Kodi Sou Siimafa?
MWAKACHETECHETE, mabwenzi ndi a banja akudutsa pa bokosi lamaliro lotseguka. Iwo akuyang’ana mtembo wa mnyamata wazaka 17. Mabwenzi ake akusukulu satha kumzindikira. Njira yochiritsira yotchedwa chemotherapy yathothola tsitsi lake lochuluka, kansa yamuondetsa kwambiri. Kodi ameneyu ndiyedi bwenzi lawo lija? Milungu yochepa yapitapo, anali wodzala ndi nzeru, mafunso, nyonga—ndi moyo! Amake a mnyamatayu akulira ndi kubwereza mawu akuti: “Tommy akukondwera tsopano. Mulungu anafuna Tommy kukakhala naye kumwamba.”
Mayi wosweka mtima ameneyu akupezako chiyembekezo ndi chitonthozo m’lingaliro lakuti m’njira inayake mwana wake adakali ndi moyo. M’tchalitchi iye waphunzitsidwa kuti sou siimafa, ndi kuti ndiyo maziko a umunthu, malingaliro, zikumbukiro—“munthu weniweni.” Iye akukhulupirira kuti sou ya mwana wake siinafe konse; pokhala mzimu wamoyo, inachoka m’thupi la mwanayo pa imfa ndi kupita kumwamba kukakhala pamodzi ndi Mulungu ndi angelo.
Panthaŵi ya tsoka, mtima wa munthu pothedwa nzeru umangokhulupirira chiyembekezo chilichonse choperekedwa, motero nkosavuta kuona chifukwa chake chikhulupiriro chimenechi chili chofala kwambiri. Mwachitsanzo, talingalirani njira imene wophunzitsa zaumulungu J. Paterson-Smyth akulankhulira mu The Gospel of the Hereafter: “Imfa ndi kanthu kakang’ono kwambiri poiyerekezera ndi chimene chimatsatirapo—dziko lokongola, lokongola, lokongola kwenikweni limene Imfa imatiloŵetsamo.”
Kuzungulira dziko lonse ndi m’zipembedzo ndi miyambo yambiri, anthu amakhulupirira kuti munthu ali ndi sou yosafa mkati mwake, mzimu woganiza umene umapitiriza kukhala ndi moyo thupi litafa. Chikhulupiriro chimenechi chimapezeka pafupifupi m’zikwi zonse za zipembedzo za Dziko Lachikristu ndi mipatuko yake. Chilinso chiphunzitso chalamulo m’Chiyuda. Ahindu amakhulupirira kuti atman, kapena sou, inalengedwa pamene nthaŵi inayamba, imaikidwa m’ndende ya thupi pa kubadwa, ndipo imasamukira m’thupi lina pa imfa mwa zungulirezungulire wa kubadwanso kwa sou. Asilamu amakhulupirira kuti sou imapangidwa pamodzi ndi thupi ndipo imapitiriza kukhala ndi moyo pamene thupi limwalira. Zikhulupiriro zina—chipembedzo chamwambo cha mu Afirika, Chishinto, ngakhale Chibuda m’njira ina—zimaphunzitsa zosiyanasiyana pa nkhani imodzimodzi imeneyi.
Mafunso Ena Ovutitsa Maganizo
Ngakhale kuti lingaliro la sou yosafa nlofala mosakanika ndipo nlokhulupiriridwa kuzungulira dziko lonse, limabutsa mafunso ena ovutitsa maganizo. Mwachitsanzo, anthu sakudziŵa kumene kumapita sou ya wokondedwa ngati kuti anali ndi moyo wa makhalidwe oipa. Kodi adzabadwanso m’cholengedwa china chosakhala munthu? Kapena kodi amatumizidwa ku purigatoriyo, kumene adzayeretsedwa ndi moto kufikira atayesedwa woyenera kupita kumwamba? Chovutitsanso maganizo kwenikweni nchakuti, kodi iye adzazunzidwa kosatha m’helo woyaka moto? Kapena, kodi iye ali mzimu umene umafuna kupatsidwa nsembe yotonthoza, monga momwe achipembedzo chamwambo amaphunzitsira?
Malingaliro oterowo amapereka ziyembekezo zovutitsa maganizo kwa amoyo. Kodi tiyenera kutonthoza mizimu ya akufa athu okondedwa kotero kuti isatibwezere chilango? Kodi tiyenera kuithandiza kutuluka m’purigatoriyo wosautsa? Kapena kodi tiyenera kungowopa popanda chochita poganizira za kuzunzika kwawo mu helo? Kapena kodi tiyenera kuona nyama zina zamoyo monga zonyamula sou za anthu akufa?
Mafunso amene amabuka ponena za Mulungu mwini alinso ovutitsa maganizo. Mwachitsanzo, makolo ambiri, mofanana ndi mayi wotchulidwa kuchiyambi, poyamba amatonthozedwa ndi lingaliro lakuti Mulungu “anatenga” sou yosafa ya mwana wawo ndi kukhala nayo kumwamba. Komabe, sipamapita nthaŵi kuti ambiri ayambe kudabwa kuti ndi Mulungu wamtundu wanji amene angachititse mwana wopanda mlandu kudwala nthenda yowopsa, kukwatula mwanayo wamtengo wapatali kwa makolo ake osweka mtimawo kokha kuti asamutsire mwanayo kumwamba ndi imfa yosayembekezereka. Kodi chili kuti chilungamo chake Mulungu woteroyo, chikondi chake, ndi chifundo chake? Ena amakayikira ngakhale nzeru ya Mulungu wotero. Amafunsa kuti, kodi Mulungu wanzeru angaikirenji sou zonsezi padziko lapansi ngati kuti zonse zidzapita kumwamba? Kodi zimenezo sizikutanthauza kuti chilengedwe cha dziko lapansi changokhala kuwonongera mphamvu pachabe kwakukulu?—Yerekezerani ndi Deuteronomo 32:4; Salmo 103:8; Yesaya 45:18; 1 Yohane 4:8.
Mwachionekere pamenepa, chiphunzitso cha kusafa kwa sou ya munthu, m’njira iliyonse imene chingaphunzitsidwire, chimabutsa mafunso othetsa nzeru, ndi owombananso. Chifukwa ninji? Chochititsa vuto kwambiri ndicho magwero a chiphunzitso chimenechi. Mungadziŵe zambiri ngati mufufuza magwero amenewo mwachidule; ndipo mungadabwe kudziŵa zimene Baibulo limanena za sou. Limapereka chiyembekezo chabwino koposa cha moyo wa pambuyo pa imfa kuposa zimene zipembedzo zadziko zonse zimaphunzitsa.