‘Muyenera Kukhala Oyera Pakuti Ine Ndine Woyera’
“Muzikhala oyera; pakuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.”—LEVITIKO 19:2.
1. Kodi ndi anthu ena ati amene dziko limawayesa oyera?
ZIPEMBEDZO zazikulu zochuluka za dzikoli zili ndi awo amene zimawayesa oyera. Mayi Teresa wotchuka ku India amayesedwa woyera nthaŵi zambiri chifukwa cha kudzipereka kwake kwa osauka. Papa amatchedwa “Atate Woyera.” Akatolika ena amaona José María Escrivá, woyambitsa kagulu kamakono kachikatolika kotchedwa Opus Dei, kukhala “chitsanzo cha chiyero.” Chihindu chili ndi aswami ake, kapena amuna oyera. Gandhi analemekezedwa monga munthu woyera. Chibuda chili ndi amonke ake, ndipo Chisilamu mneneri wake woyera. Koma kodi kukhala woyera kumatanthauzanji kwenikweni?
2, 3. (a) Kodi mawuwo “choyera” ndi “chiyero” amatanthauzanji? (b) Kodi ndi mafunso ena otani amene afunikira kuyankhidwa?
2 Liwu lakuti “choyera” latanthauzidwa kukhala “1. . . . chogwirizana ndi mphamvu yaumulungu; chopatulika. 2. Choyesedwa kukhala choyenera kulambiridwa kapena kulemekezedwa . . . 3. Kutsatira njira yosamalitsa kapena ya makhalidwe apamwamba yachipembedzo kapena yauzimu . . . 4. Chosankhidwa kapena chopatulidwa kaamba ka chifuno cha chipembedzo.” M’Baibulo, chiyero chimatanthauza “ungwiro wachipembedzo kapena kuyera; kupatulika.” Malinga ndi buku la maumboni a Baibulo la Insight on the Scriptures, “[liwu] loyambirira lachihebri qoʹdhesh limapereka lingaliro la kulekanitsidwa, kukhala padera, kupatulira kwa Mulungu, . . . mkhalidwe wa kupatulidwa kaamba ka utumiki wa Mulungu.”a
3 Mtundu wa Israyeli unalamulidwa kukhala woyera. Chilamulo cha Mulungu chinati: “Ine ndine Yehova Mulungu wanu; potero dzipatuleni, ndipo muzikhala oyera; pakuti ine ndine woyera.” Kodi ndani anali Magwero a chiyero? Kodi Aisrayeli opanda ungwiro akanakhala motani oyera? Ndipo ndi maphunziro otani amene tingatengepo lerolino pa pempho la Yehova la kukhala oyera?—Levitiko 11:44.
Kaimidwe ka Israyeli Kulinga ku Magwero a Chiyero
4. Kodi ndi motani mmene chiyero cha Yehova chinachitiridwa chithunzi m’Israyeli?
4 Chilichonse chokhudza kulambira Yehova Mulungu kwa Israyeli chinayenera kuyesedwa choyera ndi kuchitidwa motero. Chifukwa ninji? Chifukwa Yehova mwiniyo ndiye chiyambi cha chiyero ndipo ndiye magwero ake. Nkhani ya Mose yonena za kukonza chihema choyera ndi zovala ndi zokometsera imatha ndi mawu akuti: “Ndipo anapanga phanthiphanthi wa korona wopatulika wa golidi woona, nalembapo lemba, ngati malochedwe a chosindikizira, Kupatulikira Yehova [“Chiyero ncha Yehova,” NW].” Phanthiphanthi ameneyu wonyezimira wa golidi woona anamangiriridwa ku nduŵira ya mkulu wa ansembe, ndipo anali kusonyeza kuti iyeyo anali wopatulidwa kaamba ka utumiki wapadera wachiyero. Pamene anaona chizindikiro cholocha chimenechi chikung’anima padzuŵa, Aisrayeli anakumbutsidwa nthaŵi zonse za chiyero cha Yehova.—Eksodo 28:36; 29:6; 39:30.
5. Kodi ndi motani mmene Aisrayeli opanda ungwiro akanalingaliridwira kukhala oyera?
5 Koma kodi ndi motani mmene Aisrayeli akanakhalira oyera? Ndi kokha mwa unansi wawo wapafupi ndi Yehova ndi kumlambira kwawo koyera. Anafunikira chidziŵitso cholongosoka cha “Woyerayo” kuti amlambire m’chiyero, chakuthupi ndi chauzimu. (Miyambo 2:1-6; 9:10) Chifukwa chake Aisrayeli anafunikira kulambira Mulungu ndi maganizo oyera ndi mtima woyera. Kulambira kulikonse kwachinyengo kukanakhala konyansa kwa Yehova.—Miyambo 21:27.
Chimene Yehova Anatsutsira Israyeli
6. Kodi ndi motani mmene Ayuda m’tsiku la Malaki anachitira ndi gome la Yehova?
6 Zimenezo zinasonyezedwa bwino pamene Aisrayeli mwamphwayi anabweretsa nsembe zachabe ndi zotsimphina ku kachisi. Kupyolera mwa mneneri wake Malaki, Yehova anatsutsa nsembe zawo zachabe akumati: “Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m’dzanja lanu. . . . Koma inu [munditonza, NW], pakunena inu, Gome la Yehova laipsidwa, ndi zipatso zake, chakudya chake, chonyozeka. Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira ku dzanja lanu? ati Yehova.”—Malaki 1:10, 12, 13.
7. Kodi ndi machitachita opanda chiyero ati amene Ayuda anali kuchita m’zaka za zana lachisanu B.C.E.?
7 Mulungu anagwiritsira ntchito Malaki kutsutsa machitachita onyenga a Ayuda, mwinamwake m’zaka za zana lachisanu B.C.E. Ansembe anali kupereka chitsanzo choipa, ndipo khalidwe lawo silinali loyera konse. Anthu, potsatira utsogoleri wawo, analibe makhalidwe abwino, ndipo anafikira ngakhale pa kusudzula akazi awo, mwinamwake kuti akwatire akazi achichepere akunja. Malaki analemba kuti: “Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika,b chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako. . . . Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana [wako, NW] ndi mmodzi yense. Pakuti ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israyeli.”—Malaki 2:14-16.
8. Kodi ena mumpingo wachikristu ayambukiridwa motani ndi lingaliro lamakono la chisudzulo?
8 M’nthaŵi zamakono, m’maiko ambiri kumene anthu amasudzulana mosavuta, chiŵerengero cha zisudzulo chakwera kwambiri. Ngakhale mpingo wachikristu wayambukiridwa. M’malo mopempha thandizo kwa akulu lolakira zopinga ndi kuyesa kuchirikiza ukwati wawo kuti upambane, ena authetsa msangamsanga. Kaŵirikaŵiri ana ndiwo amavutika mtima chifukwa cha zimenezo.—Mateyu 19:8, 9.
9, 10. Kodi tiyenera kuganiza za chiyani ponena za kulambira kwathu Yehova?
9 Monga momwe taonera kale, chifukwa cha mkhalidwe wonyansa wauzimu m’tsiku la Malaki, Yehova anatsutsiratu kulambira kwachabe kwa Yuda nasonyeza kuti adzangolandira kulambira koyera. Kodi zimenezi siziyenera kutiganizitsa za mkhalidwe wa kulambira kwathu Yehova Mulungu, Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse, Magwero a chiyero choona? Kodi tikuperekadi utumiki woyera kwa Mulungu? Kodi timadzisunga oyera mwauzimu?
10 Zimenezi sizikutanthauza kuti tiyenera kukhala angwiro, zimene sizitheka, kapena kuti tiyambe kumadziyerekezera ndi ena. Komatu zimatanthauza kuti Mkristu aliyense ayenera kumapatsa Mulungu kulambira kumene kuli kwabwino kwambiri malinga ndi mikhalidwe yake. Zimenezi zikutanthauza mkhalidwe wa kulambira kwathu. Utumiki wathu wopatulika uyenera kukhala wabwino koposa—utumiki woyera. Kodi zimenezo zimatheka bwanji?—Luka 16:10; Agalatiya 6:3, 4.
Mtima Woyera Umatsogolera ku Kulambira Koyera
11, 12. Kodi khalidwe lopanda chiyero limachokera kuti?
11 Yesu anaphunzitsa bwino kuti zimene zili mumtima zidzaonekera mwa zimene munthu amalankhula ndi kuchita. Yesu anati kwa Afarisi odzilungamitsa, koma opanda chiyero: “Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m’kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.” Pambuyo pake anasonyeza kuti ntchito zoipa zimachokera m’maganizo oipa mumtima, kapena munthu wamkati. Iye anati: “Zakutuluka m’kamwa zichokera mumtima; ndizo ziipitsa munthu. Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano; izi ndizo ziipitsa munthu.”—Mateyu 12:34; 15:18-20.
12 Zimenezi zikutithandiza kuzindikira kuti ntchito zopanda chiyero sizimangoyamba zokha kapena popanda maziko apasadakhale. Zimakhala zotulukapo za malingaliro odetsa amene akhala obisala mumtima—zilakolako zobisika ndipo mwinamwake zolingalira. Nchifukwa chake Yesu anati: “Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; koma ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.” M’mawu ena, dama ndi chigololo zimakhala zitazika kale mizu mumtima munthu asanachite kalikonse. Ndiyeno, mpata utapezeka, malingaliro opanda chiyerowo amakhala khalidwe lopanda chiyero. Dama, chigololo, mathanyula, kuba, chitonzo, ndi mpatuko zimakhala zina za zotulukapo zake.—Mateyu 5:27, 28; Agalatiya 5:19-21.
13. Kodi ndi zitsanzo zina zotani zimene zikusonyeza mmene malingaliro opanda chiyero angatsogolere ku machitachita opanda chiyero?
13 Zimenezi zingafotokozedwe ndi zitsanzo zosiyanasiyana. M’maiko ena, nyumba za juga zikuchuluka, motero zikumapereka mpata waukulu wa kutchova juga. Wina angakopeke ndi chooneka ngati chothetsera mavuto chimenechi ndi kuyesa kuthetsa mavuto ake a ndalama. Malingaliro onyenga angasonkhezere mbale kunyalanyaza kapena kululuza mapulinsipulo a Baibulo.c Nthaŵi zina, zamaliseche zosavuta kupeza, kaya pa TV, mavidiyo, makompyuta, kapena m’mabuku, zingachititse Mkristu kukhala ndi khalidwe lopanda chiyero. Amangonyalanyaza zovala zake zankhondo zauzimu, ndipo posapita nthaŵi, amagwera m’chisembwere. Koma nthaŵi zambiri kugwera mu tchimo kumayambira m’maganizo. Inde, m’mikhalidwe yotere, mawu a Yakobo amakwaniritsidwa akuti: “Munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo.”—Yakobo 1:14, 15; Aefeso 6:11-18.
14. Kodi ambiri achira motani pa khalidwe lawo lopanda chiyero?
14 Mwamwaŵi, Akristu ambiri amene amachimwa chifukwa cha kufooka amasonyeza kulapa koona, ndipo akulu amakhoza kuwachiritsa mwauzimu. Ngakhale ambiri amene amachotsedwa chifukwa cha kusalapa m’kupita kwa nthaŵi amazindikira kulakwa kwawo ndipo amabwezeretsedwanso mumpingo. Amazindikira mmene Satana anawagonjetsera mosavuta pamene iwo analola malingaliro opanda chiyero kuzika mizu mumtima mwawo.—Agalatiya 6:1; 2 Timoteo 2:24-26; 1 Petro 5:8, 9.
Vuto la Kuvomereza Zofooka Zathu
15. (a) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuvomereza zofooka zathu? (b) Kodi nchiyani chingatithandize kuzindikira zofooka zathu?
15 Tiyenera kuyesetsa kuudziŵa bwino mtima wathu. Kodi ndife okonzekera kuvomereza zofooka zathu, kuzizindikira, ndiyeno kulimbikira kuzigonjetsa? Kodi ndife okonzekera kufunsa bwenzi loona mtima mmene tingawongolere, ndiyeno kulabadira uphunguwo? Kuti tikhale oyera, tiyenera kulaka zofooka zathu. Chifukwa? Chifukwa Satana amadziŵa zofooka zathu. Adzagwiritsira ntchito machenjera ake kutisonkhezera kuchimwa ndi kuloŵa m’khalidwe lopanda chiyero. Mwa machenjera ake, amayesa kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu kuti tisakhalenso opatulika ndi ofunika pa kulambira Yehova.—Yeremiya 17:9; Aefeso 6:11; Yakobo 1:19.
16. Kodi Paulo anali pankhondo yotani?
16 Mtumwi Paulo anakumana ndi ziyeso ndi mayesero ake, malinga ndi zimene ananena m’kalata yake kwa Aroma: “Ndidziŵa kuti mkati mwanga, ndiko m’thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza. Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichita. . . . Pakuti monga mwa munthu wa mkati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziŵalo zanga.”—Aroma 7:18-23.
17. Kodi Paulo analakika motani pakulimbana kwake ndi zofooka?
17 Tsopano m’nkhani ya Paulo mfundo yofunika kwambiri njakuti iye anazindikira zofooka zake. Ngakhale kuti anali nazo, iye anatha kunena kuti: “Monga mwa munthu [wauzimu] wa mkati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu.” Paulo anakonda chabwino ndi kudana nacho choipa. Komabe anali pankhondo, nkhondo imodzimodzi yomwe ife tonse tili nayo—yolimbana ndi Satana, dziko, ndi thupi. Chotero kodi tingapambane bwanji nkhondoyo kuti tikhalebe oyera, olekana ndi dzikoli ndi kalingaliridwe kake?—2 Akorinto 4:4; Aefeso 6:12.
Kodi Ndi Motani Mmene Tingakhalirebe Oyera?
18. Kodi ndi motani mmene tingakhalirebe oyera?
18 Chiyero sichimapezeka mwa kutsatira njira yongolekerera zinthu kapena mwa kufuna kudzikhutiritsa. Munthu wotero amaŵiringula nthaŵi zonse pa khalidwe lake ndipo amayesa kuika mlandu pa ena kapena zinthu zina. Mwinamwake tifunikira kuphunzira kukhala athayo pa zochita zathu ndi kusakhala ngati ena amene amati palibe zimene angachite popeza ali ndi tsoka chifukwa cha banja limene anabadwiramo kapena chibadwa chawo. Muzu wa vutolo uli mumtima wa munthuyo. Kodi iye amakonda chilungamo? amalakalaka chiyero? amakhumba dalitso la Mulungu? Wamasalmo anamveketsa bwino lomwe kufunika kwake kwa chiyero pamene anati: “Futuka pa zoipa, nuchite zabwino, funa mtendere ndi kuulondola.” Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chikondano [chanu, NW] chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino.”—Salmo 34:14; 97:10; Aroma 12:9.
19, 20. (a) Kodi ndi motani mmene tingamangirire maganizo athu? (b) Kodi phunziro laumwini lobala zipatso limafunanji?
19 ‘Tingagwirizane nacho chabwino’ ngati timaona zinthu mmene Yehova amazionera ndipo ngati tili ndi mtima wa Kristu. (1 Akorinto 2:16) Kodi tingachite motani zimenezi? Mwa phunziro la nthaŵi zonse ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu. Ha, uphungu umenewu waperekedwa nthaŵi zambiri chotani nanga! Koma kodi timauona kukhala wofunika kwambiri? Mwachitsanzo, kodi mumaphunziradi magazini ano, kuŵerenga malemba m’Baibulo, musanabwere kumsonkhano? Mwa kuphunzira sitikutanthauza chabe kuchonga mawu angapo m’ndime iliyonse. Kungoŵerenga nkhani yophunzira ndi kuichonga kungatitengere mphindi ngati 15 zokha. Kodi zimenezo zimatanthauza kuti taiphunzira nkhaniyo? Kwenikweni, kungatenge ola limodzi kapena aŵiri kuphunzira ndi kumvetsa phindu lauzimu limene nkhani iliyonse imapereka.
20 Mwinamwake tifunikira kudziphunzitsa kuchoka ku TV maola angapo mlungu uliwonse ndi kusumikadi maganizo pa chiyero chathu. Phunziro lathu la nthaŵi zonse limatimangirira mwauzimu, kusonkhezera maganizo athu kupanga zosankha zoyenera—zosankha zotsogolera ku “mayendedwe opatulika.”—2 Petro 3:11; Aefeso 4:23; 5:15, 16.
21. Kodi ndi funso lotani limene lifunikira kuyankhidwa?
21 Tsopano funso nlakuti, Kodi ndi m’mbali zina ziti za moyo ndi khalidwe zimene ife Akristu tingakhalemo oyera, monga momwedi Yehova alili woyera? Nkhani yotsatira idzasonyeza mfundo zofuna kulingalirapo mwakuya.
[Mawu a M’munsi]
a Buku la maumboni limeneli la mavoliyumu aŵiri limafalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Kuti mupeze malongosoledwe okwanira a tanthauzo la “chosakhulupirika,” onani Galamukani! wa February 8, 1994, tsamba 30, “Kodi Nkusudzula kwa Mtundu Wotani Kumene Mulungu Amada?”
c Kuti mupeze chidziŵitso chowonjezera ponena za chifukwa chake juga ili khalidwe lopanda chiyero, onani Galamukani! wa August 8, 1994, masamba 20-1, wofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi Magwero a chiyero anadziŵikitsidwa motani m’Israyeli?
◻ Kodi ndi m’njira yotani imene kulambira kwa Israyeli kunalili kopanda chiyero m’tsiku la Malaki?
◻ Kodi khalidwe lopanda chiyero limayambira kuti?
◻ Kuti tikhale oyera, tiyenera kuzindikira chiyani?
◻ Kodi ndi motani mmene tingakhalirebe oyera?