Kalasi la 101 la Gileadi—Lachangu Pantchito Zokoma
MLENGI wathu, Yehova Mulungu, ngwachangu pantchito zokoma, momwemonso Mwana wake, Yesu Kristu. Monga wotipatsa chitsanzo, Yesu anasonyeza changu mwa kukwaniritsa ntchito yake yopatsidwa ndi Mulungu, imene inaphatikizapo kudzipereka “yekha m’malo mwa ife, . . . nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pantchito zokoma.” (Tito 2:14) Ziŵalo 48 za kalasi la 101 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower zasonyezadi changu chawo pantchito zokoma. Programu yomaliza maphunziro ya amishonale ameneŵa inachitidwa pa September 7, 1996, ku Malikulu a Maphunziro a Watchtower ku Patterson, New York.
Uphungu Wogwira Ntchito wa Kukhalabe Achangu
Tcheyamani wa programu yomaliza maphunziro anali Carey Barber, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira, wokhala ndi zaka zoposa 70 za mu utumiki wanthaŵi zonse. M’mawu ake oyamba, Mbale Barber analankhula za ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa ya Yesu, amene anali “kuunika kwa dziko lapansi.” (Yohane 8:12) Anasonyeza kuti Yesu sanadzisungire mbali yolemekezeka imeneyo koma analimbikitsa ophunzira ake nawonso kuwalitsa kuunika kwawo. (Mateyu 5:14-16) Mwaŵi wa utumiki umenewu umawonjezera chifuno cha moyo wa Mkristu ndipo umaika thayo lalikulu pa mapeŵa a awo onse amene ‘akuyenda monga ana a kuunika.’—Aefeso 5:8.
Pambuyo pa mawu otsegulira amenewo, Don Adams wa ku Maofesi Aakulu kumalikulu ku Brooklyn anaitanidwa. Analankhula pamutu wakuti “Kupita Patsogolo, Osati Kumbuyo.” Mbale Adams analankhula za Sukulu ya Gileadi imeneyo ndi chifuno chake—kufutukula kulalikira kwa uthenga wabwino ku maiko ena. Analankhula za kupita patsogolo kwa gulu la Mulungu, limene lafalitsa mabuku ofotokoza Baibulo padziko lonse m’zinenero zoposa 300. Buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa mu 1995, lilipo m’zinenero 111 ndipo lalinganizidwa kusindikizidwa m’zinanso zowonjezereka. Lakhala kale chipangizo chothandiza ophunzira atsopano a Yesu kufika pa kudzipatulira ndi ubatizo m’miyezi yoŵerengeka yokha. Choncho amishonale atsopano adzakhala ndi zothandizira kuphunzira Baibulo zatsopano kwambiri kaamba ka ntchito yawo.
Ndiyeno, Lyman Swingle, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira, analankhula pankhani yakuti “Pitirizanibe Kupereka Utumiki Wanu Wopatulika kwa Yehova,” yozikidwa pa Chivumbulutso 7:15. Popeza Yehova iye mwini ali Mulungu wachimwemwe, kumtumikira mosaleka ndiko kumene kumachititsa munthu kukhala wachimwemwe. (1 Timoteo 1:11, NW) Chifukwa cha utumiki wosangalatsa umenewu, khamu lalikulu la anthu ochokera ku mbali zonse za dziko lapansi abwera kudzamlambira. M’zaka zonsezi, awo amene aphunzitsidwa m’Sukulu ya Gileadi akhala ndi phande pa kuthandiza ochuluka a ameneŵa kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha choonadi. Choncho, tili ndi chifukwa chabwino chokhulupirira kuti Yehova adzapitirizabe kudalitsa awo amene tsopano akutumizidwa kukasonkhanitsa enanso a khamu lalikulu lomakulalo.
“Kusonyeza Chimwemwe cha Yehova” inali nkhani yokambidwa ndi Daniel Sydlik, nayenso chiŵalo cha Bungwe Lolamulira. Anasonyeza kuti atumiki onse a Mulungu, kuphatikizapo amishonale atsopanowo, ali ndi mwaŵi wa kuphunzitsa anthu njira ya moyo wosatha ndi njira yokhalira ndi moyo wabwino tsopano. “Kuphunzitsa,” Mbale Sydlik anatero, “ndi ntchito yodzifupa. Zimenezi zimasonyezedwa pankhope za anthu ophunzitsa ndi pankhope ya anthu amene akuphunzira.” (Salmo 16:8-11) Anagwira mawu mmishonale wina wa ku Estonia amene anati, “Tili ndi uthenga wapadera koposa pankhope ya dziko lapansi, ndipo ndi nkhope yathu imene imasonyeza zimenezo.” Kaonekedwe ka nkhope zathu kangachititse makomo ambiri kutseguka ndi kudzutsa chidwi. Anthu amafuna kudziŵa chimene chimachititsa atumiki a Yehova kukhala achimwemwe. “Chotero samalirani nkhope yanu,” analangiza motero Mbale Sydlik. “Anthu amasangalala kuona anthu achimwemwe.”
Ulysses Glass, amene wakhala ndi phande pa kulangiza ophunzira a Gileadi chiyambire kalasi la 12 mu 1949, analankhula ndi omvetsera pamutu wakuti “Dzitetezereni Moleza Mtima.” Kodi kuleza mtima nchiyani? Kumapereka lingaliro la kudikira chinachake modekha, kusonyeza chipiriro poputidwa kapena potsenderezedwa. Munthu woleza mtima amakhalabe wodekha; wosaleza mtima amakhala wamtima wapachala. “Ambiri amaganiza kuti kuleza mtima kumasonyeza chifooko kapena kusadziŵa chochita,” anatero Mbale Glass, koma “kwa Yehova kumasonyeza nyonga ndi chifuno.” (Miyambo 16:32) Kodi kuleza mtima kumadzetsa mapindu otani? “Kuleza mtima panthaŵi ya mkwiyo kudzakuchotserani masiku zana limodzi a chisautso,” mwambi wina wachitchaina umatero. “Kuleza mtima kumawongolera umunthu wa munthu,” Mbale Glass anatero. “Kwenikweni, kumachititsa mikhalidwe ina yabwino kukhala yokhalitsa. Kumachititsa chikhulupiriro kukhala chokhumbika, mtendere kukhala wokhalitsa, ndi chikondi kukhala chosagwedezeka.”
“Ndi mwaŵi kulandira gawo la ntchito kuchokera kwa Yehova Mulungu kudzera m’gulu lake,” anatero Mark Noumair, amene anatumikira monga mmishonale ku Kenya kwa zaka 11 ndipo tsopano ndi mlangizi wa ku Gileadi. Pamene anali kukamba nkhani yamutu wakuti “Mukapanda Chikhulupiriro, Simudzakhazikika,” Mbale Noumair ananena za chitsanzo cha Mfumu Ahazi wa Yuda. Yesaya anatsimikiza mfumuyo za chichirikizo cha Yehova pa gawo lake, koma Ahazi analepherabe kudalira mwa Iye. (Yesaya 7:2-9) Ndiyeno Mbale Noumair anasonyeza kuti amishonale—inde, tonsefe—afunikira kukhala ndi chikhulupiriro mwa Yehova kuti akhazikike m’magawo awo ateokrase. Zitokoso zakutizakuti za gawo laumishonale zimafuna chikhulupiriro cholimba. “Nthaŵi zonse kumbukirani kuti palibe mkhalidwe wangwiro m’dongosolo lino la zinthu,” Mbale Noumair anatero.
Zokumana Nazo Zimene Zimalimbikitsa Ntchito Zachangu
Mkati mwa kosi yawo ya maphunziro a Gileadi, pakutha kwa mlungu kulikonse ophunzira anali kuthera nthaŵi mu utumiki wapoyera, imene idzakhalanso ntchito yawo yaikulu m’magawo awo aumishonale. Wallace Liverance, mmodzi wa aphunzitsi a Gileadi, anafunsa ophunzira 15 amene anasimba zokumana nazo zawo. Ndiyeno Leon Weaver wa m’Komiti ya Dipatimenti Yautumiki ndi Lon Schilling wa m’Komiti Yoyang’anira Beteli anafunsa ziŵalo za m’makomiti a nthambi zochokera ku Afirika ndi Latin America zimene zinasimba zokumana nazo za m’munda wa amishonale ndi zimene zinali ndi uphungu wabwino kwa amishonale omaliza maphunziro awo. Zinasonyeza kuti ku Sierra Leone, pafupifupi 90 peresenti ya awo amene anabatizidwa m’chaka chautumiki cha 1995 anathandizidwa ndi amishonale. Ndi mbiri yabwino chotani nanga ya ntchito yachangu!
Pomalizira pake, Milton Henschel, pulezidenti wa Sosaite, analankhula ndi omvetsera 2,734 pankhani yakuti “Gulu Looneka la Yehova Nlapadera.” Kodi nchiyani chimene chimachititsa gulu la Mulungu kukhala losiyana ndi onse? Si ukulu wake kapena mphamvu yake koma choonadi chakuti limatsogozedwa ndi malamulo ndi zigamulo zachiweruzo zolungama za Mulungu. M’nthaŵi zakale anali anthu a Yehova, mtundu wa Israyeli, amene anapatsidwa zilengezo zake zopatulika zimene zinapanga mtunduwo kukhala wapadera. (Aroma 3:1, 2) Lerolino, gulu la Yehova nlogwirizana pamene likugwira ntchito motsogozedwa ndi Yesu Kristu. (Mateyu 28:19, 20) Ilo likulemera, kukula. Kodi palinso gulu lina padziko lapansi limene Bungwe lake Lolamulira limafufuza m’Mawu a Mulungu, Baibulo, lisanapange zosankha zofunika? M’njira zimenezi ndi zinanso, gulu looneka la Yehova lilidi lapadera.
Programu yosangalatsayo inatha ndi kupereka kwa madiploma ndi kuŵerenga kalata yochokera kwa kalasilo yoyamikira maphunziro apaderawo.
[Bokosi patsamba 22]
Ziŵerengero za Kalasi
Chiŵerengero cha maiko kumene anachokera: 9
Chiŵerengero cha maiko ogaŵiridwa: 12
Chiŵerengero cha ophunzira: 48
Avareji ya zaka zakubadwa: 31.7
Avareji ya zaka m’choonadi: 13.8
Avareji ya zaka mu utumiki wanthaŵi zonse: 9.8
[Chithunzi patsamba 23]
Kalasi la 101 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
M’ndandanda pansipa, mizera ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse.
(1) Swint, H.; Zezenski, A.; Highfield, L.; Mercado, S.; Diehl, A.; Chavez, V.; Smith, J.; Selenius, S. (2) Kurtz, D.; Clark, C.; Leisborn, J.; Mortensen, W.; Bromiley, A.; Toikka, L.; Marten, A.; Smith, D. (3) Zezenski, D.; Bjerregaard, L.; Garafalo, B.; Kaldal, L.; Chavez, E.; Fröding, S.; Khan, R.; Selenius, R. (4) Swint, B.; Bjerregaard, M.; Garafalo, P.; Holmblad, L.; Keyzer, M.; Fröding, T.; Palfreyman, J.; Palfreyman, D. (5) Minguez, L.; Leisborn, M.; Mercado, M.; Kurtz, M.; Diehl, H.; Toikka, J.; Clark, S.; Khan, A. (6) Minguez, F.; Marten, B.; Highfield, L.; Holmblad, B.; Bromiley, K.; Kaldal, H.; Mortensen, P.; Keyzer, R.