Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapeza makope a Nsanja ya Olonda aposachedwapa kukhala athandizo kwa inu? Pamenepo bwanji osayesa kukumbukira zinthu kwanu ndi mafunso otsatirawa:
◻ Kodi ndi phunziro lotani limene timapeza m’chiwonongeko cha Aamoni? (Zefaniya 2:9, 10)
Yehova samapeputsa kubwezera udani pa kukoma mtima kwake, ndipo panthaŵi yake, adzachitaponso kanthu, monga momwe anachitira nthaŵi zakale. (Yerekezerani ndi Salmo 2:6-12.)—12/15, tsamba 10.
◻ Kodi ndi m’njira ziti zimene Akristu alili ndi mtendere?
Yoyamba, ali ndi “mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye [wawo] Yesu Kristu.” (Aroma 5:1) Yachiŵiri, ali ndi mtendere pakati pawo mwa kukulitsa “nzeru yochokera kumwamba,” imene “iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere.” (Yakobo 3:17)—1/1, tsamba 11.
◻ Kodi Mawu a Mulungu amafanizidwa ndi zinthu zina ziti, ndipo zimenezi zimatithandiza motani?
Mawu a Mulungu amafanizidwa ndi mkaka wopatsa thanzi, chakudya chotafuna, madzi otsitsimula ndi oyeretsa, kalirole, ndi lupanga lakuthwa. Kuzindikira tanthauzo la mawu ameneŵa kumathandiza mtumiki kugwiritsira ntchito Baibulo mwaluso.—1/1, tsamba 29.
◻ Kodi maphunziro oyenera akusukulu ayenera kutithandiza kuchita chiyani?
Kuŵerenga bwino, kulemba bwino, kukula mwamaganizo ndi mwamakhalidwe, ndi kuphunzira ntchito kaamba ka moyo watsiku ndi tsiku ndi utumiki wopatulika wogwira mtima.—2/1, tsamba 10.
◻ Kodi tingapeze phunziro lofunika lotani kwa Yesu ponena za maphunziro?
Maphunziro ayenera kugwiritsiridwa ntchito, osati pa kudzipatsa thamo, koma kutamanda Mlangizi wamkulukulu, Yehova Mulungu. (Yohane 7:18)—2/1, tsamba 10.
◻ Kodi Ufumu wa Mulungu nchiyani?
Ufumuwo ndiwo boma lakumwamba loyambitsidwa ndi Mulungu limene lidzakwaniritsa chifuniro cha Mulungu cha kuchotsa ziyambukiro za uchimo ndi imfa ndi kubwezeretsa mikhalidwe yolungama padziko lapansi. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 11:15; 12:10)—2/1, tsamba 16.
◻ Kodi Baibulo limapereka motani maphunziro ofunika a kuthetseratu chiwawa?
Yehova, kupyolera m’Mawu ake, Baibulo, amaphunzitsa anthu kukhala okonda mtendere ndi chilungamo. (Yesaya 48:17, 18) Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yofika ndi kukhudza mtima wa munthu, akumasintha kuganiza ndi khalidwe lake. (Ahebri 4:12)—2/15, tsamba 6.
◻ Kodi tinganene motani kuti ulosi wa Yesaya chaputala 35 uli ndi kukwaniritsidwa kutatu?
Ulosi wa Yesaya unakwaniritsidwa choyamba pamene Ayuda anabwera kuchokera ku ukapolo wa ku Babulo mu 537 B.C.E. Ukukwaniritsidwa mwauzimu lerolino kuyambira pa kumasulidwa kwa Israyeli wauzimu ku ukapolo wa Babulo Wamkulu. Ndipo udzakwaniritsidwa kachitatu mogwirizana ndi lonjezo lotsimikizira la Baibulo lakuti padzakhala mikhalidwe yeniyeni ya paradaiso padziko lapansi. (Salmo 37:10, 11; Chivumbulutso 21:4, 5)—2/15, tsamba 17.
◻ Kodi ndi motani mmene chikondwerero chaumwini cha Mulungu mwa anthu chinasonyezedwera ndi zozizwitsa zochitidwa ndi Mwana wake, Yesu?
Popeza kuti Yesu “sakhoza . . . kuchita kanthu payekha, koma chimene aona Atate achichita,” chifundo chake chimatipatsa chinthu chogwira mtima cha nkhaŵa ya Yehova pa aliyense wa atumiki ake. (Yohane 5:19)—3/1, tsamba 5.
◻ Kodi mawu a Yesu akuti “manda achikumbukiro” ogwiritsiridwa ntchito pa Yohane 5:28, 29, NW amapereka lingaliro lotani?
Liwu lachigiriki lakuti mne·mei’on (manda achikumbukiro) logwiritsiridwa ntchito panopa likupereka lingaliro lakuti Yehova amakumbukira mbiri ya munthu amene wafa, kuphatikizapo chibadwa chake ndi zikumbukiro zake zonse. Zimenezi zimapereka umboni wamphamvu wakuti Mulungu amasamala za munthu aliyense payekha!—3/1, tsamba 6.
◻ Kodi ndi uthenga wachenjezo wotani mu ulosi wa Zefaniya umene uli wothandiza kwa ife?
Lerolino si nthaŵi ya kulola zikayikiro kuzika mizu mumtima mwathu ndi kunyalanyaza kudza kwa tsiku la Yehova. Ndiponso, tiyenera kukhala maso pa ziyambukiro zofoola za mphwayi. (Zefaniya 1:12, 13; 3:8)—3/1, tsamba 17.
◻ Kodi nchifukwa ninji kukhulupirika kulinga kwa Mulungu kuli kovuta?
Chifukwa chakuti kukhulupirikako kumawombana ndi zikhoterero zadyera zimene timalandira kwa makolo athu. (Genesis 8:21; Aroma 7:19) Makamakanso, Satana ndi ziŵanda zake ali otsimikizira kutichititsa kukhala osakhulupirika kwa Mulungu. (Aefeso 6:12; 1 Petro 5:8)—3/15, tsamba 10.
◻ Kodi ndi m’mbali zinayi ziti zimene tiyenera kupambana chiyeso cha kukhulupirika, ndipo nchiyani chimene chidzatithandiza kuchita motero?
Mbali zinayi zimenezi ndizo kukhulupirika kulinga kwa Yehova, ku gulu lake, ku mpingo, ndi kwa anzathu a muukwati. Thandizo limodzi poyang’anizana ndi ziyeso zimenezi ndilo kuzindikira kuti chiyeso cha kukhulupirika chili chogwirizana ndi kutsimikiziritsa uchifumu wa Yehova.—3/15, tsamba 20.
◻ Kodi tingapeze phunziro lotani m’chochitika cha Davide poyesa kupititsa likasa lachipangano ku Yerusalemu? (2 Samueli 6:2-7)
Davide ananyalanyaza malangizo amene Yehova anapereka ponena za kunyamulidwa kwa Likasa, ndipo zimenezi zinadzetsa tsoka. Phunziro lake nlakuti sitiyenera kuimba mlandu Yehova wa mavuto amene amachitika pamene tinyalanyaza malamulo ake achimvekere. (Miyambo 19:3)—4/1, masamba 28, 29.