Mboni za Yehova Padziko Lonse—Brazil
BRAZIL ndi dziko lalikulu kwambiri m’mbali zambiri. Mu ukulu ndi chiŵerengero cha anthunso, ndi dziko lalikulu lachisanu padziko lonse. Limatenga pafupifupi theka la dera la South America ndipo lili ndi anthu ambiri kuposa maiko ena a pa kontinentiyo ataphatikizidwa pamodzi. Brazil alinso ndi nkhalango ya mvula yaikulu koposa padziko lonse. M’nkhalango imeneyo mumadutsa mtsinje waukulu koposa pa dziko lapansi—Amazon.
Brazil alinso dziko lalikulu kwambiri m’lingaliro lina. Chiŵerengero cha ofalitsa ake a uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu chikuyandikira ku 400,000, ndipo chaka chatha oposa 1,000,000 anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Chotero dziko limeneli lilidi lapadera kwambiri ponena za ntchito ya kulalikira Ufumu. Zochitika zaposachedwa zikusonyeza mfundo imeneyi.
Kutumikira Kumene Kusoŵa Kuli Kokulira
Antonio ndi mkazi wake anapanga chosankha chovuta cha kusiya achibale awo ndi ntchito yotsimikizirika, ya malipiro abwino ku São Paulo kukatumikira kumene kusoŵa kwa olengeza Ufumu kunali kokulira m’boma la Minas Gerais. Gawo lawo linaphatikizapo mudzi wa antchito apamalo opangira shuga. Tsiku loyamba limene anachitira umboni kumeneko, anayambitsa maphunziro a Baibulo asanu ndi anayi. M’miyezi 18, anali kuchititsa maphunziro oposa 40!
Poyamba, misonkhano inali kuchitidwa pamalo opangira shuga pomwepo. Komabe, ofalitsa atsopanowo anafuna kuona Nyumba Yaufumu yeniyeni. Chotero, anahaya basi yonyamula anthu 75 kumka nawo kumpingo wapafupi. Ndiyeno msonkhano wachigawo unafika; 45 a ophunzira Baibulo atsopanowo anafikapo ndipo anafunsidwa. Mwa ameneŵa, 15 anabatizidwa panthaŵiyo. Zoonadi, panali misozi yachisangalalo!
Mabasi a kampani imodzimodziyo anagwiritsiridwa ntchito pa maulendo ofananawo, ndipo akuluakulu ake anatsitsa mtengo wake. Poyamikira zimenezi, Antonio anapatsa mwini kampaniyo buku lothandizira kuphunzira Baibulo. Iye anavomereza kuyamba kuphunzira Baibulo usiku womwewo ndipo anabatizidwa patapita miyezi yoŵerengeka ya kuphunzira kosamalitsa. Poyamba, mkazi wake anali kutsutsa phunzirolo, koma m’kupita kwa nthaŵi, mkhalidwe wake unasintha. Lerolino nayenso ndi Mboni ya Yehova yobatizidwa.
Mu February 1992 mpingo wokhala ndi ofalitsa okangalika 22 unapangidwa. Podzafika mu 1994 chiŵerengero chimenechi chinawonjezereka kufika pa 42, ndi apainiya 4 okhazikika, kapena alaliki anthaŵi yonse a uthenga wabwino. Chotero, Antonio anati: “Ine ndi mkazi wanga taona kuti ngati ‘tiyesa Yehova,’ monga momwe Malaki 3:10 amanenera, ‘adzatitsanulira mdalitso wakuti adzasoŵeka malo a kuulandirira.’”
Kugaŵira Mabuku Ofotokoza Baibulo
Mwinamwake chifukwa china chimene ntchito yolalikira ikupitira patsogolo kwambiri motero ku Brazil nchakuti Mboni zimagaŵira mabuku ofotokoza Baibulo pa mpata uliwonse. Mwachitsanzo, mpingo wina unalembera ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ukumapempha makope 250 a buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Nchifukwa ninji anapempha oda yaikulu chotero?
Kalatayo inafotokoza kuti: ‘Sukulu ina m’tauni yasankha kugwiritsira ntchito bukuli kukhala lophunzitsira m’kalasi lina. Chosankha cha akuluakulu a sukuluyo chachitika chifukwa cha umboni wamwamwaŵi umene wachitidwa ndi makolo a ophunzira amene ali Mboni za Yehova ndiponso ndi mmodzi wa oyang’anira sukuluyo. Yehova apitirizetu kudalitsa atumiki ake pamene akupereka malangizo abwino ndi bukuli.’ Inde, ndipo Yehova apitirizetu kudalitsa kupita patsogolo kwabwinoko kwa ntchito yolalikira Ufumu m’dziko limeneli lalikulu la Brazil.
[Bokosi patsamba 8]
ZIŴERENGERO Za Dzikolo
Chaka Chautumiki cha 1994
CHIŴERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OCHITIRA UMBONI: 385,099
KUGAŴA: Mboni 1 pa anthu 404
OFIKA PACHIKUMBUTSO: 1,018,210
AVAREJI YA OFALITSA AUPAINIYA: 38,348
AVAREJI YA MAPHUNZIRO A BAIBULO: 461,343
CHIŴERENGERO CHA OBATIZIDWA: 24,634
CHIŴERENGERO CHA MIPINGO: 5,928
OFESI YA NTHAMBI: CESÁRIO LANGE
[Chithunzi patsamba 9]
Galimoto ya chiŵiya chokuza mawu mu São Paulo cha m’ma 1940
[Chithunzi patsamba 9]
Kuchitira umboni mu Botanical Garden ku Rio de Janeiro
[Chithunzi patsamba 9]
Ofesi ya nthambi mu Cesário Lange