Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 1/15 tsamba 15-20
  • Nkhosa za Yehova Zimafuna Kuzisamalira Mokoma Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhosa za Yehova Zimafuna Kuzisamalira Mokoma Mtima
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Abusa Aufulu a Gulu la Nkhosa
  • Pamene Atsopano Afuna Kulalikira
  • Kusamalira Zofunika Zapadera
  • Ngati Watsopano Alakwa
  • Athandizeni “Kutsata Ukulu Msinkhu”
  • Kuthandiza Ena Kulambira Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Abusa, Tsanzirani Abusa Aakulu
    Nsanja ya Olonda—2013
  • “Wetani Gulu la Nkhosa za Mulungu Lomwe Analisiya M’manja Mwanu”
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Akulu—Samalirani Gulu la Mulungu Mokoma Mtima!
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 1/15 tsamba 15-20

Nkhosa za Yehova Zimafuna Kuzisamalira Mokoma Mtima

“Dziŵani kuti Yehova ndiye Mulungu; . . . ndife anthu ake ndi nkhosa za pabusa pake.”​—SALMO 100:3.

1. Kodi Yehova amachita nawo motani atumiki ake?

YEHOVA ndiye Mbusa Wopambana. Ngati tili atumiki ake, amationa monga nkhosa zake ndipo amatisamalira mokoma mtima. Atate wathu wakumwamba amatitonthoza ndi kutitsitsimula ndipo amatitsogolera “m’mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.” (Salmo 23:1-4) Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, amatikonda kwambiri moti anapereka moyo wake kaamba ka ife.​—Yohane 10:7-15.

2. Kodi anthu a Mulungu amapezeka mumkhalidwe wotani?

2 Pokhala osamaliridwa mokoma mtima, ife titha kunena mogwirizana ndi wamasalmo kuti: “Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera. Dziŵani kuti Yehova ndiye Mulungu; iyeyu anatilenga, ndipo [osati ife tokha, NW]; ndife anthu ake ndi nkhosa za pabusa pake.” (Salmo 100:2, 3) Inde, ndife okondwera ndi osungika. Zili monga ngati kuti tili m’khola la nkhosa lamakoma olimba amiyala, otetezereka ku zilombo zolusa.​—Numeri 32:16; 1 Samueli 24:3; Zefaniya 2:6.

Abusa Aufulu a Gulu la Nkhosa

3. Kodi akulu achikristu oikidwa amachita nalo motani gulu la nkhosa la Mulungu?

3 Nchifukwa chake tili okondwa monga nkhosa za Mulungu! Akulu oikidwa amatitsogolera. ‘Samadziyesa akalonga,’ samachita ufumu pa ife, kapena kuyesa kuchita umbuye pa chikhulupiriro chathu. (Numeri 16:13; Mateyu 20:25-28; 2 Akorinto 1:24; Ahebri 13:7) M’malo mwake, iwo ndi abusa achikondi amene amatsatira uphungu wa mtumwi Petro wakuti: “Ŵetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokangamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.” (1 Petro 5:2, 3) Mtumwi Paulo anauza akulu anzake kuti: “Mudzipenyerere nokha ndi gulu lonse la nkhosa, pamene mzimu woyera waika inu oyang’anira, kuti muŵete mpingo wa Mulungu, umene anagula ndi mwazi wa Mwana wake wayekha.” Ndipo nkhosazo zikuthokozadi kuti amuna oikidwa ndi mzimu woyera ameneŵa ‘amachita mokoma mtima ndi gulu la nkhosalo’!​—Machitidwe 20:28-30, NW.

4. Kodi Charles T. Russell anadziŵika ndi unansi wa mtundu wotani pakati pa iye ndi gulu la nkhosa?

4 Yesu anapatsa mpingo “mphatso mwa amuna,” ena monga “apasitala,” kapena abusa, amene amachita nalo mokoma mtima gulu la nkhosa la Yehova. (Aefeso 4:8, 11; King James Version) Mmodzi wa amuna ameneŵa anali Charles T. Russell, pulezidenti woyamba wa Watch Tower Society. Iye ankatchedwa Pasitala Russell chifukwa cha zochita zake zachikondi ndi zachifundo poŵeta gulu la nkhosa pansi pa Mbusa Wamkulu, Yesu Kristu. Lerolino, akulu achikristu amaikidwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, ndipo amasamala kupeŵa kugwiritsira ntchito mawu onga “pasitala,” “mkulu,” kapena “mphunzitsi” monga maina aulemu. (Mateyu 23:8-12) Komabe, akulu amakono amachita ntchito yaubusa kapena yoŵeta, ntchito yopindulitsa nkhosa za pabusa pa Yehova.

5. Kodi nchifukwa ninji atsopano afunikira kudziŵa akulu oikidwa mumpingo wachikristu?

5 Monga abusa, akulu amachita mbali yaikulu kuthandiza atsopano kupita patsogolo. Chifukwa chake, buku latsopano la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha limati patsamba 168: “Dziŵani akulu oikidwa mumpingo. Iwo akudziŵa zambiri pakugwiritsira ntchito chidziŵitso chonena za Mulungu, pakuti anakwaniritsa ziyeneretso za kukhala oyang’anira zoikidwa m’Baibulo. (1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:5-9) Musawope kufikira aliyense wa iwo ngati mukufuna chithandizo chauzimu kuti mugonjetse chizoloŵezi kapena mkhalidwe winawake umene umaombana ndi zofunika za Mulungu. Mudzapeza kuti akuluwo amatsatira uphungu wa Paulo wakuti: ‘Limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.’​—1 Atesalonika 2:7, 8; 5:14.”

Pamene Atsopano Afuna Kulalikira

6. Kodi ndi njira iti imene imatsatiridwa ngati wophunzira Baibulo akufuna kukhala wofalitsa wosabatizidwa wa Ufumu?

6 Pambuyo poti wophunzira Baibulo wapeza chidziŵitso ndipo wakhala akusonkhana kwa nthaŵi yakutiyakuti, angafune kukhala wofalitsa Ufumu, mlaliki wa uthenga wabwino. (Marko 13:10) Zitakhala choncho, Mboni imene imachititsa phunziro la Baibulo kwa iye iyenera kuuza woyang’anira wotsogoza, amene adzalinganiza kuti mmodzi wa akulu a Komiti Yautumiki Yampingo ndi mkulu wina akumane ndi wophunzira Baibuloyo ndi mphunzitsi wake. Zimene adzakambitsirana zidzachokera m’buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 98 ndi 99. Ngati akulu aŵiriwa aona kuti watsopanoyo akukhulupirira ziphunzitso zoyambirira za Baibulo ndipo akutsatira mapulinsipulo a Mulungu, adzamuuza kuti ali woyenerera kupita mu utumiki wapoyera.a Atachitira lipoti utumiki wake mwa kupereka maola ake akumunda, iwo adzalembedwa pa khadi la Cholembapo cha Wofalitsa cha Mpingo chokhala ndi dzina lake. Kuyambira nthaŵiyi watsopanoyu ayenera kumachitira lipoti ntchito yake ya umboni limodzi ndi mamiliyoni ena ambiri amene mokondwera ‘amalalikira mawu a Mulungu.’ (Machitidwe 13:5) Chilengezo chakuti iye ali wofalitsa wosabatizidwa chidzaperekedwa ku mpingo.

7, 8. Kodi wofalitsa wosabatizidwa angapatsidwe motani thandizo lofunika mu utumiki?

7 Wofalitsa wosabatizidwa amafunikira chithandizo cha akulu ndi Akristu ena okhwima. Mwachitsanzo, wochititsa Phunziro la Buku la Mpingo limene amapitako amafunitsitsa kudziŵa za kupita patsogolo kwake. Wofalitsa watsopano angapeze vuto kulankhula mogwira mtima m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba. (Machitidwe 20:20) Chotero iye mwachionekere angafune thandizo, makamaka kwa uja amene wakhala akuchititsa phunziro la Baibulo kwa iye m’buku la Chidziŵitso. Thandizo lofunika limenelo nloyenera, pakuti Yesu Kristu anakonzekeretsa ophunzira ake utumiki.​—Marko 6:7-13; Luka 10:1-22.

8 Kuti utumiki wathu ukhale wogwira mtima, tifunika kukonzekera bwino pasadakhale. Chotero, ofalitsa aŵiriwo choyamba angakhale pansi ndi kuyeseza maulaliki osonyezedwa m’makope a mwezi ndi mwezi a Utumiki Wathu Waufumu. Pamene ayamba utumiki wawo wakumunda, wofalitsa wozoloŵera angayambire pakhomo loyamba mwina ndi lachiŵiri. Pambuyo pa mawu oyamba aubwenzi, ofalitsa aŵiriwo akhoza kuthandizana kuchitira umboniwo. Kugwirira ntchito pamodzi mu utumiki kwa milungu ingapo kungachititse maulendo obwereza abwino ndipo ngakhale kuyambitsa phunziro la Baibulo lapanyumba m’buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Wofalitsa wozoloŵera kwambiriyo angachititse phunzirolo kwa nthaŵi yakutiyakuti ndiyeno nkulipatsa kwa wofalitsa watsopano wa Ufumu. Ofalitsa aŵiriwo adzakondwadi ngati wophunzira Baibuloyo asonyeza chiyamikiro kaamba ka chidziŵitso chonena za Mulungu!

9. Kodi pamapangidwa makonzedwe otani pamene wofalitsa afuna kubatizidwa?

9 Pamene wofalitsa wosabatizidwa akupita patsogolo mwauzimu, angadzipatulire kwa Mulungu m’pemphero ndipo angafune kubatizidwa. (Yerekezerani ndi Marko 1:9-11.) Ayenera kuuza woyang’anira wotsogoza wa mpingo za chifuno chake cha kubatizidwa, amene adzalinganiza kuti akulu apende ndi wofalitsayo mafunso a pamasamba 175 mpaka 218 a buku lakuti Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu. Mbali zinayi zogaŵidwa za mafunsowo ziyenera kuchitidwa m’zigawo zitatu ndi akulu atatu osiyana ngati kutheka. Ngati iwo avomerezana kuti wofalitsa wosabatizidwayo ali ndi chidziŵitso chokwana bwino cha ziphunzitso za Baibulo ndipo akuyenerera mwanjira zina, angamuuze kuti adzabatizidwa. Chifukwa cha kudzipatulira kwake ndi ubatizo, ‘amalembedwa chizindikiro’ cha chipulumutso.​—Ezekieli 9:4-6.

Kusamalira Zofunika Zapadera

10. Munthu atamaliza phunziro lake m’buku la Chidziŵitso nabatizidwa, kodi angawonjezere motani chidziŵitso chake cha Malemba?

10 Munthu atamaliza phunziro lake la Baibulo m’buku la Chidziŵitso ndipo wabatizidwa, sipangafunikire kuchititsanso phunziro kwa iye m’buku lachiŵiri, monga Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona.b Ndithudi, munthu wobatizidwa chatsopanoyo adzaphunzira zambiri pamene akonzekera misonkhano yachikristu ndi kupezekapo nthaŵi zonse. Adzapezanso chidziŵitso china chowonjezera pamene ludzu lake la choonadi limsonkhezera kuŵerenga ndi kuphunzira zofalitsa zachikristu payekha ndi pokambitsirana mfundo za Malemba ndi okhulupirira anzake. Koma bwanji ngati pakhala zofunika zapadera?

11. (a) Kodi Priskila ndi Akula anamthandiza motani Apolo? (b) Kodi ndi thandizo lotani limene lingaperekedwe kwa wachichepere wosinkhukirapo wobatizidwa posachedwa amene akuganiza zoloŵa muukwati?

11 Ngakhale Apolo, amene anali “wamphamvu m’Malembo” naphunzitsa za Yesu molondola, anapindula pamene Priskila ndi Akula, Akristu achidziŵitso, “anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.” (Machitidwe 18:24-26; yerekezerani ndi Machitidwe 19:1-7.) Chotero, bwanji ngati wachichepere wosinkhukirapo amene anabatizidwa posachedwapa akuganiza za chitomero ndi kuloŵa muukwati. Mkristu wokhwima kwambiri angamthandize kupeza chidziŵitso pankhani zimenezi mu zofalitsa za Watch Tower. Mwachitsanzo, nkhani zothandiza zokhudza zimenezi zikupezeka m’buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza, Chigawo 7.c Wofalitsa amene ankachititsa phunziro la Baibulo kwa watsopanoyo angakambitsirane naye nkhaniyi, ngakhale kuti zimenezo sizidzaŵerengedwa monga phunziro lokhazikika.

12. Kodi ndi thandizo lotani limene lingaperekedwe kwa okwatirana obatizidwa chatsopano amene ali ndi mavuto?

12 Talingalirani chitsanzo china. Tinene kuti okwatirana amene abatizidwa chatsopano akupeza vuto kutsatira mapulinsipulo aumulungu. Iwo angapemphe mkulu, yemwe angakhale nawo pansi masiku angapo madzulo kukambitsirana nawo Malemba ndi kuwasonyeza chidziŵitso chopezeka m’zofalitsa za Watch Tower. Komabe, mkulu sadzayambitsanso phunziro la Baibulo lokhazikika kwa okwatiranawo.

Ngati Watsopano Alakwa

13. Kodi nchifukwa ninji akulu ayenera kuchitira chifundo munthu wobatizidwa chatsopano amene walakwa koma ali wolapa?

13 Akulu amatsanzira Mbusa Wopambana, Yehova, yemwe amati: “Ine ndekha ndidzadyetsa nkhosa zanga, . . . ndi kulukira tchika yothyoka mwendo, ndi kulimbitsa yodwalayo.” (Ezekieli 34:15, 16; Aefeso 5:1) Mogwirizana ndi mzimu umenewo, wophunzira Yuda analimbikitsa kuti chifundo chisonyezedwe kwa Akristu odzozedwa amene anali ndi zikayikiro kapena amene anachita tchimo. (Yuda 22, 23) Popeza timayembekezera zambiri kwa Akristu achidziŵitso ndithudi chifundo chiyenera kusonyezedwa kwa munthu wobatizidwa chatsopano​—kamwana wamba ka nkhosa​—amene walakwa koma ali wolapa. (Luka 12:48; 15:1-7) Chifukwa chake, akulu amene ‘aweruzira Yehova,’ amasamalira nkhosa zotero mokoma mtima ndi kuzibweza mumzimu wachifatso.​—2 Mbiri 19:6; Machitidwe 20:28, 29; Agalatiya 6:1.d

14. Kodi nchiyani chiyenera kuchitidwa pamene wofalitsa amene wabatizidwa chatsopano wachita tchimo lalikulu, ndipo angathandizidwe motani?

14 Ndiyeno, tinene kuti wofalitsa amene wabatizidwa posachedwapa anali ndi vuto la kumwetsa moŵa kale ndipo waledzera kamodzi kapena kaŵiri. Kaya tinene kuti anagonjetsa chizoloŵezi chanthaŵi yaitali cha kusuta fodya ndiyeno wagonja pachiyesocho mwa kusuta fodya kamodzi kapena kaŵiri mseri. Ngakhale kuti mbale wathu watsopanoyo wapemphera kwa Mulungu kaamba ka chikhululukiro, ayenera kupempha akulu kumthandiza kuti tchimo lakelo lisakhale chizoloŵezi. (Salmo 32:1-5; Yakobo 5:14, 15) Pamene atchulira mkulu wina za tchimo lake, mkuluyo ayenera kuyesa kubweza watsopanoyo mwachifundo. (Salmo 130:3) Uphungu wa Malemba ungakhale wokwanira kumthandiza kuwongola njira zoyendamo mapazi ake pambuyo pake. (Ahebri 12:12, 13) Mkulu ameneyu adzakambitsirana ndi woyang’anira wotsogoza wa mpingo kuti aone thandizo lina limene lingaperekedwe.

15. Kodi nchiyani chimene chingafunike nthaŵi zina pamene munthu wobatizidwa chatsopano wachimwa?

15 Nthaŵi zina pangafunikire zochuluka. Ngati nkhaniyo ili yodziŵika, ikuika pangozi gulu la nkhosa, kapena ingabutse mavuto ena aakulu, bungwe la akulu liyenera kusankha akulu aŵiri kuti aifufuze. Ngati akulu ameneŵa apeza kuti nkhaniyo njaikulu kwambiri moti ifunikira komiti yachiweruzo, adzauza bungwe la akulu. Ndiyeno bungwe la akulu lidzasankha komiti yachiweruzo kuti ithandize wolakwayo. Komiti yachiweruzo iyenera kuchita naye mokoma mtima. Iyenera kuyesayesa kumbweza ndi Malemba. Ngati iye alabadira thandizo lokoma mtima la komiti yachiweruzo, pamenepo iwo ayenera kuona ngati pangakhale phindu lililonse kuleka kumgwiritsira ntchito m’nkhani zapapulatifomu pamisonkhano m’Nyumba ya Ufumu kapena ngati ayenera kumlola kuyankha pamisonkhano.

16. Kodi akulu angachitenji kuthandiza wolakwayo?

16 Ngati wolakwayo walabadira, mkulu mmodzi kapena aŵiri a m’komiti yachiweruzoyo angapange maulendo aubusa olinganizidwa kulimbitsa chikhulupiriro chake ndi kukulitsa chiyamikiro chake cha miyezo yolungama ya Mulungu. Nthaŵi ndi nthaŵi mmodzi wa iwo angagwire naye ntchito mu utumiki wakumunda. Iwo angakambitsirane naye za Malemba kangapo, mwinamwake mwa kugwiritsira ntchito nkhani zoyenerera za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! koma popanda kukhazikitsa phunziro la Baibulo lokhazikika. Mwa kusamaliridwa mokoma mtima chonchi, wolakwayo angapeze nyonga yokanizira zofooka za thupi lake mtsogolo.

17. Kodi ndi njira ziti zimene zimatengedwa ngati munthu wobatizidwa wolakwa salapa ndi kusiya njira yake yauchimo?

17 Ndithudi, kubatizidwa chatsopano sikuli chifukwa chomapitirizira kuchita tchimo mosalapa. (Ahebri 10:26, 27; Yuda 4) Ngati munthu wobatizidwa aliyense wolakwa salapa ndi kuleka njira yake yauchimo, adzachotsedwa mumpingo. (1 Akorinto 5:6, 11-13; 2 Atesalonika 2:11, 12; 2 Yohane 9-11) Zimenezi zitakhala zofunika, bungwe la akulu lidzasankha komiti yachiweruzo. Ngati munthuyo wachotsedwa, chilengezo chachidule chotsatirachi chidzaperekedwa: “ . . . wachotsedwa.”e

Athandizeni “Kutsata Ukulu Msinkhu”

18. Kodi nchifukwa ninji tili otsimikiza kuti Akristu obatizidwa chatsopano ndi ena nthaŵi zonse adzakhalabe ndi zambiri zoti aphunzire ponena za Yehova ndi chifuniro chake?

18 Ochuluka kwambiri mwa atumiki a Mulungu adzakhalabe m’gulu la nkhosa. Kukondweretsa kwake nkwakuti, aliyense wa ife adzakhoza kuyandikira nthaŵi zonse kwa Atate wathu wakumwamba chifukwa nthaŵi zonse tidzaphunzira zambiri ponena za iye ndi chifuniro chake. (Mlaliki 3:11; Yakobo 4:8) Ndithudi, anthu zikwi zambiri amene anabatizidwa pa Pentekoste mu 33 C.E. anali ndi zambiri zoti aphunzire. (Machitidwe 2:5, 37-41; 4:4) Momwemonso Akunja, amene analibe chidziŵitso cha Malemba. Mwachitsanzo, ndi mmene zinalili kwa aja obatizidwa pambuyo pa nkhani ya Paulo pa Areopagi ku Atene. (Machitidwe 17:33, 34) Lerolinonso, obatizidwa chatsopano ali nzambiri zoti aphunzire ndipo afunikira nthaŵi ndi chithandizo kuti alimbitse chitsimikizo chawo cha kuchitabe chabwino pamaso pa Mulungu.​—Agalatiya 6:9; 2 Atesalonika 3:13.

19. Kodi aja amene akubatizidwa angathandizidwe motani “kutsata ukulu msinkhu”?

19 Chaka ndi chaka anthu zikwi zambiri amabatizidwa ndipo amafunikira chithandizo kuti ‘atsate ukulu msinkhu.’ (Ahebri 6:1-3) Mwa mawu, chitsanzo, ndi kuwathandiza mu utumiki, mungathe kuthandiza ena kuvala umunthu watsopano ndi “kuyenda m’choonadi.” (3 Yohane 4; Akolose 3:9, 10) Ngati muli wofalitsa wozoloŵera, akulu angakupempheni kuthandiza wokhulupirira mnzanu watsopano mu utumiki wakumunda kapena kukambitsirana naye mfundo zina za Malemba kwa milungu ingapo kuti alimbitse chikhulupiriro chake mwa Mulungu, chiyamikiro chake cha misonkhano yachikristu, ndi zina zotero. Unansi wa abusa pankhosa uli wonga uja wa atate pakulangiza ndi wa amayi pakusonyeza chifatso. (1 Atesalonika 2:7, 8, 11) Komabe, akulu ndi atumiki otumikira oŵerengeka sangathe kusamalira zonse zofunika mumpingo. Ife tonse tili ngati banja limene limathandizana. Aliyense wa ife akhoza kuchita kanthu kena kuthandiza olambira anzathu. Inuyo mungakhoze kupereka chilimbikitso, kutonthoza opsinjika mtima, kuchirikiza ofooka.​—1 Atesalonika 5:14, 15.

20. Kodi mungachitenji kuti muwanditse chidziŵitso chonena za Mulungu ndi kusamalira nkhosa za pabusa pa Yehova mokoma mtima?

20 Anthu afunikira chidziŵitso chonena za Mulungu, ndipo monga Mboni ya Yehova, mungatengemo mbali mwachimwemwe m’kuchiwanditsa. Nkhosa za Yehova zimafuna kuzisamalira mokoma mtima, ndipo mungachite mbali yachikondi pothandizira kuchita zimenezi. Yehova adalitsetu utumiki wanu, ndipo akufupeni pakuyesayesa kwanu kwakhama kuthandiza nkhosa za pabusa pake.

[Mawu a M’munsi]

a Panthaŵiyi, watsopanoyo ayenera kuombola kope la buku lakuti Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu.

b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

c Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

d Makonzedwe otero a ofalitsa osabatizidwa anafotokozedwa m’nkhani yakuti “Kuthandiza Ena Kulambira Mulungu,” ya mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1988, masamba 15-20.

e Ngati pakhala chigamulo cha kuchotsa ndipo iye wachita apilo, chilengezocho chimayamba chaimitsidwa. Onani masamba 147-8 m’buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi Yehova amachita nazo motani nkhosa zake?

◻ Kodi nchiyani chimene chimachitika pamene atsopano afuna kulalikira?

◻ Kodi ndi motani mmene okhulupirira ena angathandizire anzawo atsopano amene ali ndi zofunika zapadera?

◻ Kodi ndi thandizo lotani limene akulu angapereke kwa aja amene amalakwa ndi kulapa?

◻ Kodi mungamthandize motani munthu wobatizidwa chatsopano “kutsata ukulu msinkhu”?

[Chithunzi patsamba 16]

Charles T. Russell anali kudziŵika monga mbusa wachikondi wa gulu la nkhosa

[Chithunzi patsamba 18]

Akulu achifundo amachita nalo mokoma mtima gulu la nkhosa la Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena