Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 8/1 tsamba 3-4
  • Nthaŵi Zasintha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nthaŵi Zasintha
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Solomo Anali Mfumu Yanzeru
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Kodi Solomo Ndi Chitsanzo Chabwino Kapena Choipa?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Akapolo a Umphaŵi
    Galamukani!—1998
  • Zimene Ena Achita Pofuna Kuthetsa Umphawi
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 8/1 tsamba 3-4

Nthaŵi Zasintha

HA, Kuyenera kuti kunali kosangalatsa chotani nanga kukhala mu ufumu waulemerero wa Israyeli wakale wolamuliridwa ndi Mfumu Solomo wokhulupirikayo! Inali nyengo ya mtendere, ulemerero, ndi chimwemwe. Panthaŵi imene Solomo anachirikiza mokhulupirika kulambira koona, Yehova anadalitsa mtunduwo molemerera. Kwa Mfumu Solomo, Mulungu anapereka osati chuma chokha komanso “mtima wanzeru ndi wakuzindikira” kotero kuti Solomo alamulire mwa chilungamo ndi chikondi. (1 Mafumu 3:12) Baibulo limati: “Mafumu onse a pa dziko lapansi anafuna nkhope ya Solomo, kudzamva nzeru zake Mulungu adazilonga m’mtima mwake.”​—2 Mbiri 9:23.

Kwa anthu, Yehova anapereka chisungiko, mtendere, ndi zinthu zabwino zochuluka. Mawu a Mulungu amati: “Ayuda ndi Aisrayeli anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namwa namakondwera.” Ponse paŵiri, m’lingaliro lenileni ndi mophiphiritsira, anthuwo “anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake . . . masiku onse a Solomo.”​—1 Mafumu 4:20, 25.

Nthaŵi zasintha. Moyo lerolino ngwosiyana kwambiri ndi masiku abwino akalewo. Mosiyana ndi nthaŵi ya Solomo, vuto lalikulu la lerolino ndilo umphaŵi. Ngakhale m’maiko olemera, umphaŵi ulimonso. Mwachitsanzo, mu United States ndi European Union yemwe, pafupifupi 15 peresenti ya anthu akukhala mu umphaŵi, ikutero United Nations Development Program.

Ponena za chithunzi cha dziko lonse, The State of the World’s Children 1994, lipoti lolembedwa ndi UNICEF (United Nations Children’s Fund), likunena kuti munthu mmodzi pa asanu alionse padziko lonse akukhala mu umphaŵi weniweni, likumawonjezera kuti moyo kwa amphaŵi ambiri pa dziko lonse ukukhala “wovutirapo nthaŵi zonse ndi wosoŵetsa chochita.”

M’maiko ena, kukwera mtengo kwa zinthu kukuwonjezera mavuto kwa amphaŵi. Mkazi wina mu Afirika anati: “Ukhoza kuona chinthu chinachake pamsika, ndiyeno umati, ‘Chabwino, ndikatenge ndalama kunyumba kuti ndidzachigule.’ Pamene ubweranso pambuyo pa ola limodzi ungopeza akuuza kuti simungagule ndi ndalama imeneyo chifukwa mtengo wangowonjezedwa kumene. Kodi pamenepo munthu angatani? Nzogwiritsa mwala kwabasi.”

Mkazi wina kumeneko anati: ‘Kuti tikhalitse ndi moyo, timaiŵala za zofunika zina. Nkhaŵa yathu tsopano imangokhala ya mmene tingapezere chakudya.’

Malinga ndi kunena kwa United Nations, kutsogolo kukuoneka kwamdima. Mwachitsanzo, UNICEF ikuyerekezera kuti ngati kuchuluka kwa anthu kumene kulipoku kupitiriza kuwonjezeka, chiŵerengero cha anthu osauka chidzawonjezeka kanayi “pautali wa moyo wa munthu mmodzi.”

Komabe, ngakhale kuti mikhalidwe ya zachuma ndi ya kakhalidwe ikuipiraipira, atumiki a Mulungu ali ndi chifukwa chokhalira achidaliro. Ngakhale kuti atumiki a Mulungu akukhala pakati pa awo amene amaona kuti mtsogolo muli zoipa zowonjezereka, iwo akuyang’ana kutsogolo ndi chisangalalo ndi chidaliro. Nkhani yotsatira idzafotokoza zifukwa zake.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

De Grunne/​Sipa Press

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena