Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 12/1 tsamba 2-4
  • Pamene Kugwa Masoka Achilengedwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Kugwa Masoka Achilengedwe
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Ngozi Zadzidzidzi?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • N’chifukwa Chiyani Masoka Achilengedwe Achuluka Chonchi?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Nkhondo ya Munthu ndi Masoka
    Galamukani!—1995
  • Masoka Achilengedwe—Kodi Mulungu Ndiye Amawachititsa?
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 12/1 tsamba 2-4

Pamene Kugwa Masoka Achilengedwe

Accra, Ghana, July 4, 1995: Mvula yambiri imene sinagwepo pazaka pafupifupi 60 inachititsa maliyambwe owopsa. Anthu ngati 200,000 anataya zonse anali nazo, 500,000 sanathe kukhala m’nyumba zawo, ndipo 22 anataya moyo wawo.

San Angelo, Texas, U.S.A., May 28, 1995: Mikuntho ndi matalala inasakaza mzinda wa anthu 90,000 umenewu, ikumawononga zinthu zokwana ngati $120 miliyoni (U.S.).

Kobe, Japan, January 17, 1995: Chivomezi chochitika m’masekondi 20 okha chinapha anthu zikwi zambiri, kuvulaza zikwi makumi ambiri, ndi kusiya zikwi mazana ambiri ali opanda nyumba.

TIKUKHALA m’nthaŵi imene ingatchedwe kuti nyengo ya masoka. Lipoti la United Nations likusonyeza kuti panyengo ya zaka 30 kuyambira 1963-92, chiŵerengero cha anthu ophedwa, kuvulala, kapena kuchotsedwa pamalo awo ndi masoka chinawonjezeka ndi avareji ya 6 peresenti chaka chilichonse. Mkhalidwe woipawo wachititsa UN kutcha ma 1990 kukhala “Zaka Khumi za Maiko Onse za Kuchepetsa Masoka Achilengedwe.”

Zoona, mphamvu ya chilengedwe​—monga mkuntho, kuphulika kwa volokano, kapena chivomezi​—simadzetsa tsoka nthaŵi zonse. Zimachitika mazana ambiri chaka chilichonse popanda kuvulaza anthu. Koma pamene miyoyo yambiri ndi katundu ziwonongeka, moyenera imatchedwa tsoka.

Kuwonjezeka kwa masoka achilengedwe kukuoneka kukhala kosapeŵeka. Buku lakuti Natural Disasters​—Acts of God or Acts of Man? (Masoka Achilengedwe​—Zochita za Mulungu Kapena za Munthu?) likuti: “Anthu akusintha malo awo okhala kuwapanga kukhala angozi kwambiri pa masoka ena, ndipo amachita mwanjira imene imawaika pachiswe kwambiri pangozi zimenezo.” Bukulo likupereka chitsanzo choyerekeza kuti: “Chivomezi chochepa m’shantitauni ya nyumba za njerwa zolemera patherezi locholima chingakhaledi tsoka chifukwa cha zotulukapo zake za imfa ndi kuvutika. Koma kodi tsokalo kwenikweni limachitika chifukwa cha kugwedezeka kwa nthaka kapena chifukwa chakuti anthu akukhala m’nyumba zangozi kwambiri pamalo angozi kwambiri?”

Kwa ophunzira Baibulo, palinso chifukwa china chimene kuwonjezeka kwa masoka achilengedwe sikumawadabwitsira. Pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, Yesu Kristu analosera kuti zinthu zina zimene zidzadziŵikitsa “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano” ndizo “njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti.” (Mateyu 24:3, 6-8) Baibulo linaloseranso kuti mkati mwa “masiku otsiriza,” anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, opanda chikondi chachibadwidwe, ndi osakonda chabwino.a (2 Timoteo 3:1-5) Mikhalidwe imeneyi kaŵirikaŵiri imachititsa munthu kuwononga malo okhala, akumachititsa anthu kukhala kwambiri pangozi ya mphamvu zachilengedwe. Masoka ochititsidwa ndi munthu akhalaponso chifukwa cha kupanda chikondi m’chitaganya chimene ambiri akukhalamo.

Pamene pulaneti lathu likukhala ndi anthu ochulukitsitsa, mpamenenso khalidwe la anthu liika anthu ena pangozi yaikulu, ndiponso pamene chuma cha dziko lapansi chikupitiriza kuwawanyidwa kwambiri, masoka adzapitiriza kuvutitsa munthu. Kupereka thandizo kuli ndi zovuta zake, monga momwe nkhani yotsatira idzasonyezera.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mudziŵe zambiri ponena za chizindikiro cha masiku otsiriza, onani buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, masamba 98-107, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Pamwamba: Information Services Department, Ghana; kulamanja: San Angelo Standard-Times

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

COVER: Maxie Roberts/​Courtesy of THE STATE

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena