Chipembedzo—Kodi ndi Nkhani Yosayenera Kukambitsirana?
“PALI nkhani ziŵiri zimene sindimakambitsirana konse ndi anthu: chipembedzo ndi ndale!” Ndilo yankho limene limaperekedwa kaŵirikaŵiri pamene Mboni za Yehova zilankhula kwa ena ponena za Baibulo. Ndipo lingaliro limenelo ndi lomveka.
Pamene anthu akambitsirana za ndale, pangakhale kupsetsana mtima kumene kungabutse mkangano. Ambiri amaona chinyengo m’malonjezo ndipo amadziŵa kuti andale kaŵirikaŵiri amangofuna ulamuliro, kutchuka, ndi ndalama. Mwachisoni, kusemphana pa zandale nthaŵi zina kumabutsa chiwawa.
Mungalingalire kuti, ‘koma kodi si mmene zakhaliranso ndi chipembedzo? Kodi malingaliro amphamvu a chipembedzo sanabutse mikangano yambiri yamakono?’ Ku Northern Ireland, Aroma Katolika ndi Aprotesitanti anali paudani kwa nthaŵi yaitali. M’maiko a Balkan, ziŵalo za tchalitchi cha Eastern Orthodox, Aroma Katolika, ndi ena amalimbirana dziko. Kodi chotulukapo nchiyani? Nkhalwe ndi udani wopitiriza.
Powopa kuphedwa, ambiri amabisa zikhulupiriro zawo ndi za mabanja awo. Mu Afirika, udani wa zipembedzo wa zaka mazana ambiri pakati pa anthu a Dziko Lachikristu, ndi otsatira zipembedzo zina zachilendo ndi za mtundu unachititsa makolo kupatsa ana awo maina amene amapereka chitetezo china chake, chizoloŵezi chimene chidakalipo lerolino. Motero, mnyamata wachichepere angadzisonyeze kukhala chiŵalo cha tchalitchi kapena cha chipembedzo china mwa kugwiritsira ntchito dzina limodzi koma osati linalo. Pamene zikhulupiriro za chipembedzo cha munthu zingamutayitse moyo wake, nkosadabwitsa kuti iye angakane kukambitsirana za chipembedzo poyera.
Kwa ena, chipembedzo ndi nkhani yosayenera kukambitsirana ngakhale pamene miyoyo yawo siili pangozi. Iwo amawopa kuti kukambitsirana za zikhulupiriro zawo ndi munthu wa chipembedzo china kudzangobutsa mkangano wopanda pake. Palinso ena amene amakhulupirira kuti zipembedzo zonse nzabwino. Iwo amati, malinga ngati munthu amakhutira ndi chimene amakhulupirira, kulankhula za kusiyana kwake kuli kutaya nthaŵi chabe.
Ngakhale ophunziradi za mkhalidwe weniweni wa chipembedzo amatsutsana iwo okha. M’nkhani yake yakuti “Kuphunzira ndi Kugaŵa Zipembedzo,” The New Encyclopædia Britannica imavomereza kuti: “Ndi mwa kamodzikamodzi . . . pamene akatswiri agwirizana pa nkhani ya mkhalidwe wa [chipembedzo] . . . Chifukwa chake, nkhaniyo, m’mbiri yonse, yakhala ndi mbali za mkangano.”
Dikishonale ina imamasulira chipembedzo kukhala “chinthu chosonyezera kukhulupirira ndi kulemekeza kwa munthu mphamvu yoposa yaumunthu” yodziŵika kukhala mlengi ndi wolamulira chilengedwe chonse. Zimenezi zikafuna kuti chipembedzo chichite mbali yaikulu kwambiri m’moyo. Ndithudi, chipembedzo chakhala mbali yaikulu yopanga mbiri ya anthu. “Sipanakhalepo chitaganya cha anthu,” ikutero Oxford Illustrated Encyclopedia of Peoples and Cultures, “chimene sichinayese kukhazikitsa dongosolo ndi tanthauzo la moyo mwa mtundu winawake wa chipembedzo.” Pokhala choloŵetsamo zinthu zofunika zoterozo monga “dongosolo” ndi “tanthauzo” m’moyo, ndithudi chipembedzo chimafunikira kanthu kena kabwino osati kutsutsana kapena kukangana. M’malo mwake, chimafunikira kukambitsirana—ndiko kuti, kupenda kosamalitsa—ndi wina wake. Koma kodi ndi kukambitsirana ndi yani, ndipo kodi kuli ndi ubwino wotani?