Mapemphero a m’Baibulo Ali Ofunikira Uwapenda Mosamalitsa
MKAZI woda nkhaŵa, mfumu, ndi Mwana wa Mulungu iye mwini anapereka mapemphero amene tidzapenda mosamalitsa tsopano. Pemphero lililonse linasonkhezeredwa ndi mikhalidwe yosiyana. Komabe, mikhalidwe yonga imeneyo ingatikhudze lerolino. Kodi zitsanzo zimenezi zingatiphunzitsenji?
‘Mupenyere Ndithu Kusauka kwa Mdzakazi Wanu’
Kodi mukulimbana ndi vuto losatha? Kapena kodi mwalema ndi nkhaŵa? Ndiye kuti mkhalidwe wanu ngwofanana ndi wa Hana asanabale mwana wake woyamba, Samueli. Iye analibe mwana, ndipo mkazi mnzake ankamnyodola. Kwenikweni, mkhalidwe wa Hana unamsautsa ndi kumdetsa nkhaŵa kwambiri kwakuti ankalephera kudya. (1 Samueli 1:2-8, 15, 16) Anachonderera Yehova napereka pempho lotsatirali:
“Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiŵala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.”—1 Samueli 1:11.
Onani kuti Hana sanalankhule mwachisawawa. Anapita kwa Yehova ndi pempho lolunjika (lofuna mwana wamwamuna) nawonjezapo lumbiro (la kumpereka kwa Mulungu). Kodi zimenezi zimatisonyezanji?
Pamene muli m’nsautso, perekani mapemphero olunjika. Mosasamala kanthu za vuto lanu—kaya ndi vuto la panyumba, kusungulumwa, kapena matenda—pempherani kwa Yehova za ilo. Mfotokozereni mtundu weniweni wa vuto lanu ndi mmene mukumvera. “Masiku onse madzulo ndimapereka mavuto anga onse kwa Yehova,” akutero mkazi wina wamasiye wotchedwa Louise. “Nthaŵi zina amakhala angapo ndithu, koma ndimawafotokoza bwinobwino limodzi ndi limodzi.”
Kulankhula molunjika kwa Yehova kumadzetsa mapindu. Kutero kumatithandiza kumvetsetsa vuto lathu, limene pambuyo pake lingaoneke kukhala laling’ono. Kupereka mapemphero olunjika kumatichotsera nkhaŵa. Ngakhale pamene pemphero lake linali lisanayankhidwe, Hana analimbikitsidwa, ndipo “nkhope yake siinakhalanso yachisoni.” (1 Samueli 1:18) Ndiponso, kulunjika kumatikhozetsa kuzindikira yankho la pemphero lathu. “Pamene ndilunjika kwambiri ndi mapemphero anga,” akutero Bernhard, Mkristu wina ku Germany, “mpamenenso mayankho ake amakhala oonekera bwino.”
“Ine Ndine Kamwana”
Komabe, munthu angakhale ndi nkhaŵa yamtundu wina ngati alandira ntchito imene aganiza kuti sakuiyenerera. Kodi nthaŵi zina mumathedwa mphamvu ndi thayo limene Yehova wakupatsani? Kapena kodi anthu ena amakuyesani kukhala wosayenerera ntchito yanu? Solomo wachichepere anali mumkhalidwe umenewo pamene analongedwa ufumu wa Israyeli. Amuna ena omveka anafuna kuti wina akhale pa mpando wachifumuwo. (1 Mafumu 1:5-7, 41-46; 2:13-22) Kuchiyambiyambi kwa ulamuliro wake, Solomo anapempha mwa pemphero kuti:
“Yehova inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu . . . ine ndine kamwana, sindidziŵa kutuluka kapena kuloŵa. Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa.”—1 Mafumu 3:7-9.
Solomo anasumika pemphero lake pa unansi wake ndi Yehova, pa thayo limene anapatsidwa, ndi pa luso lake la kuchita ntchitoyo. Mofananamo, pamene tipatsidwa thayo limene tiganiza kuti sitikhoza kulisamalira, tiyenera kuchonderera Mulungu kutikonzekeretsa kuchita ntchitoyo. Talingalirani zokumana nazo zotsatira:
“Pamene ndinapemphedwa kusamalira thayo lokulirapo pa ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society,” akutero Eugene, “ndinamva kukhala wopereŵeratu. Panali ena amene anayenereradi amene anali ndi chidziŵitso kundiposa. Mausiku otsatira aŵiri sindinaone tulo kwenikweni, ndikumathera nthaŵi yochulukayo m’mapemphero, amene anandipatsa nyonga ndi chilimbikitso chofunikira.”
Roy anapemphedwa kukamba nkhani ya maliro pa imfa yadzidzidzi ndi yoŵaŵa ya bwenzi lake lachichepere limene linali lomveka. Ndithudi anthu mazanamazana akapezekako. Kodi Roy anachitanji? “Si nthaŵi zambiri pamene ndinapempherapo kwambiri chotero kupempha nyonga ndi luso la kupeza mawu oyenera osonyezera mzimu womangirira ndi kupereka chitonthozo.”
Pamene Mlengi ‘akufulumiza zinthu’ ndipo gulu lake likukula, mwachibadwa chotsatirapo chake nchakuti atumiki ake owonjezereka akuikiziridwa mathayo. (Yesaya 60:22) Ngati mwapemphedwa kukhala ndi phande lowonjezera, dziŵani kuti Yehova adzakuchirikizani pa kusoŵa kwanu chidziŵitso kulikonse, maphunziro, kapena luso. Fikani kwa Mulungu mofanana ndi mmene Solomo anachitira, ndipo Iye adzakukonzekeretsani kusamalira ntchitoyo.
“Kuti Onse Akhale Amodzi”
Mkhalidwe wachitatu umene umakhalapo lerolino ndi uja wa kupemphedwa kuimira gulu m’pemphero. Titapemphedwa kupemphera m’malo mwa ena, kodi tiyenera kupempherera chiyani? Talingalirani pemphero la Yesu lolembedwa pa Yohane chaputala 17. Anapereka pempherolo madzulo pamaso pa ophunzira ake pa tsiku lake lomaliza monga munthu. Kodi zopempha zake zolunjika kwa Atate wake wakumwamba zinali zotani?
Yesu anagogomezera zonulirapo za onse omwe analipo ndi chiyembekezo cha onsewo. Anatchula za kulemekezedwa kwa dzina la Yehova Mulungu ndi za kudziŵitsa Ufumu. Yesu anagogomezera kufunika kwa unansi wa munthu mwini ndi Atate ndi Mwanayo, wozikidwa pa chidziŵitso cha Malemba. Analankhula za kulekana ndi dziko, kumene kukakonzekeretsa otsatira ake kuyang’anizana ndi chitsutso. Kristu anapemphanso Atate wake kutetezera ophunzira ake ndi kuwagwirizanitsa pa kulambira koona.
Inde, Yesu anagogomezera umodzi. (Yohane 17:20, 21) Kuchiyambiyambi madzulowo, ophunzira ake anali atakangana popanda kulingalira bwino. (Luka 22:24-27) Komabe, Kristu popemphera anafuna kuwagwirizanitsa osati kuwapatsa mlandu. Mofananamo, mapemphero a banja ndi a mpingo ayenera kuchirikiza chikondi ndipo ayenera kukhala ndi cholinga chothetsa mikangano pakati pawo. Amene akuimiridwawo ayenera kugwirizanitsidwa muumodzi.—Salmo 133:1-3.
Umodzi umenewo umasonyezedwa pamene omvetserawo anena kuti, “Amen,” kapena kuti “Zikhale tero,” pomaliza. Kuti zitheke zimenezi, iwo ayenera kumvetsetsa ndi kuvomereza zonse zonenedwazo. Chifukwa chake, kuli kosayenera kutchula m’pemphero nkhani imene ili yosadziŵika kwa ena amene alipo. Mwachitsanzo, mkulu amene akuimira mpingo m’pemphero angapemphe Yehova kudalitsa mbale kapena mlongo wauzimu amene akudwala kwambiri. Koma nthaŵi zambiri zimakhala bwino ngati achita zimenezo kokha ngati unyinji wa amene akuimiridwawo akumdziŵa munthuyo ndipo amva za matenda ake.
Onaninso kuti Yesu sanandandalike zosoŵa zaumwini za chiŵalo chilichonse cha kaguluko. Kuchita zimenezo kukanaphatikizapo kutchula nkhani zaumwini zodziŵika chabe kwa anthu oŵerengeka. Nkhani zaumwini ziyenera kuikidwa m’mapemphero a munthu mwini, amene angakhale aatali kwambiri ndi aumwini kwambiri malinga ndi kufuna kwake.
Kodi munthu ayenera kukonzekera motani kuimira msonkhano waukulu wa olambira m’pemphero? Mkristu wina wachidziŵitso akufotokoza: “Ndimalingalira pasadakhale zoyamikira, zopempha zimene abale angakhale nazo, ndi mapembedzero amene ndingatchule m’malo mwawo. Ndimandandalika malingaliro anga, kuphatikizapo zitamando, motsatizana bwino m’maganizo mwanga. Ndisanapereke pemphero lapoyera, ndimapereka pemphero la kachetechete, kupempha thandizo kuti ndiimire abalewo mwaulemu.”
Mosasamala kanthu za mikhalidwe yanu, mosakayikira mudzapeza pemphero m’Baibulo limene wina anapereka ali mumkhalidwe wonga wanu. Mapemphero osiyanasiyana amene ali m’Malemba ali umboni wa kukoma mtima kwa Mulungu. Kuŵerenga mapemphero ameneŵa ndi kuwasinkhasinkha kudzakuthandizani kuchititsa mapemphero anu kukhala atanthauzo.
[Bokosi patsamba 5]
MAPEMPHERO APADERA M’BAIBULO
Atumiki a Yehova anapereka mapemphero m’mikhalidwe yambiri yosiyanasiyana. Kodi mkhalidwe wanu ungafanane ndi umodzi kapena ingapo yotsatirayi?
Kodi mukufuna chitsogozo cha Mulungu, mofanana ndi Eliezere?—Genesis 24:12-14.
Kodi muli pafupi kuloŵa m’ngozi, mofanana ndi Yakobo?—Genesis 32:9-12.
Kodi mukufuna kudziŵa Mulungu bwino, mofanana ndi Mose?—Eksodo 33:12-17.
Kodi mukuyang’anizana ndi adani, monga Eliya?—1 Mafumu 18:36, 37.
Kodi kulalikira kumakuvutani, mofanana ndi Yeremiya?—Yeremiya 20:7-12.
Kodi mufunikira kuulula machimo ndi kupempha chikhululukiro, mofanana ndi Danieli?—Danieli 9:3-19.
Kodi mukuyang’anizana ndi chizunzo, mofanana ndi atumwi a Yesu?—Machitidwe 4:24-31.
Onaninso Mateyu 6:9-13; Yohane 17:1-26; Afilipi 4:6, 7; Yakobo 5:16.
[Bokosi patsamba 6]
ZIMENE MUYENERA KUPEMPHERERA POLIMBANA NDI CHIZOLOŴEZI CHOZAMA
Kodi mukulimbana ndi chifooko chosatha? Kodi ndimotani mmene mapemphero olembedwa m’Baibulo angakhalire othandiza? Phunzirani kwa Davide, amene anapemphera panthaŵi zosiyanasiyana ponena za zifooko zake.
Davide anaimba: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziŵe mtima wanga; mundiyese nimudziŵe zolingalira zanga.” (Salmo 139:23) Chikhumbo cha Davide chinali chakuti Yehova Mulungu asanthule zikhumbo zosayenera, malingaliro, kapena zolinga zake. Mwa mawu ena, Davide anapempha chithandizo cha Yehova chopeŵera tchimo.
Koma chifooko cha Davide chinamlaka, ndipo anachimwa kwambiri. Panonso, pemphero linamthandiza—panthaŵiyi kubwezeretsanso unansi wake ndi Mulungu. Malinga ndi kunena kwa Salmo 51:2, Davide anachonderera: “Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa.”
Nafenso modzichepetsa tingapempherere chithandizo cha Yehova kuti tiletse zikhoterero zoipa. Zimenezi zidzatilimbikitsa kulaka chifooko chozama ndipo zingatithandize kupeŵa tchimo. Titabwevuka, tiyenera kupitanso kwa Yehova ndi mapempho akuti atithandize kupitiriza nkhondoyo.
[Zithunzi patsamba 7]
Mapemphero operekedwa m’malo mwa gulu ayenera kugogomezera ziyembekezo za Malemba ndi zonulirapo zauzimu zimene onse ali nazo