Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 6/1 tsamba 25-28
  • Sukulu ya Gileadi Itumiza Kalasi Lake la 100

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sukulu ya Gileadi Itumiza Kalasi Lake la 100
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Uphungu wa m’Malemba Wochokera kwa Amuna Akulu
  • Mawu Ogwira Ntchito Kuchokera m’Munda
  • Sekerani mwa Yehova Ndipo Kondwerani
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Nyumba Yatsopano Kaamba ka Sukulu ya Mishonale ya Gileadi
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kufunitsitsa ndi Mtima Wonse Kumachititsa Anthu Kupita ku Sukulu ya Gileadi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kuchoka pa Ophunzira Okhoza Bwino Kukhala Amishonale Okhoza Bwino
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 6/1 tsamba 25-28

Sukulu ya Gileadi Itumiza Kalasi Lake la 100

SUKULU ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower yathandiza kwambiri pa kulengezedwa kwa padziko lonse kwa Ufumu wa Mulungu m’nthaŵi zamakono. Kuchokera pamene Sukulu ya Gileadi inayamba kuphunzitsa amishonale mu 1943, omaliza maphunziro ake atumikira m’maiko oposa 200. Pa March 2, 1996, kalasi la 100 linamaliza maphunziro ake.

Ophunzira anali pasukulu nthaŵi imene kunali kugwa chipale chofeŵa choposa mamita aŵiri m’dera la Malikulu a Maphunziro a Watchtower ku Patterson, New York. Choncho sizinadabwitse kuti kunali kugwa chipale chofeŵa patsiku lawo lomaliza maphunziro. Ngakhale zinali choncho, holo inadzala, ndipo ena ochuluka anamvetsera ku Patterson, Wallkill, ndi Brooklyn​—onse pamodzi anthu 2,878.

Theodore Jaracz, wa Komiti Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira, anali tcheyamani. Atapereka malonje ndi mtima wonse kwa alendo omwe analipo ochokera ku maiko ambiri, anapempha onse kuimirira ndi kuimba nyimbo nambala 52. Mu holoyo munamveka mfuu yotamanda Yehova pamene iwo anaimba “Dzina la Atate Wathu,” m’buku la Imbirani Yehova Zitamando. Nyimboyo, limodzi ndi ndemanga za tcheyamani zonena za kugwiritsira ntchito maphunziro kutamanda Yehova, zinalambula njira ya programu yomwe inatsatira.

Uphungu wa m’Malemba Wochokera kwa Amuna Akulu

Mbali yoyamba ya programu inali ndi nkhani zazifupi zokambidwa ndi atumiki a Yehova angapo azaka zambiri kwa kalasi lomaliza maphunziro. Richard Abrahamson, wogwira ntchito kumalikulu yemwe anayamba utumiki wake wanthaŵi yonse mu 1940, analimbikitsa kalasilo kuti: “Pitirizani Kukonzedwanso.” Anawakumbutsa kuti iwo anali ataona kale nyengo za kukonzedwanso m’moyo wawo monga Akristu, kuphatikizapo miyezi isanu ya maphunziro awo pa Gileadi. Chotero nchifukwa ninji iwo anayenera kupitiriza kukonzedwanso?

Mlankhuliyo anafotokoza kuti liwu limene mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito pa 2 Akorinto 13:11, NW, “limasonyeza mchitidwe womapitiriza, kugonjera komapitiriza pamene Yehova akumuumba munthu kapena kumuyenga, kumlinganiza, kuti munthuyo akwaniritse miyezo ya Yehova yofuna chisamaliro chachikulu.” M’magawo awo a kumaiko ena, a m’kalasi lomaliza maphunzirolo adzayang’anizana ndi ziyeso za chikhulupiriro chawo. Adzafunikira kuphunzira chinenero chatsopano, kuzoloŵerana ndi miyambo ndi kakhalidwe kosiyana, ndi kuzoloŵerana ndi magawo osiyanasiyana. Adzakhalanso akuchita ndi maumunthu osiyanasiyana m’nyumba zawo za amishonale ndi m’mipingo yawo yatsopano. Ngati adzagwiritsira ntchito bwino lomwe mapulinsipulo a Baibulo m’mikhalidwe yonse imeneyi, limodzi ndi kufunitsitsa kukonzedwanso, ndiye kuti, mogwirizana ndi zimene mtumwi Paulo analemba, iwo adzakhozanso ‘kupitiriza kukondwera.’

John Barr, mmodzi wa a Bungwe Lolamulira asanu amene anatengamo mbali m’programuyo, anatenga mutu wa nkhani yake pa 1 Akorinto 4:9. Anakumbutsa omvetsera ake kuti Akristu ali choonetsedwa kwa angelo ndi anthu. “Kudziŵa zimenezi,” iye anatero, “kumakulitsa kwambiri kufunika kwake kwa moyo wa Mkristu, makamaka pamene azindikira kuti mwa zonena zake ndi zochita zake, angakhudze aja amene akumuona, osaoneka ndi ooneka omwe. Ndikhulupirira kuti mungachite bwino kwambiri abale nonsenu ndi alongo okondedwa a m’kalasi la 100 la Gileadi kukumbukira zinthu zimenezi pamene mupita kungondya zakutali za dziko lapansi.”

Mbale Barr analimbikitsa ophunzira 48 kukumbukira, pamene akuthandiza onga nkhosa kuphunzira choonadi, kuti kumakhala “chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.” (Luka 15:10) Akumatchula 1 Akorinto 11:10, anasonyeza kuti maganizo a munthu kulinga ku makonzedwe ateokrase amakhudza osati abale athu ndi alongo okha amene timaona komanso ndi angelo amene sitimaona. Nkopindulitsa chotani nanga kukumbukira chithunzi chonsechi!

Winanso wa Bungwe Lolamulira, Gerrit Lösch, iye mwini womaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi, anakamba pa malemba onga Salmo 125:1, 2; Zekariya 2:4, 5 ndi Salmo 71:21 kusonyeza kuti Yehova ‘amazinga anthu ake.’ Amawatetezera kumbali zonse. Kodi Mulungu adzangopereka chitetezo chimenecho pa chisautso chachikulu pokha? “Ayi,” mlankhuliyo anayankha, “pakuti Yehova ali kale ‘linga lamoto,’ chitetezo kwa anthu ake. Chaka cha pambuyo pa nkhondo cha 1919 chinapeza otsalira a Israyeli wauzimu akufunitsitsa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse monga umboni ku mitundu yonse. Anali oimira Yerusalemu wophiphiritsira wakumwamba. Yehova akulonjeza kuti adzawapatsa chitetezo chaumulungu oimira amenewo monga gulu m’nthaŵi ya mapeto. Chotero ndani kodi amene angathe kuwaletsa? Kulibe.” Nzolimbikitsa chotani nanga zimenezi kwa iwo ndi onse oyanjana nawo kwambiri pochita chifuniro cha Mulungu!

Ulysses Glass, wakale pa aphunzitsi a sukuluyo, analimbikitsa kalasilo ‘kumaliza kulambula malo awo m’gulu la Yehova la padziko lonse.’ Malowo ndiwo mkhalidwe kapena ntchito yoyenerana kwambiri ndi kukhoza kwa munthuyo kapena umunthu wake. “Inu amene mudzakhala amishonale mwapeza malo anu m’gulu la padziko lonse la Mboni za Yehova,” anatero. “Koma, ngakhale kuti zimenezi nzofunika tsopano, zangokhala chiyambi cha moyo wanu monga amishonale.” Iwo adzafunikira kulimbikira kugwiritsira ntchito bwino maluso awo ndi kuzoloŵera magawo apadera amene Yehova ndi gulu lake anali kuwapatsa.

