Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 4/1 tsamba 6-8
  • Chitani Chikumbutso Moyenera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitani Chikumbutso Moyenera
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Moyenera​—Motani?
  • Kuzindikira Kukufunika
  • N’chifukwa Chiyani Timachita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Mgonero wa Ambuye Uli ndi Phindu Lanji kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Chifukwa Chake Mgonero wa Ambuye Uli ndi Tanthauzo kwa Inu
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Mgonero wa Ambuye Tiziukumbukira Motani?
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 4/1 tsamba 6-8

Chitani Chikumbutso Moyenera

ANALI madzulo a Nisan 14, 33 C.E., pamene Yesu anayambitsa Chikumbutso.a Anali atangotsiriza kumene kusunga Paskha ndi atumwi ake 12, chotero timatsimikiza za detilo. Atatulutsa womperekayo, Yudase, Yesu “anatenga mkate, ndipo pamene anadalitsa, ananyema, napereka kwa iwo, kuti, Tengani; thupi langa ndi ili. Ndipo anatenga chikho, ndipo pamene adayamika, anapereka kwa iwo; ndipo iwo onse anamweramo. Ndipo Iye anati kwa iwo, Ichi ndi mwazi wanga wa chipangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri.”​—Marko 14:22-24.

Yesu analamula ophunzira ake kukumbukira imfa yake chifukwa cha kufunika kwake. (Luka 22:19; 1 Akorinto 11:23-26) Nsembe yake yokhayo ndiyo inali kudzaombola anthu pa themberero la choloŵa cha uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12; 6:23) Mkate ndi vinyo amene anagwiritsira ntchito zinali zizindikiro za thupi lake langwiro ndi mwazi wake. Podziŵa deti lake loyamba, tingathe kusunga chochitikacho patsiku lake chaka chilichonse, monga momwe anachitira ndi Paskha wachiyuda. Koma tiyenera kuchita motero moyenera. Chifukwa ninji?

Mtumwi Paulo ananena kuti awo amene amadya zizindikiro za mkate ndi vinyo ‘adzalalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza iye.’ (1 Akorinto 11:26) Motero cholinga cha chochitikacho chinali kulingalira za imfa ya Yesu ndi tanthauzo lake kwa anthu. Chochitikacho chinali chapadera kwambiri, nthaŵi ya kulingalira za ukoma wa Mulungu ndi chiyamikiro chimene tiyenera kukhala nacho kwa Yehova ndi Mwana wake. (Aroma 5:8; Tito 2:14; 1 Yohane 4:9, 10) Chotero, Paulo anachenjeza kuti: “Chifukwa chake yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.”​—1 Akorinto 11:27.

Moyenera​—Motani?

Mwachionekere, Mulungu sangakondwere ngati ife tichitira chipongwe chochitikacho mwa kuchita zinthu zokayikitsa kapena mwa kutengera miyambo yachikunja. (Yakobo 1:27; 4:3, 4) Zimenezi sizikulola zochitika zotchuka za nthaŵi ya Isitala. Potsatira lamulo la Yesu lakuti “chitani ichi chikumbukiro changa,” tidzafuna kusunga Chikumbutso monga momwe anachiyambitsira. (Luka 22:19; 1 Akorinto 11:24, 25) Zimenezi sizimaloleza zokongoletsa zimene matchalitchi a Dziko Lachikristu awonjezerapo. New Catholic Encyclopedia ikuvomereza kuti “Misa yamakono imasiyana kwambiri ndi mwambo wofeŵa kwambiri umene Yesu ndi Atumwi Ake anachita.” Ndipo mwa kuchita Misa mobwerezabwereza, ngakhale tsiku ndi tsiku, Dziko Lachikristu lapatuka pa zimene Yesu analingalira ndipo laipanga kukhala chochitika wamba.

Paulo analembera Akristu a ku Korinto ponena za kudya mosayenera chifukwa chakuti vuto lonena za Chakudya Chamadzulo cha Ambuye linabuka. Ena sanalemekeze kupatulika kwake. Anabweretsa mgonero wawo ndi kuudya msonkhanowo usanayambe kapena mkati mwake. Kaŵirikaŵiri iwowo anadya ndi kumwa mopambanitsa. Zimenezi zinawapangitsa kukhala ndi maganizo oziya ndi kuwagodomalitsa. Mwa kusakhala ogalamuka mwamaganizo ndi mwauzimu, ‘sakanazindikira thupi’ ndipo motero anakhala ‘ochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.’ Izi zidakali choncho, aja amene anali asanadye mgonero anali anjala ndipo nawonso anacheukitsidwa. Kwenikweni panalibe aliyense amene anali mu mkhalidwe wa kudya zizindikiro moyamikira ndi kuzindikira mokwanira za kuwopsa kwa chochitikacho​—kuti chochitikacho chinali cha kukumbukira imfa ya Ambuye. Zimenezi zinawachititsa kupatsidwa chiweruzo, pakuti anasonyeza kupanda ulemu, kapena chipongwe.​—1 Akorinto 11:27-34.

Kuzindikira Kukufunika

Ena adya zizindikiro za Chikumbutso ngakhale kuti pambuyo pake, azindikira kuti sanayenere kuchita motero. Aja amene amadya moyenera zizindikiro za Chikumbutso asankhidwa ndi Mulungu ndipo ali ndi umboni wa mzimu wa Mulungu pankhaniyo. (Aroma 8:15-17; 2 Akorinto 1:21, 22) Chimene chimawapanga kukhala oyenerera si chosankha chawo kapena kuganiza kwawo. Mulungu waika chiŵerengero cha aja amene adzalamulira ndi Kristu kumwamba chokwanira 144,000, chiŵerengero chaching’ono kwambiri pochiyerekezera ndi awo onse amene akupindula ndi dipo la Kristu. (Chivumbulutso 14:1, 3) Kusankhako kunayambira m’tsiku la Yesu, motero lerolino pali akudya zizindikiro oŵerengeka okha. Ndipo pamene afa, chiŵerengero chimatsika.

Kodi nchifukwa ninji munthu angadye zizindikiro molakwa? Mwina chingakhale chifukwa cha malingaliro ake akale achipembedzo​—akuti anthu okhulupirika onse amapita kumwamba. Kapena mwina chingakhale chifukwa cha chikhumbo kapena dyera​—lingaliro lakuti munthuyo ali woyenerera kwambiri kuposa ena​—ndi kufuna kudziŵika. Mwina chingakhale chifukwa cha kukhudzidwa mtima kwambiri chifukwa cha mavuto aakulu kapena tsoka limene limachititsa munthu kusafunanso moyo wapadziko lapansi. Mwinanso chingakhale chifukwa cha kuyanjana kwambiri ndi winawake amene ali ndi chiyembekezo chakumwamba. Tonsefe tiyenera kukumbukira kuti chosankha chimapangidwa ndi Mulungu yekha, osati ife. (Aroma 9:16) Chotero ngati munthu, ‘atadziyesa,’ apeza kuti sanafunikiredi kudya zizindikiro, ayenera kuleka tsopano.​—1 Akorinto 11:28.

Chiyembekezo chimene Mulungu waikira anthu ochuluka ndicho chija cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. Limenelo ndi dalitso lalikulu loliyembekezera, limenenso limatikopa mosavuta. (Genesis 1:28; Salmo 37:9, 11) Ndi padziko lapansi pamene anthu okhulupirika adzagwirizana ndi okondedwa awo oukitsidwa ndi pamenenso adzakumana ndi anthu olungama akale, onga Abrahamu, Sara, Mose, Rahabi, Davide, ndi Yohane Mbatizi​—iwo onse amene anafa Yesu asanatsegule njira ya moyo wakumwamba.​—Mateyu 11:11; yerekezerani ndi 1 Akorinto 15:20-23.

Awo okhala ndi ziyembekezo za padziko lapansi amasunga Chakudya Chamadzulo cha Ambuye moyenerera mwa kufikapo kwawo ndi kumvetsera mosamalitsa, ngakhale kuti sadya mkate ndi kumwa vinyo. Nawonso amapindula ndi nsembe ya Kristu, imene imawakhozetsa kuima pamaso pa Mulungu moyanjidwa. (Chivumbulutso 7:14, 15) Pamene amvetsera nkhani yake, chiyamikiro chawo cha zinthu zopatulika chimalimbitsidwa, ndipo chikhumbo chawo cha kukhalabe ogwirizana ndi anthu a Mulungu kulikonse chimakula.

Chaka chino, pa Lachiŵiri April 2, dzuŵa litaloŵa, Chikumbutsocho chidzachitidwa m’mipingo yonse ya Mboni za Yehova yoposa 78,000 padziko lonse. Kodi mudzakhalapo?

[Mawu a M’munsi]

a Tsiku lachiyuda linkayamba madzulo. Malinga ndi kalenda yathu, Nisani 14 ameneyo anayamba madzulo pa Lachinayi, March 31, kufikira pakuloŵa kwa dzuŵa Lachisanu madzulo, April 1. Chikumbutso chinayambitsidwa pa Lachinayi madzulo, ndipo imfa ya Yesu inachitika pa Lachisanu masana a tsiku lachiyuda lomwelo. Anauka patsiku lachitatu, Sande mmamaŵa.

[Chithunzi patsamba 8]

Mboni za Yehova zimachita Chikumbutso kamodzi chaka chilichonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena