Sungani Umodzi m’Masiku Ano Otsiriza
‘Mayendedwe anu ayenere uthenga wabwino . . . kuchirimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha uthenga wabwino.’—AFILIPI 1:27.
1. Kodi ndi kusiyana kotani kumene kuli pakati pa Mboni za Yehova ndi dziko?
ANO ndi “masiku otsiriza.” Mosakayikira, “nthaŵi zoŵaŵitsa” zafika. (2 Timoteo 3:1-5) Mu “nthaŵi ya chimaliziro” ino, ndi anthu ake achiwawa, Mboni za Yehova zili zapadera mosiyana nawo kwambiri chifukwa cha mtendere wawo ndi umodzi. (Danieli 12:4) Koma munthu aliyense amene ali wa m’banja la olambira Yehova lapadziko lonse afunikira kugwira ntchito zolimba kuti asungitse umodzi umenewu.
2. Kodi Paulo ananenanji ponena za kusunga umodzi, ndipo tidzakambitsirana za funso lotani?
2 Mtumwi Paulo analangiza Akristu anzake kusunga umodzi. Analemba kuti: “Mayendedwe anu ayenere uthenga wabwino wa Kristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchirimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha uthenga wabwino; osawopa adani m’kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chiwonongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu.” (Afilipi 1:27, 28) Mawu a Paulo akusonyeza bwino kuti tiyenera kugwira ntchito pamodzi monga Akristu. Chotero, pamenepa, kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kusunga umodzi wathu wachikristu m’masiku ano oyesa?
Gonjerani Chifuniro cha Mulungu
3. Kodi ndi liti ndipo ndi motani mmene Akunja oyamba osadulidwa anakhalira otsatira a Kristu?
3 Njira imodzi yosungira umodzi wathu ndiyo kugonjera chifuniro cha Mulungu nthaŵi zonse. Zimenezi zingafunikiritse kuti ife tisinthe m’kuganiza kwathu. Lingalirani za ophunzira oyambirira a Yesu Kristu achiyuda. Pamene mtumwi Petro analalikira koyamba kwa Akunja osadulidwa mu 36 C.E., Mulungu anatsanulira mzimu woyera pa anthu ameneŵa a mitundu, ndipo anabatizidwa. (Machitidwe, chaputala 10) Panthaŵiyo, ndi Ayuda okha, otembenukira ku Chiyuda, ndi Asamariya amene anakhala otsatira a Yesu Kristu.—Machitidwe 8:4-8, 26-38.
4. Atafotokoza zimene zinachitika kwa Korneliyo, kodi Petro ananenanji, ndipo kodi zimenezi zinapereka chiyeso chotani kwa ophunzira a Yesu achiyuda?
4 Pamene atumwi ndi abale ena ku Yerusalemu anamva za kutembenuka kwa Korneliyo ndi Akunja ena, anali ndi chidwi cha kufuna kumva za lipoti la Petro. Atalongosola zimene zinachitika kwa Korneliyo ndi Akunja ena okhulupirira, mtumwiyo anamaliza ndi mawu akuti: “Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo [Akunja okhulupirirawo] mphatso yomweyi [ya mzimu woyera] yonga ya kwa ife [Ayuda], pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Kristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?” (Machitidwe 11:1-17) Zimenezi zinabweretsa chiyeso kwa otsatira a Yesu Kristu achiyuda. Kodi iwo akagonjera chifuniro cha Mulungu ndi kulandira Akunja okhulupirira kukhala olambira anzawo? Kapena kodi umodzi wa atumiki a Yehova apadziko lapansi ukaikidwa pachiswe?
5. Kodi atumwi ndi abale ena anachita motani pa umboni wakuti Mulungu anali atakhululukira Akunja, ndipo tingaphunzirenji pa mkhalidwe umenewu?
5 Nkhaniyo imati: “Ndipo pamene anamva izi [atumwiwo ndi abale ena], anakhala du, nalemekeza Mulungu, ndi kunena, Potero Mulungu anapatsa kwa amitundunso kutembenukira mtima kumoyo.” (Machitidwe 11:18) Mkhalidwewo unasungitsa ndi kuchirikiza umodzi wa otsatira a Yesu. M’nthaŵi yaifupi chabe, ntchito yolalikira inapita patsogolo pakati pa Akunja, kapena anthu amitundu, ndipo dalitso la Yehova linali pa ntchitoyo. Nafenso tiyenera kuvomereza pamene tipemphedwa kugwirizanika pa kupangidwa kwa mpingo watsopano kapena pamene kusintha kwina kwa teokrase kupangidwa motsogozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Kuchita mogwirizana kwathu ndi mtima wonse kudzakondweretsa Yehova ndipo kudzatithandiza kusunga umodzi wathu m’masiku ano otsiriza.
Mamatirani Choonadi
6. Kodi ndi chiyambukiro chotani chimene choonadi chili nacho pa umodzi wa olambira Yehova?
6 Monga mbali ya banja la olambira Yehova, timasunga umodzi chifukwa chakuti tonsefe ‘timaphunzitsidwa ndi Yehova’ ndi kugwiritsa pa choonadi chake chovumbulidwa. (Yohane 6:45, NW; Salmo 43:3) Popeza kuti ziphunzitso zathu nzozikidwa pa Mawu a Mulungu, ife tonse timalankhula mogwirizana. Timalandira mokondwera chakudya chauzimu choperekedwa ndi Yehova kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Chiphunzitso chofanana chotero chimatithandiza kusunga umodzi wathu padziko lonse.
7. Ngati ife enife tili ndi vuto la kumvetsa mfundo ina yake, tiyenera kuchitanji, ndipo sitiyenera kuchitanji?
7 Bwanji ngati ife patokha tili ndi vuto pomvetsa kapena kuvomereza mfundo ina yake? Tiyenera kupempherera nzeru ndi kufufuza m’Malemba ndi m’zofalitsa zachikristu. (Miyambo 2:4, 5; Yakobo 1:5-8) Kukambitsirana ndi mkulu kungathandize. Ngati simukumvetsabe mfundoyo, ndi bwino kwambiri kuisiya kaye nkhaniyo. Mwinamwake chidziŵitso chowonjezereka pa nkhaniyo chidzafalitsidwa, ndiyeno kumvetsa kwathu zinthu kudzakulitsidwa. Komabe, kuyesa kukhutiritsa ena maganizo mu mpingo kuti avomereze lingaliro lathu losiyana, kungakhale kulakwa. Kumeneku kungakhale kufesa kusagwirizana, mosemphana ndi kulimbikira kusungitsa umodzi. Ndi bwino koposa chotani nanga “kuyenda m’choonadi” ndi kulimbikitsa ena kuchita motero!—3 Yohane 4.
8. Kodi ndi mkhalidwe wotani kulinga ku choonadi umene uli woyenera?
8 M’zaka za zana loyamba, Paulo anati: “Tsopano tipenya m’kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.” (1 Akorinto 13:12) Ngakhale kuti Akristu oyambirira sanamvetse mbali zonse, anakhalabe mu umodzi. Ife tsopano timazindikira bwino kwambiri za chifuno cha Yehova ndi Mawu ake a choonadi. Chotero tiyeni tikhale othokoza kaamba ka choonadi chimene talandira kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika.” Ndipo tiyenitu tithokoze kuti Yehova watitsogolera mwa gulu lake. Pamene kuli kwakuti nthaŵi zonse sitinakhale ndi mlingo umodzimodziwo wa chidziŵitso, sitinafe ndi njala kapena ludzu lauzimu. M’malo mwake, Mbusa wathu, Yehova, watisunga tili muumodzi ndipo watisamalira bwino.—Salmo 23:1-3.
Gwiritsirani Ntchito Bwino Lilime!
9. Kodi lilime lingagwiritsiridwe ntchito motani kuchirikizira umodzi?
9 Kugwiritsira ntchito lilime kulimbikitsira ena ndiko njira yofunika yochirikizira umodzi ndi mzimu waubale. Kalata imene inathetsa nkhani ya mdulidwe, yotumizidwa ndi bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba, inali chinthu cholimbikitsa. Ataiŵerenga, ophunzira Akunja ku Antiokeya “anakondwera chifukwa cha chilimbikitso chake.” Yuda ndi Sila, amene anatumidwa kuchokera ku Yerusalemu ndi kalatayo, “analimbikitsa abale ndi mawu ambiri, nawalimbitsa.” Mosakayikira, kukhalapo kwa Paulo ndi Barnaba kunalimbikitsanso ndi kulimbitsa okhulupirira anzawo mu Antiokeya. (Machitidwe 15:1-3, 23-32, NW) Tingachite mofanana kwambiri pamene tisonkhana kaamba ka misonkhano yachikristu ndi ‘kulimbikitsana’ mwa kukhalapo kwathu ndi ndemanga zomangirira.—Ahebri 10:24, 25.
10. Kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa ngati pakhala kulalata, kuti tisunge umodzi?
10 Komabe, kugwiritsira ntchito lilime molakwa kungasokoneze umodzi wathu. “Lilimenso lili chiŵalo chaching’ono, ndipo lidzikuzira zazikulu,” analemba motero wophunzira Yakobo. “Taonani, kamoto kakang’ono kayatsa nkhuni zambiri!” (Yakobo 3:5) Yehova amada awo amene amachititsa mikangano. (Miyambo 6:16-19) Kalankhulidwe kameneko kangachititse kusagwirizana. Chotero, pamenepa, bwanji ngati pali kulalata, ndiko kuti, kunenera munthu zoipa zambiri kapena kumtukwana? Akulu adzayesa kuthandiza wolakwayo. Komabe, wolalata wosalapa ayenera kuchotsedwa kotero kuti mtendere wa mpingo, dongosolo, ndi umodzi zisungidwe. Ndi iko komwe, Paulo analemba kuti: “Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali . . . wolalatira, . . . kungakhale kukadya naye wotere, iyayi.”—1 Akorinto 5:11.
11. Kodi nchifukwa ninji kudzichepetsa kuli kofunika ngati tanena kanthu kamene kachititsa mkwiyo pakati pa ife ndi wokhulupirira mnzathu?
11 Kumanga lilime kumatithandiza kusunga umodzi. (Yakobo 3:10-18) Komano tinene kuti kanthu kena kamene tanena kachititsa mkwiyo pakati pa ife ndi Mkristu mnzathu. Kodi sikungakhale koyenera kuyamba kuchitapo kanthu kuti tipange mtendere ndi mbale wathu, tikumapepesa ngati kuli koyenera? (Mateyu 5:23, 24) Zoonadi, zimenezi zimafuna kudzichepetsa, kapena kudzitsitsa maganizo, koma Petro analemba kuti “Muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.” (1 Petro 5:5) Kudzichepetsa kudzatisonkhezera ‘kulondola mtendere’ ndi abale athu, tikumavomereza zophophonya zathu ndi kupepesa moyenera. Zimenezi zimathandizira kusungitsa umodzi m’banja la Yehova.—1 Petro 3:10, 11.
12. Kodi tingagwiritsire ntchito motani lilime kuchirikizira ndi kusungitsira umodzi wa anthu a Yehova?
12 Tingakulitse mowonjezereka mzimu wa banja pakati pa awo amene ali m’gulu la Yehova ngati tigwiritsira ntchito bwino lilime lathu. Popeza kuti zimenezo nzimene Paulo anachita, anali wokhoza kukumbutsa Atesalonika kuti: “Mudziŵa kuti tinachitira yense wa inu payekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha, ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu.” (1 Atesalonika 2:11, 12) Atapereka chitsanzo chabwino kwambiri pankhaniyi, Paulo anali wokhoza kulimbikitsa Akristu anzake ‘kulimbikitsa amantha mtima.’ (1 Atesalonika 5:14) Taganizani za ubwino wochuluka umene tingachite mwa kugwiritsira ntchito lilime kutonthoza, kulimbikitsa, ndi kumangirira ena. Inde, “mawu a pa nthaŵi yake kodi sali abwino?” (Miyambo 15:23) Ndiponso, mawu amenewo amachirikiza ndi kusungitsa umodzi wa anthu a Yehova.
Khalani Wokhululukira!
13. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala okhululukira?
13 Kukhululukira wochimwa amene wapepesa nkofunika ngati titi tisunge umodzi wachikristu. Ndipo kodi tiyenera kukhululukira nthaŵi zochuluka motani? Yesu anauza Petro kuti: “Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kaŵiri, koma kufikira makumi asanu ndi aŵiri kubwerezedwa kasanu ndi kaŵiri.” (Mateyu 18:22) Ngati tili osakhululukira, tikudzimana phindu. Motani? Ehe, udani ndi kusunga kanthu kukhosi zimatibera mtendere wa maganizo. Ndipo ngati tifikira pakudziŵika kukhala ndi njira zankhanza ndi zosakhululukira, tingangodzibweretsera temberero pa ife eni. (Miyambo 11:17) Kusunga kanthu kukhosi nkosasangalatsa kwa Mulungu ndipo kungachititse tchimo lalikulu. (Levitiko 19:18) Kumbukirani kuti Yohane Mbatizi anadulidwa mutu pa chiŵembu cholinganizidwa ndi Herodiya woipayo, amene “anamsungira kanthu kukhosi.”—Marko 6:19-28, NW.
14. (a) Kodi nchiyani chimene Mateyu 6:14, 15 amatiphunzitsa ponena za kukhululukira? (b) Kodi nthaŵi zonse tiyenera kuyembekezera kupepesa tisanakhululukire wina?
14 Pemphero lachitsanzo la Yesu limaphatikizapo mawu awa: “Mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu.” (Luka 11:4) Ngati tili osakhululukira, tili pangozi yakuti tsiku lina Yehova Mulungu sadzakhululukiranso machimo athu, pakuti Yesu anati: “Ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo adzakhululukira inunso Atate wanu wa kumwamba. Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.” (Mateyu 6:14, 15) Chotero ngati tikufunadi kuchita mbali yathu m’kusungitsa umodzi m’banja la Yehova la olambira, tidzakhala okhululukira, mwinamwake mwa kungoiŵala cholakwacho chimene chinachitika mwina chifukwa cha kulingalira mosasamala ndi chopanda cholinga choipa chilichonse. Paulo anati: “[Pitirizani, NW] kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso [Yehova, NW] anakhululukira inu, teroni inunso.” (Akolose 3:13) Pamene tikhala okhululukira, timathandiza pa kusungitsa umodzi wamtengo wapatali wa gulu la Yehova.
Umodzi ndi Zosankha Zamunthu Mwini
15. Kodi nchiyani chimene chimathandiza anthu a Yehova kusunga umodzi popanga zosankha zamunthu mwini?
15 Mulungu anatipanga ndi mkhalidwe wa kudzisankhira wokhala ndi mwaŵi ndi thayo la kupanga zosankha zamunthu mwini. (Deuteronomo 30:19, 20; Agalatiya 6:5) Komabe, ndife okhoza kusunga umodzi wathu chifukwa chakuti timachita mogwirizana ndi malamulo a Baibulo ndi mapulinsipulo. Timalingalira zinthu popanga zosankha zamunthu mwini. (Machitidwe 5:29; 1 Yohane 5:3) Tinene kuti pabuka nkhani ya uchete. Tikhoza kupanga chosankha chaumwini chimene tikuzindikira bwino mwa kukumbukira kuti ‘sitili a dziko lapansi’ ndi kuti ‘tasula malupanga athu kukhala zolimira.’ (Yohane 17:16; Yesaya 2:2-4) Mofananamo, pamene tipanga chosankha chathu ponena za unansi wathu ndi Boma, timalingalira zimene Baibulo limanena ponena za kupatsa “Mulungu zake za Mulungu,” pamene tikugonjera ku “maulamuliro aakulu” m’nkhani za boma. (Luka 20:25; Aroma 13:1-7, NW; Tito 3:1, 2) Inde, kulingalira malamulo ndi mapulinsipulo a Baibulo popanga zosankha zamunthu mwini kumathandizira kusungitsa umodzi wathu wachikristu.
16. Kodi tingathandizire motani kusungitsa umodzi popanga zosankha zimene sizili zolondola kapenanso zolakwa mwa Malemba? Perekani chitsanzo.
16 Tingathandizire kusungitsa umodzi wachikristu ngakhale pamene tikupanga chosankha chimene chili chaumwini kotheratu ndipo chimene sichili cholondola kapenanso cholakwa mwa Malemba. Motani? Mwa kusonyeza nkhaŵa yachikondi kwa ena amene angayambukiridwe ndi chosankha chathu. Mwachitsanzo: Mumpingo wa ku Korinto wakale, munabuka funso lonena za nyama yoperekedwa nsembe ku mafano. Zoonadi, Mkristu sanatenge nawo mbali m’mwambo wa kulambira mafano. Komanso, kudya nyama yotsala yokhetsedwa bwino mwazi ya mtundu umenewu imene inali kugulitsidwa pamsika, sikunali kuchimwa. (Machitidwe 15:28, 29; 1 Akorinto 10:25) Komabe, Akristu ena anavutika ndi zikumbumtima zawo pankhani ya kudya nyama imeneyi. Motero Paulo analimbikitsa Akristu ena kupeŵa kuwakhumudwitsa. Kwenikweni, iye analemba kuti: “Ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama ku nthaŵi yonse, kuti ndingakhumudwitse mbale wanga.” (1 Akorinto 8:13) Chotero ngakhale ngati lamulo kapena pulinsipulo la Baibulo silikukhudzidwa, nkwachikondi chotani nanga kulingalira ena popanga zosankha zamunthu mwini zimene zingayambukire umodzi wa banja la Mulungu!
17. Kodi nchiyani chimene chili chabwino kuchita popanga zosankha zamunthu mwini?
17 Ngati tili osadziŵa bwino njira imene tiyenera kutenga, kuli kwanzeru kusankha mwanjira imene ingatisiye tili ndi chikumbumtima choyera, ndipo ena ayenera kulemekeza chosankha chathu. (Aroma 14:10-12) Zoonadi, pamene tipanga chosankha chamunthu mwini, tiyenera kupempha chitsogozo cha Yehova m’pemphero. Monga momwe ananenera wamasalmo, tingapemphere mwachidaliro kuti: “Munditcherere khutu lanu . . . pakuti inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa; ndipo chifukwa cha dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.”—Salmo 31:2, 3.
Sungani Umodzi Wachikristu Nthaŵi Zonse
18. Kodi Paulo anachitira fanizo motani umodzi wa mpingo wachikristu?
18 Mu 1 Akorinto chaputala 12, Paulo anagwiritsira ntchito thupi la munthu kufanizira umodzi wa mpingo wachikristu. Anagogomezera kudalirana ndi kufunika kwa chiŵalo chilichonse. “Ngati zonse zikadakhala chiŵalo chimodzi, likadakhala kuti thupi,” anafunsa motero Paulo. “Koma tsopano pali ziŵalo zambiri, koma thupi limodzi. Ndipo diso silingathe kunena kwa dzanja, Sindikufuna iwe, kapenanso mutu kwa mapazi, Sindikufunani inu.” (1 Akorinto 12:19-21) Mofananamo, ife tonse m’gulu la olambira Yehova sitimachita ntchito yofanana. Komabe, ndife ogwirizana, ndipo timafunana.
19. Kodi tingapindule motani ndi zogaŵira zauzimu za Mulungu, ndipo mkulu wina ananenanji pa zimenezi?
19 Monga momwe thupi limafunira chakudya, chisamaliro, ndi chitsogozo, timafunikira zogaŵira zauzimu zimene Mulungu amatipatsa kupyolera m’Mawu ake, mzimu, ndi gulu lake. Kuti tipindule ndi zogaŵira zimenezi, tiyenera kukhala mbali ya banja la Yehova lapadziko lapansi. Pambuyo pa zaka zambiri mu utumiki wa Mulungu, mbale wina analemba kuti: “Ndikuthokoza kwambiri kuti ndachita mogwirizana ndi chidziŵitso cha zifuno za Yehova kuyambira m’masiku oyambirirawo 1914 asanafike pamene zonse zinali zosadziŵika bwino kwambiri . . . kufikira lero pamene choonadi chikuŵala ngati dzuŵa lamasana. Ngati palinso chinthu china chimene chakhala chofunika koposa kwa ine, ndicho nkhani ya kukhala omamatirana ndi gulu la Yehova looneka. Chokumana nacho changa choyambirira chinandiphunzitsa mmene kudalira pa kulingalira kwaumunthu kulili kopanda nzeru. Pamene maganizo anga anatsimikizira za mfundoyo, ndinatsimikiza za kumamatirana ndi gulu lokhulupirika. Kodi munthu angapezenso motani chiyanjo cha Yehova ndi dalitso?”
20. Kodi nchiyani chimene tiyenera kutsimikiza kuchita ponena za umodzi wathu monga anthu a Yehova?
20 Yehova waitana anthu ake kuchoka mu mdima wadziko ndi kusagwirizana kwake. (1 Petro 2:9) Watibweretsa mu umodzi wodalitsidwa ndi iye mwini ndi okhulupirira anzathu. Umodzi umenewu udzakhalapo m’dongosolo latsopano la zinthu limene layandikira kwambiri tsopano. Chotero, m’masiku oŵaŵitsa otsiriza ano, tiyeni tipitirize ‘kudziveka ndi chikondi’ ndi kuchita zonse zimene tingathe kuchirikiza ndi kusunga umodzi wathu wamtengo wapatali.—Akolose 3:14, NW.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuchita chifuniro cha Mulungu ndi kumamatira choonadi kungatithandize kusunga umodzi?
◻ Kodi umodzi ngwogwirizana motani ndi kugwiritsira ntchito bwino lilime?
◻ Kodi nchiyani chimene chimaloŵetsedwa m’kukhululukira?
◻ Kodi tingasunge umodzi motani popanga zosankha zamunthu mwini?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kusunga umodzi wachikristu?
[Chithunzi patsamba 16]
Monga momwe mbusa uyu amasungira pamodzi khosa zake, Yehova amasunga anthu mu umodzi
[Zithunzi patsamba 18]
Mwa kupepesa modzichepetsa pamene tikhumudwitsa wina, timathandizira kuchirikiza umodzi