Umbeta m’Nthaŵi za Mavuto a Zachuma
“NDINAFUNA kukwatira pamene ndinali ndi zaka 25,” anatero Chuks, yemwe akukhala ku West Africa. “Panali msungwana wina amene ndinali kumganizira, ndipo nayenso anandikonda. Vuto linali pa ndalama. Atate ndi mkulu wanga sanali kugwira ntchito, ndipo aphwanga ndi alongo anga aang’ono anali pasukulu. Onse anandiyembekezera kusamalira banja. Ndiyeno, choipa kwambiri chinali chakuti makolo anga anadwala, ndipo zimenezo zinafuna ndalama zina zolipirira mankhwala.”
Chuks, Mboni ya Yehova, sanafune kuloŵa mu ukwati ali wosakhoza kusamalira mkazi wake. Iye anali kukumbukira mawu a Paulo opezeka pa 1 Timoteo 5:8: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.”
“Ndinagwira ntchito zolimba,” Chuks anapitiriza motero, “koma ndalama sizinali kukwanira. Chotero, tinaimitsa zolinga zathu za ukwati nthaŵi ndi nthaŵi. Potsirizira pake, ndinalandira kalata kuchokera kwa msungwanayo yonena kuti munthu wina anafikira atate wake nafunsira kukwatirana naye. Atate wake anavomera. Patapita masiku angapo pambuyo polandira kalata yake, banjalo linachita phwando lachitomero.”
Mofanana ndi Chuks, amuna ambiri Achikristu aona zolinga zawo za ukwati zikulephera kapena kuimitsidwa chifukwa cha mikhalidwe yovuta ya zachuma. M’maiko ambiri mitengo ya zinthu njokwera kwambiri. Mwachitsanzo, m’dziko lina lapakati pa Afirika, mitengo inakwera ndi 8,319 peresenti m’chaka chimodzi! M’maiko ena ntchito nzovuta kupeza. Nthaŵi zambiri, malipironso ngochepa kwambiri kwakuti nkovuta kwa mwamuna kudzisamalira iyemwini, ngakhale mkazi wake ndi ana. Mnyamata wina ku Nigeria anadandaula kuti ntchito yanthaŵi yonse imene anapatsidwa m’fakitale inali ya malipiro a $17 chabe pamwezi—osakwanira ndi mtengo wa basi wopitira ku ntchito ndi kubwerako pamwezi!
Akazi ambiri Achikristu amene ali mbeta nawonso akuona kuti mavuto a zachuma akulepheretsa zolinga zawo za kukwatiwa. Kaŵirikaŵiri iwo amagwira ntchito kuti asamalire a m’banja mwawo. Amuna ena mbeta, poona mkhalidwewo, amaupeŵa, pozindikira kuti mwamuna wokwatira m’mikhalidwe imeneyo afunikira kupeza ndalama zambiri zosamalirira osati mkazi wake chabe komanso ndi banja la mkaziyo. Ayo, womaliza maphunziro payunivesite, akuvutikira kudzisamalira iyemwini, amake, ndi alongo ake aang’ono ndi aphwake. “Ndifuna kukwatiwa,” iye akudandaula motero, “koma pamene ena afika naona mzera wanga wautali kumbuyo [amene ndiyenera kusamalira], iwo amathaŵa.”
Ngakhale kuti ali m’mavuto a ndalama, Akristu ambiri osakwatira amapezeka kuti akukakamizidwa ndi achibale awo ndi ena kukwatira ndi kukhala ndi ana. Nthaŵi zina kukakamiza kumeneku kumachitika mwa kuwaseka. Mwachitsanzo, kumbali zina za Afirika, ndi mwambo kufunsa za mkazi kapena mwamuna wa munthu wachikulire ndi ana ake pompatsa moni. Nthaŵi zina, moni wotero umagwiritsiridwa ntchito kusereula anthu osakwatira. John, amene ali ndi zaka zakumapeto kwa ma 40, akuti: “Pamene anthu andiseka nati, ‘Kodi akazi anu ali bwanji?,’ ndimayankha kuti, ‘Akubwera.’ Kunena zoona, kodi ndingakhale bwanji ndi mkazi ngati sindikhoza kumsamalira?”
Mkhalidwe wa John ndi ena ambiri onga iye ukufotokozedwa bwino ndi mwambiwu Wachiyoruba: “Kukwatira msanga si nkhani yodzitamirapo; mtengo wa chakudya ndiwo vuto lake.”
Chitani Zimene Mungathe ndi Mkhalidwe Wanu
Kumakhala kwapafupi chotani nanga kusweka mtima pamene tilakalaka kanthu kena kamene sitikapeza. Miyambo 13:12 imati: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima.” Mwinamwake umu ndi mmene mumamvera ngati mukulakalaka kukwatira koma simukhoza kutero chifukwa cha vuto la ndalama. Zimenezi zingakhale choncho makamaka ngati muli pakati pa aja omwe mtumwi Paulo anafotokoza kukhala ‘otentha mtima.’—1 Akorinto 7:9.
Kugonjetsa mavutowo sikungakhale kwapafupi, koma pali zinthu zimene mungachite kuti mupirire ndi kupeza ngakhale chimwemwe mumkhalidwe wanu. Yesu Kristu, mwamuna wosakwatira, anatchula lamulo la Baibulo logwira ntchito limene lingakuthandizeni kulaka kukhumudwa kodzetsedwa ndi chiyembekezo chozengereza. Iye anati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
Mungatsatire zimenezi mwa kuchitira zabwino banja lanu ndi ena mumpingo. Ndiponso mwinamwake mungawonjezere ntchito yanu mu utumiki Wachikristu. Mukadzitangwanitsa kwambiri ndi kupatsa kopanda dyera, mudzapeza kuti mungakhale ‘wokhazikika mumtima mwanu, muli nawo ulamuliro wa pa chifuniro cha inu mwini.’—1 Akorinto 7:37.
Mwamuna wina wosakwatira, mtumwi Paulo, analemba uphungu wothandizawu: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.” (Aefeso 5:15, 16) Akristu ambiri osakwatira apeza ‘mpumulo wa moyo wawo’ mwa kugwiritsira ntchito nthaŵi yawo kuyandikira kwambiri kwa Yehova mwa pemphero, phunziro la Mawu a Mulungu, ndi kutenga mbali m’misonkhano Yachikristu. (Mateyu 11:28-30) Mukachita zimenezi, mudzakhoza kulimbana bwino lomwe ndi mkhalidwe wovuta wa zachuma. Zidzakuthandizaninso kusonyeza kwambiri mkhalidwe wauzimu, zikumakukhalitsani mwamuna kapena mkazi wabwinopo ngati mudzakwatira potsirizira pake.
Musaiŵale konse kuti Yehova amasamala onse amene amamtumikira. Iye akudziŵa za zothetsa nzeru ndi mavuto omwe muli nawo. Atate wathu wachikondi wakumwamba amadziŵanso zimene zidzakukomerani m’kupita kwa nthaŵi, mwauzimu ndi mwamaganizo. Mukagwiritsira ntchito moleza mtima malamulo a Mawu ake m’moyo wanu wa tsiku ndi tsiku, mungakhale wotsimikiza kuti adzakupatsani mpumulo panthaŵi yake yoyenera ndi kukhutiritsa zofuna zanu ndi zikhumbo mwa njira yokupindulitsani kosatha. Baibulo limalonjeza kuti: “[Yehova, NW] sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.”—Salmo 84:11.
Onani Mbali Yabwino ya Zinthu
Kumbukiraninso kuti kukhala mbeta kuli ndi mapindu akeake. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Iye . . . amene apereka unamwali wake mu ukwati achita bwino, koma iye amene saupereka mu ukwati adzachita bwino kwambiri.”—1 Akorinto 7:38, NW.
Kodi nchifukwa ninji umbeta uli “bwino kwambiri” kuposa ukwati? Paulo anafotokoza kuti: “Wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye; koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wake [ndipo ali wogaŵanika, NW]. Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m’thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.”—1 Akorinto 7:32-34.
Mwa mawu ena, Akristu okwatira moyenerera amada nkhaŵa ndi zimene mnzawo wa mu ukwati afuna, akonda, ndi kuda. Koma Akristu amene ali mbeta angasumike maganizo kwambiri pa utumiki wa Yehova. Kuwayerekezera ndi aja okwatira, Akristu amene ali mbeta ali m’malo abwinopo a kukhala ‘otsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa.’—1 Akorinto 7:35.
Paulo sakunena kuti Mkristu amene ali mbeta alibe zocheukitsa. Ngati muli ndi mtolo wa zothetsa nzeru zachuma, mungamve ngati kuti pali zinthu zambiri zimene zikuyesa kukucheukitsani pa utumiki wanu. Chikhalirechobe, mwamuna kapena mkazi wosakwatiwa kaŵirikaŵiri amakhala ndi ufulu waumwini wokulirapo wa kutumikira Mulungu kuposa uja wa aja okwatira.
Pamene kuli kwakuti mtumwi Paulo anayamikira umbeta kukhala njira yabwinopo, iye sananene kuti kukwatira nkulakwa. Analemba kuti: “Ungakhale ukwatira, sunachimwa.” Komabe, anachenjeza kuti: “Koma otere [okwatira] adzakhala nacho chisautso m’thupi.”—1 Akorinto 7:28.
Kodi anatanthauzanji mwa kunena zimenezo? Ukwati umadzetsa nkhaŵa zina. M’nthaŵi za mavuto a zachuma, chisautso chotero chingaphatikizepo nkhaŵa ya atate ya kusamalira mkazi wake ndi ana. Kudwala nakonso kungabweretse mtolo wina wa zandalama ndi wa kupsinjika mtima pa banja.
Chotero ngakhale kuti mkhalidwe wanu si umene mungakonde, mungakhale m’malo abwinopo kuposa mmene mungakhalire ngati munali wokwatira ndipo ngati munali ndi thayo la kusamalira ana. Zovuta zimene mukuyang’anizana nazo tsopano nzakanthaŵi; zidzachotsedwa m’dongosolo latsopano la Mulungu—ndipo zina mwina zidzachotsedwa nthaŵiyo isanafike.—Yerekezerani ndi Salmo 145:16.
Kodi Mungafutukule Utumiki Wanu?
Pamene kuli kwakuti si onse amene angachite zimenezo, ena akhoza kuloŵa mu utumiki wanthaŵi yonse mosasamala kanthu za mavuto a zandalama. Chuks, wotchulidwa poyambirira, anali kugula ndi kugulitsa ziŵiya za mu ofesi kuti asamalire banja. Pamene zolinga zake za ukwati zinangolephera, iye analandira kalata yomuitana kukagwira ntchito yomanga yakanthaŵi ku ofesi yakwawo ya nthambi ya Watch Tower Society. Pokonda ndalama, mkulu wake sanamlimbikitse kupita. Koma Chuks analingalira kuti Yehova anamthandiza kuyambitsa malonda ake ogulitsa ziŵiya za m’maofesi, choncho iye anayenera kuika zinthu za Ufumu poyamba ndi kudalira pa mphamvu ya Mulungu ya kugaŵira zofunika. (Mateyu 6:25-34) Ndiponso, iye anaganiza motero, ntchitoyo inali ya miyezi itatu chabe.
Chuks analandira chiitanocho nasiyira mkulu wakeyo malondawo. Zaka zisanu ndi chimodzi zapitapo, ndipo Chuks akali mu utumiki wanthaŵi yonse, ndi mkulu mumpingo Wachikristu, ndipo akhoza kukwatira chifukwa ali bwino m’zandalama. Kodi iye ali ndi chisoni chifukwa cha mmene zinthu zakhalira m’moyo wake? Chuks akuti: “Ndinakhumudwa kwambiri pamene ndinalephera kukwatira panthaŵi imene ndinafuna, koma zinthu zandikhalira bwino koposa. Ndapeza chimwemwe chochuluka ndi mathayo a utumiki amene mwina sindikanakhala nawo ngati ndikanakwatira panthaŵi ija ndi kukhala ndi banja.”
Chisungiko cha Mtsogolo
Panthaŵi zovuta ambiri amafuna chisungiko cha mu ukwati kuti chiwatetezere ku mavuto amtsogolo a ndalama. Maiko ena, pokhala ndi ngongole zochuluka, amapereka chithandizo chochepa kwa okalamba kapena samapereka chilichonse nkomwe. Chotero nthaŵi zambiri makolo amadalira mabanja awo, ndipo makamaka ana awo, kuwasamalira pa ukalamba wawo. Ndiponso, amuna ndi akazi amene ali mbeta kaŵirikaŵiri amakakamizidwa kukwatira ndi kubala ana, ngakhale pamene ali m’mavuto owopsa a ndalama.
Koma ukwati ndi kubala ana sizimalonjeza chisungiko. Ana ena akudziko safuna kusamalira makolo awo okalamba, ena sakhoza, pamene kuli kwakuti enanso amafa makolo awo asanafe. Akristu makamaka amayang’ana kwina kaamba ka chisungiko, pokumbukira lonjezo la Mulungu lakuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.”—Ahebri 13:5.
Aja amene aimitsa ukwati kuti atumikire Yehova kwa nthaŵi yonse sanatayidwe. Christiana ndi mbeta ndipo ali ndi zaka 32. Watumikira monga mpainiya wokhazikika ku Nigeria kwa zaka zisanu ndi zinayi zapitazo. Iye akuti: “Ndimaika chidaliro changa mwa Yehova, amene amatilonjeza kuti sadzasiya atumiki ake. Lonjezo lake ndilo chidaliro changa. Yehova amandisamalira ponse paŵiri mwauzimu ndi mwa kuthupi. Wakhaladi Atate wowoloŵa manja. Mwachitsanzo, ndinasamuka kukachita upainiya kudera kumene kuli kusoŵa kwakukulu kwa Mboni. Ngakhale kuti malowo ali ndi zothandiza zochepa zofunika pa moyo, ndaphunzira kukhala wokhutira ndi zomwe ndili nazo. Pamene ndinagonekedwa kuchipatala chifukwa chodwala typhus, abale a mumpingo wanga wakale anadzandizonda ndi kundisamalira.
“Ndine wokhutira kwambiri ndi utumiki wanthaŵi yonse. Ndimauona kukhala mwaŵi waukulu kugwira ntchito ndi Mlengi wa chilengedwe chonse ndiponso ndi abale ndi alongo ambiri padziko lonse. Ndaona achichepere ambiri amene ali ogwiritsidwa mwala ndi opanda chiyembekezo chifukwa cha zimene zikuwachitikira. Koma ine, moyo wanga uli ndi tanthauzo; ndikuyang’ana kutsogolo ndi chidaliro. Ndikudziŵa kuti kukhala pafupi ndi Yehova ndiko njira yabwino koposa yothetsera mavuto amene tikukumana nawo lerolino.”
Ngati mukulakalaka kukwatira koma simukhoza chifukwa cha mavuto a zachuma, limbikani mtima! Simuli nokha ayi. Pali ambiri amene akupirira ziyeso zonga zanu mothandizidwa ndi Yehova. Chitani zimene mungathe ndi mkhalidwe wanu mwa kuyesetsa kuchitira zabwino ena ndi mwa kuwongolera mkhalidwe wanu wauzimu. Yandikirani kwambiri kwa Mulungu; adzakuthandizani chifukwa chakuti amasamaladi za inu.—1 Petro 5:7.