Choonadi Ponena za Yesu
PAKUONEKA kuti pali ziphunzitso ndi malingaliro ambirimbiri ponena za amene anali Yesu ndi zimene anakwaniritsa. Koma bwanji ponena za Baibulo ilo leni? Kodi limatiuzanji ponena za Yesu Kristu?
Zimene Baibulo Limanena
Pamene muŵerenga Baibulo mosamalitsa, mudzapeza choonadi ichi:
◻ Yesu ndiye Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, wobadwa woyamba wachilengedwe chonse.—Yohane 3:16; Akolose 1:15.
◻ Zoposa zaka zikwi ziŵiri zapitazo, Mulungu anasamutsira moyo wa Yesu m’chibaliro cha namwali wachiyuda kuti abadwe monga munthu.—Mateyu 1:18; Yohane 1:14.
◻ Yesu sanali munthu wabwino chabe. M’mbali zonse anali chinyezimiro chokhulupirika cha umunthu wabwino kwambiri wa Atate wake, Yehova Mulungu.—Yohane 14:9, 10; Ahebri 1:3.
◻ Mkati mwa utumiki wake wa padziko lapansi, Yesu mwachikondi anasamalira zosoŵa za anthu oponderezedwa. Mozizwitsa anachiritsa odwala ndiponso anaukitsa akufa.—Mateyu 11:4-6; Yohane 11:5-45.
◻ Yesu analengeza kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo chiyembekezo chokha cha anthu ovutika, ndipo anaphunzitsa ophunzira ake kuti apitirize ntchitoyi ya kulalikira.—Mateyu 4:17; 10:5-7; 28:19, 20.
◻ Pa Nisan 14 (ku ma April 1), 33 C.E., Yesu anagwidwa, kuzengedwa mlandu, kuweruzidwa, ndi kuphedwa atamnamizira mlandu woukira boma.—Mateyu 26:18-20, 48–27:50.
◻ Imfa ya Yesu ndiyo dipo, lomasula anthu amene amakhulupirira ku mkhalidwe wawo wauchimo chotero ikumatsegula njira ya ku moyo wosatha kwa onse amene amamkhulupirira.—Aroma 3:23, 24; 1 Yohane 2:2.
◻ Pa Nisan 16, Yesu anaukitsidwa, ndipo posapita nthaŵi anakwera kubwerera kumwamba kukalipira kwa Atate wake mtengo wa dipo wa moyo wake waumunthu wangwiro.—Marko 16:1-8; Luka 24:50-53; Machitidwe 1:6-9.
◻ Monga Mfumu yoikidwa ya Yehova, Yesu woukitsidwayo ali ndi ulamuliro wonse wa kuchita chifuno choyamba cha Mulungu kaamba ka munthu.—Yesaya 9:6, 7; Luka 1:32, 33.
Chotero, Baibulo limasonyeza kuti Yesu ndiye kiyi yofunika koposa pakukwaniritsidwa kwa zifuno za Mulungu. Koma kodi mungatsimikize motani kuti ameneyu ndiye Yesu weniweniyo—Yesu wa m’mbiri, yemwe anabadwira ku Betelehemu ndi kuyenda padziko lapansili zaka pafupifupi 2,000 zapitazo?
Maziko a Chidaliro
Zikayiko zambiri zingachotsedwepo mwa kungoŵerenga Malemba Achigiriki Achikristu ndi malingaliro omasuka. Mukachita zimenezo, mudzapeza kuti nkhani ya m’Baibulo si mafotokozedwe osatsatirika a zochitika, monga momwe nthanthi zilili. M’malo mwake, maina, nthaŵi yeniyeni, ndi malo enieni zimatchulidwa. (Mwachitsanzo, onani Luka 3:1, 2.) Ndiponso, ophunzira a Yesu akusonyezedwa kukhala oona mtima mwapadera, othembeka kwakuti woŵerenga amakhala ndi chidaliro. Olemba sanabise zolakwa za aliyense—ngakhale za iwo eni—chifukwa chofuna kulemba mbiri yokhulupirika. Inde, mudzaona kuti Baibulo lili ndi choonadi.—Mateyu 14:28-31; 16:21-23; 26:56, 69-75; Marko 9:33, 34; Agalatiya 2:11-14; 2 Petro 1:16.
Kombe pali zambiri. Zofukulidwa m’mabwinja mobwerezabwereza zatsimikiza mbiri ya m’Baibulo. Mwachitsanzo, ngati mwakacheza ku Israel Museum ku Jerusalem, mudzaona mwala umene uli ndi zolembedwa zimene zimatchula Pontiyo Pilato. Zofukulidwa m’mabwinja zina zimatsimikiza kuti Lusaniyo ndi Sergio Paulo, amene Baibulo limatchula, anali anthu enieni m’malo mwa zopeka za Akristu oyambirira. Zochitika zotchulidwa m’Malemba Achigiriki Achikristu (Chipangano Chatsopano) zatsimikizidwa nthaŵi zambirimbiri m’zolembedwa za olemba akale, kuphatikizapo Juvenal, Tacitus, Seneca, Suetonius, Pliny Wamng’ono, Lucian, Celsus, ndi wolemba mbiri wachiyuda Josephus.a
Nkhani zomwe zili m’Malemba Achigiriki Achikristu zinalandiridwa mosavuta ndi zikwi za amene analiko m’zaka za zana loyamba. Ngakhale adani a Chikristu sanakane choonadi ponena za zimene anthu anati Yesu anazinena ndi kuzichita. Ponena za kuthekera kwakuti umunthu wa Yesu unakometseredwa ndi ophunzira ake pambuyo pa imfa yake, Profesa F. F. Bruce akuti: “Kupeka mawu ndi zochita za Yesu m’zaka zoyambirirazo, pamene ambiri a ophunzira Ake analipo, amene anali kukumbukira zimene zinachitika ndi zimene sizinachitike, sikukanakhala kwapafupi choncho monga momwe olemba ena akulingalirira. . . . Ophunzira sanalole kusalongosoka (ngakhale kusintha dala choonadi sitingakutchule nkomwe), kumene kukanavumbulidwa mwamsanga ndi aja omwe akanakhala ofunitsitsa kutero.”
Chifukwa Chake Sakhulupirira
Ngakhale zili choncho, akatswiri ena akukayikabe. Pamene kuli kwakuti amalingalira kuti mbiri ya m’Baibulo njopeka, iwo mwachangu amafufuza zolembedwa za Apocrypha ndi kuzilandira kukhala zodalirika! Chifukwa ninji? Mwachionekere, mbiri ya Baibulo ili ndi zinthu zimene anthu ambiri ophunzira amakono samafuna kukhulupirira.
Mu Union Bible Companion yake yofalitsidwa mu 1871, S. Austin Allibone anapereka chitokoso kwa okayikira. Iye analemba kuti: “Funsani aliyense amene amanena kuti akukayikira choonadi cha mbiri ya Mauthenga Abwino chifukwa chimene ali nacho chokhulupirira kuti Kaisara anafera mu Capitol, kapena kuti Mfumu Charlemagne anaikidwa kukhala Mfumu ya Kumadzulo ndi Papa Leo III. mu 800? . . . Timakhulupirira zonenedwa zonse . . . pa amuna ameneŵa; ndipo timatero chifukwa chakuti tili ndi umboni wa m’mbiri wa choonadi chake. . . . Ngati pali ena amene akanabe kukhulupirira, umboni wonga uwu utaperekedwa, timawasiya monga ouma khosi mopusa kapena mbuli zotheratu ntchito. Ndiyeno tidzati bwanji za aja amene, mosasamala kanthu za umboni wambirimbiri umene tsopano watulutsidwa wa kudalirika kwa Malemba Oyera, anena kuti sanakhutire? . . . Safuna kukhulupirira chinthu chimene chitsitsa kunyada kwawo, ndi chimene chingawakakamize kusintha moyo wawo.”
Inde, okayikira ena ali ndi zifukwa zobisika zokanira Malemba Achigiriki Achikristu. Vuto limene amapeza si la kudalirika kwake koma la miyezo yake. Mwachitsanzo, ponena za otsatira ake Yesu anati: “Sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.” (Yohane 17:14) Komabe, ambiri amene amati ndi Akristu ngoloŵerera kwambiri m’nkhani zandale za dzikoli, ngakhale kuloŵa m’nkhondo zokhetsa mwazi. M’malo mogwirizana ndi miyezo ya Baibulo, anthu ambiri amafuna kuti Baibulo ligwirizane ndi miyezo yawoyawo.
Talingaliraninso za nkhani ya khalidwe. Yesu anapereka uphungu wamphamvu ku mpingo wa ku Tiyatira chifukwa cha kulekerera chigololo. “Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima,” anawauza motero, “ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.”b (Chivumbulutso 2:18-23) Komabe, kodi si zoona kuti ambiri amene amadzitcha Akristu amanyalanyaza miyezo ya khalidwe? Iwo amakonda kukana zimene Yesu ananena m’malo mwa kukana khalidwe lawo loipa.
Posafuna kulandira Yesu wa m’Baibulo, akatswiri apanga Yesu wawowawo. Iwo akhala ndi liwongo la kupeka nthanthi, mlandu umene akupatsa olemba Mauthenga Abwino. Iwo amakhulupirira mbali za moyo wa Yesu zimene akufuna kulandira, kukana zina zonse, ndi kuwonjezera zinthu zingapo zopeka iwo. Kwenikweni, munthu wawo wanzeru woyenda peyupeyu kapena munthu wofuna kusintha makhalidwe a anthu sindiye Yesu wa m’mbiri amene amati akumfunafuna; m’malo mwake, iye ali wongopeka wa m’malingaliro onyada a akatsŵiri.
Kupeza Yesu Weniweni
Yesu anafunitsitsa kutsegula mitima ya aja amene moona mtima anali ndi njala ya choonadi ndi chilungamo. (Mateyu 5:3, 6; 13:10-15) Oterowo amalabadira chiitano cha Yesu chakuti: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”—Mateyu 11:28-30.
Yesu weniweni sangapezedwe m’mabuku olembedwa ndi akatswiri amakono; ndiponso sangapezedwe m’matchalitchi a Dziko Lachikristu, amene akhala mobadwira miyambo ya anthu. Mungapeze Yesu wa m’mbiri m’kope lanu la Baibulo. Kodi mukufuna kuphunzira zambiri ponena za iye? Mboni za Yehova zingakonde kukuthandizani kuchita motero.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mudziŵe zambiri onani Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, mutu 5, masamba 55-70, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b M’Baibulo, impso nthaŵi zina zimaimira maganizo ndi malingaliro amkatikati a munthu.
[Bokosi patsamba 6]
ZAKA MAZANA ZA KUSULIZA
Kusuliza Malemba Achigiriki Achikristu kunayambika zaka zoposa 200 zapitazo, pamene wafilosofi wachijeremani Hermann Samuel Reimarus (1694-1768) ananena kuti: “Tili ndi chifukwa chabwino cha kusiyanitsiratu ziphunzitso za Atumwi m’zolemba zawo ndi zimene Yesu Iyemwini m’nthaŵi Yake ya moyo ananena ndi kuphunzitsa.” Chiyambire nthaŵi ya Reimarus, akatswiri ambiri aphunzitsidwa kulingalira mofananamo.
Buku lakuti The Real Jesus limanena kuti akatswiri ambiri akale sanadziyese kukhala ampatuko. M’malo mwake, “ankadziyesa Akristu enieni pokhala atamasuka ku nsinga za ziphunzitso za tchalitchi ndi mwambo.” Maphunziro apamwamba ofufuza Baibulo, iwo analingalira motero, anali “mtundu woyera wa Chikristu.”
Choonadi chomvetsa chisoni ndicho chakuti Dziko Lachikristu lakhala malo okulirako miyambo ya anthu. Ziphunzitso za sou yosafa, Utatu, ndi helo wamoto zili chabe ziphunzitso zina zimene zili zotsutsana ndi Baibulo. Koma olemba Malemba Achigiriki Achikristu sindiwo anachititsa kupotoza choonadi kumeneku. M’malo mwake, analimbana ndi chiyambi cha ziphunzitso zonyenga chapakati pa zaka za zana loyamba, pamene Paulo analemba kuti mpatuko pakati pa odzitcha Akristu unali ‘utayambadi kuchita.’ (2 Atesalonika 2:3, 7) Tili ndi chidaliro chakuti zimene zili m’Malemba Achigiriki Achikristu ndizo zolembedwa za choonadi cha m’mbiri ndi cha ziphunzitso.
[Bokosi patsamba 7]
KODI MAUTHENGA ABWINO ANALEMBEDWA LITI?
Ofufuza Chipangano Chatsopano ambiri amalimbikira kunena kuti Mauthenga Abwino analembedwa patapita nthaŵi yaitali kuchokera pamene zinthu zimene amafotokoza zinachitika ndipo motero ayenera kuti si olongosoka.
Komabe, umboni umasonyeza kuti Mateyu, Marko, ndi Luka analembedwa isanafike nthaŵiyo. Zilembo zamunsi m’makope ena a malembo a pamanja a Mateyu zimasonyeza kuti kope lake loyamba linalembedwa kale mu 41 C.E. Luka akuoneka kuti analembedwa pakati pa 56 ndi 58 C.E., popeza kuti buku la Machitidwe (mwinamwake lotsirizidwa mu 61 C.E.) limasonyeza kuti wolemba wake, Luka, anali atalemba kale ‘mawu ake oyamba,’ Uthenga Wabwinowo. (Machitidwe 1:1) Uthenga Wabwino wa Marko umalingaliridwa kuti unalembedwera ku Roma mkati mwa kumangidwa koyamba kapena kwachiŵiri kwa mtumwi Paulo—mwinamwake pakati pa 60 ndi 65 C.E.
Profesa Craig L. Blomberg amavomerezana ndi madeti akale a Mauthenga Abwino amenewo. Iye akusonyeza kuti ngakhale pamene tiwonjezerapo Uthenga Wabwino wa Yohane, umene unalembedwa kumapeto kwa zaka za zana loyamba, “timakhalabe pafupi kwambiri ndi zochitika zenizenizo kuposa ndi mbiri zakale zambiri za moyo wa anthu ena. Mwachitsanzo, olemba za moyo wa Alexander Wamkulu aŵiri akale koposa, Arrian ndi Plutarch, analemba nkhanizo patapita zaka zoposa mazana anayi pambuyo pa imfa ya Alexander mu 323 B.C., komabe olemba mbiri pafupifupi onse amaziona kukhala zodalirika. Nthanthi zopeka ponena za moyo wa Alexander zinayambadi m’kupita kwa nthaŵi, koma kwenikweni zimenezo zinangochitika m’zaka mazana ambiri pambuyo pa olemba aŵiriwa.” Ndithudi mbali za m’Malemba Achigiriki Achikristu zokhala ndi mbiri nzolandirika monga momwe mbiri za kudziko zilili.
[Chithunzi patsamba 8]
Anthu onse m’dziko lapansi la Paradaiso likudzalo adzakhala ndi chimwemwe chachikulu