Tsiku Lochititsa Mantha la Yehova Lili Pafupi
“Buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuwopa Yehova, nakumbukira dzina lake.”—MALAKI 3:16.
1, 2. Kodi Malaki amachenjezeratu za tsiku lochititsa mantha liti?
LOCHITITSA MANTHA! Pamene kunayamba kucha tsikulo pa August 6, 1945, mzinda waukulu unaphwasulidwa m’nthaŵi yochepa. Anthu pafupifupi 80,000 anafa! Zikwi makumi ambiri anavulazidwa mwakayakaya! Moto unalilima! Bomba la nyukliya linali litachita ntchito yake. Kodi ndimotani mmene zinthu zinalili kwa Mboni za Yehova mkati mwa chiwonongeko chimenecho? Panali Mboni imodzi yokha mu Hiroshima—yobindikiritsidwa mkati mwa makoma a ndende otetezera chifukwa cha umphumphu wake Wachikristu. Ndendeyo inaphwasuka, koma mbale wathuyo sanavulale. Monga momwe iye ananenera, anaphulitsidwira kunja kwa ndende ndi bomba la atomulo—mwinamwake ndiyo mbali yabwino yokha imene bombalo linachita.
2 Kuphulika kwa bomba kumeneko kunali kochititsa mantha, koma kumakhala kosanunkha kanthu pamene kuyerekezeredwa ndi “tsiku lalikulu ndi lowopsa la Yehova” limene lili patsogolopa. (Malaki 4:5) O, inde, pakhala masiku ochititsa mantha m’nthaŵi yapita, koma tsiku limeneli la Yehova lidzaposa masiku onse.—Marko 13:19.
3. Kodi ndi kusiyana kotani kumene kuyenera kuonedwa pakati pa “anthu onse” ndi banja la Nowa pamene anayang’anizana ndi Chigumula?
3 M’tsiku la Nowa “anthu onse anavunditsa njira yawo pa dziko lapansi,” ndipo Mulungu analengeza kuti: “Dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzawononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.” (Genesis 6:12, 13) Monga momwe kwalembedwera pa Mateyu 24:39, Yesu anati anthu “sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.” Koma Nowa wokhulupirika, “mlaliki wa chilungamo,” limodzi ndi banja lake lowopa Mulungu, anapulumuka Chigumula chimenecho.—2 Petro 2:5.
4. Kodi ndi chitsanzo cha chenjezo chotani chimene chimaperekedwa ndi Sodomu ndi Gomora?
4 Yuda 7 akusimba kuti, “monga Sodoma ndi Gomora, ndi midzi yakuizungulira, . . . idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.” Anthu osapembedza amenewo anawonongeka chifukwa cha moyo wawo wonyansawo. Anthu okonda chisembwere a dziko lamakono lino achenjezedwetu! Komabe, onani kuti Loti wowopa Mulunguyo ndi ana ake aakazi anapulumutsidwa pa chiwonongeko chimenecho, monga momwedi olambira Yehova adzatetezeredwera pa chisautso chachikulu chimene chikuyandikira mofulumiracho.—2 Petro 2:6-9.
5. Kodi tingaphunzirenji pa ziweruzo zoperekedwa pa Yerusalemu?
5 Ndiyeno lingalirani za zitsanzo za chenjezo zoperekedwa pamene Yehova anagwiritsira ntchito magulu ankhondo oukira kufafaniza Yerusalemu, mzinda waulemerero umene panthaŵi ina unali “chimwemwe cha dziko lonse lapansi.” (Salmo 48:2) Zochitika zatsoka zimenezi zinachitika, choyamba mu 607 B.C.E. ndipo kachiŵiri mu 70 C.E., chifukwa chakuti anthuwo amene anati anali a Mulungu analeka kulambira koona. Mwamwaŵi, atumiki okhulupirika a Yehova anapulumuka. Chiwonongeko cha mu 70 C.E. (chosonyezedwa pansipa) chafotokozedwa kukhala “chisautso, chonga sichinakhala chinzake kuyambira chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu anachilenga ndi kufikira tsopano.” Chinachotseratu dongosolo la zinthu Lachiyuda la mpatuko, ndipotu chifukwa cha zimenezo “sichidzakhalanso nthaŵi zonse.” (Marko 13:19) Komabe kuperekedwa kwa chiweruzo cha Mulungu kumeneku kunangokhala mthunzi wa “chisautso chachikulu” chimene tsopano chikuwopseza dongosolo lonse la zinthu la dziko.—Chivumbulutso 7:14.
6. Kodi nchifukwa ninji Yehova amalola masoka?
6 Kodi nchifukwa ninji Mulungu angalole masoka owopsa kuchitika, anthu ambiri akumafa? Ponena za Nowa, Sodomu ndi Gomora, ndiponso ponena za Yerusalemu, Yehova anapereka chiweruzo pa awo amene anavunditsa njira yawo pa dziko lapansi, amene anadzaza pulaneti lokongolali ndi zoipa zenizeni ndi makhalidwe oluluzika, ndi amene anachita mpatuko, kapena kukana kulambira koona. Lerolino taima pamphembenu pa kuperekedwa kwa chiweruzo chotheratu chimene chidzakuta dziko lonse.—2 Atesalonika 1:6-9.
“Masiku Otsiriza”
7. (a) Kodi ziweruzo za Mulungu za munthaŵi yakale zinaloseranji? (b) Kodi ndi chiyembekezo chaulemerero chotani chimene chili mtsogolomu?
7 Ziwonongeko za m’nthaŵi zakale zimenezo zinalosera za chisautso chachikulu chochititsa mantha chofotokozedwa pa 2 Petro 3:3-13. Mtumwiyo amati: “Ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni.” Ndiyeno, pofotokoza za nthaŵi ya Nowa, Petro analemba kuti: “Dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidaonongeka; koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.” Pambuyo pa chisautso chachikulu koposacho, ulamuliro wa Ufumu wa Mesiya woyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitaliwo udzayamba kugwira ntchito m’njira yatsopano—“miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” Ha, nchiyembekezo chosangalatsa chotani nanga chimenechi!
8. Kodi zochitika za dziko zikumka motani kuchimake?
8 Mkati mwa zaka za zana lathu la 20 zino, zochitika za dziko zapita patsogolo kumka kuchimake. Ngakhale kuti kuwonongedwa kwa Hiroshima sikunali tsiku la kuyang’anira la Mulungu, kumeneku kungaphatikizidwe mu “zowopsa” zimene Yesu analosera kaamba ka nthaŵi ya mapeto. (Luka 21:11) Kunayambitsa chiwopsezo cha nyukliya chimene chidakali kuwopseza kwambiri anthu. Nchifukwa chake, mutu wina wa nkhani mu The New York Times ya November 29, 1993, unati: “Mfuti Zingakhale Zili ndi Dzimbiri Pang’ono Koma Zida za Nyukliya Zikali Zonyezimira.” Pakali pano, nkhondo za kumenyana kwa maiko, za utundu, ndi za mafuko zikupitirizabe kusakaza anthu mowopsa. Kale, unyinji wa ophedwa munkhondo unali pakati pa asilikali. Lerolino, 80 peresenti ya ophedwa mu nkhondo amati ndi anthu wamba, osanena za miyandamiyanda imene imachoka kwawo monga othaŵa.
9. Kodi atsogoleri achipembedzo asonyeza motani ubwenzi ndi dziko?
9 Kaŵirikaŵiri atsogoleri achipembedzo asonyeza, ndipo akupitirizabe kusonyeza, ‘ubwenzi ndi dziko’ mwa kukhala okangalika mu nkhondo ndi zipolowe zokhetsa mwazi. (Yakobo 4:4) Ena agwirizana ndi eni malonda aumbombo pamene akundika zida zankhondo zakupha ndi kupanga magulu amphamvu ogulitsa anamgoneka. Mwachitsanzo, posimba za kuphedwa kwa mtsogoleri wina wa bizinesi ya anamgoneka wa ku South America, The New York Times inati: “Pobisa zochita zake za kugulitsa anamgoneka mwa kunena kuti anali ndi chuma chopezedwa ndi bizinesi yololedwa ndi lamulo ndi popereka chithunzi chonga cha mwini bizinesi, iyeyo anali ndi programu yakeyake pa wailesi ndipo kaŵirikaŵiri anali kukhala ndi ansembe a Roma Katolika.” The Wall Street Journal inasimba kuti kuwonjezera pa kuwononga miyoyo miyandamiyanda ya anthu amene anakhala omwerekera ndi anamgoneka, mtsogoleri wa bizinesi ya anamgoneka ameneyu analamulira kuphedwa kwa anthu zikwi zambiri. The Times ya ku London inati: “Kaŵirikaŵiri anthu akuphawo amalipirira Misa yapadera ya chiyamiko . . . panthaŵi imodzimodziyo pamene maliro a wophedwayo akuchitika kwina kwake.” Ha, ndi uchiŵanda wotani nanga!
10. Kodi tiyenera kuona motani mikhalidwe yomaipa ya dzikoli?
10 Ndani amene angadziŵe za kusakaza kumene anthu olamuliridwa ndi ziŵandawo ati achitenso pa dziko lapansili? Monga momwe 1 Yohane 5:19 amanenera, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. Lerolino kuli “tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:12) Komabe, mwamwaŵi, Aroma 10:13 amatitsimikizira kuti “amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”
Mulungu Akuyandikira Kudzapereka Chiweruzo
11. Kodi ndi mikhalidwe yotani ya mu Israyeli imene inasonkhezera ulosi wa Malaki?
11 Ponena za mtsogolo mwa anthu mmene muli pafupi kudza, ulosi wa Malaki umasonyeza bwino zimene ziti zichitike. Malaki ndiye wotsiriza mumzera wautali wa aneneri Achihebri akale. Israyeli anali ataona chipasuko cha Yerusalemu mu 607 B.C.E. Koma patapita zaka 70 Yehova anasonyeza chifundo chokoma mtima pobwezeretsa mtundu umenewo kudziko lake. Komabe, m’zaka zana limodzi, Israyeli anali kuloŵanso mumpatuko ndi kuipa. Anthu anali kululuza dzina la Yehova, kunyalanyaza malamulo ake olungama, ndi kuipitsa kachisi wake mwa kubweretsa nyama zakhungu, zotsimphina ndi zodwala kaamba ka nsembe. Anali kusudzulanso akazi a ubwana wawo kotero kuti akwatire akazi achilendo.—Malaki 1:6-8; 2:13-16.
12, 13. (a) Kodi ndi kuyeretsa kotani kumene kwakhala kofunikira pa kagulu ka ansembe odzozedwa? (b) Kodi nalonso khamu lalikulu limapindula motani ndi kuyeretsako?
12 Panafunikiradi ntchito ya kuyeretsa. Yafotokozedwa pa Malaki 3:1-4. Monga Israyeli wakale, Mboni za Yehova zamakono zinafunikira kuyeretsedwa, chotero ntchito yoyeretsa yofotokozedwa ndi Malaki iyenera kuwakhudza. Pamene nkhondo yadziko yoyamba inayandikira mapeto ake, ena a Ophunzira Baibulo, monga momwe Mboni zinkatchedwera panthaŵiyo, sanapeŵe mwamphamvu kuloŵa mu zochitika za dziko. Mu 1918, Yehova anatumiza ‘mthenga Wake wachipangano,’ Kristu Yesu, kumakonzedwe Ake a kachisi wauzimu kukayeretsa maŵanga a dziko pa kagulu kakang’ono ka olambira Ake. Mwaulosi, Yehova anafunsa kuti: “Ndani adzapirira tsiku la kudza kwake [mthengayo]? Ndipo adzaima ndani pooneka iye? Pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka; ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi [kagulu ka ansembe odzozedwa], nadzawayengetsa ngati golidi ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m’chilungamo.” Monga anthu oyeretsedwa, iwo achita zimenezo kumene!
13 Kagulu ka ansembe odzozedwa kameneko nkokwanira 144,000 chabe. (Chivumbulutso 7:4-8; 14:1, 3) Komabe, bwanji nanga za Akristu ena odzipatulirawo lerolino? Ameneŵa, amene tsopano akuwonjezereka m’mamiliyoni ambiri, amapanga “khamu lalikulu” limenenso liyenera kuyeretsedwa pa njira za dziko, ‘akumatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.’ (Chivumbulutso 7:9, 14) Motero, mwa kusonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya dipo ya Mwanawankhosa, Kristu Yesu, iwo amakhoza kukhalabe ndi kaimidwe koyera pamaso pa Yehova. Iwo alonjezedwa kupulumuka chisautso chonse chachikulu, tsiku lochititsa manthalo la Yehova.—Zefaniya 2:2, 3.
14. Kodi anthu a Mulungu lerolino ayenera kulabadira mawu ati pamene akupitiriza kukulitsa umunthu watsopano?
14 Pamodzi ndi ansembe otsalira, khamu lalikulu limeneli liyenera kulabadira mawu ena a Mulungu: “Ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiwopa ine . . . Pakuti ine Yehova sindisinthika.” (Malaki 3:5, 6) Ayi, miyezo ya Yehova simasintha, chotero powopa Yehova, anthu ake lerolino ayenera kuda kulambira mafano a mtundu uliwonse ndi kukhala oona, okhulupirika, ndi owoloŵa manja pamene akupitirizabe kukulitsa umunthu Wachikristu.—Akolose 3:9-14.
15. (a) Kodi ndi chiitano chachifundo chotani chimene Yehova akupereka? (b) Kodi tingapeŵe bwanji ‘kulanda’ Yehova?
15 Yehova akupereka chiitano kwa aliyense amene angakhale atapatuka kuchoka m’njira zake zolungama, akumati: “Bwererani kudza kwa ine, ndipo ine ndidzabwerera kwa inu.” Ngati ameneŵa afunsa kuti: “Tibwerere motani?” iye akuyankha kuti: “Inu mundilanda ine.” Ndipo poyankha funso lina lakuti: “Takulandani zotani?” Yehova akunena kuti amlanda mwa kulephera kubweretsa zopereka zawo zabwino koposa kaamba ka utumiki wake wa pakachisi. (Malaki 3:7, 8) Pokhala tili mbali ya anthu a Yehova, ndithudi ife tiyenera kufuna kupereka zopereka zathu zabwino koposa za nyonga yathu, maluso, ndi chuma chakuthupi ku utumiki wa Yehova. Motero, m’malo mwa kulanda Mulungu, ‘timapitirizabe kufunafuna choyamba ufumuwo ndi chilungamo chake.’—Mateyu 6:33, NW.
16. Kodi ndi chilimbikitso chotani chimene timapeza pa Malaki 3:10-12?
16 Pali mphotho yaikulu kwa onse amene amakana njira za dziko za kukondetsa zinthu zakuthupi kwadyera, monga momwe Malaki 3:10-12 akusonyezera: “Mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoŵeka malo akuulandira.” Kwa onse amene ali oyamikira, Yehova akulonjeza kulemerera kwauzimu ndi mapindu ochuluka. Iye akuwonjezera: “Amitundu onse adzatcha inu odala; pakuti mudzakhala dziko lokondweretsa.” Kodi zimenezo sizinakhaledi choncho lerolino pakati pa mamiliyoni a anthu a Mulungu oyamikira pa dziko lonse lapansi?
Osunga Umphumphu m’Buku la Moyo
17-19. (a) Kodi chipwirikiti cha ku Rwanda chayambukira motani abale athu kumeneko? (b) Kodi okhulupirika onseŵa apitabe patsogolo ndi chitsimikizo chotani?
17 Tsopano, tinganene za umphumphu wa abale ndi alongo athu a ku Rwanda. Iwo nthaŵi zonse abweretsa zopereka zauzimu zabwino kwambiri ku nyumba yauzimu yolambirira ya Yehova. Mwachitsanzo, pa Msonkhano wawo Wachigawo wa “Chiphunzitso Chaumulungu” mu December 1993, ofalitsa Ufumu awo 2,080 anali ndi chiwonkhetso cha ofikapo 4,075. Panali Mboni zatsopano zobatizidwa 230, ndipo mwa zimenezi, pafupifupi 150 zinalembetsa utumiki waupainiya wothandiza mwezi wotsatira.
18 Pamene kumenyana kwa mafuko kunaulika mu April 1994, pafupifupi Mboni 180, kuphatikizapo woyang’anira mzinda mu Kigali, likulu lake, ndi banja lake lonse, anaphedwa. Otembenuza chinenero asanu ndi mmodzi pa ofesi ya Watch Tower Society mu Kigali, anayi Ahutu ndipo aŵiri Atutsi, anapitirizabe kugwira ntchito kwa milungu ingapo ngakhale kuti anali kuwopsezedwa kwambiri, kufikira pamene Atutsiwo anathaŵa, koma anaphedwa atafika pamalo ofufuzira. Potsirizira pake, atanyamula makompyuta amene anatsala nawo, anayi otsalawo anathaŵira ku Goma, ku Zaire, kumene akupitiriza kutembenuza mokhulupirika Nsanja ya Olonda m’chinenero cha Kinyarwanda.—Yesaya 54:17.
19 Mboni zothaŵa kwawo zimenezi, ngakhale kuti zili m’mikhalidwe yovuta, nthaŵi zonse zinapempha chakudya chauzimu choyamba m’malo mwa thandizo la kuthupi. Posonyeza kudzimana kwakukulu, abale achikondi akumaiko osiyanasiyana anakhoza kuwatumizira katundu wachithandizo. Mwa kulankhula kwawo ndi makhalidwe olongosoka m’mikhalidwe yotsendereza imeneyi, othaŵa kwawo ameneŵa apereka umboni wabwino kwambiri. Iwo apitirizadi kubweretsa zopereka zawo zabwino koposa ku kulambira Yehova. Asonyeza chitsimikizo chofanana ndi chimene Paulo ananena pa Aroma 14:8: “Tingakhale tili ndi moyo, tikhalira [Yehova, NW] moyo; kapena tikafa, tifera [Yehova]; chifukwa chake tingakhale tili ndi moyo, kapena tikafa, tikhala ake a [Yehova].”
20, 21. (a) Kodi ndi maina a ayani amene sanalembedwa m’buku la chikumbutso la Yehova? (b) Kodi ndi maina a ayani amene ali m’bukulo, ndipo chifukwa ninji?
20 Yehova amasunga mbiri ya onse amene amamtumikira mu umphumphu. Ulosi wa Malaki umapitirizabe kuti: “Pamenepo iwo akuwopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuwopa Yehova, nakumbukira dzina lake.”—Malaki 3:16.
21 Nkofunika chotani nanga lerolino kuti ife tisoyeze mantha aumulungu polemekeza dzina la Yehova! Mwa kuchita motero, sitidzapatsidwa chilango, monga mmene kudzakhalira kwa awo amene mosirira amachirikiza madongosolo a dziko lino. Chivumbulutso 17:8 chimasimba kuti ‘maina awo sanalembedwa m’buku la moyo.’ Moyenerera, dzina lokwezeka lolembedwa m’buku la Yehova la moyo ndilo lija la Mkulu wa moyo, Mwana wa Mulungu mwiniyo, Yesu Kristu. Mateyu 12:21 amalengeza kuti: “Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lake.” Nsembe ya dipo ya Yesu imapereka moyo wosatha kwa onse amene amaikhulupirira. Ha, ndi mwaŵi wapadera chotani nanga kukhala ndi maina athu atawonjezeredwa pa dzina la Yesu m’buku limenelo!
22. Kodi ndi kusiyana kotani kumene kudzaonekera pamene Yehova adzapereka chiweruzo?
22 Kodi zinthu zidzakhala motani kwa atumiki a Mulungu pa chiweruzocho? Yehova akuyankha pa Malaki 3:17, 18: “Ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wake womtumikira. Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.” Kugaŵanikako kudzakhala kwachionekere kwa onse: oipa, akumalekanitsidwa kumka kuchilango cha nthaŵi zonse, ndipo olungama akumavomerezedwa kukhala ndi moyo wosatha mu Ufumu. (Mateyu 25:31-46) Motero khamu lalikulu la anthu onga nkhosa lidzapulumuka patsiku lalikulu lochititsa mantha la Yehova.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndi ziweruzo zotani zimene Yehova anapereka m’nthaŵi za Baibulo?
◻ Kodi ndimotani mmene mikhalidwe lerolino ilili yogwirizana ndi ija ya m’nthaŵi zakale?
◻ Kodi ndi kuyeretsa kotani kumene kwachitika pokwaniritsa ulosi wa Malaki?
◻ Kodi ndi maina a ayani amene amalembedwa m’buku la chikumbutso la Mulungu?