Nkhani yomaliza m’mbali imeneyi ya programu inaperekedwa ndi Wallace Liverance, mmodzi wa aphunzitsi a Gileadi yemwe anatumikira zaka 17 ku Bolivia. “Kodi mudzayesa Mulungu?” anafunsa ophunzirawo. Kodi ndi motani mmene ayenera kuchitira zimenezo? Mtundu wa Israyeli unayesa Mulungu m’njira yolakwika. (Deuteronomo 6:16) “Mwachionekere, kuyesa Mulungu mwa kudandaula kapena kung’ung’udza kapena mwinamwake mwa kusonyeza kusoŵa chikhulupiriro m’njira imene iye amasamalirira zinthu nkulakwa,” mlankhuliyo anatero. “Mutafika kumagawo anu atsopano, kanizani chikhoterero chimenecho,” analimbikitsa motero. Nanga kodi njira yoyenera yoyesera Mulungu njotani? “Ndiyo mwa kukhulupirira mawu ake, mwa kuchita ndendende zimene anena, ndiyeno kumsiyira nkhaniyo kuti apereke zotulukapo zake,” Mbale Liverance anafotokoza motero. Malinga ndi zimene zili pa Malaki 3:10, Yehova akupempha anthu ake kuti: “Mundiyese . . . tsono.” Iye analonjeza kuti ngati iwo anabweretsa cha chikhumi chawo mokhulupirika m’nyumba yosungiramo ya kachisi, adzawadalitsa. “Bwanji osaona gawo lanu laumishonale m’njira imodzimodzi?” mlankhuliyo anafunsa. “Yehova akufuna kuti mupambane, chotero muyeseni. Khalani m’gawo lanu. Pangani masinthidwe amene iye akufuna kuti mupange. Pirirani. Onani ngati sadzakudalitsani.” Ndi uphungu wabwino chotani nanga kwa onse amene akutumikira Yehova!

Pambuyo pa nyimbo programuyo inasintha kukhala kufunsa kosangalatsa m’malo mwa nkhani.

Mawu Ogwira Ntchito Kuchokera m’Munda

Mark Noumair, watsopano pa aphunzitsi a Gileadi anapempha ophunzirawo kusimba zokumana nazo zimene anakhala nazo mu utumiki wakumunda pamene anali pasukulu. Zimenezi zinasonyeza phindu la kukhala watcheru mu utumiki ndipo zinapatsa omvetsera malingaliro ogwira ntchito amene angagwiritsire ntchito.

Panyengo yawo ya sukulu, ophunzira a m’kalasi la Gileadi limeneli anapindula makamaka mwa kukhoza kuyanjana ndi a m’Makomiti Anthambi ochokera ku maiko 42, amenenso anali pa Malikulu a Maphunziro ku Patterson kaamba ka maphunziro apadera. Ambiri a iwo anamaliza maphunziro awo a Gileadi kalelo. Paprogramuyo, oimira kalasi la 3, la 5, la 51, ndi la 92, limodzi ndi a m’Sukulu ya Gileadi Yowonjezera ku Germany ndiwo anafunsidwa. Ndemanga zawo zinali zopindulitsa zedi!

Iwo anasimba mmene amishonale amamvera pamene aona chiŵerengero cha otamanda Yehova chikuwonjezeka m’magawo awo kuchoka pa anthu angapo kukhala zikwi makumi ambiri. Anasimba za mbali imene anakhala nayo m’kupereka uthenga wabwino kunyumba zotalikirana m’mapiri a Andes ndi kumidzi ya kumagwero kwa mtsinje wa Amazon. Anasimba za kuchitira umboni kwa anthu osadziŵa kuŵerenga ndi kulemba. Anasimba za vuto lawo la kuphunzira zinenero zatsopano ndi zimene omaliza maphunzirowo angayembekezeredi ponena za nthaŵi imene idzapitapo kuti achitire umboni ndi kupereka nkhani m’chinenero chonga Chitchaina. Anachita ndi zitsanzo kusonyeza maulaliki m’Chispanya, ndi m’Chitchaina. Anagogomezera kuti amishonale amakhala ogwira mtima kwambiri pamene aphunzira osati chinenero chokha komanso kaganizidwe ka anthu. Anasimba za kakhalidwe koipa kamene nthaŵi zambiri kamapezeka kumaiko osauka nati: “Amishonale ayenera kudziŵa kuti chimene chimachititsa mkhalidwewo ndi kudyerera ena. Mmishonale angachite bwino ngati amva mmene Yesu anamvera​—iye anawachitira chifundo anthu, amene anali ngati nkhosa zopanda mbusa.”

Pambuyo pa nyimbo programuyo inapitiriza ndi nkhani ya A. D. Schroeder, wa Bungwe Lolamulira. Anali ndi mwaŵi wa kukhala mmodzi wa alangizi oyambirira a Sukulu ya Gileadi pamene inatsegulidwa mu 1943. Monga chimake choyenerera cha programu, anakamba nkhani yakuti “Kuzindikira Yehova monga Ambuye Mfumu.” Nkhani yogwira mtima ya Mbale Schroeder yozikidwa pa Salmo la 24 inakopa chidwi omvetsera onse kudziŵa mmene ulili mwaŵi waukulu kuzindikira Yehova monga Ambuye Mfumu.

Pambuyo pogaŵira madipuloma, ndi nyimbo yomaliza, Karl Klein wa Bungwe Lolamulira anatsiriza ndi pemphero. Inali programu yothandiza ndi yotsitsimula mwauzimu chotani nanga!

Masiku otsatira pambuyo pa programu yomaliza maphunziro, a m’kalasi la 100 okwanira 48 anayamba kupita ku magawo aumishonale kumaiko 17. Koma sindiko kunali kuyamba utumiki wawo. Iwo anali kale ndi mbiri yokwanira ya utumiki wachikristu wanthaŵi yonse. Pamene analembetsa Gileadi, anali ndi avareji ya zaka zakubadwa 33 ndipo anali atathera zaka zoposa 12 mu utumiki wanthaŵi yonse. Ena a iwo anali a banja la Beteli la padziko lonse la Watch Tower Society. Ena anali oyang’anira oyendayenda. Ophunzira angapo anali atachitapo kale utumiki wakudziko lina​—mu Afirika, South America, Ulaya, zisumbu za m’nyanja, ndi kwa anthu a m’maiko akwawo olankhula zinenero zakunja. Koma tsopano akugwirizana ndi amishonale ena ambiri amene akhala okondwa kunena kuti, ‘Tidzatumikira kulikonse m’dziko kumene akutifuna.’ Chikhumbo chawo chachikulu ndicho kugwiritsira ntchito moyo wawo kulemekeza Yehova.

[Bokosi patsamba 27]

Ziŵerengero za Kalasi:

Chiŵerengero cha maiko kumene anachokera: 8

Chiŵerengero cha maiko ogaŵiridwako: 17

Chiŵerengero cha ophunzira: 48

Avareji ya zaka zakubadwa: 33.75

Avareji ya zaka m’choonadi: 17.31

Avareji ya zaka mu utumiki wanthaŵi yonse: 12.06

[Chithunzi patsamba 26]

Kalasi la 100 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

M’ndandanda pansipa, mizera ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse.

(1) Shirley, M.; Grundström, M.; Genardini, D.; Giaimo, J.; Shood, W.; Phair, P.; Buchanan, C.; Robinson, D. (2) Pine, C.; Kraus, B.; Racicot, T.; Hansen, A.; Beets, T.; Berg, J.; Garcia, N.; Fleming, K. (3) Whinery, L.; Whinery, L.; Harps, C.; Giaimo, C.; Berg, T.; Mann, C.; Berrios, V.; Pfeifer, C. (4) Randall, L.; Genardini, S.; Kraus, H.; Fleming, R.; D’Abadie, S.; Shirley, T.; Stevenson, G.; Buchanan, B. (5) Robinson, T.; Garcia, J.; Harps, P.; Racicot, D.; D’Abadie, F.; Phair, M.; Stevenson, G.; Shood, D. (6) Beets, L.; Pfeifer, A.; Berrios, M.; Pine, J.; Mann, L.; Randall, P.; Grundström, J.; Hansen, G.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena