Enoke Wopanda Mantha Zivute Zitani
KWA munthu wabwino, zinali nthaŵi zoipitsitsa. Kupanda umulungu kunafalikira padziko lonse lapansi. Panali kunyonyotsoka kopitirizabe kwa makhalidwe a anthu. Ndithudi, posapita nthaŵi kunadzanenedwa kuti: “Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.”—Genesis 6:5.
Enoke, munthu wachisanu ndi chiŵiri m’mzera wa Adamu, analimba mtima pokhala wosiyana. Anaima nji m’chilungamo mosasamala kanthu za zotsatirapo zake. Uthenga wa Enoke unawazunza kwambiri ochimwa opanda umulunguwo kwakuti anatsimikiza mtima za kumupha, ndipo Yehova yekha ndiye akanatha kumthandiza.—Yuda 14, 15.
Enoke ndi Nkhani ya Chilengedwe Chonse
Kalekale Enoke asanabadwe, panabuka nkhani ya uchifumu waponseponse. Kodi Mulungu anali woyenera kulamulira? Satana Mdyerekezi anati ayi. Anati zolengedwa zanzeru zikanakhala bwinopo ngati zikanadziimira pazokha mosadalira chitsogozo cha Mulungu. Satana anayesa kusonkhanitsa maumboni ochirikiza chigomeko chake chotsutsa Yehova Mulungu mwa kukokera anthu kumbali yake mwa machenjera ndi chinyengo. Adamu, mkazi wake Hava, ndi mwana wawo woyamba, Kaini, amadziŵika ndi kupulupudza kwawo potenga mbali ya Satana mwa kusankha kudzilamulira m’malo mwa kulamuliridwa ndi Mulungu. Anthu aŵiri oyambawo anatero mwa kudya chipatso chimene Mulungu analetsa, ndipo Kaini anatero mwa kupha mwadala mbale wake wolungamayo, Abele.—Genesis 3:4-6; 4:8.
Molimba mtima Abele anaima nji kumbali ya Yehova. Popeza kuti umphumphu wa Abele unachirikiza kulambira koyera, mosakaikira Satana anasangalala kuona Kaini akumkwiyira ndi ukali wambanda. Kuyambira pa nthaŵiyo kumkabe mtsogolo, Satana wakhala akugwiritsira ntchito “kuopa imfa” monga chida chake choopsezera. Amafuna kuika mantha mu mtima mwa aliyense wofuna kulambira Mulungu woona.—Ahebri 2:14, 15; Yohane 8:44; 1 Yohane 3:12.
Mmene Enoke amadzabadwa, lingaliro la Satana lakuti anthu sadzalemekeza ulamuliro wa Yehova linaonekera kukhala litachirikizidwa bwino. Abele anali atafa, ndipo chitsanzo chake chokhulupirika sichinali kutsanziridwa. Komabe, Enoke anakhaladi wosiyana. Anali ndi maziko olimba achikhulupiriro pakuti anali kuzidziŵa bwinobwino zimene zinachitika m’munda wa Edene.a Ha, mmene ayenera kukhala ataukonda nanga ulosi wa Yehova wosonyeza kuti Mbewu yolonjezedwayo idzawononga Satana ndi njira zake zamachenjera!—Genesis 3:15.
Ali ndi chiyembekezo chimenechi patsogolo pake, Enoke sanaopsezedwe ndi imfa yotchuka ya Abele yosonkhezeredwa ndi Mdyerekezi. M’malo mwake, anapitirizabe kuyenda ndi Yehova, akumatsatira njira yachilungamo kwa moyo wake wonse. Enoke anakhala wolekana ndi dziko, akumapeŵa mzimu wake wakudzigangira.—Genesis 5:23, 24.
Ndiponso, Enoke molimba mtima analankhula ndi kumveketsa kuti ntchito zoipa za Mdyerekezi zidzalephera. Mosonkhezeredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito, Enoke analosera ponena za oipa kuti: “Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi, kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zawo zonse zosapembedza, zimene anazichita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye.”—Yuda 14, 15.
Chifukwa cha zilengezo zopanda mantha za Enoke, mtumwi Paulo polembera Akristu achihebri, anamphatikizapo pa “mtambo waukulu wa mboni” zimene zinapereka chitsanzo chopambana cha chikhulupiriro chogwira ntchito.b (Ahebri 11:5; 12:1) Monga munthu wachikhulupiriro, Enoke anapirirabe m’njira yaumphumphu kwa zaka zoposa 300. (Genesis 5:22) Kukhulupirika kwa Enoke kuyenera kukhala kutawanyong’onya chotani nanga adani a Mulungu kumwamba ndi padziko lapansi! Ulosi wa Enoke wopyoza mtimawo unanyanyula udani wa Satana, koma unadzetsa chitetezo cha Yehova.
Mulungu Anamtenga Enoke—Motani?
Yehova sanalole Satana kapena atumiki ake apadziko lapansi kupha Enoke. M’malo mwake, nkhani youziridwayo imati: “Mulungu anamtenga.” (Genesis 5:24) Mtumwi Paulo akufotokoza nkhaniyo motere: “Ndi chikhulupiriro Enoke anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu.”—Ahebri 11:5.
Kodi ndi motani mmene Enoke ‘anatengedwera kuti angaone imfa’? Kapena monga momwe matembenuzidwe a R. A. Knox amanenera, kodi ndi motani mmene Enoke “anatengedwera popanda kukumana ndi imfa”? Mulungu anauthetsa moyo wa Enoke mwa mtendere, akumpeŵetsa zoŵaŵa za imfa kaya mwa matenda kapena mwa chiwawa kwa adani ake. Inde, Yehova anafupikitsa moyo wa Enoke pa usinkhu wa zaka 365—ali wachichepere ndithu poyerekezera ndi ena a m’nthaŵi yake.
Kodi ndi motani mmene Enoke ‘anachitidwira umboni kuti anakondweretsa Mulungu’? Unali umboni wotani womwe anali nawo? Kuchita ngati Mulungu anamgoneka Enoke tulo, monga mmene mtumwi Paulo “anakwatulidwa” kapena kutengedwa, mwachionekere akumaona masomphenya a paradaiso wauzimu wamtsogolo wa mpingo wachikristu. (2 Akorinto 12:3, 4) Umboni wakuti Enoke anali kukondweretsa Mulungu ungakhale utaphatikizapo zideruderu zamasomphenya a paradaiso wapadziko lapansi mtsogolomu mmene onse okhala ndi moyo adzachirikiza ulamuliro wa Mulungu. Kapena kunali pamene Enoke anali chipenyere masomphenya osangalatsa ameneŵa pamene Mulungu anamtenga mu imfa yopanda ululu kuti agone kufikira tsiku lachiukiriro chake. Kukuoneka kuti monga momwe zinachitikira kwa Mose, Yehova anachotsa thupi la Enoke, pakuti “sanapezeka.”—Ahebri 11:5; Deuteronomo 34:5, 6; Yuda 9.
Ulosi Ukwaniritsidwa
Lero, Mboni za Yehova zikulengeza tanthauzo la ulosi wa Enoke. Mwa Malemba, zimasonyeza mmene udzakwaniritsidwira pamene Mulungu adzawononga osapembedza mtsogolo posachedwapa. (2 Atesalonika 1:6-10) Uthenga wawo umachititsa anthu kusawakonda chifukwa ndi wosiyana kwambiri ndi malingaliro ndi zolinga zadziko lino. Chitsutso chomwe amakumana nacho sichimawadabwitsa, chifukwa Yesu anachenjeza atsatiri ake kuti: “Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa.”—Mateyu 10:22; Yohane 17:14.
Komabe, mofanana ndi Enoke, Akristu amakono atsimikizidwa kuti adzalanditsidwa kwa adani awo potsirizira pake. Mtumwi Petro analemba kuti: “Ambuye adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe.” (2 Petro 2:9) Mulungu angaone kukhala koyenera kuthetsa vuto kapena mkhalidwe wopereka chiyeso. Chizunzo chingathe. Komabe, ngati sizitero, iye amadziŵa ‘kuikanso populumukirapo’ kuti anthu ake athe kupirira ziyeso zawo mwachipambano. Yehova amaperekanso ngakhale “ukulu woposa wamphamvu” pamene kuli kofunikira.—1 Akorinto 10:13; 2 Akorinto 4:7.
Monga “wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye,” Yehova adzadalitsanso atumiki ake okhulupirika ndi moyo wosatha. (Ahebri 11:6) Kwa unyinji wa iwo, umenewu udzakhala moyo wosatha padziko lapansi laparadaiso. Mofanana ndi Enoke, tiyenitu tilengeze mopanda mantha uthenga wa Mulungu. Tiyeni titero mwa chikhulupiriro, zivute zitani.
[Mawu a M’munsi]
a Adamu anali wazaka 622 pamene Enoke anabadwa. Enoke anakhala ndi moyo zaka 57 pambuyo pa imfa ya Adamu. Chotero, anakhala ndi moyo limodzi kwa nthaŵi yaitali ndithu.
b Matembenuzidwe akuti “mboni” pa Ahebri 12:1 amachokera ku liwu lachigiriki marʹtys. Malinga ndi Wuest’s Word Studies From the Greek New Testament, liwu limeneli limatanthauza “amene amachitira umboni, kapena amene angachitire umboni, chimene waona, kapena kumva kapena chimene amadziŵa mwanjira ina iliyonse.” Christian words, lolembedwa ndi Nigel Turner, limati liwu limeneli limatanthauza amene amalankhula “zodzionera yekha . . . , ndipo motsimikizira ponena za choonadi ndi malingaliro.”
[Bokosi patsamba 30]
Dzina la Mulungu Lichitidwa Mwano
Pafupifupi zaka mazana anayi Enoke asanakhaleko, mdzukulu wa Adamu Enosi anabadwa. “Pomwepo anthu anayamba kutchula dzina la Yehova,” amatero Genesis 4:26. Akatswiri ena achinenero chachihebri amakhulupirira kuti mavesi ameneŵa anayenera kunena motere: “anatchula mwamwano” dzina la Mulungu kapena, “pomwepo mwano unayamba.” Ponena za nyengo imeneyo m’mbiri, Jerusalem Targum imati: “Anayamba kumalakwa m’masiku a mbadwo umenewo, akumadzipangira mafano, natcha mafano awowo dzina la Mawu a Ambuye.”
M’nthaŵi ya Enosi kugwiritsira ntchito molakwa dzina la Yehova kunali kofala. Nkotheka kuti anthu anali kumadzitcha dzina la Mulungu kapena kutcha anthu ena kupyolera mwa amene anali kunamizira kufikira Yehova Mulungu polambira. Kapena angakhale anali kutchula mafano ndi dzina la Mulungu. M’njira iliyonse, Satana Mdyerekezi anakola fuko la anthu ndi msampha wakulambira mafano. Mmene Enoke amadzabadwa, kulambira koona kunali patalipatali. Aliyense wonga Enoke, yemwe anakhala m’choonadi ndi kuchilalikira, anali wodedwa ndipo anali kuzunzidwa.—Yerekezerani ndi Mateyu 5:11, 12.
[Bokosi patsamba 31]
Kodi Enoke Anapita Kumwamba?
“Ndi chikhulupiriro Enoke anatengedwa kuti angaone imfa.” Potembenuza chigawo chimenechi cha Ahebri 11:5, ma Baibulo ena amasonyeza kuti Enoke sanafe kwenikweni. Mwa chitsanzo, A new Translation of the Bible, la James Moffat, limati: “Kunali mwa chikhulupiriro mmene Enoke anatengedwera kumwamba kotero kuti sanafe konse.”
Komabe, zaka 3,000 pambuyo pa tsiku la Enoke, Yesu Kristu anati: “Kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu.” (Yohane 3:13) The New English Bible limati: “Palibe aliyense anakwerapo kumwamba kusiyapo iye amene anatsika kumwamba, Mwana wa Munthuyo.” Pamene Yesu ananena mawu amenewo, ngakhale iye anali asanakwere kumwamba.—Yerekezerani ndi Luka 7:28.
Mtumwi Paulo anatero kuti Enoke ndi ena amene ali mtambo waukulu wa mboni zoyambirira Chikristu chisanakhale ‘onse anamwalira’ ndipo “sanalandira lonjezanolo.” (Ahebri 11:13, 39) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti anthu onse, kuphatikizapo Enoke, analandira choloŵa chauchimo kuchokera kwa Adamu. (Salmo 51:5; Aroma 5:12) Njira yokha yachipulumutso ndiyo kupyolera mwa nsembe ya dipo ya Kristu Yesu. (Machitidwe 4:12; 1 Yohane 2:1, 2) M’tsiku la Enoke dipo limenelo linali lisanalipiridwe. Chotero, Enoke sanapite kumwamba, koma ali chigonere mtulo taimfa kudikira chiukiriro padziko lapansi.—Yohane 5:28, 29.
[Mawu a Chithunzi patsamba 29]
Yotengedwa mu Illustrirte Pracht - Bibel/Heilige Schrift des Alten und Neuen Testaments, nach der deutschen Uebersetzung D. Martin Luther’s