Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 1/15 tsamba 20-23
  • Chitonthozo ndi Chilimbikitso—Ngale za Mbali Zambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitonthozo ndi Chilimbikitso—Ngale za Mbali Zambiri
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mwa Unansi Wathu Waumwini ndi Mulungu
  • Mwa Phunziro Laumwini la Mawu a Mulungu
  • Kupyolera Mumpingo
  • Kupyolera mwa “Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru”
  • ‘Tonthozani Anthu Onse Olira’
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Tonthozani Amene ali ndi Chisoni
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Mulungu Amatilimbikitsa Bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Tizilimbikitsa Anthu Amene Achitiridwa Zoipa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 1/15 tsamba 20-23

Chitonthozo ndi Chilimbikitso​—Ngale za Mbali Zambiri

AMBIRI a ife tinakhalapo ndi nthaŵi pamene tinamvadi kukhala osoŵa​—osati osoŵa ndalama koma osoŵa chimwemwe. Tinali olefulidwa kwenikweni, ndipo ngakhale kuchita tondovi kwambiri. Komabe, panthaŵi ngati zimenezi mwinamwake pafupi ndi ife panali chinthu chinachake chamtengo wapatali chimene chikanatithandiza kwambiri. “Ngale” imeneyo ndiyo chilimbikitso.

M’Baibulo liwu limodzi lachigiriki limagwiritsiridwa ntchito kutanthauza “limbikitsa” ndi “tonthoza.” Mawu aŵiri onsewo amasonyeza lingaliro la kupatsa chilimbikitso, nyonga, kapena chiyembekezo. Motero, nkwachionekere kuti, pamene timafooka kapena kusoŵa chimwemwe, chitonthozo ndi chilimbikitso ndizo zimene timafunikira kwenikweni. Kodi zingapezeke kuti?

Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova ndiye “Mulungu wa chitonthozo chonse.” (2 Akorinto 1:3) Limatiuzanso kuti “sakhala patali ndi yense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Motero chitonthozo ndi chilimbikitso zilipo. Tiyeni tikambitsirane mbali zazikulu zinayi m’zimene Yehova amaperekeramo chilimbikitso.

Mwa Unansi Wathu Waumwini ndi Mulungu

Magwero aakulu koposa achitonthozo ndiwo unansi wathu waumwini ndi Yehova Mulungu. Kungodziŵa kuti unansi wotero ngwotheka nkolimbikitsa. Ndiponso, ndi wolamulira wadziko uti amene angayankhe makalata athu kapena amene angafune kudziŵa yekha za mavuto athu? Yehova ndi wamphamvu kuposa anthu wamba ameneŵa. Komabe, ngwodzichepetsa​—wofunitsitsa kwambiri kuchita ndi anthu ofooka ndi opanda ungwiro. (Salmo 18:35) Yehova wachitaponso kanthu kutisonyeza chikondi chake. Yohane woyamba 4:10 amati: “Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.” Ndiponso, mwachikondi Yehova amatiyandikizitsa kwa Mwana wake.​—Yohane 6:44.

Kodi mwayamikira zimenezo ndi kufunafuna chitonthozo mwa ubwenzi ndi Mulungu? (Yerekezerani ndi Yakobo 2:23.) Mwachitsanzo, ngati muli ndi bwenzi lanu lapamtima limene mumakonda kwambiri, kodi sikumakhala kokondweretsa kuthera nthaŵi ina muli nokha ndi bwenzilo, mukumalankhula momasuka za nkhaŵa zanu ndi malingaliro anu, ziyembekezo zanu ndi chimwemwe chanu? Yehova akutipempha kuchita chimodzimodzi ndi iye. Iye saika utali wanthaŵi imene tingalankhuzane naye m’pemphero​—ndipo amamvetseradi. (Salmo 65:2; 1 Atesalonika 5:17) Yesu anapemphera nthaŵi zonse kuchokera pansi pa mtima. Ndipotu, asanasankhe atumwi ake 12, anapemphera usiku wonse.​—Luka 6:12-16; Ahebri 5:7.

Nthaŵi ndi nthaŵi, aliyense wa ife angathe kukhala yekha ndi Yehova. Kungokhala chete kudzenera kapena kupita kokawongola miyendo kungapereke mwaŵi wabwino wotsegula mtima wathu kwa Yehova m’pemphero. Kuchita motero kungatipumulitse kwambiri ndi kutipatsa chitonthozo. Ngati pali chilengedwe china cha Yehova chimene tingayang’ane pamene tisinkhasinkha​—ngati pali mbali ina ya mlengalenga, mitengo kapena mbalame​—tingapezemo zikumbutso zotonthoza za chikondi cha Yehova ndi chisamaliro chake pa ife.​—Aroma 1:20.

Mwa Phunziro Laumwini la Mawu a Mulungu

Komabe, mikhalidwe ya Yehova imaonekera kwa ife kupyolera m’phunziro laumwini la Baibulo. Baibulo mobwerezabwereza limasonyeza Yehova kukhala “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi waukoma mtima wochuluka.” (Eksodo 34:6; Nehemiya 9:17; Salmo 86:15) Chikhumbo cha kutonthoza atumiki ake apadziko lapansi ndicho mbali yaikulu ya umunthu wa Yehova.

Mwachitsanzo, talingalirani mawu a Yehova pa Yesaya 66:13: “Monga munthu amene amake amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu.” Yehova anapanga chikondi cha amayi pa ana ake kukhala chodzimana ndi chokhulupirika. Ngati munaonapo amayi wachikondi akutonthoza mwana wake wovulala, mukudziŵa zimene Yehova akutanthauza pamene amati adzatonthoza anthu ake.

Nkhani zambiri za m’Baibulo zimasonyeza mmene chitonthozo chimenechi chinagwirira ntchito. Pamene mneneri Eliya anawopsezedwa kuti adzaphedwa ndi Mfumukazi yoipayo Yezebeli, iye anachita mantha nathaŵa kupulumutsa moyo wake. Anapsinjika mtima kwambiri kotero kuti anayenda m’chipululu tsiku lonse, mwachionekere popanda madzi kapena zakudya. Ndi chisoni chachikulu Eliya anauza Yehova kuti anafuna kuti afe. (1 Mafumu 19:1-4) Kodi Yehova anachitanji kutonthoza ndi kulimbikitsa mneneri wake?

Yehova sanadzudzule Eliya chifukwa cha kusungulumwa, kudziyesa wopanda pake, ndi kumva mantha. M’malo mwake, mneneriyo anamva “liwu lachifatse ndi lotsika.” (1 Mafumu 19:12, NW) Mutaŵerenga 1 Mafumu chaputala 19, mudzaona mmene Yehova anatonthozera Eliya, ndi kulimbitsa chikhulupiriro chake. Chitonthozo chimenechi sichinali chachiphamaso. Chinaloŵa mkati mwa mtima wovutika wa Eliya, chikumalimbikitsa mneneriyo kupitirizabe. (Yerekezerani ndi Yesaya 40:1, 2.) Posapita nthaŵi, anayambanso ntchito yake.

Yesu Kristu mofananamo amatonthoza ndi kulimbikitsa atsatiri ake okhulupirika. Kwenikweni, Yesaya analosera za Mesiya kuti: “Ambuye Yehova . . . wanditumiza ndikamange osweka mtima, . . . ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro.” (Yesaya 61:1-3) M’nthaŵi ya moyo wake, Yesu sanasiye chikayikiro chilichonse chakuti mawu ameneŵa anasonya kwa iye. (Luka 4:17-21) Ngati mukufuna chitonthozo, sinkhasinkhani za mmene Yesu modekha ndi mwachikondi anachitira ndi anthu amene anali osweka mtima ndi ofuna thandizo. Indedi, phunziro losamala la Baibulo limapatsa chitonthozo ndi chilimbikitso chachikulu.

Kupyolera Mumpingo

Mumpingo wachikristu, ngale za chitonthozo ndi chilimbikitso zimanyezimira m’mbali zake zambiri. Mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “[Tonthozanani, NW], ndipo mangiriranani wina ndi mnzake.” (1 Atesalonika 5:11) Kodi ndi motani mmene chitonthozo ndi chilimbikitso zingapezedwere pamisonkhano yampingo?

Zoonadi, timapita ku misonkhano yachikristu makamaka kuti ‘tikaphunzitsidwe ndi Yehova,’ kukalandira malangizo ponena za iye ndi njira zake. (Yohane 6:45, NW) Chifuno cha malangizo otero ndicho kutilimbikitsa ndi kutitonthoza. Pa Machitidwe 15:32 timaŵerenga kuti: “Yuda ndi Sila, . . . anasangalatsa abale ndi mawu ambiri, nawalimbikitsa.”

Kodi chinachitikapo kwa inu kuti munapita ku msonkhano wachikristu muli wopsinjika mtima kwambiri ndi kubwerera kunyumba mulikumva bwinopo? Mwinamwake kenakake konenedwa m’nkhani, m’ndemanga, kapena m’pemphero kanakhudza mtima wanu ndi kukupatsani chitonthozo chofunika ndi chilimbikitso. Motero musaleke kupezeka pamisonkhano yachikristu.​—Ahebri 10:24, 25.

Kuyanjana ndi abale ndi alongo athu mu utumiki ndi pazochitika zina kungakhale ndi zotulukapo zofanana. M’Chihebri maverebu ambiri otanthauza “kumanga pamodzi” anatanthauzanso “nyonga” kapena “kulimbitsa”​—lingaliro lake mwachionekere ndilo lakuti zinthu zimalimba pamene zimangidwa pamodzi. Umu ndi mmenenso zimakhalira mumpingo. Timatonthozedwa, kulimbikitsidwa, inde, kulimbitsidwa, mwa kuyanjana pamodzi. Ndipo timamangidwa pamodzi ndi chikondi, chomangira cholimba koposa.​—Akolose 3:14.

Nthaŵi zina kukhulupirika kwa abale athu kapena alongo athu auzimu ndiko kumatilimbikitsa. (1 Atesalonika 3:7, 8) Nthaŵi zina ndi chikondi chimene amasonyeza. (Filemoni 7) Ndipo nthaŵi zina ndi kungogwirira ntchito pamodzi mogwirizana, polankhuzana ndi ena ponena za Ufumu wa Mulungu. Ngati mukumva kufooka ndipo mukufuna chilimbikitso ponena za utumiki, bwanji osapanga makonzedwe kuti mugwire ntchito pamodzi ndi wofalitsa Ufumu wachikulirepo kapena wachidziŵitso? Pochita zimenezo mwachionekere mudzapeza chitonthozo chachikulu.​—Mlaliki 4:9-12; Afilipi 1:27.

Kupyolera mwa “Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru”

Kodi ndani amalinganiza mbali zotonthoza za kulambira kwathu? Yesu anaika kagulu kamene anatcha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti kazipereka “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake.” (Mateyu 24:45) Bungwe la Akristu odzozedwa ndi mzimu limeneli linalipo kale mu zaka za zana loyamba C.E. Bungwe lolamulira la akulu mu Yerusalemu linatumiza makalata a malangizo ndi zitsogozo ku mipingo. Ndi zotulukapo zotani? Baibulo limasimba mmene mipingo inachitira ndi imodzi ya makalata ameneŵa: “Pamene anaŵerenga, anakondwera chifukwa cha [chilimbikitso, NW] chake.”​—Machitidwe 15:23-33.

Mofananamo, m’masiku ovuta ano otsiriza, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru akupereka chakudya chauzimu chimene chimapatsa anthu a Yehova chitonthozo chachikulu ndi chilimbikitso. Kodi inu mumadyako chakudyacho? Chimapezeka m’mabuku osindikizidwa amene kagulu ka kapolo kamapereka padziko lonse lapansi. Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! limodzinso ndi mabuku, mabrosha, ndi matrakiti amene Watch Tower Society imafalitsa adzetsa chitonthozo kwa oŵerenga osaŵerengeka.

Woyang’anira woyendayenda wina analemba kuti: “Abale athu ndi alongo ambiri amafuna kuchita zimene zili zoyenera, koma kaŵirikaŵiri amalimbana ndi kugwiritsidwa mwala, mantha, ndi malingaliro akuti sangathe kuchitapo kalikonse kudzithandiza iwo eni. Nkhani za m’makope athu zikuthandiza ambiri kulamuliranso moyo wawo ndi malingaliro. Nkhanizo zimapatsanso akulu zinthu zambiri zimene angachite m’malo mwa kungopereka chilimbikitso chabe.”

Gwiritsirani ntchito mokwanira mabuku ochokera kwa kagulu ka kapolo. Magazini, mabuku, ndi zofalitsa zina zapanthaŵi yake zingatithandize kupeza chitonthozo pamene zinthu zivuta. Ndipo ngati mufunikira kulimbikitsa wochita tondovi, gwiritsirani ntchito chidziŵitso cha Malemba chopezeka m’magazini ameneŵa. Nkhani zake zimalembedwa mosamala kwambiri, kaŵirikaŵiri pambuyo pa milungu kapena miyezi yambiri ya kufufuza kwakuya, kuŵerenga, ndi pemphero. Uphungu wake ngwozikidwa pa Baibulo, woyengedwa ndi woona. Ena aziona kukhala zothandiza kwambiri kuŵerenga nkhani imodzi kapena ziŵiri zoyenera pamodzi ndi wovutika maganizoyo. Zimenezi zingamtonthoze ndi kumlimbikitsa kwambiri.

Tinene kuti mwapeza ngale za mtengo wake, kodi mugazibise, kapena kodi mungagaŵane china cha chumacho mooloŵa manja ndi ena? Khalani ndi chonulirapo cha kutonthoza ndi kulimbikitsa abale anu ndi alongo mumpingo. Ngati mumamangirira m’malo mogwetsa, kuyamikira m’malo mosuliza, kulankhula ndi “lilime la ophunzira” m’malo mwa kulankhula “mwasontho ngati kupyoza kwa lupanga,” mukhoza kukhala wothandiza m’moyo wa ena. (Yesaya 50:4; Miyambo 12:18) Indedi, inu mwini mwachionekere mudzaonedwa ngati ngale​—munthu wotonthoza zedi ndi wolimbikitsa!

[Bokosi patsamba 20]

Chitonthozo kwa Ochifuna

AMBIRI athirira ndemanga pa mmene nkhani zina za mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! zakulitsira unansi wawo waumwini ndi Yehova. Mkazi wina anati: “Nditaŵerenga nkhani imeneyi, ndinamva ngati kuti Yehova ndi mphamvu yake yonse ndi ukulu wake wonse anali pamenepo ndi ine. Ndinamuona kukhala munthu weniweni.” Kalata ina inati: “Mitima yathu ndi maganizo athu ponena za Yehova zasinthidwa kwambiri kwakuti sitilinso monga kale. Zili ngati kuti wina wake anayeretsa magalasi athu, ndipo tsopano tikuona zilizonse bwinobwino.”

Ena amalemba kunena mmene magaziniwo amawathandizira kuchita ndi mavuto kapena zitokoso zosiyanasiyana, motero akumawatsimikiza za chikondi cha Yehova pa iwo. Woŵerenga wina ananena kuti: “Zikomo kwambiri potionetsa kachiŵirinso mmene Yehova amasamalira ndi kukonda anthu ake.” Mkazi wina ku Japan amene anafedwa mwana anati ponena za nkhani za mu Galamukani! pankhaniyo: “Ukulu wa chifundo cha Mulungu unatuluka m’masamba ake, ndipo ndinalira kwambiri. Ndaika makope ameneŵa pa malo poti ndingawaŵerenge nthaŵi iliyonse pamene ndimva chisoni ndi pamene ndisungulumwa.” Mkazi wina yemwe anali kulira maliro analemba kuti: “Nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi brosha lakuti “Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira” zandipatsa nyonga imene ndinakufunikira kuti ndipirire chisoni changa.”

Malemba Oyera ndiwo magwero aakulu a chitonthozo. (Aroma 15:4) Nsanja ya Olonda ndi magazini inzake Galamukani! amatsatira Baibulo monga maziko ake. Chifukwa cha zimenezi, magazini ameneŵa akhala otonthoza ndi olimbikitsa kwa oŵerenga ake.

[Chithunzi patsamba 23]

Mulungu wachitonthozo chonse alinso Wakumva pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena