Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 7/15 tsamba 10-15
  • Malo Olemekezeka a Akazi Pakati pa Atumiki A Mulungu Oyambirira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malo Olemekezeka a Akazi Pakati pa Atumiki A Mulungu Oyambirira
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Womthangatira” ndi “Womkwaniritsa”
  • Kuzindikira Miyambo ya m’Nthaŵi za Baibulo
  • Malo Olemekezeka
  • Akazi Amene Anayanjidwa Mwapadera ndi Mulungu
  • Kodi Mulungu Amaona Kuti Akazi Ndi Otsika?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Mbali ya Mkazi m’Malemba
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Akazi Amathandiza Pokwaniritsa Cholinga cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kodi Mulungu ndi Khristu Amaona Akazi Motani?
    Galamukani!—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 7/15 tsamba 10-15

Malo Olemekezeka a Akazi Pakati pa Atumiki A Mulungu Oyambirira

“Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye [monga womkwaniritsa, NW].”​—GENESIS 2:18.

1. Kodi dikishonale ya Baibulo imafotokoza motani ponena za malo a akazi m’nthaŵi zakale?

“PALIBE malo alionse a Mediterranean wakale kapena a Near East kumene akazi anapatsidwa ufulu umene ali nawo m’chitaganya chamakono cha Kumadzulo. Mkhalidwe wofala unali wakuti akazi anamvera amuna, monga momwe akapolo anamvera mfulu, ndi monga momwe achichepere anamvera achikulire. . . . Ana aamuna anali kuŵerengeredwa kwambiri kuposa ana aakazi, ndipo makanda aakazi nthaŵi zina anali kusiyidwa kuti adzifere.” Umo ndimo mmene dikishonale ina ya Baibulo imafotokozera mkhalidwe wa akazi m’nthaŵi zakale.

2, 3. (a) Malinga ndi kunena kwa lipoti lina, kodi pali mkhalidwe wotani kwa akazi ambiri lerolino? (b) Kodi ndi mafunso otani amene akudzutsidwa?

2 Mkhalidwewo uli woipabe ku mbali zambiri za dziko lerolino. Mu 1994, kwa nthaŵi yoyamba, lipoti la pachaka la zoyenera za munthu la State Department ya United States linasonyeza zimene akazi akuchitiridwa. “Malipoti a ku Maiko 193 Akusonyeza Kuti Tsankho la Tsiku ndi Tsiku Lilipodi,” unatero mutu wina wa nkhani ya New York Times ponena za lipotilo.

3 Popeza kuti m’mipingo ya anthu a Yehova padziko lonse muli akazi ambiri a m’mafuko osiyanasiyana, pakubuka mafunso ena: Kodi mkhalidwe umene wangolongosoledwa kumenewu ndiwo umene Mulungu analinganiza poyamba kaamba ka akazi? Kodi akazi anachitiridwa motani pakati pa olambira Yehova a m’nthaŵi za Baibulo? Ndipo kodi ndimotani mmene akazi ayenera kuchitiridwa lerolino?

“Womthangatira” ndi “Womkwaniritsa”

4. Kodi Yehova analankhula mawu otani munthu woyamba atakhala m’munda wa Edene yekha kwa nthaŵi ina, ndiyeno Mulungu anachitanji?

4 Adamu atakhala m’munda wa Edene ali yekha kwa nthaŵi ina yake, Yehova anati: “Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye [monga womkwaniritsa, NW].” (Genesis 2:18) Ngakhale kuti Adamu anali mwamuna wangwiro, panafunikira kanthu kenanso kuti achite chifuno cha Mlengi. Kuti kanthuko kakhalepo, Yehova analenga mkazi ndi kuchititsa ukwati woyamba.​—Genesis 2:21-24.

5. (a) Kodi nauni Yachihebri yotembenuzidwa kuti “womthangatira” kaŵirikaŵiri yagwiritsiridwa ntchito motani ndi olemba Baibulo? (b) Kodi nchiyani chimene chikusonyezedwa ndi kutchula kwenikweniko kwa Yehova mkazi woyamba kukhala “womkwaniritsa”?

5 Kodi mawu akuti “womthangatira” ndi “womkwaniritsa” amasonyeza kuti malo a mkazi opatsidwa ndi Mulungu anali apansi? Kutalitali. Kaŵirikaŵiri olemba Baibulo ponena za Mulungu amagwiritsira ntchito nauni Yachihebri (ʽeʹzer) yotembenuzidwa kuti “womthangatira.” Mwachitsanzo, Yehova amakhaladi “thandizo lathu ndi chikopa chathu.” (Salmo 33:20; Eksodo 18:4; Deuteronomo 33:7) Pa Hoseya 13:9, Yehova amatchuladi za iye mwini kukhala “chithandizo” cha Israyeli. Ponena za liwu Lachihebri lakuti (neʹghedh) lotembenuzidwa kuti “womkwaniritsa,” katswiri wina wa Baibulo akufotokoza kuti: “Thangato lofunikalo si la kungothandiza pantchito yake ya tsiku ndi tsiku kapena pa kubala ana . . . koma kuchirikizana kumene ubwenzi umatheketsa.”

6. Kodi nchiyani chimene chinanenedwa mkazi atalengedwa, ndipo chifukwa ninji?

6 Chotero palibe kanthu kalikonse kochepetsa munthuyo pa zimene Yehova anatchula ponena za mkazi kukhala “womthangatira” ndi “womkwaniritsa.” Mkazi anali ndi mpangidwe wakewake wa maganizo, mtima, ndi thupi. Iye anali mnzake woyenera womkwaniritsa. Aliyense anali wosiyana, komabe wofunika pa ‘kudzaza dziko lapansi’ mogwirizana ndi chifuno cha Mlengi. Mwachionekere panali pambuyo pa kulenga mwamuna ndi mkazi pamene “anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.”​—Genesis 1:28, 31.

7, 8. (a) Uchimo utaloŵa mu Edene, kodi malo a mkazi anayambukiridwa motani? (b) Kodi ndi mafunso otani amene akudzutsidwa ponena za kukwaniritsidwa kwa Genesis 3:16 pakati pa olambira Yehova?

7 Uchimo utaloŵa, zinthu zinasintha kwa mwamuna ndi mkazi. Yehova anapereka chilango pa aŵiri onsewo monga ochimwa. “Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako,” Yehova anauza Hava, polankhula za mkhalidwe umene amalola monga ngati kuti iyeyo ndiye anauchititsa. Anawonjezera kuti: “Udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.” (Genesis 3:16) Kuyambira pamenepo, akazi ambiri alamuliridwa, kaŵirikaŵiri, mwankhanza ndi amuna awo. M’malo mwa kuŵerengeredwa kukhala othangata ndi okwaniritsa, kaŵirikaŵiri achitiridwa monga antchito kapena akapolo.

8 Komabe, kodi kukwaniritsidwa kwa Genesis 3:16 kunatanthauzanji kwa olambira Yehova achikazi? Kodi iwo anapatsidwa malo otsika ndi onyazitsa? Kutalitali! Komano bwanji nanga za nkhani za m’Baibulo zimene zimatiuza za miyambo ndi machitachita okhudza akazi amene angaonedwe kukhala osavomerezedwa pakati pa anthu ena lerolino?

Kuzindikira Miyambo ya m’Nthaŵi za Baibulo

9. Pamene tilingalira za miyambo yokhudza akazi m’nthaŵi za Baibulo, kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene tiyenera kukumbukira?

9 Akazi anachitiridwa moyenera pakati pa atumiki a Mulungu m’nthaŵi za Baibulo. Zoonadi, polingalira za miyambo yokhudza akazi m’masiku amenewo, nkothandiza kukumbukira zinthu zingapo. Choyamba, pamene Baibulo limasimba za mikhalidwe yoipa imene inakhalapo chifukwa cha kulamulira kwadyera kwa amuna oipa, zimenezo sizimatanthauza kuti Mulungu anavomereza machitidwe otero kwa akazi. Chachiŵiri, ngakhale kuti Yehova analekerera miyambo ina pakati pa atumiki ake kwa nthaŵi ina yake, iye anayang’anira miyamboyo kuti atetezere akazi. Chachitatu, tiyenera kusamala poyerekezera miyambo yakale ndi miyezo yamakomo. Miyambo ina imene ingaoneke kukhala yoipa kwa anthu amene aliko lerolino kwenikweni sinaonedwe ndi akazi apanthaŵiyo kukhala yowachepetsa. Tiyeni tilingalire za zitsanzo zina.

10. Kodi Yehova anaona motani mchitidwe wa mitala, ndipo kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti sanasiye muyezo wake woyamba wa kukwatira mkazi mmodzi?

10 Mitala: Malinga ndi chifuno cha Yehova choyamba, mkazi wokwatiwa sanayenere kukhala ndi mkazi wina wokwatiwanso kwa mwamuna wake. Mulungu analengera Adamu mkazi mmodzi yekha. (Genesis 2:21, 22) Chipanduko chitachitika m’Edene, mchitidwe wa mitala unaonekera choyamba mu mzera wa Kaini. Pambuyo pake unakhala mwambo ndipo olambira Yehova ena anautengera. (Genesis 4:19; 16:1-3; 29:21-28) Ngakhale kuti Yehova analola mitala ndipo inachititsa kuchuluka kwa anthu a Israyeli, iye analingalira za akazi mwa kuyang’anira mchitidwewo kotero kuti akazi ndi ana awo atetezeredwe. (Eksodo 21:10, 11; Deuteronomo 21:15-17) Ndiponso, Yehova sanasiye muyezo wake woyamba wa kukwatira mkazi mmodzi yekha. Nowa ndi ana ake aamuna onse, kwa amene lamulo la ‘kuchuluka ndi kudzaza dziko lapansi’ linabwerezedwako, onse anali ndi mkazi wakewake mmodzi. (Genesis 7:7; 9:1; 2 Petro 2:5) Mulungu anadzisonyeza kukhala mwamuna wa mkazi mmodzi posonyeza mophiphiritsa unansi wake ndi Israyeli. (Yesaya 54:1, 5) Ndiyenso, muyezo woyamba wa Mulungu wa kukwatira mkazi mmodzi unakhazikitsidwanso ndi Yesu Kristu ndipo unatsatiridwa ndi mpingo woyambirira Wachikristu.​—Mateyu 19:4-8; 1 Timoteo 3:2, 12.

11. Kodi nchifukwa ninji malowolo analipiridwa m’nthaŵi za Baibulo, ndipo kodi zimenezi zinali zochepetsa akazi?

11 Kulipira malowolo: Bukulo lakuti Ancient Israel​—Its Life and Institutions likunena kuti: “Chofunika chimenechi cha kulipira ndalama zakutizakuti, kapena kanthu kena kolingana ndi mtengowo, ku banja la msungwana mwachionekere chimachititsa ukwati Wachiisrayeli kuoneka ngati kuti uli wochita kugula. Koma [malowolo] amenewo akuchita ngati kuti sanali kwenikweni mtengo wolipirira mkazi monga cholipira ku banjalo.” (Kanyenye ngwathu.) Chotero kulipirira malowolo kunali kubwezera banja la mkaziyo mautumiki ake amene iwo anatayikiridwa ndiponso zoyesayesa za banja lake ndi ndalama zimene linawononga pomsamalira. Pamenepo, m’malo mwa kuchepetsa mkazi, anasonyeza kuŵerengeredwa kwake m’banja lake.​—Genesis 34:11, 12; Eksodo 22:16; onani Nsanja ya Olonda, ya January 15, 1989, masamba 21-4.

12. (a) Kodi amuna ndi akazi a mu ukwati nthaŵi zina anatchedwa motani m’Malemba, ndipo kodi maina ameneŵa anali oipa kwa akazi? (b) Kodi nchiyani chimene chili chofunika kudziŵidwa ponena za mawu amene Yehova anagwiritsira ntchito mu Edene? (Onani mawu amtsinde.)

12 Amuna monga ‘eni’: Chochitika china m’moyo wa Abrahamu ndi Sara pafupifupi 1918 B.C.E. chimasonyeza kuti mwachionekere panthaŵi yawoyo unali mwambo wachionekere kuona mwamuna wokwatira monga “mwini” (Chihebri, baʹʽal) ndipo mkazi wokwatiwa monga ‘wa mwini’ (Chihebri beʽu·lahʹ). (Genesis 20:3) Mawu ameneŵa akugwiritsiridwa ntchito nthaŵi zina m’Malemba, ndipo palibe chisonyezero chakuti akazi okhalako Chikristu chisanadze anawalingalira kukhala oipa.a (Deuteronomo 22:22) Komabe, akazi sanayenera kuchitiridwa ngati katundu. Katundu kapena chuma zikhoza kugulidwa, kugulitsidwa, ndipo ngakhale kukhala choloŵa, koma zimenezi sizinali choncho ndi mkazi. “Nyumba ndi chuma ndizo choloŵa cha atate,” umatero mwambi wa Baibulo, “koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.”​—Miyambo 19:14; Deuteronomo 21:14.

Malo Olemekezeka

13. Pamene amuna owopa Mulungu anatsatira chitsanzo cha Yehova ndi kumvera Chilamulo chake, kodi chinachitika nchiyani kwa akazi?

13 Nangano, malo a akazi anali otani pakati pa atumiki a Mulungu m’nthaŵiyo Chikristu chisanadze? Kodi anaonedwa ndi kuchitiridwa motani? Kuti tinene mosavuta, pamene amuna owopa Mulungu anatsatira chitsanzo cha Yehova mwiniyo ndi kumvera Chilamulo chake, akazi anakhalabe ndi ulemu wawo ndi kukhala ndi zoyenera zambiri ndi mathayo.

14, 15. Kodi ndi zisonyezero zotani zimene zilipo zakuti akazi anachitiridwa ulemu mu Israyeli, ndipo nchifukwa ninji Yehova anali ndi chifukwa chabwino choyembekezerera olambira ake achimuna kuwachitira ulemu?

14 Akazi anayenera kulemekezedwa. Chilamulo cha Mulungu kwa Israyeli chinalamula kuti atate ndi amayi omwe ayenera kulemekezedwa. (Eksodo 20:12; 21:15, 17) “Aliyense awope mayi wake, ndi atate wake,” amatero Levitiko 19:3. Pamene Batiseba anafikira mwana wake Solomo panthaŵi ina, “mfumu inanyamuka kukomana naye, namuŵeramira” mwaulemu. (1 Mafumu 2:19) Encyclopaedia Judaica ikuti: “Kuyerekezera kwa ulosi kwa chikondi cha Mulungu kwa Israyeli ndi chikondi cha mwamuna kwa mkazi wake kungakhale kutachitidwa kokha m’chitaganya chimene akazi anali kulemekezedwa.”

15 Yehova amayembekezera olambira ake achimuna kuchitira ulemu akazi, pakuti iye amawachitira ulemu. Zimenezi zikusonyezedwa m’malemba amene Yehova akugwiritsira ntchito zochitika za akazi mwafanizo ndi kuyerekezera malingaliro a iye mwini ndi aja a akazi. (Yesaya 42:14; 49:15; 66:13) Zimenezi zimathandiza oŵerenga kumvetsa mmene Yehova amamvera. Mokondweretsa, liwu Lachihebri la “chifundo,” kapena “chisoni,” limene Yehova amagwiritsira ntchito kwa iye mwini, nlogwirizana kwambiri ndi liwu la “mimba” ndipo lingafotokozedwe kukhala “kumva kwa nakubala.”​—Eksodo 33:19; Yesaya 54:7.

16. Kodi ndi zitsanzo zotani zimene zikusonyeza kuti chilangizo cha akazi owopa Mulungu chinaŵerengeredwa?

16 Chilangizo cha akazi owopa Mulungu chinaŵerengeredwa. Pamene nthaŵi ina Abrahamu woopa Mulungu anazengereza kuchitapo kanthu pa chilangizo cha mkazi wake Sara, woopa Mulunguyo, Yehova anamuuza kuti: “Umvere iwe mawu ake.” (Genesis 21:10-12) Akazi Achihiti a Esau “anapweteka mtima wa Isake ndi wa Rebeka.” Pambuyo pake, Rebeka anasonyeza nsautso imene adzakhala nayo ngati mwana wawo Yakobo akakwatira Mhiti. Kodi Isake anachita motani? “Ndipo,” nkhaniyo imatero, “Isake anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani.” Inde, ngakhale kuti Rebeka sanapereka mwachindunji chilangizo, mwamuna wake anapanga chosankha chimene sichinanyalanyaze malingaliro ake. (Genesis 26:34, 35; 27:46; 28:1) Pambuyo pake Mfumu Davide anapeŵa liwongo la mwazi chifukwa chakuti anamvetsera pempho la Abigayeli.​—1 Samueli 25:32-35.

17. Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti akazi anali ndi ulamuliro wina m’banja?

17 Akazi anali ndi ulamuliro wina m’banja. Ana analimbikitsidwa kuti: “Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amako.” (Miyambo 1:8) Mafotokozedwe a “mkazi wangwiro” mu Miyambo chaputala 31 amasonyeza kuti mkazi wokwatiwa wokangalika pantchito sanangosamalira za m’banja mwake zokha komanso anachita malonda a kugulitsa malo, analima munda wopatsa, anali ndi bizinesi yaing’ono, ndipo anali wodziŵika chifukwa cha mawu ake anzeru. Chinthu chofunika koposa chinali kuwopa Yehova kwaulemu kwa mkaziyo koyamikiridwa. Mposadabwitsa kuti mtengo wa mkazi wotero ‘unaposa wa ngale’! Ngale zofiira zinaonedwa kukhala zamtengo wapatali kaamba ka majuwelo ndi zokongoletsera zina.​—Miyambo 31:10-31.

Akazi Amene Anayanjidwa Mwapadera ndi Mulungu

18. Kodi akazi ena m’nthaŵi za Baibulo anasonyezedwa chiyanjo motani m’njira yapadera?

18 Kuŵerengera akazi kwa Yehova kunasonyezedwa m’chiyanjo chapadera chimene anasonyeza kwa ena a iwo m’nthaŵi za Baibulo. Hagara, Sara, ndi mkazi wa Manowa anafikiridwa ndi angelo amene anapereka malangizo a Mulungu kwa iwo. (Genesis 16:7-12; 18:9-15; Oweruza 13:2-5) Panali “akazi otumikira” pa chihema ndi akazi oimba m’bwalo la Solomo.​—Eksodo 38:8; 1 Samueli 2:22; Mlaliki 2:8.

19. Kodi Yehova anagwiritsira ntchito akazi kumuimira m’njira yotani panthaŵi ina?

19 Nthaŵi zingapo m’mbiri ya Israyeli, Yehova anagwiritsira ntchito mkazi kumuimira kapena kumlankhulira. Ponena za mneneri wamkaziyo Debora, timaŵerenga kuti: “Ana a Israyeli anakwera kwa iye awaweruze.” (Oweruza 4:5) Israyeli atagonjetsa mfumu ya Akanani Yabini, Debora anali ndi thayo lapaderadi. Mwachionekere ndiye amene anapeka mbali ina ya nyimbo ya chilakiko imene potsirizira pake inakhala mbali ya cholembedwa cha Yehova chouziridwa.b (Oweruza, chaputala 5) Zaka mazana angapo pambuyo pake, pofunsira kwa Yehova, Mfumu Yosiya inatumiza nthumwi zimene zinaphatikizapo mkulu wa ansembe kwa mneneri wamkazi Hulida. Hulida anayankha mwaulamuliro kuti: “Atero Yehova Mulungu wa Israyeli.” (2 Mafumu 22:11-15) Pa chochitika chimenecho mfumu inalamula nthumwi kumka kwa mneneri wamkazi, koma chimenechi chinachitidwa kuti akalandire chitsogozo chochokera kwa Yehova.​—Yerekezerani ndi Malaki 2:7.

20. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza nkhaŵa ya Yehova pa malingaliro ndi ubwino wa akazi?

20 Nkhaŵa ya Yehova kaamba ka ubwino wa akazi ili yooneka mu zochitika zimene anachitapo kanthu kaamba ka olambira ake ena achikazi. Iye anatetezera kaŵiri mkazi wa Abrahamu wokongola, Sara, kuti asaipitsidwe. (Genesis 12:14-20; 20:1-7) Mulungu anasonyeza chiyanjo kwa mkazi wosakondedwa kwambiri wa Yakobo, Leya, mwa ‘kutsegula m’mimba mwake’ kotero kuti anabala mwana wamwamuna. (Genesis 29:31, 32) Pamene anamwino aŵiri Achiisrayeli owopa Mulungu anaika miyoyo yawo pachiswe kuti apulumutse makanda achimuna Achihebri pa kuphedwa ku Igupto, Yehova moyamikira “anawamangitsira mabanja.” (Eksodo 1:17, 20, 21) Iye anayankhanso pemphero laphamphu la Hana. (1 Samueli 1:10, 20) Ndipo pamene mkazi wamasiye wa mneneri wina anayang’anizana ndi womkongoza amene anali wokonzekera kutenga ana ake kulipirira ngongoleyo, Yehova sanamtaye. Mwachikondi, Mulungu anakhozetsa mneneri Elisa kuchulukitsa mafuta a mkaziyo kotero kuti akalipirire ngongoleyo. Motero anapulumutsa banja lake ndi ulemu wake.​—Eksodo 22:22, 23; 2 Mafumu 4:1-7.

21. Kodi Malemba Achihebri amasonyeza chithunzi choyenera chotani ponena za malo a akazi?

21 Motero, m’malo mwa kulimbikitsa lingaliro lonyoza akazi, Malemba Achihebri amasonyeza chithunzi choyenera cha malo awo pakati pa atumiki a Mulungu. Ngakhale kuti Yehova sanatetezere olambira ake achikazi pa kukwaniritsidwa kwa Genesis 3:16, akazi anachitiridwa mwaulemu ndi amuna aumulungu amene anatsatira chitsanzo cha Yehova ndi kulabadira Chilamulo chake.

22. Podzafika nthaŵi imene Yesu anali pa dziko lapansi, kodi malo a akazi anasintha motani, ndipo ndi mafunso otani amene akufunsidwa?

22 M’zaka mazana ambiri pambuyo pa kumalizidwa kwa Malemba Achihebri, malo a akazi anasintha pakati pa Ayuda. Pamene Yesu anaonekera pa dziko lapansi, miyambo yachirabi inali yoletsa kwambiri akazi pamathayo awo achipembedzo ndi a m’chitaganya. Kodi miyambo imeneyo inayambukira khalidwe la Yesu pochita ndi akazi? Kodi akazi Achikristu ayenera kuchitiridwa motani lerolino? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a M’Malemba Achihebri monse, amuna ndi akazi a mu ukwati kaŵirikaŵiri amatchedwa monga “mwamuna” (Chihebri, ʼish) ndi “mkazi” (Chihebri, ʼish·shahʹ). Mwachitsanzo, mu Edene, mawu amene Yehova anagwiritsira ntchito anali, osati “mwini” ndi ‘wa mwini,’ koma “mwamuna” ndi “mkazi.” (Genesis 2:24; 3:16, 17) Ulosi wa Hoseya unaneneratu kuti atabwerako ku ukapolo, Israyeli molapa akatcha Yehova kuti “Mwamuna wanga,” ndipo osatinso ‘mwini wake wa ine.’ Zimene zikupereka lingaliro lakuti liwulo “mwamuna” linali lopereka lingaliro lachikondi kwambiri kuposa lakuti “mwini.”​—Hoseya 2:16.

b Chapadera ndicho kudzitchula kwa Debora iye mwini mu nkhaniyo pa Oweruza 5:7.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi mawu akuti “womthangatira” ndi “womkwaniritsa” amasonyezanji ponena za malo a mkazi opatsidwa ndi Mulungu?

◻ Polingalira za miyambo yokhudza akazi m’nthaŵi za Baibulo, kodi tiyenera kukumbukiranji?

◻ Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti akazi anali ndi malo olemekezeka pakati pa atumiki a Mulungu a m’nthaŵi zakale?

◻ Kodi Yehova anasonyeza motani chiyanjo chapadera kwa akazi okhalako Chikristu chisanadze?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena