Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 11/15 tsamba 24-25
  • Kuunika Kwawo Sikunazime

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuunika Kwawo Sikunazime
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Khalani Wolimba Mtima Ngati Yeremiya
    Nsanja ya Olonda—2004
  • “Ndidzatsitsimutsa Wolefuka”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Yeremiya—Mneneri Wachilendo wa Ziweruzo za Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • “Ndaika Mawu Anga M’kamwa Mwako”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 11/15 tsamba 24-25

Kuunika Kwawo Sikunazime

MU NTHAŴI za Baibulo, kunali Mboni zokhulupirika za Yehova zimene zinakumana ndi zopinga ndi mavuto. Iwo anakumana ndi chitsutso ndi zimene zinaoneka ngati kulephera. Komabe, sanaleke chifukwa cha kulefulidwa. M’malo mwake, kuunika kwawo sikunazime.

Mwachitsanzo, mneneri Yeremiya anapatsidwa ntchito ya kukhala mneneri wa Mulungu kwa mtundu wampatuko wa Yuda. Iye anachenjeza za chiwonongeko cha Yerusalemu chimene chinalinkudza. (Yeremiya 1:11-19) Motero, Yeremiya nthaŵi zambiri analimbana ndi anthu a mtundu wake, amene anamuyesa ngati wolengeza tsoka.

Wansembe Pasuri, kapitao wamkulu m’nyumba ya Mulungu, panthaŵi ina anamenya Yeremiya ndi kumuika m’matangaza chifukwa cha zimene ananenera. Chifukwa cha chimene chinaoneka ngati chopinga, Yeremiya anati: “Ndikhala choseketsa dzuŵa lonse, onse andiseka. Pakuti paliponse ndinena, ndifuula; ndifuula, chiwawa ndi chofunkha; pakuti mawu a Mulungu ayesedwa kwa ine chitonzo, ndi choseketsa, dzuŵa lonse.” Mneneriyo analefulidwa kwakuti anati: “Sindizamtchula iye [Yehova], sindidzanenanso m’dzina lake.”​—Yeremiya 20:1, 2, 7-9.

Komabe, Yeremiya sanalole kulefulidwa. Ponena za “mawu a Mulungu,” iye anati: “M’mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m’mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.” (Yeremiya 20:8, 9) Atasonkhezeredwa mwamphamvu kulankhula mawu a Mulungu, Yeremiya analimbikitsidwa ndi mzimu woyera ndipo anakwaniritsa ntchito yake.

Mtumwi Paulo nayenso anali ndi zifukwa zambiri zakulefuka, ngati akanazigonjera. Anapirira ngozi za chilengedwe, kusweka kwa chombo, chizunzo, ndi kumenyedwa. Ndiponso, ‘chomusindikiza tsiku ndi tsiku, chinali chilabadiro cha mipingo yonse.’ (2 Akorinto 11:23-28) Inde, Paulo anali kukumana ndi mavuto tsiku ndi tsiku, akumadera nkhaŵa za mipingo yatsopano imene anathandizira kukhazikitsa. Ndiponso, iye anali wopanda ungwiro ndipo anafunikira kulimbana ndi “munga m’thupi,” mwinamwake kusapenya bwino. (2 Akorinto 12:7; Aroma 7:15; Agalatiya 4:15) Ena ananeneza Paulo kumbali, ndipo iye anazimva zimenezi.​—2 Akorinto 10:10.

Ngakhale zinali choncho, Paulo sanalole kulefulako kumgonjetsa. Ayi, iye sanali munthu wapadera. (2 Akorinto 11:29, 30) Kodi nchiyani chimene chinachititsa ‘moto wake wamkati’ kuyakabe? Choyamba, anali ndi mabwenzi ochirikiza, ena ngakhale kupita naye ku Roma kumene anamangidwa. (Machitidwe 28:14-16) Chachiŵiri, mtumwiyo anali ndi kaonedwe kachikatikati ka mkhalidwe wake. Omuzunza ndi omtsutsa ndiwo amene anali olakwa, osati Paulo. Chakumapeto kwa moyo wake wa pa dziko lapansi, iye anapenda utumiki wake m’njira yabwino ndipo ananena kuti: “Chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine.”​—2 Timothy 4:8.

Koposa zonse, Paulo anafika kwa Yehova Mulungu m’pemphero nthaŵi zonse, ndipo ‘Ambuye anaima naye nampatsa mphamvu.’ (2 Timothy 4:17) “Ndikhoza zonse,” anatero Paulo, “mwa iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13) Kulankhulana ndi Mulungu ndi Akristu anzake, pamodzi ndi kaonedwe kake kabwino ka utumiki wake, zinathandiza Paulo kulimbikira mu utumiki wa Yehova.

Mulungu anauzira Paulo kulemba kuti: “Tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufoka.” (Agalatiya 6:7-9) Kututanji? Moyo wosatha. Motero, khalani monga Yeremiya, Paulo, ndi mboni zina zambiri zokhulupirika za Yehova zotchulidwa m’Malemba. Inde, khalani monga iwo, ndipo musalefuke. Musalole kuunika kwanu kuzima.​—Yerekezerani ndi Mateyu 5:14-16.

[Zithunzi patsamba 25]

Paulo ndi Yeremiya sanalole kuunika kwawo kuzima

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena