Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 7/15 tsamba 26-29
  • Gamaliyeli—Anaphunzitsa Saulo wa ku Tariso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gamaliyeli—Anaphunzitsa Saulo wa ku Tariso
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Gamaliyeli Anali Yani?
  • Kuphunzitsidwa ndi Gamaliyeli​—Motani?
  • Mzimu wa Ziphunzitso za Gamaliyeli
  • Kodi Kunatanthauzanji kwa Paulo?
  • ‘Sitingaleke Kulankhula za Yesu’
    Nsanja ya Olonda—2006
  • “Ife Tiyenera Kumvera Mulungu Monga Wolamulira”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Mishnah—ndi Chilamulo cha Mulungu kwa Mose
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kupita Patsogolo Kukagonjetsa Komaliza!
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 7/15 tsamba 26-29

Gamaliyeli​—Anaphunzitsa Saulo wa ku Tariso

KHAMULO linakhala chete. Nthaŵi pang’ono zimenezo zisanachitike, linali litatsala pang’ono kupha mtumwi Paulo. Wotchedwanso Saulo wa ku Tariso, iye anapulumutsidwa ndi asilikali a Roma ndipo apa anaimirira pa makwerero pafupi ndi kachisi m’Yerusalemu kuyang’anizana ndi anthuwo.

Atatontholetsa anthu ndi mkono, Paulo anayamba kulankhula m’Chihebri, akumati: “Amuna, abale, ndi atate, mverani chodzikanira changa tsopano, . . . Ine ndine munthu Myuda, wobadwa m’Tariso wa Kilikiya, koma [ndinaphunzitsidwa m’mzinda uno, NW] pa mapazi a Gamaliyeli, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero.”​—Machitidwe 22:1-3.

Pokhala moyo wake unali pangozi, kodi nchifukwa ninji Paulo anayamba chodzikanira chake mwa kunena kuti anaphunzitsidwa ndi Gamaliyeli? Kodi Gamaliyeli anali yani, ndipo kuphunzitsidwa ndi iye kunaphatikizapo chiyani? Kodi maphunziro ameneŵa anakhudza Saulo ngakhale pamene anakhala mtumwi Paulo wachikristu?

Kodi Gamaliyeli Anali Yani?

Gamaliyeli anali Mfarisi wodziŵika kwambiri. Anali mdzukulu wa Hillel Wamkulu, amene anayambitsa limodzi la magulu aakulu aŵiri a chiphunzitso m’Chiyuda cha Afarisi.a Anthu anaona kaphunzitsidwe ka Hillel kukhala kololera kwambiri kuposa ka mnzake, Shammai. Pambuyo pa kuwonongedwa kwa kachisi wa Yerusalemu mu 70 C.E., anthu anakonda Bet Hillel (Nyumba ya Hillel) m’malo mwa Bet Shammai (Nyumba ya Shammai). Nyumba ya Hillel inakhala njira yalamulo yotsatirira Chiyuda, pakuti timagulu tina tonse tinazimiririka pa kuwonongedwa kwa kachisi. Nthaŵi zambiri zigamulo za Bet Hillel ndizo zimakhala maziko a chilamulo chachiyuda m’Mishnah, imene inakhala maziko a Talmud, ndipo zikuchita ngati kuti chisonkhezero cha Gamaliyeli chinathandizira kwambiri kutchuka kwake.

Gamaliyeli analemekezedwa kwambiri kwakuti anali woyamba kutchedwa rabani dzina laulemu loposa lija lakuti rabi. Kwenikweni, Gamaliyeli anakhala munthu wolemekezeka kwambiri kwakuti Mishnah imati za iye: “Pamene Rabani Gamaliyeli wamkulu anamwalira ulemerero wa Torah unatha, ndipo chiyero ndi kupatulika zinawonongeka.”​—Sotah 9:15.

Kuphunzitsidwa ndi Gamaliyeli​—Motani?

Pamene mtumwi Paulo anauza khamulo m’Yerusalemu kuti ‘anaphunzitsidwa pa mapazi a Gamaliyeli,’ anatanthauzanji? Kodi kukhala wophunzira wa mphunzitsi wonga Gamaliyeli kunaphatikizaponji?

Ponena za maphunziro otero, Profesa Dov Zlotnick wa Jewish Theological Seminary ya America akulemba kuti: “Kulondola kwa chilamulo cha pakamwa, ndiponso kudalirika kwake, kunadalira kwambiri pa unansi wa mbuye ndi wophunzira wake: chisamaliro choperekedwa ndi mbuyeyo pophunzitsa chilamulo ndi chifuno cha wophunzirayo pophunzira. . . . Chifukwa chake, ophunzira analimbikitsidwa kukhala pa mapazi a akatswiriwo . . . ‘ndi kumwa mawu awo ndi ludzu.’”​—Avot 1:4, Mishnah.

M’buku lake lakuti A History of the Jewish People in the Time of Jesus Christ, Emil Schürer akusonyeza njira zimene aphunzitsi achirabi a m’zaka za zana loyamba anali kugwiritsira ntchito. Iye akulemba kuti: “Arabi otchuka kwambiri anali kusonkhanitsa mowazinga achichepere ambiri ofuna kuphunzira, ndi cholinga chowaphunzitsa bwino lomwe ‘chilamulo cha pakamwa’ chokhala ndi zosiyanasiyana ndi mawu ochuluka. . . . Maphunzirowo anaphatikizapo mayeso osatha anthaŵi zonse oyesa chikumbuko. . . . Mphunzitsi anali kufunsa ophunzira ake mafunso angapo pa zamalamulo kuti iwo agamule ndi kuwalola kuyankha kapena iyemwini anawayankhira. Ndiponso ophunzirawo analoledwa kufunsa mphunzitsi.”

Malinga ndi chikhulupiriro cha arabi, zimene zinali kufunika kwa ophunzirawo zinali zazikulu kuposa kungopeza magiredi apamwamba. Ophunzitsidwa ndi aphunzitsi otero anachenjezedwa kuti: “Yense woiŵala ngakhale kanthu kamodzi kokha pa zimene waphunzira​—Malemba amasonyeza kuti iye amachita ngati wapereka moyo wake.” (Avot 3:8) Thamo lalikulu koposa linaperekedwa kwa wophunzira amene anali ngati “chitsime chakonkire, chimene sichimataya ndi dontho la madzi.” (Avot 2:8) Amenewo ndiwo maphunziro omwe Paulo, wodziŵika panthaŵiyo ndi dzina lake lachihebri, Saulo wa ku Tariso, analandira kwa Gamaliyeli.

Mzimu wa Ziphunzitso za Gamaliyeli

Malinga ndi chiphunzitso cha Afarisi, Gamaliyeli anachirikiza chilamulo cha pakamwa. Motero iye anagogomezera kwambiri miyambo ya arabi m’malo mwa Malemba ouziridwa. (Mateyu 15:3-9) Mishnah imagwira mawu a Gamaliyeli akuti: “Dzipezere mphunzitsi [rabi] ndipo sudzakhala ndi zikayikiro, pakuti suyenera kupereka chachikhumi chopambanitsa mwa kungoyerekezera.” (Avot 1:16) Zimenezi zinatanthauza kuti pamene Malemba Achihebri sanasonyeze chochita, munthu sanayenera kugwiritsira ntchito malingaliro ake kapena kutsatira chikumbumtima chake popanga chosankha. M’malo mwake, anafunikira kupeza rabi woyenerera amene akanampangira chosankha. Malinga ndi Gamaliyeli, ndi mwanjira imeneyi yokha imene munthu akanapeŵera kuchimwa.​—Yerekezerani ndi Aroma 14:1-12.

Komabe, Gamaliyeli anadziŵika kwambiri ndi mzimu wake wololera ndi waufulu pa zigamulo zake za milandu yachipembedzo. Mwachitsanzo, anasonyeza chifundo kwa akazi pamene anagamula kuti “adzalola mkazi kukwatiwanso pamaso pa mboni imodzi [imene inaona imfa ya mwamuna wake].” (Yevamot 16:7, Mishnah) Ndiponso, kuti atetezere mkazi wosudzulidwa, Gamaliyeli anapereka ziletso zingapo zokhudza kuperekedwa kwa chikalata cha chisudzulo.

Mzimu umenewu ukuonekanso m’zochita za Gamaliyeli ndi otsatira oyambirira a Yesu Kristu. Buku la Machitidwe limasimba kuti pamene atsogoleri ena achiyuda anafuna kupha atumwi a Yesu amene anali atawagwira akulalikira, “wina pa bwalo la akulu, ndiye Mfarisi, dzina lake Gamaliyeli, mphunzitsi wa chilamulo, wochitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang’ono. Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israyeli, kadzichenjerani nokha za anthu aŵa, chimene muti muwachitire. . . . Ndinena ndi inu, Lekani anthu ameneŵa, nimuwalole akhale; . . . kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.” Uphungu wa Gamaliyeli unatsatiridwa ndipo atumwiwo anamasulidwa.​—Machitidwe 5:34-40.

Kodi Kunatanthauzanji kwa Paulo?

Paulo analangizidwa ndi kuphunzitsidwa ndi mmodzi wa aphunzitsi achirabi aakulu koposa a m’zaka za zana loyamba C.E. Mosakayikira kutchula Gamaliyeli kwa mtumwiyo kunachititsa khamulo m’Yerusalemu kutchera khutu kwambiri ku zokamba zake. Koma iye analankhula nawo za Mphunzitsi woposa Gamaliyeli​—Yesu, Mesiya. Apa Paulo analankhula ndi khamulo monga wophunzira wa Yesu osati wa Gamaliyeli.​—Machitidwe 22:4-21.

Kodi kuphunzitsidwa ndi Gamaliyeli kunakhudza chiphunzitso cha Paulo monga Mkristu? Nzotheka kuti malangizo okhwima a m’Malemba ndi chilamulo chachiyuda anamthandiza kwambiri Paulo monga mphunzitsi wachikristu. Komabe, makalata a Paulo ouziridwa ndi Mulungu opezeka m’Baibulo amasonyeza bwino lomwe kuti iye anakana maziko a chikhulupiriro cha Gamaliyeli cha Afarisi. Paulo analozera Ayuda anzake ndi ena onse kwa Yesu Kristu, osati kwa arabi a Chiyuda kapena miyambo ya anthu.​—Aroma 10:1-4.

Ngati Paulo akanapitiriza kukhala wophunzira wa Gamaliyeli, akanakhala wotchuka kwambiri. Ena a m’gulu la Gamaliyeli anathandiza kulinganiza mtsogolo mwa Chiyuda. Mwachitsanzo, mwana wa Gamaliyeli Simeon, mwinamwake wophunzira mnzake wa Paulo, anachirikiza kwambiri kupandukira Roma kwa Ayuda. Pambuyo pa chiwonongeko cha kachisi, mdzukulu wa Gamaliyeli, Gamaliyeli II anabwezeretsa mphamvu ya Sanhedrin, akumaisamutsira ku Yavneh. Mdzukulu wa Gamaliyeli II, Judah Ha-Nasi ndiye anasonkhanitsa Mishnah, imene yakhala maziko a chiphunzitso chachiyuda mpaka lero.

Monga wophunzira wa Gamaliyeli, mwina Saulo wa ku Tariso anakhala wotchuka kwambiri m’Chiyuda. Komabe, ponena za ntchito imeneyo, Paulo analemba kuti: “Zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa chitayiko chifukwa cha Kristu. Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Kristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadziwonjezere Kristu.”​—Afilipi 3:7, 8.

Mwa kusiya ntchito yake monga Mfarisi ndi kukhala wotsatira wa Yesu Kristu, Paulo anali kugwiritsira ntchito uphungu wa kupeŵa ‘kupezeka otsutsana’ ndi Mulungu woperekedwa ndi yemwe kale anali mphunzitsi wake. Mwa kuleka kwake kuzunza ophunzira a Yesu, Paulo anasiya kutsutsana ndi Mulungu. M’malo mwake, mwa kukhala wotsatira wa Kristu, anakhala mmodzi wa “antchito anzake a Mulungu.”​—1 Akorinto 3:9.

Uthenga wa Chikristu choona ukupitiriza kulengezedwa ndi Mboni zachangu za Yehova m’tsiku lathu. Monga Paulo, ambiri mwa ameneŵa asintha kwambiri moyo wawo. Ena alepa ntchito zabwino kwambiri kuti atengemo mbali kwambiri m’ntchito yolalikira Ufumu, inde ntchito ‘yochokera kwa Mulungu.’ (Machitidwe 5:39) Ali okondwa chotani nanga kuti atsanzira chitsanzo cha Paulo m’malo mwa chija cha amene kale anali mphunzitsi wake, Gamaliyeli!

[Mawu a M’munsi]

a Maumboni ena amasonyeza kuti Gamaliyeli anali mwana wa Hillel. Talmud simanena bwinobwino pankhaniyi.

[Chithunzi patsamba 28]

Atakhala mtumwi Paulo, Saulo wa ku Tariso analengeza uthenga wabwino kwa anthu a mitundu yonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena