Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 2/15 tsamba 5-7
  • Kutheratu kwa Chiwawa—Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutheratu kwa Chiwawa—Motani?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchiyani Chimene Chingachitidwe?
  • Mphamvu ya Mawu a Mulungu
  • Mkupiti Umene Umathetsa Chiwawa
  • Phunziro Lofunika
  • Kodi Zachiwawa Zidzatha Padzikoli?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Kodi Mulungu Amachiona Bwanji Chiwawa?
    Galamukani!—2002
  • Chiwawa
    Galamukani!—2015
  • Chiwawa—Mapeto Akuwonekera!
    Galamukani!—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 2/15 tsamba 5-7

Kutheratu kwa Chiwawa​—Motani?

POFUNA kuletsa kuwanda kwa chiwawa, mizinda yambiri mu United States inayesa lingaliro lina latsopano​—ndalama kapena katundu mosinthanitsa ndi mfuti popanda kuimbidwa mlandu. Chotulukapo chake? Mwachitsanzo, mzinda wa St. Louis unasonkhanitsa mfuti 8,500, pa mtengo wa $341,000. M’programu yofanana nayo ku New York City anasonkhanitsa mfuti zoposa chikwi.

Kodi zonsezi zinali ndi chiyambukiro chotani pa upandu? Mwachisoni, chochepa kwambiri. Kupha munthu ndi mfuti kunafikira chiŵerengero chapamwamba koposa mu St. Louis chaka chotsatirapo. Mu New York City, mudakali mfuti zoyerekezeredwa kukhala mamiliyoni aŵiri m’manja mwa anthu wamba. Mu United States, muli mfuti pafupifupi mamiliyoni 200 zimene zili za anthu wamba, pafupifupi mwamuna, mkazi, ndi mwana aliyense akumakhala ndi yake. M’maiko ena, chiwawa cha mfuti chikuwonjezereka pamlingo wochititsa mantha. Ku Britain “pakati pa 1983 ndi 1993, chiŵerengero cha kuswa lamulo cholembedwa ndi apolisi chimene mfuti zinaloŵetsedwamo chanatsala pang’ono kuŵirikiza kaŵiri, kufika pa 14,000,” ikutero The Economist. Ngakhale kuti mlingo wa kupha munthu uli wotsikirapo, pali pafupifupi miliyoni imodzi ya mfuti zosungidwa mopanda lamulo m’dzikolo.

Ndithudi, kuchepetsa kulikonse chiŵerengero chowopsa chimenecho kuli sitepe yachipambano. Komabe, njira zonga zimene zafotokozedwa poyambapo sizimafika pa phata lenileni la zochititsa chiwawa. Kodi zochititsazo nchiyani? Zochititsa zambiri zasonyezedwa, koma zoŵerengeka nzimene zili zazikulu. Kupanda bata ndi mwambo kwa banja kwachititsa achichepere ambiri kugwirizana ndi timagulu tachiwawa pokhumba kugwirizana ndi ena. Chikoka cha kupeza phindu lalikulu chimasonkhezera ambiri kutembenukira pa chiwawa. Kupanda chilungamo kumasonkhezera ena kulimbana ndi mkhalidwewo mwachiwawa. Kunyadira dziko, fuko, kapena udindo m’moyo kumachititsa anthu kunyalanyaza mavuto a ena. Zimenezi ndizo zochichititsa zozika mizu kwambiri zimene zilibe njira zosavuta zozithetsera.

Kodi Nchiyani Chimene Chingachitidwe?

Apolisi ambiri, zilango za m’ndende zouma, kuika ziletso pa mfuti, chilango cha imfa​—zonsezi zalingaliridwa ndi kuyesedwa monga njira zoletsera upandu ndi chiwawa. Zapereka chipambano chosiyanasiyana, koma chomvetsa chisoni nchakuti chiwawa chikuchitikabe pakati pathu. Chifukwa ninji? Chili chifukwa chakuti njira zimenezi zimangothetsa zizindikiro zake chabe.

Komanso, akatswiri ambiri amalingalira kuti mfungulo ya kuthetsa chiwawa ndiyo maphunziro. Pamene kuli kwakuti lingaliro limeneli nlomveka, tiyenera kuzindikira kuti chiwawa sichimachitidwa kokha m’maiko amene ali ndi maphunziro ochepa. Kwenikweni, zichita ngati kuti maiko ena amene muli chiwawa chochuluka alinso aja amene ali ndi miyezo yapamwamba kwambiri ya maphunziro. Mposavuta kuona kuti chimene chikufunika si maphunziro chabe koma mtundu woyenera wa maphunziro. Kodi umenewo ungakhale mtundu wotani? Kodi pali munthu amene akhoza kuphunzitsa anthu kukhala okonda mtendere ndi owongoka mtima?

‘Ine ndine Yehova, Mulungu wako, Amene ndikuphunzitsa kupindula, Amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.’ (Yesaya 48:17, 18) Kodi Yehova Mulungu amaphunzitsa bwanji anthu kukhala okonda mtendere ndi chilungamo? Kwenikweni kudzera m’Mawu ake, Baibulo.

Mphamvu ya Mawu a Mulungu

Baibulo silili konse kusonkhanitsidwa kwa nthano zakale chabe ndi miyambi zimene zili zakutha ntchito ndi zopanda pake. Lili ndi njira ndi malingaliro zochokera kwa Mlengi wa anthu, amene, m’lingaliro lake lapamwambamwamba, amadziŵa bwino kwambiri chibadwa cha anthu kuposa wina aliyense. “Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu,” akutero Yehova Mulungu.​—Yesaya 55:9.

Pa chifukwa chimenechi mtumwi Paulo amachitira umboni kuti “mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugaŵira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Ahebri 4:12) Inde, Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yofika ndi kukhudza mtima wa munthu ndi kusintha maganizo ake ndi khalidwe. Kodi izi si zimene zikufunika kuti anthu asinthe njira zawo zachiwawa lerolino?

Mboni za Yehova, tsopano zimene zili pafupifupi mamiliyoni asanu m’maiko oposa 230, zimapereka umboni weniweni wakuti ndithudi, Mawu a Mulungu, ali ndi mphamvu yosanduliza moyo kukhala wabwino kwambiri. Pakati pawo pali anthu a mumtundu uliwonse, chinenero, ndi fuko. Akuchokeranso m’mikhalidwe yonse ya moyo ndi zitaganya. Ena a iwo kale, anali ndi moyo wachiwawa ndi wovuta. Koma m’malo kwa kulola zochititsa zimenezo kusonkhezera nkhwidzi, mpikisano, tsankhu, ndi udani pakati pawo, aphunzira kuthetsa zopinga zimenezi ndipo akhala anthu okonda mtendere ndi ogwirizana padziko lonse. Kodi nchiyani chimene chatheketsa zimenezi?

Mkupiti Umene Umathetsa Chiwawa

Mboni za Yehova zili zodzipereka kuthandiza ena kupeza chidziŵitso cholongosoka cha chifuno cha Mulungu monga momwe chasonyezedwera m’Mawu ake, Baibulo. Ku ngodya iliyonse ya dziko lapansi, izo zikufunafuna awo amene akufuna kuphunzira njira za Yehova ndi kuphunzitsidwa ndi iye. Zoyesayesa zawo zikubala zipatso. Chotulukapo cha mkupiti umenewu wa maphunziro nchakuti ulosi waukulu ukukwaniritsidwa.

Zaka pafupifupi 2,700 zapitazo, mneneri Yesaya anauziridwa kulemba kuti: “Padzakhala masiku otsiriza, kuti . . . anthu ambiri adzamka, nati, Tiyeni tikwere kumka ku phiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.”​—Yesaya 2:2, 3.

Kukhala ophunzitsidwa ndi Yehova ndi kuyenda m’njira zake kungachititse masinthidwe odabwitsa m’miyoyo ya anthu. Amodzi a masinthidwe ameneŵa anenedweratu mu ulosi umodzimodziwu: “Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:4) Anthu ambiri aŵerenga lemba limeneli. Kwenikweni, vesi limeneli lazokotedwa pakhoma la United Nations Plaza ku New York City. Ndilo chikumbutso cha zimene United Nations ikuyesa kupeza koma yalephera. Kuchotsedwa kwa nkhondo ndi chiwawa kumeneku sikudzachitidwa ndi gulu landale lililonse lopangidwa ndi anthu. Ndicho chinthu chimene Yehova Mulungu yekha akhoza kuchita. Kodi adzachita zimenezi motani?

Mwachionekere si onse amene adzalabadira chiitano cha ‘kukwera ku phiri la Yehova’ ndi ‘kuphunzitsidwa za njira zake’ ndi ‘kuyenda m’mayendedwe ake’; ndiponso si onse amene adzafunitsitsa ‘kusula malupanga awo kukhala zolimira, ndi nthungo zawo kukhala anangwape.’ Kodi nchiyani chimene Yehova adzachita kwa otero? Sadzasiya chitsegukire khomo la mwaŵiwo kapena kuwayembekezera kusintha. Kuti athetse chiwawa, Yehova adzawononganso awo amene amaumirira njira zawo zachiwawa.

Phunziro Lofunika

Zimene Mulungu anachita m’tsiku la Nowa zimapereka phunziro lachenjezo kwa ife lerolino. Nkhani ya Baibuloyo imasonyeza mtundu wa anthu amene analiko panthaŵiyo: “Dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.” Pa chifukwa chimenechi, Mulungu anadziŵitsa Nowa kuti: “Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzawononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.”​—Genesis 6:11, 13.

Tiyenera kuzindikira mfundo imodzi yofunika. Pamene Mulungu anabweretsa Chigumula pa mbadwo umenewo, anapulumutsa Nowa ndi banja lake. Chifukwa ninji? Baibulo limayankha kuti: “Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m’mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.” (Genesis 6:9; 7:1) Ngakhale kuti si onse amene anakhalako panthaŵiyo amene anali achiwawa, Nowa yekha ndi banja lake “anayendabe ndi Mulungu.” Chifukwa cha zimenezo anapulumuka pamene dziko lachiwawalo linawonongedwa.

Pamene tikuona kachiŵirinso dziko lapansi ‘likudzala ndi chiwawa,’ tingakhulupirire kuti Mulungu akuona. Monga momwe anachitira m’tsiku la Nowa, chotero adzachitapo kanthu posachedwa ndi kuthetsa chiwawa​—kwamuyaya. Koma iye adzaperekanso njira yopulumukira kwa aja amene tsopano akuphunzira ‘kuyenda ndi Mulungu woona,’ aja amene akulabadira mkupiti wake waukulu wa maphunziro a mtendere.

Kupyolera mwa wamasalmo, Yehova akupereka chitsimikizo ichi: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—Salmo 37:10, 11.

Mboni za Yehova zidzakhala zachimwemwe kuphunzira nanu Baibulo kotero kuti mugwirizane ndi awo amene amati: “Tiyeni tikwere kumka ku phiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.” (Yesaya 2:3) Mwa kuchita motero, mungakhale pakati pa awo amene adzaona mapeto a kuipa konse ndi chiwawa. Mungathe ‘kukondwera nawo mtendere wochuluka.’

[Mawu a Chithunzi patsamba 5]

Reuters/​Bettman

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena