Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 11/1 tsamba 3-6
  • Chitonthozo kwa Otsenderezedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitonthozo kwa Otsenderezedwa
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Wophunzira Wakale wa Chitsenderezo
  • Kutsendereza Kudzatha Posachedwa
  • Alipo Amene Amasamaladi
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Tonthozani Amene ali ndi Chisoni
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Chitonthozo Chenicheni Chingapezeke Kuti?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Ndani Angathandize Anthu Ovutika?
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 11/1 tsamba 3-6

Chitonthozo kwa Otsenderezedwa

KODI mwaona kuti m’moyo wanu wonse mawu ena abwerezedwa nthaŵi zambiri m’mitu ya nkhani? Kodi mwatopa nako kuŵerenga mawu onga akuti nkhondo, upandu, tsoka, njala, ndi kuvutika? Koma liwu limodzi lakhala likusoŵeka kwambiri m’nkhani. Komabe, limenelo ndi liwu limene limasonyeza kanthu kena kamene anthu afunikira kwambiri. Liwulo ndilo “chitonthozo.”

“Kutonthoza” kumatanthauza “kupereka chilimbikitso ndi chiyembekezo kwa” ndi “kupepuza chisoni kapena mavuto a” wina. Chifukwa cha chipwirikiti chimene dziko laona m’zaka za zana la 20, chiyembekezo ndi kupepuza chisoni zikufunika kwambiri. Zoonadi, ena a ife lerolino tili ndi zofunika za moyo zimene makolo athu sanaziganizepo nkomwe. Zimenezi zatheka makamaka chifukwa cha kupita patsogolo kwa sayansi. Koma sayansi ndi tekinoloji sizinatitonthoze m’lingaliro la kuchotsera anthu zinthu zonse zovutitsa. Kodi zimenezo nziti?

Zaka mazana ambiri zapitazo mwamuna wanzeru Solomo analankhula za chochititsa kuvutika chachikulu pamene anati: “Wina apweteka mnzake pomlamulira.” (Mlaliki 8:9) Sayansi ndi tekinoloji sizinathe kusintha mkhalidwe wa munthu wofuna kulamulira munthu mnzake. M’zaka za zana la 20, zimenezi zadzetsa maulamuliro otsendereza m’maiko ndi nkhondo zowopsa za maiko.

Kuyambira 1914 anthu oposa mamiliyoni chikwi chimodzi aphedwa chifukwa cha nkhondo. Talingalirani za nsautso imene chiŵerengero chimenechi chimadzetsa​—mabanja mamiliyoni ambiri olira maliro amene akufunikira chitonthozo. Ndipo nkhondo zimadzetsanso mavuto ena kuwonjezera pa imfa yachiwawa. Nkhondo yadziko yachiŵiri itatha, panali othaŵa kwawo oposa 12 miliyoni ku Ulaya. M’zaka za posachedwapa, oposa miliyoni imodzi ndi theka anathaŵa madera a nkhondo ku Southeast Asia. Nkhondo kudera la Balkans yakakamiza anthu oposa mamiliyoni aŵiri kuthaŵa kwawo​—nthaŵi zambiri kuti apulumuke “kuyeretsa fuko.”

Ndithudi othaŵa kwawo akufuna chitonthozo, makamaka aja amene amathaŵa kwawo popanda kalikonse kusiyapo katundu amene anganyamule, osadziŵa kumene angapite kapena zimene zili mtsogolo mwawo ndi mwa mabanja awo. Oterowo ali pakati pa anthu otsenderezedwa omvetsa chisoni koposa; iwo afunikira chitonthozo.

Kumadera amene ali ndi mtendere wochulukirapo padziko lapansi, anthu mamiliyoni ambiri ali muukapolo weniweni wa chuma cha dziko. Zoonadi, ena ali ndi chuma chakuthupi chochuluka. Komabe, ochuluka akuvutika tsiku ndi tsiku kuti apeze zofunika za moyo. Ambiri akufunafuna nyumba zabwino. Ochuluka ali paulova. “Dziko,” ikuneneratu motero nyuzipepala ina ya mu Afirika, “likuyang’anizana ndi tsoka la ulova limene silinachitikepo, ndi anthu enanso oposa 1,300,000,000 omafunafuna ntchito podzafika chaka cha 2020.” Ndithudi otsenderezedwa m’zachumawo afunikira “chilimbikitso ndi chiyembekezo”​—chitonthozo.

Chifukwa cha mikhalidwe yovuta, ena amayamba upandu. Ndithudi, zimenezi zimangodzetsa mavuto kwa amene amawavutitsa, ndipo kuchuluka kwa upandu kumawonjezera mzimu wa chitsenderezo. Mutu wa nkhani yaposachedwapa mu The Star, nyuzipepala ya ku Johannesburg, South Africa, unati: “Tsiku m’moyo wa ‘m’dziko lambanda koposa padziko lonse.’” Nkhaniyo inasimba za tsiku lina m’Johannesburg ndi malo apafupi. Tsiku limodzi limenelo, anthu anayi anaphedwa ndipo asanu ndi atatu anaberedwa galimoto zawo. M’dera lina la anthu opeza bwino munamveka nkhani yakuti nyumba 17 zinathyoledwa. Ndiponso, panali kuba ndi mfuti kungapo. Malinga ndi kunena kwa nyuzipepalayo, apolisi anati tsiku limenelo “linali labata pang’ono.” Nkomveka kuti achibale a ophedwa ndi aja amene nyumba zawo zinathyoledwa ndi amene anaberedwa galimoto zawo ali otsenderezeka kwambiri. Afunikira chilimbikitso ndi chiyembekezo​—chitonthozo.

M’maiko ena, muli makolo amene amagulitsa ana awo kukhala mahule. Dziko lina la ku Asia limene alendo oona malo amapitako pa “maulendo achiwerewere” akuti lili ndi mahule mamiliyoni aŵiri, amene ambiri anagulidwa kapena kufwambidwa akali ana. Kodi pali anthu ena otsenderezedwa kwambiri kuposa omvetsa chisoni ameneŵa? Pofotokoza za malonda onyansa ameneŵa, magazini a Time anasimba za msonkhano wa mu 1991 wa magulu a akazi a ku Southeast Asia. Kumeneko, kunayerekezeredwa kuti “akazi 30 miliyoni anali atagulitsidwa padziko lonse kuyambira chapakati pa ma 1970.”

Ndithudi, sikuti ana afunikira kugulitsidwa kukhala mahule kuti azivutika. Ambiri akumenyedwa kapena kugonedwa m’nyumba za iwo eni ndi makolo ndi achibale. Ana otero angakhale osweka mtima kwa nthaŵi yaitali. Indedi, monga anthu otsenderezedwa, iwo afunikira chitonthozo.

Wophunzira Wakale wa Chitsenderezo

Mfumu Solomo anazizwa ndi kukula kwa chitsenderezo pa anthu. Analemba kuti: “Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.”​—Mlaliki 4:1.

Ngati mfumu yanzeruyo inazindikira zaka 3,000 zapitazo kuti otsenderezedwa anafunikira kwambiri wakuwatonthoza, kodi ikananenanji lerolino? Chikhalirechobe, Solomo anadziŵa kuti kulibe munthu wopanda ungwiro, kuphatikizapo iye mwiniyo, amene akanapereka chitonthozo chofunikira kwa anthu. Panafunikira wina woposa wakuti alande mphamvu otsenderezawo. Kodi munthu wotero aliko?

M’Baibulo, Salmo 72 limalankhula za wotonthoza wamkulu wa anthu onse. Salmo limenelo linalembedwa ndi Mfumu Davide, atate wake wa Solomo. Mawu ake apamwamba amati: “Salmo la kwa Solomo.” Umboni umasonyeza kuti linalembedwa ndi Mfumu Davide wokalamba ponena za Iye amene anali kudzaloŵa mpando wake wachifumu. Ameneyu, malinga ndi kunena kwa salmolo, adzachotsa chitsenderezo ndi kubweretsa mpumulo wachikhalire. “Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi. Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja. Ndi . . . kufikira malekezero a dziko lapansi.”​—Salmo 72:7, 8.

