Kodi Amithenga Enieni a Mtendere Ndani?
PA May 31, 1996, ofalitsa nkhani analengeza uthenga umene unamveka ngati wamtendere. Dzulo lake, chilengezo chalamulo chinaperekedwa chotsimikizira kuti Benjamin Netanyahu, amene anali pafupi kukhala nduna yaikulu ya Israel, anali “woloŵetsedwa kwambiri m’kupitiriza makambitsirano a mtendere, mtendere ndi chisungiko, pakati pa boma la Israel ndi maiko oyandikana naye onse, kuphatikizapo Apalestina.”
Kusankhidwa kwa Netanyahu kofalitsidwa kwambiri kumeneko kunachititsa ambiri kuphanaphana ndi mtima ngati mtendere ku Middle East udzakhala weniweni. Ngati nchoncho, kodi mitundu ina ingachitenso chimodzimodzi, kuiŵala mikangano yawo?
Komabe, kulonjeza mtendere nkwapafupi kuposa kuubweretsa. Podziŵa zimenezi, ambiri ankakayikira. Monga momwe mtolankhani Hemi Shalev ananenera, “theka la anthu ku Israel tsopano akuganiza kuti ali pafupi kuwonjoka, ndipo theka linanso akukhulupirira kuti agwidwa mumkhalidwe wozunza wopanda pothaŵira.” Mwachidule, iye anati: “Ena akukondwa; ena akulira.”
Ndi mmene zoyesayesa za munthu za kubweretsa mtendere zimakhalira. Kupambana kwa mtsogoleri mmodzi ndi anthu ake kumatanthauza kugonjetsedwa kwa gulu lotsutsa. Kusakhutira kumachititsa kugwiritsidwa mwala, ndipo kugwiritsidwa mwala, kaŵirikaŵiri kumachititsa chipanduko. Kaya ndi ku Middle East, Latin America, Eastern Europe, kapena kwina kulikonse—zoyesayesa za anthu za kudzetsa mtendere zimakhala zachiphamaso kwambiri.
Mtendere Weniweni Wayandikira!
Nthaŵi pamene mtendere ku Middle East unali nkhani yaikulu kwambiri panyuzi, uthenga winanso wa mtendere unamveka. Umenewu sunali nkhani yandale yofalitsidwa kwambiri; ndipo sunalinso pangano la mtendere pakati pa mitundu. M’malo mwake, uthenga umenewu unalengeza mtendere umene udzabwera kokha kudzera mwa Ufumu wa Mulungu. Kodi uthenga umenewu unamvekera kuti? Pamisonkhano Yachigawo ya “Amithenga a Mtendere Waumulungu” yoposa 1,900 yochitidwa ndi Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse mu 1996/97.
Pamisonkhano imeneyi anafotokoza kuti palibe boma la anthu limene lingabweretse mtendere weniweni ndi chisungiko. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti zimenezi zidzafuna kuchotsapo zinthu zimene zimatisoŵetsa mtendere tsiku ndi tsiku. Mtendere weniweni umatanthauza kudzuka mmaŵa ulionse mosaopa nkhondo kapena chiwawa. Umatanthauza kutheratu kwa upandu, kusakhalanso ndi maloko pazitseko zathu, kusaopanso kuyenda m’makwalala, mabanja kusaswekanso. Ndi boma lanji padziko lapansi limene lingachite zonse zimenezo? Ndithudi, ndi boma lanji padziko lapansi limene lingayese ngakhale kuulonjeza?
Komabe, Ufumu wa Mulungu ungabweretse zinthu zimenezi ndipo udzatero. Baibulo limalonjeza kuti: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Zimenezo zidzabweretsa mpumulo waukulu chotani nanga kwa anthu ovutika!
Lonjezo la Yehova Mulungu si loto chabe. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita? Kapena kulankhula, osachitsimikiza?” (Numeri 23:19, 20) Inde, zimene Mulungu walonjeza zidzachitika—ndi kudalitsa onsewo omwe aima kumbali yake.
Amithenga a Mtendere a Mulungu
Mboni za Yehova nzodziŵika kwambiri chifukwa cha kulalikira kwawo mokangalika Ufumu wa Mulungu. Chaka chilichonse, zonse pamodzi zimathera maola oposa 1,000,000,000 akumagaŵana ndi ena uthenga wotonthoza wa Baibulo. Kumeneku nkukwaniritsa mawu a Yesu akuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Uthenga umene Mboni zimabweretsa ulidi ‘uthenga wabwino,’ chifukwa umalengeza Ufumu wakumwamba wa Mulungu monga chiyembekezo chokha cha anthu. Ndipo ulidi chiyembekezo chamtsogolo cholimba chotani nanga!
Ngakhale tsopano Ufumu wa Mulungu ukupanga chomangira chenicheni cha mtendere ndi chikondi chapaubale pakati pa nzika zake. Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Mboni za Yehova zikuyesayesa kutsatira chiyeneretso choyamba chimenechi cha Chikristu choona. Ndiye chifukwa chake, wawo ndi ubale wochititsa chidwi wogwirizanitsa Ayuda ndi Aluya, Akroatiya ndi Asebu, Ahutu ndi Atutsi. Mtendere uwu umene anthu ochuluka amangoulota Mboni za Yehova miyandamiyanda kuzungulira dziko lonse lapansi zili nawo tsopano.
Chilimbikitso cha kupitirizabe kutsatira mapulinsipulo a Baibulo ndi kupitirizabe kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu chinaperekedwa paprogramu ya Msonkhano Wachigawo wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu.” Tikukupemphani kuŵerenga lipoti lotsatira la msonkhano wosonkhezera wa masiku atatu umene mamiliyoni asangalala nawo.