Kodi Kukayikira za Yesu Kuli Koyenera?
KODI Yesu wa ku Nazarete anachitadi zozizwitsa? Kodi anaukadi kwa akufa, monga momwe ophunzira ake ananenera? Kodi iye analikodi? M’nyengo yathu yamakono ino, ambiri amakhala osakhoza kuyankha motsimikizira mafunso otero. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti amakayikira za Yesu, ndipo kukayikira ndiko kusatsimikizira, kusadziŵa kaya ngati kanthu kena kali koona kapena kotheka. Koma kodi kukayikira za Yesu nkoyenera? Tiyeni tione.
Mmene Kukayikira za Yesu Kunafesedwera
Akatswiri azaumulungu ena Achijeremani a kumapeto kwa zaka za zana la 19 ndi kuchiyambiyambi kwa zaka za zana la 20 anasonyeza Yesu kukhala “munthu wopekedwa wa Tchalitchi chakale.” Kukana kwawo mbiri ya Yesu kunayambitsa mkangano pakati pa akatswiri kuchiyambiyambi kwa zaka za zana lino umene unayambukira anthu panthaŵiyo ndipo ukali kuwayambukira lerolino. Mwachitsanzo, kufufuza kwaposachedwapa kochitidwa ku Germany kunasonyeza kuti 3 peresenti ya awo amene anafunsidwa amakhulupirira kuti Yesu “sanakhaleko” ndi kuti “atumwi anangopeka za iye.” Inde, mbewu za kukayikira za Yesu zimene zinafesedwa kuchiyambiyambi kwa zaka za zana lino zapeza nthaka yachonde m’mitima ya anthu ngakhale tsopano lino.
Kodi nchifukwa ninji kunena kuti Yesu anali ‘wopekedwa’ kuli kosayenera? Katswiri wa Baibulo Wolfgang Trilling akunena kuti: “Mkangano wonena za kuti kaya Yesu anakhalako, mwa mawu ena kaya ngati anali munthu wa m’mbiri kapena wa m’nthano, unatha. Nkhaniyo inathetsedwa m’njira yaukatswiri, kwakuti ngakhale anthu oganiza kwambiri samaonanso vutolo kukhala nkhani ya zamaphunziro.” Komabe, ena amakayikirabe za kukhalapo kwa Yesu. Motero, tiyeni tipende za mmene munthu angatsimikizirire kukhalako kwa Yesu m’mbiri ndiponso ndi kuthetsa zikayikiro zonse ponena za iye.
Maumboni Amene Amathetsa Zikayikiro
Kuphedwa kochititsa manyazi kwa Yesu monga mpandu wonyansa kumapereka “chigomeko chokhutiritsa koposa kwa otsutsa kukhalako kwa Yesu m’mbiri,” akutero Trilling. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kuphedwako “kunapinga, kapena kudodometsa, kuwanditsidwa kwa chikhulupiriro chatsopano pakati pa Ayuda ndi osakhala Ayuda.” (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 1:23.) Ngati kuphedwa kwa Yesu Mesiyayo kunali chokhumudwitsa kwa Ayuda ndi Akunja omwe, sikunali konse kopekedwa ndi atumwi! Ndiponso, imfa ya Yesu yachitiridwa umboni monga chochitika cha m’mbiri osati m’Mauthenga Abwino anayi okha komanso ndi wolemba mbiri Wachiroma Tacitus ndi Talmud Yachiyuda.a
Zochitika zina m’moyo wa Yesu zimalingaliridwanso monga umboni wa mkati mwa Mauthenga Abwino wa kukhulupirika kwawo, ndipo motero wa zimene amatiuza ponena za iye. Mwachitsanzo, kodi otsatira a Yesu akanapeka nkhani ya kufika kwake kuchokera ku Nazarete, malo amene mwachionekere anali osaŵerengeredwa? Kapena kodi nkotheka kuti iwo akanapeka kuperekedwa kwake ndi Yudase, bwenzi lake lolidalira? Kodi kukuonekera kukhala kwanzeru kuganiza kuti akanapeka nkhani yonena za kusiyidwa kwa Yesu ndi ophunzira ake onse mwamantha chotero? Kulidi kupanda nzeru kuganiza kuti ophunzirawo akanapeka maumboni amene anali ovulaza kwambiri ndi kuwalengeza konsekonse! Ndiponso, luso la kuphunzitsa limene Yesu anagwiritsira ntchito linali lapadera. Mabuku Achiyuda a m’zaka za zana loyamba alibe mafanizo ofanana ndi ake. Kodi ndi munthu wosadziŵika wotani amene ‘akanapeka’ chinthu chotero chonga Ulaliki wa pa Phiri wochititsa chidwi? Zigomeko zimenezi zimangochirikiza kudalirika kwa Mauthenga Abwino monga nkhani za moyo wa Yesu.
Palinso umboni wakunja wa kukhalako kwa Yesu m’mbiri. Mauthenga Abwino anayi amasonyeza za malo kumene anakhala, ndi maumboni olondola ndi mbiri yake. Malo, onga Betelehemu ndi Galileya; anthu ndi magulu otchuka, onga Pontiyo Pilato ndi Afarisi; ndiponso miyambo ya Ayuda ndi zinthu zina zapadera sizinangopekedwa. Zinali mbali ya moyo wa m’zaka za zana loyamba, ndipo zatsimikiziridwa ndi maumboni ena osakhala a m’Baibulo ndi zopezedwa pofukula mabwinja.
Motero, pali umboni wokhutiritsa, wamkati ndi wakunja womwe, wakuti Yesu ndi munthu wa m’mbiri.
Komabe, anthu ochulukirapo ali ndi zikayikiro za mtundu wina. Zoonadi, malinga ndi kufufuza kogwidwa mawuko, ndi Ajeremani ochepa okha opita kutchalitchi amene amakhulupirira mwamphamvu kuti zozizwitsa za Yesu ndi chiukiriro chake “zinachitikadi.” Kodi kukayikira zozizwitsa za Yesu ndi chiukiriro nkoyenera?
Chifukwa Chake Ena Amakayikira Zozizwitsa za Yesu
Mateyu 9:18-36 amasimba kuti Yesu anachiritsa odwala mozizwitsa, anaukitsa akufa, ndipo anatulutsa ziŵanda. Profesa Hugo Staudinger, wolemba mbiri, akunena kuti: “Nzosakhulupirika nkomwe, ndipo malinga ndi mmene mbiri ilili nzosatheka, kunena kuti nkhani zachilendo zimenezi zangokhala zongoyerekezera.” Chifukwa ninji? Chifukwa zichita ngati kuti Mauthenga Abwino oyambirira analembedwa panthaŵiyo pamene mboni zochuluka za zozizwitsa zimenezi zinali ndi moyo! Umboni winanso umapezeka mu mfundo yakuti, monga momwe Staudinger akupitirizira kunena, adani ake Achiyuda “sanatsutse konse kuti Yesu anachita zozizwitsa zachilendo.” Titanyalanyaza maumboni ena onse, ndi kungoumirira pa umboni wakunja umenewu wokha, tidzapeza kuti kukhulupirira kwathu zozizwitsa za Yesu kuli koyenera.—2 Timoteo 3:16.
Ngakhale kuti “Ajeremani ochuluka amakhulupirira kuti Yesu anachiritsa odwala,” ambiri amakayikira mphamvu ya machiritso ameneŵa. Mwachitsanzo, katswiri wina wazaumulungu wotchuka Wachijeremani anafotokoza poyera kuti machiritso ochitidwa ndi Yesu anachitika chifukwa cha mphamvu ya kugonetsa munthu tulo yogwira ntchito pa anthu amene anali opsinjika maganizo. Kodi kumeneku ndi kufotokoza komveka?
Tangolingalirani. Marko 3:3-5 amasimba kuti Yesu anachiritsa munthu wa dzanja lopuwala. Koma kodi kupuwala dzanja kumachititsidwa ndi kupsinjika maganizo? Ndithudi ayi. Motero, kuchiritsa kumeneku sikunachitike ndi mphamvu ya kugonetsa munthu tulo. Nanga nchiyani chimene chinakhozetsa Yesu kuchita zozizwitsa? Profesa Staudinger akuvomereza kuti: “Ngati palibe malamulo amene ali otsimikizirika kwenikweni, ndipo ngati munthu sakana Mulungu kotheratu, pamenepotu munthu sangakane kuthekera kwakuti Mulungu, amene ali ndi mphamvu yoposa ya munthu, ngwokhoza kuchita zinthu zimene zili zachilendo.” Zoonadi, mwa thandizo la “mphamvu ya Mulungu,” Yesu anachiritsadi anthu amene anali kudwala. Motero palibe chifukwa chokayikirira kuona kwa zozizwitsa zake.—Luka 9:43, NW; Mateyu 12:28.
Monga momwe The American Peoples Encyclopedia ikunenera, ngati chozizwitsa chachikulu koposa—chiukiriro cha Yesu—chinachitika, ndiye kuti zozizwitsa zina zonse zosimbidwa m’Mauthenga Abwino “zili zotheka.” Kodi Yesu anaukadi kwa akufa?
Kodi Zikayikiro Zonena za Chiukiriro cha Yesu Nzoyenera?
Lingalirani choyamba umboni wamphamvu wa zochitika umene umachirikiza kuona kwa chiukiriro cha Yesu—manda ake apululu. Kupezedwa kwa manda a Yesu ali apululu kwenikweniko sikunatsutsidwe ndi anthu okhalapo panthaŵi yake, ngakhalenso ndi adani ake. (Mateyu 28:11-15) Chinyengo chikanadziŵidwa mosavuta! Buku la maumboni limene latchulidwalo limanena bwino kuti: “Palibe malongosoledwe omveka onena za manda apululuwo amene aperekedwa kusiyapo kunena kwa Baibulo kwakuti, ‘Iye mulibe muno iyayi; pakuti anauka’ (Mat. 28:6).”
Ena amatsutsa, akumati ophunzira a Yesu okha ndiwo amene analengeza ponseponse kuti iye anali Mesiya woukitsidwa. Zimenezi nzoona. Koma kodi kukhulupirika kwa uthenga wawo sikunali kozikidwa zolimba pa umboni wa mu mbiri, makamaka imfa ndi kuuka kwa Yesu? Indedi. Mtumwi Paulo anadziŵa za kugwirizana kumeneku pamene analemba kuti: “Ngati Kristu sanaukitsidwa kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chili chabe. Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; chifukwa tinachita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Kristu.”—1 Akorinto 15:14, 15; yerekezerani ndi Yohane 19:35; 21:24; Ahebri 2:3.
M’zaka za zana loyamba, munali anthu ambiri amene anali odziŵika bwino lomwe ndi amene anachitira umboni za kuonekera kwa Yesu imfa yake itachitika. Pakati pawo panali atumwi 12 ndi Paulo, ndiponso mboni zina 500 zoona ndi maso.b (1 Akorinto 15:6) Kumbukiraninso chifukwa chake Matiya anakwaniritsa ziyeneretso zoloŵera m’malo mwa mtumwi wosakhulupirikayo Yudase. Machitidwe 1:21-23 amasimba kuti Matiya anatha kuchitira umboni za kuuka kwa Yesu ndi zochitika zina zoyambirira zonena za Iye. Ngati moyo ndi chiukiriro cha Yesu zinali zopeka osati zenizeni, chofunika chimenecho choyeneretsa kuikidwa kwa munthu chikakhala chopanda pake.
Chifukwa chakuti mboni zambiri zoona ndi maso za m’zaka za zana loyamba zinachitira umboni za moyo, zozizwitsa, imfa, ndi kuuka kwa Yesu, Chikristu chinafalikira mofulumira mu Ufumu wonse wa Roma, ngakhale kuti panali zopinga zotchulidwazo. Otsatira ake anali okonzekera kulimbana ndi mavuto, chizunzo, ndipo ngakhale imfa kuti alengeze ponseponse chiukirirocho ndi choonadi chake chofunika. Choonadi chotani? Chakuti kuuka kwake kunatheka kokha chifukwa cha mphamvu ya Mulungu. Ndipo kodi nchifukwa ninji Yehova Mulungu anaukitsa Yesu kwa akufa? Yankho la funso limenelo limasonyeza kuti Yesu wa mu mbiriyo anali yani.
Patsiku la Pentekoste, mtumwi Petro analengeza momasuka kwa Ayuda odabwa mu Yerusalemu kuti: “Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse. Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la mzimu woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva. Pakuti Davide sanakwera kumwamba ayi; koma anena yekha, [Yehova, NW] anati kwa Mbuye wanga, Khalani ku dzanja lamanja langa, kufikira ndikaike adani ako chopondapo mapazi ako. Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israyeli, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munampachika.” (Machitidwe 2:32-36) Inde, Yehova Mulungu anayesa Yesu wa ku Nazarete “Ambuye ndi Kristu.” Kodi kukayikira za thayo lake pa mbali imeneyi ya chifuno cha Mulungu nkoyenera?
Kodi Nkukayikiriranji za Thayo Limene Yesu Ali Nalo Pakali Pano?
Kodi ndimotani mmene zikayikiro zonse zonena za amene Yesu ali ndi thayo lake zingathetsedwere? Chifukwa cha kukhala kwake mneneri woona kwenikweniko. Iye ananeneratu za nkhondo, njala, zivomezi, upandu, kusoŵeka kwa chikondi zimene timaona lerolino. Ndiponso, ananeneratu kuti: “Uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:3-14) Kukwaniritsidwa kwa maulosi ameneŵa kumasonyeza kuti Yesu ndiye Kristu woukitsidwa, wolamulira ‘pakati pa adani ake’ mosaoneka, ndipo posachedwa adzadzetsa dziko latsopano la Mulungu.—Salmo 110:1, 2; Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:1-5.
Tsopano kuposa ndi kale lonse, anthu mofulumira afunikira Mpulumutsi wokhala ndi nzeru zoposa za munthu. Kodi tingakayikirirenji kuti Yesu ndiye munthu amene wasankhidwa moyenera kupulumutsa anthu? Yohane, amene anali mboni yoona ndi maso ya zozizwitsa zake zochititsa chidwi ndi ya kuuka kwa Yesu, ananenetsa kuti: “Ndipo ife tapenyera, ndipo tichita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi.” (1 Yohane 4:14; yerekezerani ndi Yohane 4:42.) Popeza kuti tilibe maziko enieni okayikirira kukhalako kwa Yesu, zozizwitsa, imfa, ndi chiukiriro chake, tilibenso chifukwa chokayikirira kuikidwa kwake pa mpando wachifumu ndi Yehova Mulungu monga Mfumu yoyenera ku dzanja Lake lamanja. Mosakayikira, Yesu wa ku Nazarete ndiye Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndi “Mpulumutsi wa dziko lapansi.”—Mateyu 6:10.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu ochirikiza Yesu mu Talmud amavomerezedwa kukhala enieni ndi akatswiri ena chabe. Komanso, kutchula Yesu kwa Tacitus, Suetonius, Pliny the Younger, ndiponso mwapang’ono kwa Flavius Josephus, kumavomerezedwa ndi anthu ambiri kukhala umboni wa kukhalako kwa Yesu kwa m’mbiri.
b Panthaŵi ina, Yesu woukitsidwayo anadya nsomba ndi ophunzira ake, zimene zimasonyeza kuti kuonekera kwake sikunali masomphenya ayi, monga momwe ena amanenera lerolino.—Luka 24:36-43.