Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 10/1 tsamba 20-23
  • Apolo—Mlaliki wa Choonadi Chachikristu Wolankhula Mwanzeru

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Apolo—Mlaliki wa Choonadi Chachikristu Wolankhula Mwanzeru
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Wodziŵa Bwino Malemba”
  • Wachangu Komano Wodzichepetsa
  • Ku Korinto
  • Mikhalidwe Yaumulungu Imene Imachititsa Kukula Kwauzimu Kukhala Kosavuta
  • Lalikirani ndi Cholinga Chopanga Ophunzira
    Nsanja ya Olonda—2003
  • “Anapitiriza kufalikira Ndipo Sankagonjetseka” Ngakhale Kuti Panali Otsutsa
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Zimene Mungachite Kuti Muzipindula Powerenga Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Muzipewa Kuyambitsa Mpikisano Koma Muzilimbikitsa Mtendere
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 10/1 tsamba 20-23

Apolo​—Mlaliki wa Choonadi Chachikristu Wolankhula Mwanzeru

KAYA akhala ali ziŵalo za mpingo wachikristu za zaka zambiri kapena za zaka zoŵerengeka chabe, olengeza Ufumu onse ayenera kukondweretsedwa ndi kupita patsogolo monga alaliki a uthenga wabwino. Zimenezo zikutanthauza kuwonjezera kudziŵa kwathu Mawu a Mulungu ndi kukhoza kwathu kuwaphunzitsa kwa ena. Kwa ena, zingatanthauze kuyang’anizana ndi zitokoso, kugonjetsa zovuta, kapena kudzipereka ku ntchito yowonjezereka.

Baibulo lili ndi zitsanzo zingapo za amuna ndi akazi a nthaŵi zakale amene anapita patsogolo kwambiri mwauzimu mwachipambano m’njira zosiyanasiyana ndi kulandira mfupo zambiri chifukwa cha kuyesayesa kwawo. Mmodzi wa iwo anali Apolo. Pamene Malemba akumdziŵikitsa kwa ife, akumsonyeza kukhala munthu amene ali wosazindikira bwino ziphunzitso zachikristu; komabe, zaka zingapo zitapita, iyeyo akutumikira monga woimira woyendayenda wa mpingo wa m’zaka za zana loyamba. Kodi nchiyani chimene chinamkhozetsa kupanga kupita patsogolo kumeneko? Anali ndi mikhalidwe imene ife tonse tingachite bwino kuitsanzira.

“Wodziŵa Bwino Malemba”

Cha ku ma 52 C.E., malinga ndi kunena kwa wolemba Baibulo Luka, “anafika ku Efeso Myuda wina dzina lake Apolo, fuko lake la ku Alesandreya, munthu wolankhula mwanzeru; ndipo anali [wodziŵa bwino Malemba, NW]. Iyeyo anaphunzitsidwa m’njira ya Ambuye; pokhala nawo mzimu wachangu, ananena ndi kuphunzitsa [molondola, NW] zinthu za Yesu, ndiye wodziŵa ubatizo wa Yohane wokha; ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m’sunagoge.”​—Machitidwe 18:24-26.

Alesandreya, ku Aigupto, unali mzinda wachiŵiri waukulu koposa m’dziko pambuyo pa Roma ndipo unali umodzi wa malo ofunika koposa a zamaphunziro apanthaŵiyo kwa Ayuda ndi Agiriki omwe. Mwinamwake, Apolo anapeza chidziŵitso chake chanzeru cha Malemba Achihebri ndi kulankhula kwina kwanzeru chifukwa cha maphunziro m’chitaganya chachikulu cha Ayuda cha mzinda umenewo. Nkovuta kwambiri kudziŵa kumene Apolo anaphunzira za Yesu. “Malinga ndi umboni iye anali woyendayenda​—mwinamwake wamalonda woyendayenda,” akulingalira motero katswiriyo F. F. Bruce, “ndipo mwina anakumana ndi alaliki achikristu mu alionse a malo ambiri amene anafikako.” Mulimonse mmene zingakhalire, ngakhale kuti analankhula molondola za Yesu, zichita ngati kuti anali atachitiridwapo umboni Pentekoste wa 33 C.E. asanafike, popeza ‘anadziŵa ubatizo wa Yohane wokha.’

Monga wapatsogolo wa Yesu, Yohane Mbatizi anali atapereka umboni wamphamvu ku mtundu wonse wa Aisrayeli, ndipo ambiri anabatizidwa ndi iye monga chizindikiro cha kulapa. (Marko 1:5; Luka 3:15, 16) Malinga ndi kunena kwa olemba mbiri ambiri, anthu okhala pakati pa Ayuda mu Ulamuliro wa Roma sanadziŵe zambiri ponena za Yesu zoposa zimene zinalalikidwa m’mbali mwa Yordano. “Chikristu chawo sichinapyole pa zimene anadziŵa pa kuyamba kwa utumiki wa Ambuye wathu,” akutero W. J. Conybeare ndi J. S. Howson. “Sanali kudziŵa za tanthauzo lonse la imfa ya Kristu; mwinamwake sanadziŵenso za kuuka Kwake kwenikweniko.” Zichita ngati kuti nayenso Apolo sanadziŵe za kutsanulidwa kwa mzimu woyera pa Pentekoste wa 33 C.E. Komabe, iye anapeza chidziŵitso cholondola chonena za Yesu, ndipo sanangokhala nacho. Kwenikweni, iye anafunafuna mipata ya kulankhula zimene anadziŵa. Komano, changu chake ndi kutenthedwa maganizo zinali zisanagwirizanebe ndi chidziŵitso cholongosoka.

Wachangu Komano Wodzichepetsa

Luka akupitiriza kusimba kuti: “Pamene anamumva iye Priskila ndi Akula, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu [molondola kwambiri, NW].” (Machitidwe 18:26) Akula ndi Priskila ayenera kukhala atazindikira kuti chikhulupiriro cha Apolo chinali chofanana kwambiri ndi chawo, komano iwo mwanzeru sanayese kuwongolera kuzindikira kwake kosakwanirako poyera. Mwinamwake anakambitsirana kangapo ndi Apolo, ali ndi cholinga cha kumthandiza. Kodi Apolo, munthu “wamphamvu m’malembo,” anachita motani? (Machitidwe 18:24) Mosakayikira konse, Apolo anali atalalikira uthenga wake wosakwanirawo poyera kwa nthaŵi ina asanakumane ndi Akula ndi Priskila. Munthu wonyada akanakana mosavuta kuwongoleredwa kulikonse, koma Apolo anali wodzichepetsa ndi wothokoza kukhoza kuwonjezera chidziŵitso chake.

Mzimu wodzichepetsa umodzimodziwo wa Apolo ukuonekeranso pa kufunitsitsa kwake kulandira kalata yachivomerezo yochokera kwa abale a ku Efeso kumka ku mpingo wa ku Korinto. Nkhaniyo imati: “Ndipo pamene iye anafuna kuoloka kumka ku Akaya, abale anamfulumiza, ndi kulembera akalata kwa akuphunzira kuti amlandire.” (Machitidwe 18:27; 19:1) Apolo sanakakamize ena kuti amlandire chifukwa cha zoyenera za iye mwini koma modzichepetsa anatsatira makonzedwe a mpingo wachikristu.

Ku Korinto

Zotulukapo zoyamba za utumiki wa Apolo ku Korinto zinali zabwino kwambiri. Buku la Machitidwe limasimba kuti: “Pamene anafika, iye anathangata ndithu iwo akukhulupira mwa chisomo; pakuti ndi mphamvu anatsutsa Ayuda, pamaso pa anthu, nasonyeza mwa malembo kuti Yesu ndiye Kristu.”​—Machitidwe 18:27, 28.

Apolo anadzipatsa ntchito ya kutumikira mpingo, kulimbikitsa abale mwa kukonzekera kwake ndi changu. Kodi nchiyani chimene chinali mfungulo ya chipambano chake? Ndithudi Apolo anali ndi luso lachibadwa ndipo anali wolimba mtima potsutsana poyera ndi Ayuda. Komano chofunika koposa nchakuti, anakambitsirana nawo mogwiritsira ntchito Malemba.

Ngakhale kuti Apolo anali ndi chisonkhezero champhamvu pakati pa Akorinto, mwachisoni kulalikira kwake kunabweretsa ziyambukiro zoipa zosayembekezereka. Motani? Paulo ndi Apolo yemwe anali atachita zambiri m’kufesa ndi kuthirira mbewu za choonadi cha Ufumu mu Korinto. Paulo anali atalalikira kumeneko cha ku ma 50 C.E., zaka ziŵiri Apolo asanafikeko. Podzafika nthaŵi imene Paulo analemba kalata yake yoyamba kwa Akorinto, cha ku ma 55 C.E., malekano anali atayamba. Ena anali kuona Apolo monga mtsogoleri wawo, pamene ena anasankha Paulo kapena Petro kapena kungomamatira kwa Kristu. (1 Akorinto 1:10-12) Ena anali kunena kuti: ‘Ine ndine wa Apolo.’ Chifukwa ninji?

Uthenga umene Paulo ndi Apolo analalikira unali wofanana, komano iwowo anali ndi maumunthu osiyana. Mwa kuvomereza kwa iye mwini, Paulo anali “wosatha kulankhula bwino”; komano Apolo anali “wolankhula mwanzeru.” (2 Akorinto 10:10, NW; 11:6) Anali ndi maluso amene anamkhozetsa kuchititsa Ayuda ena okhala pakati pa chitaganyacho ku Korinto kumumvetsera. Iye anatha ‘kutsutsa Ayuda ndi mphamvu,’ pamene kuli kwakuti Paulo, anali atangochoka kumene pa sunagoge.​—Machitidwe 18:1, 4-6.

Kodi mwina chimenechi chingakhale chifukwa chimene ena anasankhira Apolo? Othirira ndemanga ambiri amalingalira kuti chilakolako chachibadwa cha makambitsirano amtsutsano pakati pa Agiriki mwina chinachititsa ena kukonda malongosoledwe a zinthu otsitsimula kwambiri a Apolo. Giuseppe Ricciotti akulingalira kuti “kalankhulidwe ka [Apolo] kokometsera ndi mafanizo ake abwino kwambiri zinamchititsa kuyamikiridwa ndi ambiri amene anamkonda m’malo mwa Paulo, munthu wolankhula movutikira.” Ngati ena analoladi kukonda munthu kwaumwini kumeneko kuchititsa malekano pakati pa abale, nkosavuta kumvetsa chifukwa chake Paulo anatsutsa mwaphamvu kukweza “nzeru za anzeru.”​—1 Akorinto 1:17-25.

Komabe, kutsutsa kumeneko sikumasonyeza kusamvana pakati pa Paulo ndi Apolo. Ngakhale kuti ena alingalira kuti alaliki aŵiriwa anali adani kwambiri olimbirana kukondedwa ndi Akorinto, Malemba samanena zinthu zilizonse zotero. Mosiyana kwambiri ndi kufuna kudzikweza monga mtsogoleri wa malekano, Apolo anachoka ku Korinto, anabwerera ku Efeso, ndipo anali ndi Paulo pamene iye analemba kalata yoyamba ku mpingo wogaŵanikawo.

Pakati pawo panalibe udani kapena kusagwirizana; m’malo mwake, aŵiriwo mwachionekere anali kuthetsa vuto ku Korinto ndi chidaliro chimodzi mogwirizana. Mwina Paulo anali ndi zikayikiro zina kwa ena ku Korinto komatu osati kwa Apolo. Ntchito ya amuna aŵiriwo inali yogwirizana kotheratu; ziphunzitso zawo zinali zothandizana. Kugwira mawu Paulo mwiniyo, anati: “Ndinawoka ine, anathirira Apolo,” pakuti onsewo anali “antchito anzake a Mulungu.”​—1 Akorinto 3:6, 9, 21-23.

Monga Paulo, Akorinto anachitira Apolo ulemu waukulu, akumakhumba kuchezetsedwanso naye kachiŵiri. Koma pamene Paulo anapempha Apolo kubwerera ku Akorinto, nzika ya Alesandreyayo inakana. Paulo amati: “Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu . . . ndipo sichinali chifuniro chake kuti adze tsopano, koma adzafika pamene aona nthaŵi.” (1 Akorinto 16:12) Apolo mwina angakhale anali wosafuna kubwererako chifukwa cha kuwopa kusonkhezera malekano owonjezereka, kapena mwina chifukwa chakuti anali wotanganitsidwa kwina kwake.

Nthaŵi yotsiriza pamene Apolo akutchulidwa m’Malemba, anali paulendo wa ku Krete ndipo mwinamwake kupyola kumeneko. Kachiŵirinso Paulo akusonyeza kuŵerengera mwapadera bwenzi lakelo ndi wantchito mnzake, akumapempha Tito kukonzera Apolo ndi bwenzi lake lapaulendo, Zena, zonse zimene adzafuna paulendo. (Tito 3:13) Pofika nthaŵiyi, zaka khumi za maphunziro achikristu zitapyola, Apolo anali atapita patsogolo mokwanira kukhala woimira woyendayenda wa mpingo.

Mikhalidwe Yaumulungu Imene Imachititsa Kukula Kwauzimu Kukhala Kosavuta

Mlaliki wa ku Alesandreyayo anapereka chitsanzo chabwino kwa ofalitsa uthenga wabwino onse amakono ndipo, ndithudi, kwa onse amene amakhumba kupita patsogolo mwauzimu. Sitingakhale olankhula mwanzeru monga momwe iye analili, koma tingayesetsedi kutsanzira chidziŵitso chake ndi luso pa kugwiritsira ntchito Malemba, motero tikumathandiza ofuna choonadi oona mtima. Mwa chitsanzo chake cha ntchito yachangu, Apolo “anathangata ndithu iwo akukhulupirira.” (Machitidwe 18:27) Apolo anali wodzichepetsa, wodzimana, ndi wofunitsitsa kutumikira ena. Anazindikira bwino kwambiri kuti mumpingo wachikristu mulibe malo a udani kapena kukhumba kutchuka, pakuti ife tonse ndife “antchito anzake a Mulungu.”​—1 Akorinto 3:4-9; Luka 17:10.

Ife, mofanana ndi Apolo, tingapite patsogolo mwauzimu. Kodi tikufunitsitsa kuwongolera kapena kufutukula utumiki wathu wopatulika, tikumadzipereka m’malo akugwiritsiridwa ntchito mokwanira ndi Yehova ndi gulu lake? Ngati zili choncho tidzakhala ophunzira ndi alaliki achangu a choonadi chachikristu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena