Yehova Anakhala Nane
YOSIMBIDWA NDI MAX HENNING
Munali mu 1933, ndipo Adolf Hitler anali atangokhala kumene paulamuliro m’Germany. Komabe, Mboni za Yehova pafupifupi 500 m’dera la Berlin sizinagwedere. Achichepere ambiri anakhala apainiya, kapena kuti atumiki anthaŵi yonse, ndipo ena analandira magawo ngakhale opita ku maiko ena a mu Ulaya. Ineyo ndi bwenzi langa Werner Flatten tinkalimbikitsana kuti: “Kodi nchifukwa ninji tikungozengereza, kutaya nthaŵi yathu? Nchifukwa ninji sitikupita kukachita upainiya?”
MASIKU asanu ndi atatu pambuyo pa kubadwa kwanga mu 1909, ndinayamba kusamaliridwa ndi makolo olera achikondi. Mu 1918 banja lathu linakanthidwa pamene mlongo wanga wamng’ono wopeza m’banjalo anamwalira mwadzidzidzi. Posapita nthaŵi pambuyo pake Ophunzira Baibulo, monga mmene Mboni za Yehova zinkadziŵikira panthaŵiyo, anafika pakhomo pathu, ndipo mitima ya makolo anga ondilera inatseguka kulandira choonadi cha Baibulo. Iwo anandiphunzitsanso kuyamikira zinthu zauzimu.
Ndinasumika maganizo anga pa sukulu yanga yakudziko ndipo ndinakhala wokonza mipope. Koma chofunika koposa chinali chakuti, ndinaima nji mwauzimu. Ineyo ndi Werner tinayamba upainiya pa May 5, 1933. Tinkatchova njinga kupita ku tauni imene inali pafupifupi makilomita 100 kunja kwa Berlin, kumene tinkakhala ndi kulalikira kwa milungu iŵiri. Ndiyeno tinkabwerera ku Berlin kukasamalira zinthu zina zofunika. Pambuyo pake tinkabwereranso ku gawo lathu la kulalikira kwa milungu inanso iŵiri.
Tinapempha kukatumikira m’dziko lina, ndipo mu December 1933 tinalandira gawo la kumene panthaŵiyo kunali ku Yugoslavia. Komabe, tisanapite, gawo lathu linasinthidwira ku Utrecht ku Netherlands. Mwamsanga pambuyo pake ndinabatizidwa. M’masiku amenewo ubatizo sunkagogomezeredwa kwambiri; utumiki ndiwo umene unali chinthu chofunika koposa. Kudalira Yehova tsopano kunakhala chinthu chanthaŵi zonse m’moyo wanga. Ndinapeza chitonthozo chachikulu m’mawu a wamasalmo wa m’Baibulo akuti: “Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga: Ambuye ndiye wachirikiza moyo wanga.”—Salmo 54:4.
Kuchita Upainiya ku Netherlands
Pasanapite nthaŵi yaitali titafika ku Netherlands, tinapatsidwanso gawo la kumzinda wa Rotterdam. Atate ndi mwana wake wamwamuna m’banja limene tinkakhala nalo analinso apainiya. Miyezi yochepa pambuyo pake, nyumba yaikulu ku Leersum, mzinda wapafupi ndi Utrecht, inagulidwa monga nyumba ya apainiya, ndipo ineyo ndi Werner tinasamukira kumeneko.
Pamene tinkakhala m’nyumba ya apainiya imeneyo, tinkayenda pa njinga kumagawo apafupi ndipo tinagwiritsira ntchito galimoto lokhoza kunyamula anthu asanu ndi aŵiri kupita kumagawo akutali. Panthaŵiyo, m’Netherlands yense munali Mboni zana limodzi zokha. Lerolino, zaka 60 pambuyo pake, gawo limene tinkagwiriramo ntchito tikumakhala m’nyumba ya apainiyayo lili ndi ofalitsa oposa 4,000 m’mipingo pafupifupi 50!
Tinagwira ntchito zolimba, tikumachita maola 14 a mu utumiki tsiku lililonse, ndipo zimenezo zinatisangalatsa. Chonulirapo chachikulu chinali kugaŵira mabuku ambiri malinga ndi kukhoza kwathu. Kaŵirikaŵiri tinkasiya timabuku toposa zana limodzi tsiku lililonse kwa okondwerera. Kupanga maulendo obwereza ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo kunali kusanakhale mbali yantchito yathu yanthaŵi zonse panthaŵiyo.
Tsiku lina ineyo ndi mnzanga tinali kugwira ntchito m’tauni ya Vreeswijk. Pamene anali kupereka umboni kwa mwamuna wina pachipata cha malo alinga a asilikali, ndinagwiritsira ntchito nthaŵiyo kuŵerenga Baibulo langa. Linali lochongedwa kwambiri ndi mizera yofiira ndi ya bluu. Pambuyo pake, wopala matabwa wina amene anali kugwira ntchito padenga lina limene linali pafupi anachenjeza mwamuna amene anali pachipatapo kuti mwinamwake ndinali mzondi. Monga chotulukapo chake, tsiku lomwelo anandimanga pamene ndinali kuchitira umboni kwa mwini sitolo wina, ndipo anandilanda Baibulo langa.
Anandipereka ku khoti. Kumeneko ananena kuti zizindikiro zimene zinali m’Baibulo langa zinali zoyesayesa za kujambula malowo. Anandipatsa mlandu, ndipo woweruza anandipatsa chilango cha zaka ziŵiri m’ndende. Komabe, mlanduwo unachitiridwa apilo, ndipo anandimasula. Ndinali wachimwemwe chotani nanga kumasuka, koma ndinali wachimwemwe koposa pamene anandibwezera Baibulo langa ndi manotsi ake onse!
Mchilimwe cha 1936, ineyo ndi Richard Brauning, mmodzi wa apainiya m’nyumbamo, tinathera chilimwe chonse tikulalikira kumpoto kwa dzikolo. Mwezi woyamba, tinathera maola 240 mu utumiki ndipo tinagaŵira chiŵerengero chachikulu cha mabuku. Tinkakhala m’hema ndipo tinasamalira zosoŵa zathu zonse, kudzichapira tokha, kuphika, ndi zina zotero.
Pambuyo pake anandisinthira ku bwato lotchedwa Lightbearer, limene linadzadziŵika kwambiri kumpoto kwa Netherlands. Apainiya asanu ankakhala m’bwatolo, ndipo ndi ilo tinatha kufikira magawo okhala kutali kwaokha.
Mwaŵi Wowonjezereka
Mu 1938, ndinapatsidwa ntchito ya kukhala mtumiki wadera, monga momwe oyang’anira dera a Mboni za Yehova ankawatchera panthaŵiyo. Motero ndinasiya Lightbearer ndi kuyamba kuchezera mipingo ndi Mboni zokhala kwazokha m’zigawo zitatu zakummwera.
Kuyenda kwathu kunali kwa panjinga basi. Kaŵirikaŵiri tinkatenga tsiku lonse kuti tiyende kuchokera pampingo umodzi kapena gulu la okondwerera kumka pa lotsatira. Pakati pa mizinda imene ndinachezera panali Breda, kumene ndikukhala tsopano. Panthaŵiyo, Breda analibe mpingo uliwonse koma Mboni zokwatirana ziŵiri zokha zachikulire.
Pamene ndinali kutumikira abale ku Limburg, ndinaitanidwa kukayankha mafunso ambiri ofunsidwa ndi Johan Pieper wogwira ntchito mumgodi. Anatenga kaimidwe kolimba kaamba ka choonadi cha Baibulo ndi kukhala mlaliki wolimba mtima. Zaka zinayi pambuyo pake anaponyedwa mumsasa wachibalo, kumene anathera zaka zitatu ndi theka. Pambuyo pa kumasulidwa kwake anayambanso kulalikira mwachangu, ndipo lerolino adakali mkulu wokhulupirika. Mpingo umenewo wa Mboni 12 ku Limburg tsopano wakula kukhala mipingo 17 ndi ofalitsa pafupifupi 1,550!
Pansi pa Ulamuliro wa Nazi
Mu May 1940 Anazi anaukira Netherlands. Ndinalandira ntchito ya ku ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ku Amsterdam. Tinafunikira kupitirizabe ndi ntchito yathu mochenjera kwambiri, zimene zinatichititsa kuzindikira bwino mwambi wa Baibulo wakuti: “Bwenzi lenileni . . . ndilo mbale wobadwira kukuthandiza pooneka tsoka.” (Miyambo 17:17, NW) Chomangira chamgwirizano chokondweretsacho chimene chinakula mkati mwa nthaŵi imeneyi yachipsinjo chinali ndi chiyambukiro chachikulu pa kukula kwanga kwauzimu, ndipo chinandikonzekeretsa kaamba ka masiku ovuta koposa a mtsogolo.
Ntchito yanga inali ya kuyang’anira kuperekedwa kwa mabuku ku mipingo, kumene kaŵirikaŵiri kunkachitidwa ndi onyamula katundu. Nthaŵi zonse a Gestapo anali kufunafuna anyamata okagwira ntchito yachibalo ku Germany, motero tinagwiritsira ntchito alongo achikristu monga onyamula katundu. M’kupita kwa nthaŵi Wilhelmina Bakker, nthaŵi zonse wodziŵika monga Nonnie, anatumizidwa kwa ife kuchokera ku The Hague, ndipo ndinampititsa kumene woyang’anira nthambi wathu, Arthur Winkler, anali kubisala. Poyesetsa kudzizimbaitsa monga momwe ndikanathera, ndinavala monga mlimi wachidatchi, nsapato zamitengo ndi zina zonse, ndi kuperekeza Nonnie pa sitima ya m’msewu. Pambuyo pake ndinauzidwa kuti anavutika kudziletsa kuti asaseke, popeza anaona kuti ndinali kudziŵika kwambiri.
Pa October 21, 1941, malo osungiramo mabuku ndi mapepala ku Amsterdam anaperekedwa kwa mdani. Mkati mwa kuukira kwa Gestapo, Winkler ndi Nonnie anamangidwa. Pamene anaperekedwa kundende, anamva nthumwi za Gestapo ziŵiri zikulankhula za mmene anali kulondolera “mwamuna wina wamng’ono thupi wa tsitsi lakuda” amene anawasoŵa m’makwalala odzaza anthu. Mosakayikira anali kunena za ine, motero Winkler anakwanitsa kutumiza uthenga kwa abale. Pomwepo, anandisamutsira ku The Hague.
Zikali choncho Nonnie anamasulidwa m’ndende, ndipo anabwerera ku The Hague kukachita upainiya. Ndinakumana nayenso kumeneko. Koma pamene mtumiki wampingo ku Rotterdam anamangidwa, ndinatumizidwa kukatenga malo ake. Pambuyo pake mtumiki wampingo ku mpingo wa Gouda anamangidwa, ndipo anandisamutsira kumeneko kukamloŵa malo. Pomalizira pake, pa March 29, 1943, ndinagwidwa. Pamene ndinali kuŵerengera mabuku athu ofotokoza Baibulo, a Gestapo anandifikira mwadzidzidzi.
Pa mabuku ofotokoza Baibulo amene anali omwazikana pathebulo, panalinso mpambo wa maina a abale ndi alongo achikristu, ngakhale kuti ameneŵa anali olembedwa m’njira yachinsinsi. Movutitsidwa maganizo, ndinapemphera kuti Yehova apereke njira yakuti nditetezere amene anali adakali aufulu kulalikira. Popanda kundiona, ndinakwanitsa kuika dzanja langa lotseguka pamwamba pa mpambo wa mainawo ndi kuukwinyakwinya m’dzanja langa. Ndiyeno ndinapempha kupita kuchimbudzi, kumene ndinang’ambang’amba mpambowo ndi kuugujumula.
Pokhala m’nthaŵi zowopsa zotero, ndinaphunzira kupeza nyonga kuchokera pa mmene Yehova anachitira ndi anthu ake kalelo ndi kuchokera pa malonjezo ake a chipulumutso. Ichi nchitsimikiziro chimodzi chouziridwa chimene ndimakumbukira bwino lomwe nthaŵi zonse: “Akadapanda kukhala nafe Yehova, pakutiukira anthu: akadatimeza amoyo.”—Salmo 124:2, 3.
Ndende ndi Misasa Yachibalo
Anandipititsa kundende ya Rotterdam, kumene ndinayamikira kukhala ndi Baibulo langa. Ndinalinso ndi buku la Salvation, mbali zina za buku la Children, ndi nthaŵi yochuluka ya kuŵerenga mabuku onsewa. Pambuyo pa miyezi isanu ndi umodzi ndinadwala kwambiri ndipo ndinapita kuchipatala. Ndisanachoke m’ndende, ndinabisa mabuku anga pansi pa matiresi anga. Pambuyo pake ndinamva kuti Mboni ina, Piet Broertjes, inasamutsidwira ku chipinda changa cha ndende ndipo anawatulukira. Motero mabukuwo anali kugwiritsidwa ntchito kulimbitsabe ena m’chikhulupiriro.
Pamene ndinachira anandisamutsira kundende ya ku The Hague. Pamene ndinali kumeneko ndinakumana ndi Leo C. van der Tas, wophunzira uloya amene anali m’ndende chifukwa cha kutsutsa kulanda dziko kwa Nazi. Anali asanamvepo za Mboni za Yehova, ndipo ndinali ndi mpata wa kupereka umboni kwa iye. Nthaŵi zina ankandidzutsa pakati pa usiku ndi kufunsa mafunso. Sankabisa kusirira kwake Mboni, makamaka atamva kuti tikanamasulidwa ngati tikanangosaina pepala la kukana chikhulupiriro chathu. Pambuyo pa nkhondo, Leo anakhala loya ndipo anamenyera Watch Tower Society nkhondo zambiri za nkhani zokhudza ufulu wa kulambira.
Pa April 29, 1944, ndinalongedwa m’sitima kaamba ka ulendo wopweteka wamasiku 18 wopita ku Germany. Pa May 18 ananditsekera mumsasa wachibalo wa Buchenwald. Mpaka pamene tinamasulidwa ndi magulu ankhondo Ogwirizana pafupifupi chaka chimodzi pambuyo pake, moyo unali wowopsa kosaneneka. Zikwi zambiri anafa, ambiri a ife tikupenya. Popeza ndinakana kugwirira ntchito m’fakitale yopanga zinthu zankhondo imene inali pafupi, anandipatsa ntchito ya pamalo ofikira zamchimbudzi.
Tsiku lina fakitaleyo inaphulitsidwa ndi bomba. Ambiri anathaŵira m’malo a asilikali kaamba ka chitetezero, pamene ena anathaŵira m’nkhalango. Mabomba omwazikana anaphulitsa mudzi wa asilikaliwo, ndipo mabomba amoto anatentha nkhalangoyo. Chinali chinthu chowopsa kuchiona! Ambiri anatenthedwa amoyo! Ndinapeza pobisala pabwino, ndipo pamene moto unayamba kutha, ndinayenda pakati pa mitembo yambiri kubwerera ku msasa.
Anthu ambiri lerolino akudziŵa za nkhanza zowopsa za Chipululutso cha Anazi. Ndikuyamikira Yehova kuti analimbitsa kuganiza kwanga, kotero kuti nkhanza zowopsa zimene ndinakumana nazo sizinalamulire maganizo anga kwa zaka zonsezi. Pamene ndiganiza za nthaŵi yanga yaundende, malingaliro anga oyamba ndiwo aja a chimwemwe pokhala ndinasunga umphumphu kwa Yehova ndi kupereka ulemerero ku dzina lake.—Salmo 124:6-8.
Ntchito ya Pambuyo pa Nkhondo
Nditamasulidwa ndi kubwerera ku Amsterdam, ndinakaonekera mwachindunji ku ofesi yanthambi kaamba ka ntchito. Ndinali wofunitsitsa kudziŵa zimene zinadzachitika pamene ine kunalibe. Nonnie anali kale kugwira ntchito kumeneko. M’chaka chomaliza cha nkhondo, anali atatumikira monga wonyamula katundu akumapereka mabuku ofotokoza Baibulo ku mipingo. Sanamangidwenso, ngakhale kuti nthaŵi zambiri ankatsala pang’ono kumangidwa.
Kwa kanthaŵi ndinachita upainiya ku Haarlem, koma mu 1946, ndinapemphedwa kupita ku nthambi ku Amsterdam kukagwira ntchito mu Dipatimenti Yotumiza Katundu. Chakumapeto a 1948, ineyo ndi Nonnie tinakwatirana, ndipo tinachoka panthambi kukachita upainiya pamodzi. Gawo lathu laupainiya linali ku Assen. Zaka khumi ndi ziŵiri kalelo ineyo ndi Richard Brauning tinathera chilimwe kumeneko, tikumakhala m’chihema ndi kulalikira. Ndinauzidwa kuti Richard anawomberedwa mfuti ndi kufa pamene anali paulendo wopita kumsasa wachibalo.
Nthaŵi yanga yaundende mosakayikira inawononga thanzi langa. Zaka zisanu ndi chimodzi pambuyo pa kumasulidwa ku Buchenwald, ndinadwala kwambiri kwa miyezi inayi. Zaka zambiri pambuyo pake, mu 1957, ndinadwala TB kwa chaka chonse. Thupi langa linatha mphamvu, koma mzimu wanga waupainiya unali wolimbabe. Pamene ndinali kudwala, ndinagwiritsira ntchito mpata uliwonse kuchitira umboni. Ndikulingalira kuti mzimu waupainiya umenewu unali mbali yofunika kwambiri kuti ndisalole kudwaladwala kwanga kumeneku kundipangitsa kukhala munthu wodwala wopanda pake. Ineyo ndi Nonnie tili otsimikizira kumamatira ku utumiki wanthaŵi zonse malinga ngati thanzi lathu lilola.
Nditachira, anatigaŵira kumzinda wa Breda. Panali patapita zaka 21 kuchokera pamene ndinachezera mzindawo monga mtumiki wadera. Pamene tinafika mu 1959, panali mpingo waung’ono wa Mboni 34. Lerolino, zaka 37 pambuyo pake, wakula kukhala mipingo isanu ndi umodzi ndi Mboni zoposa 500, zimene zimakumana m’Nyumba za Ufumu zitatu! Pamisonkhano yathu yakuno ndi pamisonkhano yaikulu, timaona ambiri amene analandira chidziŵitso cha choonadi cha Baibulo chifukwa cha zoyesayesa zathu zina. Kaŵirikaŵiri timamva monga mtumwi Yohane pamene analemba kuti: “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m’choonadi.”—3 Yohane 4.
Tsopano takalamba. Ndili ndi zaka 86 ndipo Nonnie ali ndi zaka 78, koma ndiyenera kunena kuti upainiya ndi ntchito yopatsa thanzi. Kuyambira pamene ndinayamba kukhala ku Breda, ndagonjetsa matenda ambiri amene ndinatenga pamene ndinali m’ndende. Ndakhalanso ndi zaka zobala zipatso zambiri mu utumiki wa Yehova.
Kukumbukira zaka zambiri za utumiki wopindulitsa ndiko magwero a chimwemwe kwa tonse aŵirife. Pemphero lathu ndilo lakuti Yehova adzatipatsa mzimu ndi mphamvu kuti tipitirize mu utumiki wake malinga ngati tikupuma. Mwachidaliro, tikunena m’mawu a wamasalmo kuti: “Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga: Ambuye ndiye wachirikiza moyo wanga.”—Salmo 54:4.
[Chithunzi patsamba 23]
Nditaimirira pafupi ndi hema amene tinagwiritsira ntchito pamene tinali kuchita upainiya m’ma 1930.
[Chithunzi patsamba 23]
Boti limene tinagwiritsira ntchito kupita ku magawo okhala kutali kwaokha.
[Chithunzi patsamba 23]
Kufunsidwa pa programu yamsonkhano wachigawo mu 1957
[Chithunzi patsamba 24]
Ndi mkazi wanga lerolino