Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwakondwa kuŵerenga makope a Nsanja ya Olonda a posachedwapa? Chabwino, taonani ngati mungayankhe mafunso otsatirawa:
▫ Kodi nchifukwa ninji Akristu oyambirira sanachite phwando la tsiku la kubadwa kwa Yesu?
Malinga ndi The World Book Encyclopedia, “Akristu Oyambirira sanachite phwando la kubadwa [kwa Yesu] chifukwa chakuti anaona kuchitira phwando kubadwa kwa munthu aliyense kukhala mwambo wachikunja.”—12/15, tsamba 4.
▫ Kodi mapemphero ayenera kulunjikitsidwa kwa Yesu?
Iyayi, chifukwa chakuti mapemphero ali mtundu wina wa kulambira kumene kuyenera kuperekedwa kokha kwa Mulungu Wamphamvuyonse. Mwa kupereka mapemphero athu onse kwa Yehova Mulungu, timasonyeza kuti talabadira chilangizo cha Yesu cha kupemphera kuti: “Atate wathu wa Kumwamba.” (Mateyu 6:9)—12/15, tsamba 25.
▫ Kodi nchifukwa ninji chiweruzo chosiyana chinaperekedwa pa tchimo lowopsa la Mfumu Davide poyerekezera ndi machimo a Hananiya ndi Safira? (2 Samueli 11:2-24; 12:1-14; Machitidwe 5:1-11)
Mfumu Davide anagwera m’tchimo chifukwa cha kufooka kwakuthupi. Pamene zimene anachita zinaikidwa pamaso pake, iye analapa, ndipo Yehova anamkhululukira—ngakhale kuti anakumana ndi zotsatirapo za tchimo lake. Hananiya ndi Safira anachimwa mwa kulinganiza mwadala kunyenga mpingo Wachikristu ndipo motero ‘anachitira chinyengo mzimu woyera ndi Mulungu.’ (Machitidwe 5:3, 4) Zimenezo zinakhala umboni wa mtima woipa, chotero iwo anaweruzidwa mowopsa kwambiri.—1/1, masamba 27, 28.
▫ Kodi nchiyani chimene chingatithandize kutumikira Yehova mokondwera mtima?
Tiyenera kukhala ndi lingaliro labwino ndi loyamikira madalitso athu ndi mwaŵi wa mathayo wopatsidwa ndi Mulungu, ndipo sitiyenera kuiŵala kuti mwa kutsatira Mawu a Mulungu, timamkondweretsa iye.—1/15, tsamba 16.
▫ Kodi tiyenera kukumbukira zinthu ziŵiri ziti kuti tipereke chilimbikitso chogwira mtima?
Choyamba, lingalirani zimene mudzakamba, kotero kuti chilimbikitso chanu chikhale cholunjika. Chachiŵiri, funafunani mpata wa kupita kwa munthu amene ayenera kuyamikiridwa kapena amene afunikira kulimbikitsidwa.—1/15, tsamba 23.
▫ Kodi nchifukwa ninji “khamu lalikulu” lili ndi “makhwatha a kanjedza m’manja mwawo”? (Chivumbulutso 7:9)
Kugwedeza makhwatha a kanjedza kumasonyeza kuti “khamu lalikulu” likutamanda Ufumu wa Yehova ndi Mfumu yake yodzozedwayo, Yesu Kristu, mwachisangalalo. (Onani Levitiko 23:39, 40.)—2/1, tsamba 17.
▫ Kodi ndi maphunziro othandiza otani amene amapezeka m’buku la Yobu?
Buku la Yobu limatisonyeza mmene tingasamalilire mavuto. Limapereka zitsanzo zabwino kwambiri za mmene munthu wina amene akuyang’anizana ndi mayesero ayenera—ndi mmene sayenera—kupatsidwira uphungu. Ndiponso, chokumana nacho cha Yobu mwiniyo chingatithandize kuchita zinthu m’njira yoyenera pamene tikanthidwa ndi mavuto aakulu.—2/15, tsamba 27.
▫ Kodi zozizwitsa za Yesu zimatiphunzitsanji?
Zozizwitsa za Yesu zimalemekeza Mulungu, zikumapereka chitsanzo kwa Akristu cha kulemekeza Mulungu. (Aroma 15:6) Zimalimbikitsa kuchita zabwino, kusonyeza kuoloŵa manja, ndi kusonyeza chifundo.—3/1, tsamba 8.
▫ Kodi kupenda mafunso okonzedwa kumene akulu amachita ndi odzipatulira chatsopano kumakwaniritsanji?
Kuchita zimenezi kumatsimikizira kuti woyembekezera ubatizo aliyense akumvetsetsa bwino lomwe ziphunzitso zoyambirira za Baibulo ndipo akuzindikira zimene kukhala Mboni ya Yehova kumatanthauza.—3/1, tsamba 13.
▫ Kodi mapemphero a m’Baibulo angatipindule motani?
Mwa kupenda mosamalitsa mapemphero a m’Malemba, tingapeze aja amene anaperekedwa m’mikhalidwe yonga yathu. Kupeza, kuŵerenga, ndi kusinkhasinkha mapemphero otero kudzatithandiza kuwongolera kulankhula kwathu ndi Yehova.—3/15, masamba 3, 4.
▫ Kodi mantha aumulungu nchiyani?
Mantha aumulungu ndiwo kuwopa Yehova, ulemu waukulu kwa iye, limodzi ndi chinthenthe choyenera cha kusamkondweretsa. (Salmo 89:7)—3/15, tsamba 10.
▫ Kodi ndi njira zitatu ziti zimene Baibulo limasonyeza kuti tili a mtengo wapatali pamaso pa Mulungu?
Baibulo limaphunzitsa kuti aliyense wa ife ali woŵerengeredwa pamaso pa Mulungu (Luka 12:6, 7); limamveketsa bwino zimene Yehova amaŵerengera mwa ife (Malaki 3:16); ndipo limasimba zimene Yehova wachita kusonyeza chikondi chake pa ife. (Yohane 3:16)—4/1, masamba 11, 12, 14.
▫ Kodi nchifukwa ninji mawu a Ahebri 10:24, 25 si lamulo chabe lakuti Akristu azisonkhana pamodzi?
Mawu a Paulo ameneŵa amapereka muyezo wouziridwa waumulungu wa misonkhano yonse Yachikristu—ndipo ndithudi, wa chochitika chilichonse pamene Akristu asonkhana pamodzi.—4/1, tsamba 16.