Munthu Wanjiru
CHINENERO Chachihebri chili ndi magwero amodzi okha a liwu la “nsanje.” Pofotokoza anthu ochimwa, liwulo Lachihebri lingatembenuzidwe kukhala “njiru” kapena “kupikisana.” (Genesis 26:14, NW; Mlaliki 4:4, NW) Komabe, chinenero Chachigiriki chili ndi mawu angapo a “nsanje.” Liwulo zeʹlos, monga liwu Lachihebri lolingana nalo, lingatanthauze nsanje yolungama ndi yoipa yomwe. Liwu lina Lachigiriki, phthoʹnos, limangotanthauza nsanje yoipa. New World Translation nthaŵi zonse imamasulira liwulo kukhala “njiru.”
Kodi liwulo phthoʹnos linagwira motani ntchito m’Chigiriki chakale? The Anchor Bible Dictionary imati: “Mosiyana ndi munthu waumbombo, munthu wa phthonos kwenikweni samafuna chuma chimene safuna kuti mnzake akhale nacho; iye samangofuna kuti mnzake akhale nacho. Amasiyana ndi munthu wampikisano pakuti cholinga chake, chosiyana ndi chija cha munthu wampikisano, sindicho kupambana koma kulepheretsa anzake kupambana.”
Kaŵirikaŵiri munthu wanjiru samazindikira kuti khalidwe lake ndilo choputira mavuto ake chachikulu. “Umodzi wa mikhalidwe yapadera ya phthonos,” dikishonale imodzimodziyo ikufotokoza motero, “ndiwo wakuti munthu samazindikira umunthu wake. Munthu wa phthoneros akati apereke zifukwa za khalidwe lake, nthaŵi zonse amadziuza iye mwini ndi ena kuti aja amene iye amawaneneza amayenerera zimenezo ndi kuti amachita zimenezo chifukwa chakuti mkhalidwewo wosakhala bwino umamkakamiza kufunira ena zifukwa. Atamfunsa kuti angalankhule bwanji zotero ponena za bwenzi lake, amati kufunira kwake mnzake zifukwa kuli kaamba ka ubwino wa bwenzi lakelo.”
Mateyu ndi Marko, alembi a Mauthenga Abwino, amagwiritsira ntchito liwulo Lachigiriki phthoʹnos pofotokoza chimene chinasonkhezera aja amene anaphetsa Yesu. (Mateyu 27:18; Marko 15:10) Inde, njiru inawasonkhezera. Mtima woipa umodzimodziwo wachititsa ampatuko kukhala adani anjiru kwa amene kale anali abale awo. (1 Timoteo 6:3-5) Nchifukwa chake anthu anjiru saloledwa kuloŵa Ufumu wa Mulungu! Yehova Mulungu walamula kuti onse opitiriza kukhala “odzala ndi kaduka [“njiru,” NW] . . . ayenera imfa.”—Aroma 1:29, 32; Agalatiya 5:21.
[Zithunzi patsamba 7]
Musalole njiru kuwononga moyo wanu