Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 6/1 tsamba 4-7
  • Pamene Sikudzakhalanso Tsankhu!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Sikudzakhalanso Tsankhu!
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Alibe Tsankhu
  • Chisonkhezero cha Baibulo
  • Kuchotsa Zopinga za Tsankhu
  • Mmene Mungachitire
  • “Sizidzaipitsa”
  • Kodi Tsankho Lidzatha Liti?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Tsankho Likuchitika Padziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Ndinu Wochitiridwa Tsankhu?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Mapeto a Tsankho
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 6/1 tsamba 4-7

Pamene Sikudzakhalanso Tsankhu!

MONGA momwe kwasimbidwira, panthaŵi ina wasayansi Albert Einstein ananena kuti m’dziko lino lomvetsa chisoni, nkovuta kwambiri kuthetsa tsankhu koposa kugaŵa atomu. Mofananamo, Edward R. Murrow, mtolankhani amene anakhala wotchuka mkati mwa Nkhondo Yadziko II ndipo pambuyo pake amene anakhala mkulu wa Information Agency ya United States, ananena kuti “palibe munthu amene angathetse tsankhu​—amangolizindikira chabe.”

Kodi ndemanga zimenezi zikumveka kukhala zoona? Kodi kuthetsa kusankhana ndi ufuko nkosatheka? Kodi Mulungu amalingalira bwanji ponena za tsankhu?

Mulungu Alibe Tsankhu

Baibulo limatsutsa tsankhu. (Miyambo 24:23; 28:21) Limanena kuti “nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, yosadzikometsera pamaso.” (Yakobo 3:17) Nzeru imeneyo inagogomezeredwa kwa oweruza mu Israyeli wakale. “Musamachita chisalungamo pakuweruza mlandu,” analangizidwa motero. “[Usamachitire tsankhu, NW] wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka.”​—Levitiko 19:15.

Kanenedwe kamphamvu ka Baibulo motsutsa kukondera kapena tsankhu kanagogomezeredwa ndi Yesu Kristu ndi atumwi ake Petro ndi Paulo. Yesu anali wopanda tsankhu kulinga kwa aja amene anali “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Iye anaphunzitsa kuti: “Musaweruze monga mwamaonekedwe, koma weruzani chiweruziro cholungama.”​—Yohane 7:24.

Petro ndi Paulo amatitsimikizira kuti Yehova Mulungu mwiniyo alibe tsankhu. Petro ananena kuti: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Mtumwi Paulo amatiuza kuti: “Mulungu alibe tsankhu.”​—Aroma 2:11.

Chisonkhezero cha Baibulo

Baibulo lili ndi mphamvu ya kusintha maumunthu a awo amene limawatsogolera. Ahebri 4:12 amati: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita.” Ndi thandizo la Yehova munthu watsankhu angathedi kusintha kaganizidwe kake ndi kukhala wopanda tsankhu pochita ndi ena.

Mwachitsanzo, tengani nkhani ya Saulo wa ku Tariso. Malinga ndi mmene Baibulo limasimbira, panthaŵi ina iyeyo anatsutsa mwachiwawa mpingo wachikristu chifukwa chakuti ankatsatira miyambo yachipembedzo yamphamvu. (Machitidwe 8:1-3) Anakhulupirira kotheratu mwambo wachiyuda kuti Akristu onse anali ampatuko ndi adani a kulambira koona. Tsankhu lake linamchititsa kuchirikiza kupha Akristu. Baibulo limanena kuti anali “kupumira pa akuphunzira a Ambuye kuwopsa ndi kupha.” (Machitidwe 9:1) Pamene anali kuchita zimenezo, anaganiza kuti anali kupereka utumiki wopatulika kwa Mulungu.​—Yerekezerani ndi Yohane 16:2.

Komabe, Saulo wa ku Tariso anatha kuchotsa tsankhu lake loipitsitsalo. Iyeyo anakhaladi Mkristu! Pambuyo pake, monga Paulo, mtumwi wa Yesu Kristu, analemba kuti: “Kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira.”​—1 Timoteo 1:13.

Si Paulo yekha amene anapanga masinthidwe aakulu otero m’kaganizidwe kake. M’kalata yake yomka kwa Tito, mlaliki mnzake, Paulo analangiza Akristu kuti “asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andewu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse. Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa zamitundumitundu, okhala m’dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.”​—Tito 3:2, 3.

Kuchotsa Zopinga za Tsankhu

Lerolino, Akristu enieni amayesayesa kutsatira uphungu umenewo. Amafuna kupeŵa kuweruza anthu chifukwa cha maonekedwe akunja. Zimenezi zimawaletsa ‘kuchitira mwano’ ena. Amakhala ndi ubale wapadziko lonse umene susamala za dziko, mtundu, ndi malire a fuko a dzikoli.

Talingalirani za chokumana nacho cha Henrique, Mbrazilu wakhungu lakuda. Pokhala iye mwiniyo wochitiridwa tsankhu, anakulitsa udani waukulu kulinga kwa anthu achiyera. Akufotokoza kuti: “Mboni ziŵiri za khungu loyera zinafika panyumba panga kudzalankhula za dzina la Mulungu. Poyamba sindinafune kumvetsera chifukwa chakuti sindinkadalira anthu achiyera. Komano posapita nthaŵi ndinaona kuti uthenga wawo unamveka kukhala wa choonadi. Ndiyeno, ndinavomereza phunziro la Baibulo. Funso loyamba limene ndinali nalo linali lakuti, ‘Kodi m’tchalitchi mwanu muli anthu akuda ambiri?’ Iwo anayankha kuti, ‘Inde.’ Ndiyeno anandisonyeza chithunzithunzi chotsirizira m’buku la Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo,a chosonyeza achichepere a mafuko osiyanasiyana. Pakati pawo panali mnyamata wachikuda, ndipo zimenezi zinandilimbikitsa. Pambuyo pake ndinafika pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, pamene ndinaonapo anthu a mafuko osiyanasiyana akumalemekezana. Zimenezi zinali zofunika kwambiri kwa ine.”

Tsopano, monga mmodzi wa Mboni za Yehova, Henrique ngokondwa kukhala mu ubale wachikristu weniweni. Amadziŵa bwino kuti thamo lake silimapita kwa munthu aliyense. Akunena kuti: “Lero ndili wothokoza Yehova ndi Yesu kaamba ka zonse zimene andichitira. Ndimagwira ntchito ndi mamiliyoni ambiri a atumiki okhulupirika a Yehova a mafuko onse, maonekedwe, ndi makulidwe, ogwirizana pa chifuno chimodzi.”

Pamene Dario anali kukula, anamchitiranso tsankhu. Pausinkhu wa zaka 16 zakubadwa, anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iye anati: “Pakati pa Mboni, ndapeza kuti palibe malingaliro a kudzikweza chifukwa cha fuko.” Anachita chidwi ndi mkhalidwe wa chikondi chenicheni. Makamaka iyeyo anaona kuti anthu a mafuko osiyanasiyana anatumikira m’malo a mathayo mumpingo. Nthaŵi iliyonse pamene asonyezedwa tsankhu linalake ndi anthu osakhala a mumpingo, Dario amakumbukira kuti Yehova amakonda anthu a mitundu yonse, mafuko, ndi malirime.

Mmene Mungachitire

Ife tonse timakonda kuchitiridwa mwaulemu. Nchifukwa chake kusonyezedwa tsankhu kuli chiyeso chovuta kupirira. Mpingo wachikristu sumatitetezera pa mikhalidwe yonse ya tsankhu la dziko loipali. Malinga ngati Satana Mdyerekezi akulamulirabe zochitika za dziko, padzakhala zisalungamo. (1 Yohane 5:19) Chivumbulutso 12:12 chimatichenjeza kuti: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” Cholinga chake sichili cha kungovutitsa chabe. Iye amayerekezeredwa ndi nyama yolusa. Mtumwi Petro amatiuza kuti: “Mdani wanu Mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.”​—1 Petro 5:8.

Baibulo limatiuzanso kuti: “Potero mverani Mulungu; koma kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.” (Yakobo 4:7) Thandizo labwino lochitira ndi tsankhu ndilo kuyang’ana kwa Mulungu kaamba ka chitetezero, monga momwe Mfumu Davide anachitira: “Ndilanditseni, Mulungu wanga, m’dzanja la woipa, m’dzanja la munthu wosalungama ndi wachiwawa.” (Salmo 71:4) Tingapempheredi monga wamasalmo kuti: “Mundichitire chifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza: andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.”​—Salmo 56:1.

Kodi Mulungu adzayankha motani mapemphero amenewo? Baibulo limayankha kuti: “Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.” (Salmo 72:12, 13) Nkwabwino chotani nanga kudziŵa kuti m’nthaŵi yokwanira Yehova adzapereka mpumulo kwa onse ochitiridwa mosalungama!

“Sizidzaipitsa”

Maboma a dzikoli angapitirize kulimbana ndi tsankhu ndi malamulo awo ndi maprogramu. Angapitirize kulonjeza kulingana ndi kuchitirana moyenera. Koma sangapambane. (Salmo 146:3) Ndi Mulungu yekha amene angathe ndi amene adzachotsa tsankhu lonse. Adzasanduliza mtundu wa anthu kukhala banja limodzi logwirizana. “Khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe” lidzapulumuka mapeto a dongosolo loipali ndi kukhala mu mtendere.​—Chivumbulutso 7:9, 10.

Yehova adzathetsa ngozi zonse zochititsidwa ndi tsankhu la fuko ndi chitaganya. Tangoganizani, palibe amene adzamchitira mosayenera! “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.” (Mika 4:4) Ndipo Yesaya 11:9 amati: “Sizidzaipitsa.”

Ngati amakuchitirani tsankhu tsopano lino, chiyembekezo chabwino kwambiri chimenechi chamtsogolo chidzalimbitsa unansi wanu ndi Yehova. Chidzakuthandizani kupirira ndi zisalungamo za dongosolo loipali. Pamene mukulimbana ndi tsankhu ndi kuyembekezera zamtsogolo, tsatirani uphungu wanzeru wa Baibulo wakuti: “Limbikani, ndipo [mtima wanu ukhaletu wamphamvu, NW], inu nonse akuyembekeza Yehova.”​—Salmo 31:24.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

Chinthunzi cha U.S. National Archives

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena