Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 3/1 tsamba 3-5
  • Zozizwitsa za Yesu ndi Mbiri Yeniyeni Kapena ndi Nthano Chabe?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zozizwitsa za Yesu ndi Mbiri Yeniyeni Kapena ndi Nthano Chabe?
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zosatheka?
  • Umboni wa Kuona Kwake
  • Umboni Wadziko
  • Kodi pa Zozizwitsa za Yesu Mungaphunzirepo Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Zozizwitsa Zimachitikadi Kapena Ayi?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Umboni Woti Zozizwitsa Zotchulidwa M’Baibulo Zinachitikadi
    Nsanja ya Olonda—2012
  • N’chifukwa Chiyani Nkhani Yokhudza Zozizwitsa Ili Yofunika Kuidziwa Bwino?
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 3/1 tsamba 3-5

Zozizwitsa za Yesu ndi Mbiri Yeniyeni Kapena ndi Nthano Chabe?

“Pa ulonda wachinayi wa usiku, iye anadza kwa iwo, nayenda pamwamba pa nyanja.”​—Mateyu 14:25.

KWA mamiliyoni ambiri kuzungulira dziko lonse, chikhulupiriro chakuti Yesu Kristu anachita zozizwitsa nchofunika kwambiri monga mmene kulili kukhulupirira Mulungu mwiniyo. Olemba Uthenga Wabwino​—Mateyu, Marko, Luka, ndi Yohane​—amafotokoza zozizwitsa za Yesu zokwanira pafupifupi 35. Komabe, nkhani zawo zimasonyeza kuti iye anachita zozizwitsa zina zambiri.​—Mateyu 9:35; Luka 9:11.

Zozizwitsa zimenezi sizinachitidwe kuti zingosangalatsa anthu. Zinali umboni wofunika wa kunena kwa Yesu kuti anali Mwana wa Mulungu, Mesiya woyembekezeredwa kwanthaŵi yaitaliyo. (Yohane 14:11) Mose anachita zizindikiro zozizwitsa pamene anapita kumtundu wa Israyeli wokhala muukapolo. (Eksodo 4:1-9) Ndithudi, Mesiya, uyo amene analoseredwa kuti adzapambana Mose, akanayembekezeredwanso kuchita zizindikiro zina zochirikizidwa ndi Mulungu. (Deuteronomo 18:15) Motero Baibulo limatcha Yesu kuti “mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa [Ayuda] ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro.”​—Machitidwe 2:22.

M’nthaŵi yapitayo, anthu ambiri anavomereza mosakayikira mmene Baibulo limasonyezera Yesu monga wochita zozizwitsa. Koma m’zaka makumi zaposachedwapa, nkhani za Uthenga Wabwinozo zatsutsidwa ndi ozipenda. M’buku lake lakuti Deceptions and Myths of the Bible, Lloyd Graham amatchula za nkhani ya Baibulo yonena za kuyenda kwa Yesu pamadzi ndipo amanenanso kuti: “Kukhulupirira zimenezi ndiko umbuli waukulu, komabe, kwenikweni, mamiliyoni ambiri amatero. Ndiyeno timadabwa chimene chalakwika ndi dziko lathuli. Kodi ndi umbuli umenewu mungayembekezere kukhala ndi dziko labwino?”

Zosatheka?

Komabe, kutsutsa kumeneko sikwanzeru. The World Book Encyclopedia imatanthauzira chozizwitsa kukhala “chochitika chimene sichingafotokozedwe ndi malamulo odziŵika a chilengedwe.” Malinga ndi tanthauzo limenelo, TV yosonyeza maonekedwe achinthu, telefoni ya cellular, kapena kompyuta ya laptop zikanalingaliridwa kukhala zozizwitsa m’zaka zana zokha zapitazo! Kodi nkwanzeru kukhala woumirira ndi kunena kuti kanthu kena nkosatheka kokha chifukwa chakuti sitingathe kukafotokoza malinga ndi chidziŵitso chamakono cha sayansi?

Nayi mbali ina yofuna kulingaliridwa: M’chinenero cha Chigiriki choyambirira chimene “Chipangano Chatsopano” chinalembedwamo, liwu logwiritsiridwa ntchito kaamba ka “chozizwitsa” linali lakuti dyʹna·mis​—liwu limene makamaka limatanthauza “mphamvu.” Limamasuliridwanso kuti “ntchito zamphamvu” kapena “nzeru.” (Luka 6:19; 1 Akorinto 12:10, NW; Mateyu 25:15) Baibulo limanena kuti zozizwitsa za Yesu zinali chisonyezero cha “mphamvu yaikulu ya Mulungu.” (Luka 9:43, NW) Kodi ntchito zotero zikanakhala zosatheka kwa Mulungu wamphamvuyonse​—Uyo amene ali ndi “mphamvu . . . zazikulu”?​—Yesaya 40:26.

Umboni wa Kuona Kwake

Kupenda kosamalitsa Mauthenga Abwino anayi kumatulutsanso umboni wowonjezereka wa kukhoza kukhulupiririka kwawo. Choyamba, nkhani zimenezi nzosiyana kwambiri ndi nthano kapena nthanthi. Mwachitsanzo, lingalirani za nkhani zonama zimene zinafalitsidwa ponena za Yesu m’zaka mazana za pambuyo pa imfa yake. “Uthenga Wabwino wa Thomas” wa apocrypha umasimba kuti: “Pamene mnyamatayu Yesu anali ndi zaka zisanu . . . , analoŵa m’mudzi, ndipo mwana wina anathamanga ndi kumgunda paphewa lake. Yesu anakwiya namuuza kuti: ‘Supitirira ndi ulendo wako’, ndipo pomwepo mwanayo anagwa nafa.” Nkosavuta kuona zimene nkhaniyi ili​—nkhani yongopeka. Ndiponso, mwana wokakala mtima wosonyezedwa pano samafanana konse ndi Yesu wa m’Baibulo.​—Siyanitsani ndi Luka 2:51, 52.

Tsopano lingalirani za nkhani zoona za Uthenga Wabwino. Zilibe malingaliro owonjezera kapena opeka. Yesu anachita zozizwitsa malinga ndi kusoŵa kwenikweni komwe kunalipo, osati chifukwa cha phuma wamba. (Marko 10:46-52) Yesu sanagwiritsire ntchito konse mphamvu zake kuti adzipezere phindu. (Mateyu 4:2-4) Ndipo sanazigwiritsire ntchito kuti adzionetsere. Kwenikweni, pamene Mfumu Herode wachidwiyo anafuna kuti Yesu amchitire “chizindikiro” chozizwitsa, Yesu “sanamyankha kanthu.”​—Luka 23:8, 9.

Zozizwitsa za Yesu zimakhala zosiyana kwambirinso ndi zochita za a maere, amatsenga, ndi ochiritsa ndi chikhulupiriro. Nthaŵi zonse ntchito zake zamphamvuzo zinalemekeza Mulungu. (Yohane 9:3; 11:1-4) Zozizwitsa zake zinalibe madzoma ochitidwa motengeka, mawu onenera amatsenga, zionetsero, tsenga ndi mchitidwe wogoneka tulo munthu. Pamene Yesu anapeza wopemphapempha wina wakhungu wotchedwa Bartimeyu amene anafuula kuti, “Raboni, ndilandire kuona kwanga,” Yesu anangonena kuti: “Muka; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso.”​—Marko 10:46-52.

Zolembedwa za Uthenga Wabwino zimasonyeza kuti Yesu anachita ntchito zake zamphamvu popanda zinthu zina zochirikizira, zisonyezero zolinganizidwiratu kwambiri, kapena njira ya machenjera. Zinachitidwa poyerayera, kaŵirikaŵiri pamaso pa mboni zambirimbiri. (Marko 5:24-29; Luka 7:11-15) Mosiyana ndi zoyesayesa za ochiritsa ndi chikhulupiriro amakono, zoyesayesa zake za kuchiritsa sizinalephere konse chifukwa cha kusoŵa chikhulupiriro kwa munthu wina amene anali kudwala. Mateyu 8:16 akuti: “Nachiritsa akudwala onse.”

M’buku lake lakuti “Many Infallible Proofs:” The Evidences of Christianity, katswiri Arthur Pierson akunena za zozizwitsa za Kristu kuti: “Chiŵerengero chake, machiritso amene anachita apanthaŵi yomweyo ndi okwanira, ndi kusalephereka ngakhale nkumodzi komwe ngakhale poutsa akufa, zimapangitsa zozizwitsa zimenezi kukhala zosiyana kwambiri ndi zodabwitsa zongoyerekezera za nyengo ino kapena ina iliyonse.”

Umboni Wadziko

Arthur Pierson akupereka chigomeko chinanso chimene chimachirikiza nkhani za Uthenga Wabwino pamene akuti: “Palibe umboni wa zozizwitsa za m’malemba umene uli wapadera kwambiri kuposa wa kutonthola kwa adani ake.” Atsogoleri Achiyuda anali ndi chifuno chachikulu kwambiri chofuna kusambula Yesu, komano zozizwitsa zake zinali zodziŵika kwambiri kwakuti omtsutsawo sanathe kuzikana. Chimene anangonena chinali chakuti zozizwitsa zakezo zinali za mphamvu ya ziŵanda. (Mateyu 12:22-24) Zaka mazana ambiri imfa ya Yesu itachitika, alembi a Talmud Yachiyuda anapitiriza kuvomereza Yesu kuti anali ndi mphamvu zochita zozizwitsa. Malinga nkunena kwa buku lakuti Jewish Expressions on Jesus, anamsuliza kukhala munthu amene “anali kuchita matsenga.” Kodi ndemanga imeneyo ikananenedwa ngati kunali kotheka pang’ono chabe kunyalanyaza zozizwitsa za Yesu kukhala nthano wamba?

Umboni wina ukuchokera kwa wolemba mbiri ya tchalitchi wina wa m’zaka za zana lachinayi Eusebius. M’buku lake lakuti The History of the Church From Christ to Constantine, akugwira mawu munthu wina wotchedwa Quadratus amene anatumiza kalata kwa mfumu kutetezera Chikristu. Quadratus analemba kuti: “Ntchito za Mpulumutsi wathu nthaŵi zonse zinali poyerayera, pakuti zinali zoona​—anthu amene anachiritsidwa ndi awo amene anaukitsidwa kwa akufa, amene sanangoonedwa chabe panthaŵiyo pamene anachiritsidwa kapena kuukitsidwa, koma amene nthaŵi zonse anaonekera, osati kokha pamene Mpulumutsiyo anali pakati pathu, koma kwanthaŵi yaitali pambuyo pa kuchoka Kwake; kunena zoona ena a iwo adakalipo kufikira nthaŵi ino ya moyo wanga.” Katswiri William Barclay anati: “Quadratus akunena kuti anthu amene anachitiridwa zozizwitsa akanatulutsidwa kukhala umboni ngakhale munthaŵi yakeyo. Ngati zimenezo zinali zonama kukanakhala kosavuta kuti boma la Roma lizitche kuti zabodza.”

Kukhulupirira zozizwitsa za Yesu nkoyenera, nkwanzeru, ndipo nkogwirizana kwambiri ndi umboni. Chikhalirechobe, zozizwitsa za Yesu sizili mbiri yakutha. Ahebri 13:8 amatikumbutsa kuti: “Yesu Kristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kunthaŵi zonse.” Inde, iye ngwamoyo kumwamba lerolino, wokhoza kugwiritsira ntchito mphamvu zochita zozizwitsa m’njira yaikulu kuposa mmene anachitira pamene anali pa dziko lapansi monga munthu. Ndiponso, nkhani za Uthenga Wabwino zonena za zozizwitsa zake (1) zimaphunzitsa Akristu maphunziro othandiza lerolino, (2) zimasonyeza mbali zochititsa chidwi za umunthu wa Yesu, ndipo (3) zimasonya nthaŵi imene ili mtsogolomu posachedwa pamene ngakhale zochitika zozizwitsa kwambiri zidzachitika!

Nkhani yotsatira idzafotokoza nkhani zitatu zodziŵika bwino za Baibulo kusonyeza mfundo zimenezi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena