazo kuti: “Pamene pali ponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri, ndi iwo ali mkati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumiraga asaloŵemo.” (Luka 21:20, 21) Ayuda amene anali Akristu, osankhidwa, pomwepo anasiya mzinda wa Yerusalemu umenewo woyembekezera kuwonongedwa ndipo motero anapulumuka chiwonongeko chowopsa chimene chinadza pa uwo mwamsanga. Mu 70 C.E., magulu a nkhondo a Roma otsogozedwa ndi Kazembe Titus anabweranso. Iwo anamanga misasa mozinga Yerusalemu, kulalira mzindawo, ndi kuuwononga.

5. Kodi chisautso pa Yerusalemu chinafupikitsidwa m’lingaliro lotani mu 70 C.E.?

5 Wolemba mbiri Wachiyuda Josephus akusimba kuti Ayuda 1,100,000 anafa, pamene kuli kwakuti 97,000 anapulumuka ndipo anatengeredwa ku ukapolo. Opulumuka Achiyuda osakhala Akristu amenewo sanali konse “osankhidwa” a ulosi wa Yesu. Polankhula ku mtundu Wachiyuda wopanduka, Yesu anati: “Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja. Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandionanso ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena, Wolemekezedwa iye amene akudza m’dzina la Ambuye.” (Mateyu 23:38, 39) Palibe umboni wakuti Ayudawo amene anatsekerezedwa m’Yerusalemu analandira Yesu monga Mesiya panthaŵi yovuta yomalizirayo, nakhala Akristu, ndi kupeza chiyanjo cha Yehova. Komabe, chisautso chimene chinadzera Yerusalemu mu 70 C.E. chinafupikitsidwa. Kulalira komaliza kochitidwa ndi magulu a nkhondo a Roma sikunatenge nthaŵi yaitali. Zimenezi zinalola Ayuda ena kupulumuka, mwa kutengeredwa ku mbali zosiyanasiyana za Ufumu wa Roma monga akapolo.

Khamu Lalikulu la Opulumuka

6, 7. (a) Kodi ndi mzinda uti waukulu wachipembedzo umene udzawonongedwa, monga mbali ya chisautso chiti chosalingana ndi china chilichonse? (b) Kodi Yohane analosera chiyani ponena za chisautso chachikulu chilinkudza pa dziko ili?

6 Pamene kuli kwakuti chiwonongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E. chinadzetsadi “chisautso chachikulu” pa mzinda wachipembedzo umenewo, kukwaniritsidwa kwakukulu kwa mawu a Yesu kudzachitikabe mtsogolo. Mzinda wokulirapo wachipembedzo, Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, udzayang’anizana ndi chisautso chachikulu chakupha chimene chidzatsatiridwa mwamsanga ndi chisautso chosalingana ndi china chilichonse pa dongosolo lonse la zinthu la Satana. (Mateyu 24:29, 30; Chivumbulutso 18:21) Pafupifupi zaka 26 pambuyo pa chiwonongeko cha Yerusalemu, mtumwi Yohane analemba za chisautso chachikulu chokuta dziko lonse chimenechi pa Chivumbulutso 7:9-14. Anasonyeza kuti “khamu lalikulu” la anthu likapulumuka.

7 Opulumuka ameneŵa, otchedwa “khamu lalikulu,” amadziŵika mwa njira yotsimikizirika imene amaitenga. Malinga ndi kunena kwa Chivumbulutso 7:14, mmodzi wa akulu 24 kumwamba anauza Yohane kuti: “Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.” Inde, khamu lalikulu limatamanda Yehova monga magwero a chipulumutso chawo. Limasonyeza chikhulupiriro m’mwazi wokhetsedwa wa Yesu ndipo lili ndi kaimidwe kolungama pamaso pa Mlengi wawo ndi Mfumu yake yoikidwa, Yesu Kristu.

8. Kodi ndi unansi wabwino wotani umene ulipo pakati pa “khamu lalikulu” ndi otsalira a abale odzozedwa a Yesu?

8 Lerolino, pafupifupi ziŵalo mamiliyoni asanu za khamu lalikululo zili pansi pa utsogoleri wokangalika wa Mfumu yakumwamba Yesu Kristu. Zimagonjera kwa Kristu ndipo zikugwirizana kwambiri ndi abale ake odzozedwa amene akali pa dziko lapansi. Ponena za chisamaliro chimene khamu lalikulu limapereka kwa odzozedwa ameneŵa, Yesu anati: “Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang’onong’ono aŵa, munandichitira ichi ine.” (Mateyu 25:40) A khamu lalikuluwo akuweruzidwa kukhala atachitira Yesu mwiniyo chokoma chifukwa chakuti akupereka thandizo mopanda dyera kwa abale odzozedwa a Kristu. Zimenezi zimawachititsa kuloŵa muunansi wosungika ndi Yesu Kristu ndi Yehova Mulungu. Iwo apatsidwa mwaŵi wa kugwirizana ndi otsalira odzozedwa kukhala Mboni za Mulungu ndi onyamula dzina lake.​—Yesaya 43:10, 11; Yoweli 2:31, 32.

Kukhala Odikira

9, 10. (a) Kodi tiyenera kuchitanji kuti tisunge kaimidwe kolungama pamaso pa Mwana wa munthu? (b) Kodi tiyenera kuchita motani kuti ‘tikhale odikira’?

9 A khamu lalikulu ayenera kusunga kaimidwe kawo kolungama pamaso pa Mwana wa munthu mosalekeza, kumene kumafuna kuti iwo akhalebe maso kufikiradi mapeto. Yesu ananena bwino lomwe zimenezi pamene anati: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi. Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.”​—Luka 21:34-36.

10 Kuti tikhoze kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu, tiyenera kukhala ndi chiyanjo chake, chimene sitingakhale nacho ngati tilola kalingaliridwe ka dzikoli kutiyambukira. Kalingaliridwe ka dziko nkokopa ndipo kangasonkhezere munthu kuloŵerera mosadziletsa m’zokondweretsa zathupi kapena kulemetsedwa kwambiri ndi mavuto a moyo kwakuti saikanso zinthu za Ufumu poyamba. (Mateyu 6:33) Njira yotero ingafooketse munthu mwauzimu ndi kumchititsa kukhala wamphwayi ponena za mathayo ake kulinga kwa Mulungu ndi ena. Angakhale wofooka kapena angaike malo amene ali nawo mumpingo pachiswe chifukwa cha kuchita tchimo lalikulu, mwina mwake ngakhale kusonyeza mkhalidwe wa kusalapa. Munthu aliyense wa m’khamu lalikulu ayenera kudzipenyerera. Ayenera kupitiriza kukhala wolekana ndi dziko losapembedzali ndi machitachita ake.​—Yohane 17:16.

11. Kodi ndi kugwiritsira ntchito malangizo a Malemba ati kumene kungatithandize kupulumuka Armagedo?

11 Kuti tichite zimenezo, Yehova wapereka zimene tifunikira mwa Mawu ake, mzimu wake woyera, ndi gulu lake looneka. Tiyenera kugwiritsira ntchito zimenezi mokwanira. Ndiponso, tiyenera kumapemphera kwa Mulungu ndi kumumvera ngati titi tikhale ndi chiyanjo chake. Makamaka, tiyenera kukulitsa udani wamphamvu pa choipa. Wamasalmoyo anati: “Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nawo anthu othyasika. Ndidana nawo msonkhano wa ochimwa, ndipo sindidzakhala nawo pansi ochita zoipa. Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa, kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi.” (Salmo 26:4, 5, 9) Mumpingo Wachikristu, achichepere ndi achikulire omwe afunikira kupeŵa kuyanjana kwambiri ndi awo amene sali odzipatulira kwa Yehova. Kuti tilandire chiyanjo cha Mulungu, tiyenera kuyesetsa kukhala opanda chilema ndi osachitidwa mawanga ndi dziko. (Salmo 26:1-5; Yakobo 1:27; 4:4) Motero, tidzakhala ndi chitsimikizo chakuti pa Armagedo, Yehova sadzatipululutsa mu imfa limodzi ndi osapembedza.

Ena “Sadzamwalira Nthaŵi Yonse”

12, 13. (a) Asanaukitse Lazaro, kodi Yesu ananena mawu otani amene Marita sanamvetsetse? (b) Kodi nchiyani chimene mawu a Yesu sanatanthauze ponena za ena amene “sadzamwalira nthaŵi yonse”?

12 Nkosangalatsa kulingalira za kupulumuka mapeto a dongosolo ili la zinthu ndi kuthekera kwa kusamwalira nthaŵi yonse. Chimenechi ndicho chiyembekezo chimene Yesu anatipatsa. Kutatsala pang’ono kuti autse Lazaro bwenzi lake lakufa, Yesu anauza mlongo wa Lazaro Marita kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira ine, sadzamwalira nthaŵi yonse. Kodi ukhulupirira ichi?” Marita anakhulupirira chiukiriro, koma sanamvetsetse zonse zimene Yesu anali kunena.​—Yohane 11:25, 26.

13 Yesu sanatanthauze kuti atumwi ake okhulupirika akapitirizabe kukhala ndi moyo m’thupi ndi kuti sakamwalira nthaŵi yonse. M’malo mwake, iye pambuyo pake anasonyeza kuti ophunzira ake akamwalira. (Yohane 21:16-23) Ndithudi, kudzozedwa kwawo ndi mzimu woyera pa Pentekoste wa 33 C.E. kunatanthauza kuti iwo akamwalira kuti akalandire choloŵa chawo chakumwamba monga mafumu ndi ansembe. (Chivumbulutso 20:4, 6) Chotero, ndi kupita kwa nthaŵi, Akristu onse a m’zaka za zana loyamba anamwalira. Komabe, Yesu ananena motero ali ndi chifuno. Mawu ake onena za kukhala ndi moyo popanda kumwalira adzakwaniritsidwa.

14, 15. (a) Kodi mawu a Yesu onena za ena amene “sadzamwalira nthaŵi yonse” adzakwaniritsidwa motani? (b) Kodi mkhalidwe wa dzikoli uli wotani, koma kodi olungama ali ndi chiyembekezo chotani?

14 Ndipotu, Akristu odzozedwa okhulupirika sadzalaŵa imfa yosatha. (Chivumbulutso 20:6) Ndiponso, mawu a Yesu amalankhula za nthaŵi ina yapadera pamene Mulungu adzaloŵerera m’zochita za anthu ndi kuchotsa kuipa konse pa dziko lapansi, monga momwedi anachitira m’tsiku la Nowa. Anthu okhulupirika amene adzapezeka akuchita chifuniro cha Mulungu panthaŵiyo sadzaphedwa ndi ziweruzo za Mulungu. M’malo mwake, monga Nowa ndi banja lake, adzakhala ndi mpata wa kupulumuka chiwonongeko cha dzikoli. Chiyembekezo chotero ncholimba, popeza nchozikidwa pa ziphunzitso za Baibulo ndipo chimasonyezedwa mwa zitsanzo. (Yerekezerani ndi Ahebri 6:19; 2 Petro 2:4-9.) Kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo kumasonyeza kuti posachedwapa dziko limene lilipoli lopangidwa ndi chitaganya cha anthu osalungama lidzathera m’chiwonongeko. Mkhalidwe umene ulipo sukhoza kusinthidwa, pakuti kuipa kwa dziko kuli kosakonzeka. Zimene Mulungu ananena ponena za dziko la m’tsiku la Nowa zikuchitikanso m’dziko lerolino. Mitima ya anthu ochuluka yadzala ndi kuipa kokhakokha, ndipo ndingaliro zawo nzoipa nthaŵi zonse.​—Genesis 6:5.

15 Yehova walola anthu kulamulira dziko lapansi kwa zaka mazana ambiri popanda kuloŵerera kwaumulungu, koma nthaŵi yawo yangotsala pang’ono kutha. Posachedwa Yehova adzasakaza oipa onse pa dziko lapansi, monga momwedi Baibulo limanenera. (Salmo 145:20; Miyambo 2:21, 22) Komabe, adzawononga oipa osatinso ndi olungama omwe. Mulungu sanachitepo zoterozo! (Yerekezerani ndi Genesis 18:22, 23, 26.) Kodi angawonongerenji awo amene akuyesayesa kumtumikira mokhulupirika, ndi mantha aumulungu? Kulidi koyenera kuti olambira okhulupirika a Yehova amene adzakhala ndi moyo pamene chisautso chachikulu chiyamba adzapeza chiyanjo chake ndipo sadzawonongedwa, monga momwedi Nowa ndi banja lake sanawonongedwe pamene dziko loipa la m’tsiku lake linafika pamapeto ake opululutsa. (Genesis 7:23) Adzatetezeredwa ndi Mulungu ndipo adzapulumuka mapeto a dzikoli.

16. Kodi ndi zinthu ziti zabwino kwambiri zimene zidzachitika m’dziko latsopano, zikumatanthauzanji kwa opulumuka?

16 Kodi chidzatsatira nchiyani? M’dziko latsopano, madalitso ochiritsa adzadza pa mtundu wa anthu pamene mapindu a nsembe ya dipo ya Yesu adzagwiritsiridwa ntchito kotheratu. Baibulo limanena za “mtsinje [wophiphiritsira] wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa. Pakati pa khwalala lake, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziŵiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nawo amitundu.” (Chivumbulutso 22:1, 2) Nkokondweretsa kunena kuti “kuchiritsa” kumeneko kumaphatikizapo kugonjetsedwa kwa imfa ya Adamu yeniyeniyo! “Iye wameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.” (Yesaya 25:8) Chotero, awo opulumuka chisautso chachikulu kuloŵa m’dziko latsopano sadzayang’anizana ndi imfa!

Chiyembekezo Chotsimikizirika

17. Kodi chiyembekezo chakuti ena adzapulumuka Armagedo ndi ‘kusamwalira nthaŵi yonse’ chili chotsimikizirika motani?

17 Kodi tingakhale ndi chidaliro cholimba m’chiyembekezo chodabwitsa chimenechi? Ntheradi! Yesu anauza Marita kuti pakakhala nthaŵi pamene anthu akakhala ndi moyo popanda kumwalira nthaŵi yonse. (Yohane 11:26) Ndiponso, m’chaputala 7 cha Chivumbulutso chimene Yesu anapereka kwa Yohane, munavumbulidwa kuti khamu lalikulu likatuluka m’chisautso chachikulu, kupulumukamo. Kodi tingakhulupirire Yesu Kristu ndi nkhani ya m’mbiri yonena za Chigumula cha m’tsiku la Nowa? Ndithudi tingatero! Ndiponso, Baibulo lili ndi nkhani za zochitika zina pamene Mulungu anasunga atumiki ake ali amoyo kupyola nyengo za chiweruzo ndi kuwonongedwa kwa mitundu. Kodi iye angayembekezeredwe kuchita zochepa m’nthaŵi ino ya mapeto? Kodi pali zosatheka kwa Mlengi?​—Yerekezerani ndi Mateyu 19:26.

18. Kodi tingapeze motani moyo m’dziko latsopano lolungama la Yehova?

18 Mwa kutumikira Yehova mokhulupirika tsopano lino, tidzapezadi moyo wosatha m’dziko lake latsopano. Kwa anthu mamiliyoni osaŵerengeka, moyo m’dziko latsopano limenelo udzadza mwa chiukiriro. Komabe, m’tsiku lathu, anthu a Yehova ambirimbiri​—inde, khamu lalikulu limene palibe munthu akhoza kuliŵerenga​—adzakhala ndi mwaŵi wapadera wa kupulumutsidwa ali amoyo kupyola chisautso chachikulu. Ndipo sadzafa nthaŵi yonse.

Fotokozani Chonde

◻ Kodi kupulumuka Armagedo kunasonyezedwa motani m’tsiku la Nowa?

◻ Kodi tiyenera kuchitanji kuti tikaime pamene Yesu adza kudzapereka ziweruzo za Yehova?

◻ Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti opulumuka Armagedo “sadzamwalira nthaŵi yonse”?

[Chithunzi patsamba 15]

Akristu anapulumuka chisautso cha Yerusalemu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena