Moyo Wabwino Kwambiri—Posachedwapa!
TAGANIZIRANI za wopenda nyengo amene zoneneratu zake kaŵirikaŵiri zimakhala zolondola. Ngati aneneratu pa nkhani za madzulo kuti maŵa kudzagwa mvula, simumazengereza zotenga mwafuli pamene muchoka panyumba mmaŵa wotsatira. Kuneneratu kwake kwapapitapo kwakupatsani chidaliro. Mumachita mogwirizana ndi zimene akunena.
Tsopano, kodi lonjezo la Yehova la moyo wabwino kwambiri m’paradaiso wa pa dziko lapansi nlodalirika motani? Chabwino, kodi zoneneratu zake zakale zimasonyezanji? Kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo kumapereka umboni wachionekere wa mbiri ya Yehova. Iye ndiye Mulungu wolunjika ndi wa choonadi chosalephera. (Yoswa 23:14; Yesaya 55:11) Malonjezo a Yehova Mulungu ngodalirika kwambiri kwakuti nthaŵi zina iye amanenadi za zochitika za mtsogolo zolonjezedwa monga ngati kuti zachitika kale. Mwachitsanzo, pambuyo pa lonjezo lake la dziko latsopano mmene simudzakhalanso imfa ndi maliro, timaŵerenganso kuti: “Zachitika [madalitso olonjezedwawo].” Mwa mawu ena, “Nzoona!”—Chivumbulutso 21:5, 6, mawu amtsinde, NW.
Inde, kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova akale kumatipatsa chidaliro cha kukwaniritsa kwake lonjezo la moyo wabwino kwambiri kwa anthu. Koma kodi moyo wabwino kwambiri umenewu udzafika liti?
Moyo Wabwino Kwambiri—Liti?
Moyo wabwino kwambiri udzafika posachedwapa! Timatsimikizira zimenezo chifukwa chakuti Baibulo limanena kuti zinthu zambiri zoipa zidzachitika pa dziko lapansi Paradaiso atatsala pang’ono kubweretsa moyo wabwino kwambiri. Zinthu zoipa zimenezo zikuchitika tsopano lino.
Mwachitsanzo, Yesu Kristu ananeneratu kuti padzakhala nkhondo zazikulu. Iye anati: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Ulosi umenewu wachitikadi. Mkati mwa zakazo 1914 mpaka 1945 pakhala nkhondo ziŵiri za dziko lonse, ndipo zimenezi zatsatiridwa ndi nkhondo zina zambiri zimene maiko amenyana. “Pa avareji ya pachaka, chiŵerengero cha ophedwa mu nkhondo m’nyengo imeneyi [chiyambire Nkhondo Yadziko II] chaŵirikiza mlingo kuposa kaŵiri chiŵerengero cha ophedwa a m’zaka za zana la 19 ndipo nthaŵi zisanu ndi ziŵiri kuposa cha m’zaka za zana la 18.”—World Military and Social Expenditures 1993.
Kufalikira kwa matenda kuli umboni wina wa kuyandikira kwa moyo wabwino kwambiri m’Paradaiso. Yesu ananeneratu kuti kudzakhala “miliri m’malo akutiakuti.” (Luka 21:11) Kodi ulosi umenewu wachitikadi? Inde. Nkhondo ya dziko yoyamba itatha, fuluwenza ya Spanya inapha anthu oposa 20 miliyoni. Kuyambira pamenepo, kansa, nthenda ya mtima, malungo, AIDS, ndi matenda ena apha anthu ambirimbiri. M’maiko omatukuka, nthenda zokhalapo chifukwa cha madzi oipa (kuphatikizapo matenda a kutseguka m’mimba ndi njoka za m’mimba) zimapha anthu mamiliyoni ambiri chaka chilichonse.
Yesu ananenanso kuti: “kudzakhala kupereŵera kwa chakudya.” (Mateyu 24:7, NW) Monga momwe taonera m’nkhani yoyambirira, anthu osauka a m’dziko samakhala ndi chakudya chokwanira. Imeneyi ndi mbali ina ya umboni wakuti moyo wabwino kwambiri mu Paradaiso udzafika posachedwapa.
“Kudzakhala zivomezi zazikulu,” Yesu anatero. (Luka 21:11) Zimenezinso zachitikadi mu nthaŵi yathu. Chiyambire 1914 chiwonongeko chochitidwa ndi zivomezi zosakaza chapha anthu zikwi mazana ambiri.
Ndiponso Baibulo limanena kuti “masiku otsiriza” adzadziŵika ndi kusintha mkhalidwe kwa anthu. Iwo adzakhala “odzikonda okha” ndi “okonda ndalama,” ndipo ana adzakhala “osamvera akuwabala.” Anthu ambiri adzakhala “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” (2 Timoteo 3:1-5) Kodi simukuvomereza kuti zambiri zikugwirizana ndi malongosoledwe ameneŵa?
Pamene anthu owonjezereka akuchita zinthu zoipa, pakhala kuwonjezereka kwa kusayeruzika. Zimenezinso zinanenedweratu. Malinga ndi kunena kwa Mateyu 24:12, Yesu analankhula za “kuchuluka kwa kusayeruzika.” Mwachionekere inu mungavomereze kuti upandu wakhala woipa kwambiri tsopano kuposa mmene unalili zaka zapitazo. Anthu kulikonse amawopa kuti adzaberedwa, kunyengedwa, kapena kuvulazidwa mwa mtundu wina.
Nkhondo, kufalikira kwa matenda, kupereŵera kwa chakudya, zivomezi, kuwonjezereka kwa upandu, ndi kuipiraipira kwa maunansi a anthu—zonsezi zikuchitika lerolino, monga momwe Baibulo linaneneratu. ‘Koma kodi zinthu zimenezi sizinachitikepo m’mbiri yonse ya anthu?’ mungafunse motero. ‘Kodi kusiyana kwake nkotani ndi tsiku lathu?’
Pali mbali zina zofunika kwambiri za zimene zikuchitika lerolino. Baibulo silimanena kuti mbali imodzi yokha, monga ngati kupereŵera kwa chakudya, kudzapereka umboni wakuti tili mu nthaŵi ya mapeto ndi kuti moyo wabwino kwambiri uli pafupi. Maulosi a Baibulo onena za nthaŵi ya mapeto anafunikira kudzakwaniritsidwa pa mbadwo wopanda umulungu.—Mateyu 24:34-39; Luka 17:26, 27.
Ndiponso, nzodabwitsa kwambiri kuti mbali zina za ulosi wa Yesu—makamaka zija zonena za kupereŵera kwa chakudya ndi kufalikira kwa matenda—zikukwaniritsidwa lerolino. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ukatswiri wa asayansi wakhala waukulu kuposa kale. Chidziŵitso cha madokotala ndi mitundu ya kuchiritsa zakhala zapamwamba kwambiri kapena zodziŵika kwambiri kuposa kale. Ndi Mulungu yekha amene anganeneretu m’Mawu ake, Baibulo, kuti panthaŵiyo, nthenda ndi njala zidzakula kwambiri, osati kuchepa.
Popeza kuti maulosi onse a Baibulo onena za nthaŵi ya mapeto, kapena “masiku otsiriza,” akukwaniritsidwa, kodi tinganenenji? Tinganene kuti moyo wabwino kwambiri wayandikira! Koma kodi udzafika motani?
Moyo Wabwino Kwambiri—Motani?
Kodi muganiza kuti anthu angabweretse Paradaiso? M’mbiri yonse kudzafika lero, mwakhala mitundu yambiri ya maboma a anthu. Ena ayesa kwambiri kukhutiritsa zofuna za anthu. Komabe, mavuto ambiri akukula. M’maiko olemera ndi osauka omwe, maboma akulimbana ndi anamgoneka, nyumba zoipa, umphaŵi, upandu, ulova, ndi nkhondo.
Ngakhale ngati maboma angathetse ena a mavuto ameneŵa, sangathetseretu matenda; ndiponso sangathetse ukalamba ndi imfa. Mwachionekere, anthu sangabweretse Paradaiso pa dziko lino lapansi.
Mwanzeru Baibulo limati: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” Nangano, tiyenera kukhulupirira yani? Baibulo limayankha kuti: “Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.” (Salmo 146:3, 5) Ngati tiika chiyembekezo chathu pa Yehova Mulungu, sitidzagwiritsidwa mwala.
Ndithudi Uyo amene ali ndi nzeru ndi mphamvu yolengera dziko lapansi, dzuŵa, ndi nyenyezi angathenso kupanga dziko lapansi kukhala paradaiso. Akhoza kuchititsa anthu kukhala ndi moyo wabwino kwambiri. Chilichonse chimene Yehova Mulungu afuna kuchita, akhoza ndipo adzachikwaniritsa. Mawu ake amati: “Palibe mawu amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.” (Luka 1:37) Koma kodi ndimotani mmene Mulungu adzabweretsera moyo wabwino kwambiri?
Yehova adzabweretsa moyo wabwino kwambiri kwa anthu mwa njira ya Ufumu wake. Ndipo kodi Ufumu wa Mulungu nchiyani? Ndiwo boma lenileni lokhala ndi Wolamulira woikidwa ndi Mulungu, Yesu Kristu. Ufumu wa Mulungu uli kumwamba, koma posachedwapa udzabweretsa madalitso aakulu ndi moyo wabwino koposa kwa nzika za m’Paradaiso wa pa dziko lapansi.—Yesaya 9:6, 7.
Mwina mukudziŵa kale pemphero la chitsanzo la Yesu, lopezeka m’Baibulo pa Mateyu 6:9-13. Mbali ina ya pemphero lopita kwa Mulungulo imati: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” Mogwirizana ndi pemphero limenelo, Ufumu wa Mulungu ‘udzadza’ kudzachita chifuno cha Yehova Mulungu cha dziko lapansi. Ndipo nchifuno chake kuti dziko lapansi likhale paradaiso.
Funso limodzi lomaliza likubuka: Kodi muyenera kuchitanji kuti mudzalandire moyo wabwino kwambiri m’Paradaiso amene akudzayo?
Zimene Mufunikira Kuchita
Mwachikondi Yehova Mulungu akupereka chiyembekezo cha moyo wabwino kwambiri m’Paradaiso kwa onse amene amachita chifuniro chake. Baibulo limatiuza kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Koma kodi nchiyani chimene chimapangitsa munthu kukhala wolungama pamaso pa Mulungu?
Kuti tikondweretse Yehova tifunikira kudziŵa zambiri ponena za zimene amafuna kuti ife tichite. Ngati tipeza chidziŵitso chonena za Mulungu ndi kuchigwiritsira ntchito m’moyo wathu, tingathe kukhala ndi moyo kosatha. Popemphera kwa Mulungu, Yesu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—Yohane 17:3.
Buku limene limatiuza za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu ndilo Mawu a Mulungu, Baibulo. Ndilo chimodzi cha mphatso za mtengo wapatali zochokera kwa Yehova. Baibulo lili ngati kalata yochokera kwa atate wachikondi kumka kwa ana ake. Limatiuza za lonjezo la Mulungu la kubweretsa moyo wabwino kwambiri kwa anthu ndipo limatisonyeza mmene tingaupezere. Baibulo limatidziŵitsa zimene Mulungu anachita kalelo ndi zimene adzachita mtsogolo. Ndiponso limatipatsa uphungu wothandiza wonena za mmene tingachitire ndi mavuto athu mwachipambano tsopano lino. Indedi, Mawu a Mulungu amatiphunzitsa mmene tingapezere mlingo wina wa chimwemwe ngakhale m’dziko lamavutoli.—2 Timoteo 3:16, 17.
Mboni za Yehova zingalinganize nanu mokondwa phunziro la Baibulo lapanyumba laulere. Dziŵani mmene mungakhalire ndi moyo wachimwemwepo tsopano lino, ndi chiyembekezo cha moyo wabwino kwambiri mtsogolomu posachedwapa.
[Chithunzi patsamba 5]
Maulosi a Baibulo amasonyeza kuti moyo wabwino kwambiri wayandikira
[Chithunzi patsamba 7]
Ufumu wa Mulungu udzabweretsa moyo wabwino kwambiri kwa anthu