Zikuchita ngati kuti, pamene Davide analemba mawu ameneŵa, anali kuganiza za mwana wake Solomo. Koma Solomo anazindikira kuti sakanatha kutumikira anthu ndi mphamvu zake mwanjira yofotokozedwa m’salmo limenelo. Anakwaniritsa mawu a salmolo mwapang’ono chabe ndipo kwa mtundu wa Israyeli, osati kupindulitsa dziko lonse lapansi. Umboni umasonyeza kuti salmo la ulosi louziridwa limeneli linasonya kwa wina woposa Solomo. Kodi ameneyo anali yani? Sakanakhala munthu wina kusiyapo Yesu Kristu yekha.

Pamene mngelo analengeza za kubadwa kwa Yesu, anati: “Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake.” (Luka 1:32) Ndiponso, Yesu anadzitcha “woposa Solomo.” (Luka 11:31) Kuyambira kuuka kwa Yesu kukakhala kudzanja lamanja la Mulungu, iye wakhala kumwamba, malo amene angakwaniritsireko mawu a Salmo 72. Ndiponso, walandira mphamvu ndi ulamuliro kwa Mulungu ya kuthyola goli la anthu otsendereza. (Salmo 2:7-9; Danieli 2:44) Chotero Yesu ndiye adzakwaniritsa mawu a Salmo 72.

Kutsendereza Kudzatha Posachedwa

Kodi zimenezi zikutanthauzanji? Zikutanthauza kuti kumasuka ku kutsendereza kwaumunthu kwa mtundu uliwonse kudzachitika posachedwa. Kuvutika kumene sikunachitikepo ndi chitsenderezo chimene chaoneka m’zaka za zana la 20 lino zinaloseredwa ndi Yesu monga mbali ya chizindikiro chodziŵikitsa “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 24:3) Pakati pa zinthu zina zimene analosera panali zotsatirazi: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Mbali imeneyo ya ulosi inayamba kukwaniritsidwa panthaŵi imene nkhondo yadziko yoyamba inaulika mu 1914. “Chifukwa cha kuchuluka kwa kusayeruzika,” Yesu anawonjezera motero, “chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala.” (Mateyu 24:12) Kusayeruzika ndi kupanda chikondi kwatulutsa mbadwo woipa ndi wotsendereza. Chifukwa chake, nthaŵi iyenera kukhala pafupi yakuti Yesu Kristu aloŵererepo monga Mfumu yatsopano ya dziko lapansi. (Mateyu 24:32-34) Kodi zimenezo zidzatanthauzanji kwa anthu otsenderezedwa amene ali ndi chikhulupiriro mwa Yesu Kristu ndiponso amene akuyang’ana kwa iye monga Wakutonthoza anthu woikidwa ndi Mulungu?

Kuti tipeze yankho la funsolo, tiyeni tiŵerenge mawu enanso a Salmo 72 amene akukwaniritsidwa mwa Kristu Yesu: “Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo [“chitsenderezo,” NW] ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wamtengo pamaso pake.” (Salmo 72:12-14) Chotero Mfumu yoikidwa ndi Mulungu, Yesu Kristu, idzatsimikizira kuti palibe amene akuvutika chifukwa cha kutsenderezedwa. Ili ndi mphamvu ya kuthetsa chisalungamo cha mtundu uliwonse.

‘Zimenezo zikumveka zabwino kwambiri,’ wina angatero, ‘koma bwanji za lero? Kodi ndi chitonthozo chotani chimene chilipo kwa amene akuvutika tsopano lino?’ Kwenikweni, chitonthozo kwa otsenderezedwa chilipo. Nkhani ziŵiri zotsatira m’magazini ano zidzasonyeza mmene anthu mamiliyoni ambiri ayamba kale kupezera chitonthozo mwa kukulitsa unansi wapafupi ndi Mulungu woona, Yehova, ndi Mwana wake wokondedwa, Yesu Kristu. Unansi wotero ungatitonthoze m’nthaŵi zino zotsendereza ndipo ungatsogolere munthu ku moyo wosatha wopanda chitsenderezo. Yesu m’pemphero kwa Mulungu anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”​—Yohane 17:3.

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

Munthu sadzatsendereza mnzake m’dziko latsopano la Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena