Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 11/15 tsamba 5-7
  • Kodi Mulungu Amafuna Kusala Kudya?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Amafuna Kusala Kudya?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Akristu Ayenera Kusala Kudya?
  • Bwanji Nanga za Lent?
  • Pamene Kusala Kudya Kungakhale Kopindulitsa
  • Kodi Kusala Kudya Kumathandiza Munthu Kuyandikira kwa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kusala Kudya?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Kusala Kudya Nkwachikale?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Afunsidwa za Kusala Chakudya
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 11/15 tsamba 5-7

Kodi Mulungu Amafuna Kusala Kudya?

CHILAMULO cha Mulungu choperekedwa kupyolera mwa Mose chinafuna kuti anthu azisala kudya pa nthaŵi imodzi yokha​—pa Tsiku Lotetezera lapachaka. Chilamulocho chinalamula kuti patsikulo Aisrayeli anafunikira ‘kuzunza moyo wawo,’ kumene kumatanthauza kuti anasala kudya. (Levitiko 16:29-31; 23:27; Salmo 35:13) Komabe, kusala kudya kumeneku sikunali mwambo wamba. Kusungidwa kwa Tsiku Lotetezera kunasonkhezera mtundu wa Israyeli pa kuzindikira mowonjezera za mkhalidwe wawo wauchimo ndi kufunikira kwa chiwombolo. Anasalanso kudya patsikulo kuti asonyeze chisoni chifukwa cha machimo awo ndi kulapa pamaso pa Mulungu.

Ngakhale kuti kusala kudya kumeneku ndiko kokha kunali kwalamulo m’Chilamulo cha Mose, Aisrayeli anasala kudya pa nthaŵi zina. (Eksodo 34:28; 1 Samueli 7:6; 2 Mbiri 20:3; Ezara 8:21; Estere 4:3, 16) Kophatikizidwa pa zimenezi kunali kusala kudya kodzifunira monga njira yosonyezera kulapa. Yehova analimbikitsa fuko la Yuda lochimwa kuti: “Munditembenukire ine ndi mtima wanu wonse, ndi kusala, ndi kulira, ndi kuchita maliro.” Sanafunikire kuchita zimenezi modzionetsera, popeza Mulungu akupitiriza kunena kuti: “Ng’ambani mitima yanu, si zovala zanu ayi.”​—Yoweli 2:12-15.

M’kupita kwa nthaŵi, ambiri anasala kudya monga mwambo chabe. Yehova anaipidwa ndi kusala kudya kwachiphamaso kumeneko ndipo anafunsa Aisrayeli achinyengowo kuti: “Kodi kusala kudya koteroko ndiko ndinakusankha? Tsiku lakuvutitsa munthu moyo wake? Kodi ndiko kuŵeramitsa mutu wake monga bango, ndi kuyala chiguduli ndi phulusa pansi pake? Kodi uyesa kumeneko kusala kudya, ndi tsiku lovomerezeka kwa Yehova?” (Yesaya 58:5) M’malo mwa kudzionetsera kusala kudya kwawo, anthu opulupudza ameneŵa anapemphedwa kutulutsa ntchito zoyenerana ndi kulapa.

Kusala kudya kwina kokhazikitsidwa ndi Ayuda kunatsutsidwa ndi Mulungu pachiyambi chake penipeni. Mwachitsanzo, panthaŵi ina fuko la Yuda linasala kudya kanayi pokumbukira zochitika za tsoka zogwirizanitsidwa ndi kuzingidwa ndi kuwonongedwa kwa Yerusalemu m’zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E. (2 Mafumu 25:1-4, 8, 9, 22-26; Zekariya 8:19) Ayuda atamasulidwa ku ukapolo wa ku Babulo, Yehova kupyolera mwa mneneri Zekariya anati: “Muja mukasala . . . zaka izi makumi asanu ndi aŵiri, kodi mukasalira ine, inedi?” Mulungu sanavomereze kusala kudya kumeneku chifukwa chakuti Ayudawo anali kusala kudya ndi kulira maliro pa ziweruzo zimene zinali zochokera kwa Yehova mwiniyo. Anali kusala kudya chifukwa cha tsoka limene linawagwera, osati chifukwa cha tchimo la iwo eni limene linachititsa zimenezo. Atabwezeretsedwa ku dziko lakwawo, inali nthaŵi yawo yakuti akondwere m’malo mwa kumva chisoni ndi zakale.​—Zekariya 7:5.

Kodi Akristu Ayenera Kusala Kudya?

Ngakhale kuti Yesu Kristu sanalamulirepo ophunzira ake kusala kudya, iyeyo ndi otsatira ake anasala kudya pa Tsiku Lotetezera chifukwa chakuti anali pansi pa Chilamulo cha Mose. Ndiponso, ena a ophunzira ake anasala kudya modzifunira pa nthaŵi zina, popeza kuti Yesu sanawalangize kupeŵeratu mchitidwewo. (Machitidwe 13:2, 3; 14:23) Komabe, sanafunikire konse ‘kuipitsa nkhope zawo, kuti aonekere kwa anthu kuti alimkusala kudya.’ (Mateyu 6:16) Anthu ena akanasirira ndi kuyamikira kudzionetsera kwa kupembedza kotero. Komano, Mulungu samakondwera ndi kudzionetsera kotero.​—Mateyu 6:17, 18.

Yesu analankhulanso za kusala kudya kwa otsatira ake pa nthaŵi ya imfa yake. Ponena zimenezo sanali kuyambitsa mwambo wa kusala kudya. M’malo mwake, iye anali kusonyeza za mchitidwe wa chisoni chachikulu chimene akakumana nacho. Atauka, akakhala nawo kachiŵirinso, ndipo sipakakhalanso chifukwa chosalira kudya kwa iwo.​—Luka 5:34, 35.

Chilamulo cha Mose chinatha pamene ‘Kristu anaperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri.’ (Ahebri 9:24-28) Ndipo limodzi ndi kutha kwa Chilamulo, lamulo la kusala kudya pa Tsiku Lotetezera linatha. Motero, kusala kudya kumodzi kokha kwalamulo kotchulidwa m’Baibulo kunatha.

Bwanji Nanga za Lent?

Nangano, kodi kusala kudya kwa Dziko Lachikristu mkati mwa Lent kumachitidwa pa maziko otani? Matchalitchi a Akatolika ndi a Aprotesitanti omwe amavomereza Lent, ngakhale kuti njira zawo zoisungira zimasiyana m’matchalitchi ambiri. Ena amadya chakudya kamodzi patsiku mkati mwa nyengo yonse ya masiku 40 Isitala isanafike. Ena amasala kudya chilichonse pa Ash Wednesday ndi Good Friday pokha. Kwa ena, amafunikira kuti asale nyama, nsomba, mazira, ndi zakudya za mkaka pa Lent.

Lent ikunenedwa kukhala yozikidwa pa kusala kudya kwa Yesu kwa masiku 40 atabatizidwa. Kodi ndiye kuti iyeyo anayambitsa mwambo wofunikira kuutsatira chaka ndi chaka? Kutalitali. Timaona zimenezi pa umboni wakuti Baibulo silimafotokoza za mchitidwe wina uliwonse wotero pakati pa Akristu oyambirira. Lent inasungidwa kwa nthaŵi yoyamba m’zaka za zana lachinayi pambuyo pa Kristu. Monga momwe kulili ndi ziphunzitso zina za Dziko Lachikristu, inatengedwa kwa anthu akunja.

Ngati Lent ili kutsanzira kusala kudya kwa Yesu m’chipululu atabatizidwa, kodi nchifukwa ninji imasungidwa m’masabata oyandikira ku Isitala​—nthaŵi imene amati ndiyo ya kuuka kwake? Yesu sanasale kudya pa masiku oyandikira ku imfa yake. Nkhani za Mauthenga Abwino zimasonyeza kuti iyeyo ndi ophunzira ake anacheza m’nyumba zambiri ndi kudya chakudya ku Betaniya patangotsala masiku oŵerengeka asanafe. Ndipo anadya chakudya cha Paskha pa usikuwo imfa yake isanachitike.​—Mateyu 26:6, 7; Luka 22:15; Yohane 12:2.

Pali kanthu kena koti tiphunzire pa kusala kudya kwa Yesu atabatizidwa. Iyeyo anali kufuna kuyamba utumiki wofunika kwambiri. Kuchirikizidwa kwa uchifumu wa Yehova ndi mtsogolo mwa mtundu wonse wa anthu zinaloŵetsedwamo. Imeneyi inali nthaŵi ya kusinkhasinkha kwakukulu ndi ya kutembenukira mwapemphero kwa Yehova kaamba ka thandizo ndi chitsogozo. Mu nthaŵi imeneyi Yesu moyenerera anasala kudya. Zimenezi zikusonyeza kuti kusala kudya kungakhale kothandiza pamene kuchitidwa ndi cholinga chabwino ndiponso pa chochitika choyenera.​—Yerekezerani ndi Akolose 2:20-23.

Pamene Kusala Kudya Kungakhale Kopindulitsa

Tiyeni tilingalire lerolino za nthaŵi zina pamene wolambira Mulungu angasale kudya. Munthu amene wachita tchimo sangafune kudya kwa nyengo ina. Iye sadzachita zimenezi kuti adzionetsere kwa ena kapena chifukwa cha kupsa mtima ndi uphungu umene walandira. Ndipo, ndithudi, kusala kudya kwenikweniko sikungawongole zinthu ndi Mulungu. Komabe, munthu wolapadi moona mtima amakhala ndi chisoni chachikulu pa kukhumudwitsa Yehova ndipo mwinamwake mabwenzi ndi banja. Kuvutika mtima ndi pemphero laphamphu lopempha chikhululukiro zingamchititse kukhala wosafuna kudya.

Mfumu Davide ya Israyeli inali ndi chochitika chofananacho. Pamene inayang’anizana ndi chiyembekezo cha kutaya mwana wake wamwamuna wobadwa kwa Bateseba, inaika maganizo ake onse pa kuyesayesa kupemphera kwa Yehova kuti aichitire chifundo ponena za mwanayo. Pamene anaika malingaliro ake ndi nyonga m’pempherolo, iye anasala kudya. Moteronso, kudya chakudya kungaonekere kukhala kosayenera pamene munthu ali m’mikhalidwe ina yotsendereza lerolino.​—2 Samueli 12:15-17.

Pangakhalenso nthaŵi zina pamene munthu woopa Mulungu angafune kuika maganizo pa nkhani zina zakuya zauzimu. Kungafunikire kuti afufuze m’Baibulo ndi m’zofalitsa zina zachikristu. Angafune nthaŵi ina yapadera kuti asinkhesinkhe. Mkati mwa nyengo ya kuphunzira kosamalitsa yotero, munthu angasankhe kusacheukitsidwa ndi kudya chakudya.​—Yerekezerani ndi Yeremiya 36:8-10.

Pali zitsanzo za m’Malemba za atumiki a Mulungu amene anasala kudya pamene anafunikira kupanga zosankha zazikulu. M’tsiku la Nehemiya Ayuda anafunikira kupanga lumbiro kwa Yehova, ndipo anayenerera temberero ngati analiswa. Anafunikira kulonjeza za kuchotsa akazi awo achilendo ndi kudzilekanitsa ndi mitundu yowazinga. Asanapange lumbiro limeneli ndiponso mu nthaŵi ya kuulula kuchimwa kwawo, khamu lonse linasala kudya. (Nehemiya 9:1, 38; 10:29, 30) Motero, Mkristu pamene wayang’anizana ndi zosankha zazikulu kwambiri, angaleke kudya kwa nyengo yaifupi.

Kupanga zosankha kwa mabungwe aakulu mumpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba nthaŵi zina kunali kuchitidwa limodzi ndi kusala kudya. Lerolino, akulu a mumpingo oyang’anizana ndi zosankha zovuta kupanga, mwina za nkhani yachiweruzo, angaleke kudya pamene akusinkhasinkha za nkhaniyo.

Kusankha kusala kudya m’mikhalidwe ina kuli chosankha cha munthu mwini. Munthu sayenera kuweruza mnzake pa nkhaniyi. Sitiyenera kufuna ‘kuonekera olungama pamaso pa anthu’; ndiponso sitiyenera kupanga chakudya kukhala chofunika koposa kwakuti chidodometse kusamalira kwathu mathayo ofunika kwambiri. (Mateyu 23:28; Luka 12:22, 23) Ndipo Baibulo limasonyeza kuti Mulungu samatilamulira kusala kudya kapenanso kutiletsa.

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi mumadziŵa chifukwa chake Yesu anasala kudya kwa masiku 40 atabatizidwa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena